Mawonekedwe ndi Maukulu Osiyana A Madinosaur
PA MITUNDU yonse ya zamoyo imene tsopano inasoloka, mwinamwake madinosaur adzutsa kulingalira kwa anthu. Kaŵiriŵiri madinosaur amalingaliridwa kukhala anali aakulu ndiponso owopsya. Pamene dzinalo linatengedwa choyamba kuchokera ku mawu Achigriki otanthauza “buluzi wowopsya,” analingaliridwa kukhala anali aakulu mowopsya chifukwa chakuti zinthu zakale za dinosaur zodziŵika pa nthaŵiyo zinali zazikulu.
Mitundu ina ya madinosaur inalidi yaikulu ndipo inawonekadi yowopsya, mwachidziŵikire ikumalemera kuwirikiza nthaŵi khumi kuposa njovu yaikulu ya ku Africa. Komabe, mkati mwa zaka makumi, akatswiri a zinthu zakale afukula mafupa a madinosaur ambiri aang’ono. Ena ali a ukulu wa bulu, ndipo ena siakulu kuposa nkhuku! Tiyeni tiwone zina za zokwawa zakale zosangalatsa zimenezi.
Zokwawa Zimene Zimawuluka
Mtundu wina wozizwitsa wa zokwawa zakale unali pterosaur (“buluzi wamapiko”), womwe umaphatikizapo pterodactyl (“chala chamapiko”). Koma zimenezi sizinali madinosaur, ndiponso sizinali mbalame. Izo zinali zokwawa zowuluka ndipo zinaikidwa m’gulu la zokwawa zina monga madinosaur ndi ng’ona. Zina za izo zinali ndi mapiko a utali wa mamita 8. Lina lopezedwa mu Texas mu 1975 limasonyeza kuti ena anali ndi mapiko a utali wa mamita oposa 15. Mwinamwake izi zinali nyama zazikulu koposa zimene zinkauluka.
Pamene kuli kwakuti mapterosaur anali ndi manu, chigaza, m’chuuno, ndi mapazi akumbuyo a zokwawa, iwo sanafanane konse ndi madinosaur okwawa. Ndipo pamene kuli kwakuti anawoneka kukhala mbalame zokhala ndi mapiko olimba ozoloŵera kuuluka, anali osiyana kwambiri. Mofanana ndi mbalame, mapterosaur anali ndi mafupa okhala ndi mphako ndi mfundo zokhoza kuthifuka zoŵerengeka m’mapiko ndi akakolo. Komabe, mapiko a mbalame amagwiritsira ntchito nthenga osati mtsempha monga mmene zinaliri ndi mapterosaur. Ndipo chala chachinayi cha pterosaur chinafutukuka kuchilikiza mtsempha wa phiko. M’mbalame chala chachiŵiri chiri m’chilikizi weniweni wa phiko.
Ma“ornithischian”
Maornithischian (“okhala ndi thako ngati la mbalame”) anali gulu limodzi la magulu aŵiri achisawawa a madinosaur ogawidwa mogwiritsira ntchito mpangidwe wa matako awo. Aja a m’gululi anali ndi mpangidwe wa thako wofanana ndi wa mbalame, komabe, lalikulu koposa. Ena anali aang’ono mu ukulu wonse, ena aakulu. Iguanodon inafikira utali wa mamita 9. Mafupa a mitundu ingapo ya mahadrosaur amasonyeza chigama chonga mlomo wa bakha chapamwamba ndi chapansi, chokhala ndi manu ambirimbiri. Mwachiwonekere mahadrosaur anali amiyendo iŵiri, oyenda kapena kuthamanga ndi miyendo iŵiri. Ena a iwo anafika utali wa mamita 10.
Mastegosaur anali gulu la maornithischian limene linali ndi mipeni yamafupa yaikulu yokhala m’dongosolo kumsana kwawo. Iwo ankayenda ndi miyendo yonse inayi ndipo anali a utali wa mamita 6, ndi msinkhu wa mamita 2.4 m’matako. Posachedwapa kwenikweni, zalingaliridwa kuti mipeni yakumbuyo yamafupayo inatumikira osati kokha monga chotetezera komanso monga dongosolo loziziritsa thupi lawo. Miyendo yakumbuyo inali yolemera ndipo yokhala ngati ya njovu, pamene miyendo yakutsogolo inali yaing’ono, kupangitsa mutu waung’onowo kukhala pafupi kukhudza pansi. Mchirawo unali ndi zisonga zazitali, zamafupa zoyambira kumapeto.
