Kupeza ‘Zokwawa Zazikulu’ Zakale
PAMENE muimirira pamphepete pa chigwa cha Mtsinje wa Red Deer, chakum’mwera kwa tauni ya Drumheller mu Alberta, Canada, mukuima pamphepete pa maiko aŵiri osiyana. Kumalekezero a maso, kulikonse kumene mungayang’ane, kuli minda yosatha ya tirigu m’madambo a Alberta. Koma mutayang’ana kunsi kwa materezi ku chigwa chowuma chosabala, alendo angalingalire za dziko lina lokhala kutali ndi dziko lawo—dziko la madinosaur.
M’chigwa chimenechi, chokhala ndi zigwa za mitundu yosiyanasiyana ya miyalo ya matanthwe okochezedwa ndi madzi, mafupa mazanamazana a dinosaur anafukulidwa. Anthu ena m’derali amatcha chigwa chosabalachi kukhala “maiko oipa.” Koma alendo, achichepere ndi achikulire mofananamo, amadzazidwa ndi chidwi pamene awona umboni wa zinthu zakale za nyama zina zosangalatsa kwambiri zimene zinakhalapo pa dziko lapansi.
Kupeza Ma“dinosaur”
Isanafike 1824, madinosaur anali osadziŵika kwa anthu. M’chaka chimenecho mafupa a mitundu yosiyanasiyana ya zokwawa zakale anafukulidwa mu England. Katswiri wa zinthu zakale wa ku Britain Richard Owen anazitcha nyama zimenezi kukhala Dinosauria, kuchokera ku mawu aŵiri Achigriki deinos ndi sauros, otanthauza “buluzi wowopsya.” Dzinalo lidakagwiritsiridwabe ntchito mofala mpaka lerolino, ngakhale kuti madinosaur alidi zokwawa, iwo siabuluzi.
Chiyambire 1824, zinthu zakale za dinosaur zapezedwa pa kontinenti iriyonse. Cholembedwa cha zinthu zakale, zosiyidwa m’miyalo ya matanthwe opangidwa ndi madzi, kapena matanthwe apansi pamadzi, chimasonyeza kuti panali unyinji waukulu ndithu ndi mitundu yosiyanasiyana ya dinosaur pa nthaŵi inayake m’mbiri ya dziko lapansi yotchedwa Nyengo ya Dinosaurs. Ena anapanga malo awo okhala pamtunda, pamene kulikwakuti ena anakhala m’matenjetenje. Mwinamwake ena anakhaladi m’madzi, mofananadi ndi mvuu zamasiku ano.
Unyinji waukulu wa zotsalira za dinosaur—kuphatikizapo umboni wosakhala wamafupa monga ngati mopita mapazi—zafukulidwa mu Great Central Plain of North America. Madambo a pakati pa Alberta atulutsa zotsalira zambiri za dinosaur, kuphatikizapo chifupifupi mafupa athunthu okwanira 500. M’ma 1920, ofufuza anapeza mafupa a dinosaur m’Chipululu cha Gobi cha pakati pa Asia. M’ma 1940 ofufuza a ku Soviet mu Mongolia anapeza mafupa a dinosaur a utali wa mamita 12.
Mu 1986 asayansi a ku Argentina anapeza zinthu zakale za dinosaur yodya zomera mu Antarctica. Kufikira pa nthaŵiyo, Antarctica inali malo aakulu a dziko kumene zinthu zakale za dinosaur zinali zisanapezedwe. Isanafike nthaŵi imeneyo, wofufuza wa ku America anapeza mafupa a dinosaur pa North Slope ya Alaska. Mkati mwa zaka zana limodzi zapitazi, mafupa a dinosaur afukulidwa m’malo ambiri kotero kuti chatsimikizirika kuti madinosaur anali ofalikira nthaŵi yakale kwambiri.
Kodi Anakhalako Liti?
Madinosaur anachita mbali yaikulu m’moyo wawo pa dziko lapansi mkati mwa nyengo yawo. Koma kenaka anatha. Miyalo ya matanthwe yokhala ndi zinthu zakale za anthu mokhazikika imawoneka pamwamba pa miyalo yokhala ndi zinthu zakale za dinosaur. Chifukwa cha zimenezi, akatswiri asayansi mwachisawawa amamaliza kuti anthu anabwera pa dziko lapansi mochedwerako.
