Nyama za M’nkhalango Zomazimiririka za ku Africa—Kodi Zidzapulumuka?
MULI mmawa, ndipo zonse ziri za bata m’chigwa cha mu Africa. Njovu yaimuna ikudya pakati pa zitsamba. Ikumakhotetsa chitamba chake chachitalicho mozungulira zomera zazing’ono ndi zophukira, izizula izo, kuchotsako dothi mwa kugwedeza, ndi kuziika izo mkamwa mwake, kuzitafuna mobwerezabwereza; iyo iridi pa njira yake bwino lomwe yakudya mapaundi ake a tsiku ndi tsiku 300 (136 kg) a zomera. Iyo siizidziwa izo, koma yawona zaka 40 zikupita pa chidikha cha udzu chimenechi; nyanga yake yaikuluyo imawunikira msinkhu wake. Iyo ingapitirize bwino lomwe kubala ana kwa zaka zina khumi ndi kukhala ndi moyo kwa zaka zina khumi zoposa pamenepo.
Kulira kwa mfuti kumvekera, kukumasokoneza bata la mmawamo.
Chipolopolo chibwera kuchokera ku mfuti yamphamvu kwambiri; icho chilowerera mozama cha m’mbali mwa yaimunayo. Iyo ibangula mowirikiza, kudzandira, ndipo iyesa kuimirira mosokonezeka, koma zipolopolo zochulukira zibwerabe. Iyo potsirizira pake igwada pa mawondo ake ndi kugwa pansi. Galimoto laling’ono liyandikira, ndipo unyinji wa amuna adzikonzekeretsa mwachikondwerero ku ntchito. Iwo asakaza nkhope ya njovu kuti atenge minyanga kuchokera ku mizu yake m’mutumo ndi kuizula iyo mwamsanga. Mkati mwa mphindi zoŵerengeka akupha nyama popanda lamulowo apita. Bata libwereranso ku chigwacho. Njovu yakale yaimuna yomwe pa nthaŵi imodzi inali yodzimva tsopano iri kokha mapaundi 14,000 (6,300 kg) a nyama, yomwe yangosiidwa kuti iwole.
Mwachisoni, iyi iri kutalitali ndi kukhala nkhani ya apo ndi apo. M’chenicheni, kuyerekeza pa ziŵerengero za njovu zophedwa chaka ndi chaka ndi akupha nyama popanda lamulo zimasiyanasiyana kuchokera pa 45,000 kufika ku 400,000. Ofufuza nyama za m’nkhalango asonyeza kuti chiŵerengero chonse pamodzi cha njovu za mu Africa chazimiririka kuchokera ku mamiliyoni ake akale kufika ku chifupifupi nyama 900,000. Ngati kupha nyama kopanda lamulo kupitirizabe pa mlingo wake wamakono, chiŵerengero chimenecho chidzafupikitsidwa kufika ku theka mkati mwa zaka khumi zikudzazo. Pamene zazimuna zachikulire, kapena zokhala ndi minyanga, zicheperachepera mowonjezereka, zazimuna zazing’ono zowonjezereka ndipo ngakhale zazikazi zimaphedwa.
Nchifukwa ninji kusakaza koteroko? Malonda a minyanga a ku Africa odzetsa $50 miliyoni pa chaka, limodzinso ndi kupezeka kopepuka kwa zida zodzigwirira ntchito pa zokha, kwapangitsa njovu kukhala m’nkhole wosakhoza kudzichinjiriza kaamba ka akupha nyama popanda lamulo.
Zipembere za mu Africa ziridi ngakhale mu ngozi yaikulu. Mwa kusakidwa kwakukulu kupyola m’zana lapita, chiŵerengero chawo chatsika kale ku chifupifupi mazana chikwi chimodzi mu mbadwo umodzi wapita. Lerolino, izo ziri kokha 11,000 zozingidwa. Pakati pa 1972 ndi 1978, zipembere 2,580 zinaphedwa chaka chirichonse; chakuti odziŵa za umoyo wanyama ambiri akuwopa kuti zidzatheratu podzafika chaka cha 2000.