Gulu lomalizira la maornithischian—lofalikira pa dziko lonse lapansi—linali lija la maceratopsian, kapena madinosaur okhala ndi nyanga. Iwo anali ndi utali wa mamita 1.8 kufika ku mamita 8 m’litali. Osasiyana ndi chipembere cha ku Africa, “akasinja” okhala ndi zida ameneŵa anali ndi chigaza chofutukuka kupanga chochinjiriza cha khosi. Gulu la nyanga zitatu, matriceratop, linali lofala m’dziko la dinosaur. Nyanga ziŵiri zokhala pamwamba pa maso zinkakula kufika utali wa mamita 0.9. Zinthu zakale zingapo za matriceratop zapezedwa kuchokera m’chigwa cha Mtsinje wa Red Deer mu Alberta.
Ma“saurischian”—Zimphona za “Dinosaur”
Gulu lina lofala la madinosaur limadziŵika monga masaurischian (“okhala ndi matako ngati a buluzi”), okhala ndi mpangidwe wa matako wofanana ndi a buluzi, ngakhale kuti, kachiŵirinso, aakulu kwambiri. Iwo amayenerera lingaliro lofala la madinosaur: aakulu ndipo owopsya. Pakati pa zimenezi panali apatosaurus (kalelo yotchedwa brontosaurus), dinosaur yodya zomera imene inkayenda ndi miyendo inayi. Inkafika utali wa mamita 21 ndipo inali ndi kulemera koyerekezedwa kukhala matani 30. Madinosaur ameneŵa afukulidwa mu North America ndi Europe.
Mofananamo diplodocus yaikulu inali yofanana kwambiri ndi njoka, yokhala ndi khosi lalitali ndi mchira koma yokhala ndi miyendo. Iyo iri dinosaur yaitali koposa yodziŵika, ikumafutukuka ku utali wa mamita 27, ngakhale kuti imalemera pang’ono kusiyana ndi apatosaurus. Yofukulidwa mu North America, diplodocus inali ndi mphuno pamwamba pa mutu wake, kuitheketsa kumiza chifupifupi mutu wake wonse m’madzi.
Ndiyeno pali brachiosaurus. Mafupa opezedwa mu Tanzania anafika utali wa mamita 21. Kukuyerekezedwa kuti ena analemera matani 85. Anali ndi msinkhu wa mamita 12, okhala ndi thupi limene linapendekekera pansi cha kumchira, mofanana ndi nswala.
Mu 1985 msana wofukulidwa pansi wa ukulu wachilendo unafukulidwa mu New Mexico, U.S.A. Woyang’anira wa malo osungira zinthu zakale wa pa New Mexico Museum of Natural History anaitcha iyo kukhala seismosaurus. Nyamayo inayerekezedwa kukhala ya utali wa mamita makumi atatu ndi kulemera kwa chifupifupi matani zana limodzi!
Tyrannosaurus rex (“buluzi wachifumu wotsendereza”) wowoneka wowopsya anali wa msinkhu wa chifupifupi mamita 3 m’matako. Pamene anaimirira, akanafika msinkhu wa mamita 6. Anali wa utali wa mamita 12. Mutu wake unafika mamita 1.2 m’litali, ndipo kamwa yake yaikulu inali yokonzekeretsedwa ndi manu ambiri ombulungirako a utali wa masentimita 15. Miyendo yakumbuyo inali yofanana ndi ya njovu, pamene kuli kwakuti miyendo yakutsogolo inali yaing’ono kwambiri. Mchira waukulu wofanana ndi wa buluzi unakweza kumbuyoko. M’malo moyenda chowongoka, zapezedwa kuti matyrannosaur ankalambalitsa matupi awo, kumachilikiza kulemera kwa thupi lawo ndi mchira wawo wautali.
Kusintha kwa Chochitika
Nsonga yakuti madinosaur amene anakhalako mochulukira pa dziko lapansi, m’malo amakedzana anazimiririka kalekale, iri yowonekera ku cholembedwa cha zinthu zakale. Koma zolengedwa zozizwitsa zimenezi, limodzi ndi mitundu ina yosaŵerengeka ya nyama ndi zomera, inasoloka. Ponena za nthaŵi imene zimenezi zinachitika, katswiri wa zinthu zakale D. A. Russell akulongosola kuti: “Mwatsoka, njira zimene ziripo zoyesera kukhalako kwa zochitika zimene zinachitika kale kwambiri nzosatsimikizika kwenikweni.”
Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa madinosaur? Kodi kuwoneka kwawo kwamwadzidzidzi ndi kusoloka kwawo kwamwadzidzidzi kumatanthauzanji? Kodi madinosaur amadzutsa chikaikiro cha malamulo ena ozikika a chisinthiko cha Darwin? Tidzasanthula mafunso amenewo m’nkhani yotsatira.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mamita 9
Mamita 6
Mamita 3