Mogwirizana ndi zimenezi bukhu lakuti Palaeontology, lolembedwa ndi James Scott, likulongosola kuti: “Ngakhale mitundu yoyambirira kwenikweni ya Homo sapiens (munthu) inakhalako patapita nthaŵi yaitali pambuyo pa kuzimiririka kwa madinosaur . . . Pambuyo pa kupendekeka (kochitika ndi kuyenda kwa dziko lapansi), matanthwe okhala ndi zinthu zakale za anthu amawoneka mokhazikika pamwamba pa aja osunga mafupa a zokwawa zazikulu za banja la dinosaur ndipo chotero zomalizirazi ziri za nyengo yakale kwambiri kuposa zotsalira za anthu.”
M’chigwa cha Mtsinje wa Red Deer, muli muyalo wa thanthwe lopangidwa ndi madzi lokhala ndi mafupa a dinosaur. Pamwamba pa zimenezi, pali muyalo wodera wabafuta umene umatsatira kayendedwe ka m’mbali mwa chitunda. Pamwamba pa muyalo wodera wabafutawo pali muyalo wa mwala wamchere wokhala ndi zinthu zakale za mafern, kusonyeza nyengo yotentha. Pamwamba pa zimenezi, pali miyalo ingapo ya malasha. Pamwamba penipeni pa m’mbali mwa chitundamo pali miyalo yokakala ya dothi. Mulibe mafupa alionse a dinosaur m’miyalo yapamwambayo.
Bukhu lakuti A Vanished World: The Dinosaurs of Western Canada likulongosola kuti “mitundu 11 yonse yaikulu ya madinosaur . . . inaleka kukhalako mkati mwa kumadzulo chifupifupi pa nthaŵi imodzi.” Zimenezi, ndi zenizeni zakuti mafupa a anthu sanapezedwe pamodzi ndi mafupa a dinosaur, ziri zifukwa zimene akatswiri asayansi ambiri amamaliza kuti Nyengo ya Dinosaurs inatha anthu asanakhaleko.
Komabe, chiyenera kudziŵidwa kuti pali ena amene amanena kuti mafupa a dinosaur ndi mafupa a anthu samapezeka pamodzi chifukwa chakuti madinosaur sanakhale m’madera mokhala anthu. Malingaliro osiyana oterowo amasonyeza kuti cholembedwa cha zinthu zakale sichimaulula zinsinsi zake mopepuka ndikuti palibe aliyense pa dziko lapansi lerolino amene amadziŵadi mayankho onse.
Mikhalidwe
Akatswiri asayansi amaliza kuti kum’mawa kwa Mapiri a Rocky a ku North America, kudali nyanja yaikulu yosaya. Nyanja imeneyi inali ya utali wa makilomita mazanamazana, ikumafutukuka kuchokera ku Arctic Ocean kufika ku Mexico. Mphepete mwa gombe lotambalala munali nkhalango zamadambo, zokhala ndi udzu. Zinthu zakale zimasonyeza kuti mitundu yambiri ya madinosaur inachuluka m’makhazikitsidwe achilengedwe ameneŵa. Edmontosaurus, dinosaur yokhala ndi mulomo wofanana ndi wa bakha ya utali wa chifupifupi mamita 9, mwachidziŵikire inkayenda m’gulu monga ng’ombe m’matenjetenjewo. Mapazi osindikiza osungidwa bwino a zala zitatu ndi zinthu zam’mimba zokwiriridwa pansi zinatsogoza akatswiri a zinthu zakale ku mapeto ameneŵa.
Umboni wina umalingalira kuti madinosaur ena anasonyeza zizoloŵezi za mayanjano. Mosakaikira anayendera pamodzi, mwinamwake m’magulu a zana limodzi kapena kuposapo. Kupezedwa kwa miyalo yotsatizana ya zisa ndi mazira m’malo amodzi kumasonyeza kuti madinosaur ena anabwerera ku malo omanga chisa amodzimodziwo chaka ndi chaka. Zotsalira za mafupa za madinosaur aang’ono pafupi ndi zisazo ‘zimasonyeza mwamphamvu mkhalidwe wa kuyanjana kwa achichepere ndiponso kumasonyeza kuthekera kwa kusamalira achichepere kwaukholo pambuyo pa kuswa kwawo,’ ikulongosola tero Scientific American.
Umboni wa zinthu zakale umasonyeza kuti panali ziŵerengero zazikulu ndi mitundu ya madinosaur. Koma kodi izo zinawoneka ngati chiyani? Kodi zonse zinali zowopsya, zilombo zazikulu—“abuluzi owopsya”? Kodi nchifukwa ninji zinawoneka kuzimiririka mwadzidzidzi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Smithsonian Institution, Washington, D.C.: Photo Number 43494