Nchifukwa ninji kupha koteroko? Kachiŵirinso ndalama zimatenga malo apamwamba mu yankho: nyanga ya chipembere ingabweretse zoposa $5,000 pa paundi limodzi ($11,000 pa kg) imagulitsidwa m’masitolo. Imagulitsidwa monga ufa mu Far East monse monga mankhwala a kuŵaŵa kwa mutu ndi malungo, ngakhale kuti zofufuza zimasonyeza kuti izo sizigwira ntchito ku matendawa. Msika waukulu ndithu kaamba ka nyangazo uli mu North Yemen, kumene anyamata achatsopano olemera amalakalaka kukhala ndi nkhalamanja wa pa phwando wokhala ndi chogwirira chotchuka cha nyanga ya chipembere—ngakhale kuti nyanga ya ng’ombe ingakhoze kutumikira chifunocho bwino lomwe.
Kutali m’miyala yotentha ya pansi pa nthaka ya m’mapiri a Rwanda ndi Zaire, ndi nkhalango yapafupi ya Bwindi ya ku Uganda, mumakhala nyani wamkulu wa m’mapiri. Chiŵerengero chawo chazimiririka kumlingo wa kutheratu. Pakali pano kokha chifupifupi 400 a iwo akalipobe mu nkhalango. Nchifukwa ninji? Iwo amaphedwa ndi akupha nyama popanda lamulo kaamba ka zizindikiro za chipambano. Mutu wa nyani wamkulu ungagulitsidwe pa msika wamba ku utali wa $1,200 kaamba ka kukometsera khoma, dzanja lake pa $600 kaamba ka kuligwiritsira ntchito monga chotaira phulusa la ndudu!
Nyama ya liŵiro koposa pa dziko lonse, cheetah, yalingaliridwanso kukhala ikuyandikira ku kusakhalako. Kokha 20,000 ya izo zikalipobe m’nkhalango. Asayansi kachiŵirinso amachenjeza kuti chiŵerengero chochepa chimenechi chiri m’ngozi m’kubalana kwake, kotero kuti chiŵerengero cha kufa kwa zachichepere chiri chokulira pakati pa a cheetah. Chotero, iwo ali ngakhale nkhole ku zodidikiza za kuchepa kwa malo awo okhalako.
M’chenicheni, kufunika kwa kusiya malo kaamba ka nyama za mu Africa kumabweretsa vuto lowopsya. Mwachitsanzo, njovu ya m’nkhalango yomapita ndi kudya pa munda waung’ono ingakhoze kuwopsyeza mopepukira umoyo weniweni wa mlimi. Ndipo komabe, ngati njovu zambiri zasungidwa mkati mwa malire osungirako nyama kapena mochinga kumene sizingakhoze kuwopsyeza mbewu za alimi, izo zingakhoze mwamsanga kutembenuza nkhalango ya mosungira nyamazo kukhala mtunda wa udzu wokhawokha kaamba ka mkhalidwe wawo wosiyanasiyana wa kadyedwe. Popeza kuti njovuzo sizingakhoze kupita patsogolo, nkhalangozo sizimakhala ndi mwaŵi wa kukulanso.
Osunga nyama, ochinjiriza nyama, ndi asayansi moyamikirika alimbana ndi mavuto amenewa ndipo akhala ndi kupita patsogolo kwinakwake ku kuyamikiridwa kwawo. Mu South Africa, mwachitsanzo, chipembere choyera posachedwapa chinafikira kokha ku chiŵerengero cha chifupifupi zana limodzi. Njira zokhutiritsa zinatengedwa kuchinjiriza izo, chotero tsopano izo zikufika ku chiŵerengero cha chifupifupi 3,000.
Ndipo komabe vuto likalipobe osati kokha ku chipembere cha mu Africa ndi nyama za m’nkhalango za mu Africa koma, m’malomwake, ku nyama zonse za m’nkhalango pa dziko lonse. Ponse paŵiri njovu ndi chipembere mu Asia ziri m’ngozi yokulira ya kusakhalako kuposa ndi mmene ziliri nyama zina za mu Africa zomwe tangokambitsirana pano. Zosokoneza kwambirinso, maphunziro ena amasonyeza kuti mtundu umodzi wonse wa moyo wa nyama umafika pa kusakhalako tsiku lirilonse. Ripoti lina linadziŵitsa kuti pakati pa tsopano ndi kothera kwa zana lino, nyama zidzatha pa mlingo wa imodzi pa ora limodzi!
Kodi tingakhoze kuchita ndi kusowa kwa mtunduwu? Kodi msika wa zosowa za munthu, kaya weniweni kapena wongoyerekezera, ungakhoze mothekera kulungamitsa kuwononga koipa koteroko?