Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 2/8 tsamba 9-11
  • Kodi Nchiyani Chimene Chinachitika kwa Madinosaur?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimene Chinachitika kwa Madinosaur?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthanthi ya Kusoloka Kwamwadzidzidzi
  • Kuika Madeti a Ma“dinosaur”
  • Cholembedwa cha Genesis ndi Ma“dinosaur”
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Nyama Zotchedwa Madainaso?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kupeza ‘Zokwawa Zazikulu’ Zakale
    Galamukani!—1990
  • Mawonekedwe ndi Maukulu Osiyana A Madinosaur
    Galamukani!—1990
  • Kodi Zamoyo Zonse Zinachokera ku Chinthu Chimodzi?
    Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 2/8 tsamba 9-11

Kodi Nchiyani Chimene Chinachitika kwa Madinosaur?

“PALAEONTOLOGY iri phunziro la zinthu zakale, ndipo zinthu zakale ziri zotsalira za zamoyo zochokera ku nyengo yakale.” Koma monga mmene katswiri wina wa zinthu zakale ananenera, iyo iri “sayansi yokaikiritsa ndi ya malingaliro aumwini koposa.” Izi nzachiwonekere polingalira za madinosaur. Pondandalitsa zikaikiro zina zonena za zimene zinachitika kwa iwo, katswiri wasayansi wa ku Princeton G. L. Jepson analongosola kuti:

“Alembi okhala ndi luso losiyana alingalira kuti madinosaur anazimiririka chifukwa cha kunyonyotsoka kwa nyengo ya kutentha ndi kuzizira . . . kapena kuti zakudya zinatero. . . . Alembi ena apatsa mlandu matenda, tizilombo, . . . kusintha kwa kudidikiza kapena mkhalidwe wa mlengalenga, magasi apaizoni, fumbi la kuphulika kwa matanthwe otentha, kuchulukitsitsa kwa okosijeni wochokera ku zomera, mameteorite, macomet, kukokoloka kwa magene kochititsidwa ndi zilombo zazing’ono zakudya mazira, . . . cheza cha chilengedwe, kusintha kwa malo ozungulira a Dziko Lapansi, zigumula, kusintha kwa kontinenti, . . . kuphwetsedwa kwa matenjetenje ndi nyanja, malo a dzuwa.”—The Riddle of the Dinosaur.

Nchachiwonekere kuchokera ku zikaikiro zimenezo kuti akatswiri asayansi sali okhoza kuyankha motsimikiza funso lakuti: Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa madinosaur?

Nthanthi ya Kusoloka Kwamwadzidzidzi

Nthanthi yaposachedwapa inapangidwa ndi gulu la tate ndi mwana, Luis ndi Walter Alvarez. Kunja kwa tauni ya Gubbio pakati pa Italy, Walter Alvarez anapeza muyalo wopyapyala wachilendo, wa makande akatondo wokhala pakati pa miyalo ya matanthwe a mwala wa njereza. Muyalo wapansi wa mwala wa njereza unali ndi zinthu zakale zambiri. Muyalo wapamwamba unalibe zinthu zakale, kutsogoza akatswiri ofukula pansi kumaliza kuti moyo unazimiririka mwadzidzidzi ndipo kuti muyalo wopyapyala, wa makande a katondo unali wogwirizana ndi kusolokako.

Kusanthula kunavumbula kuti makandewo anali odzaza ndi iridium (chitsulo), wodzaza ndi nthaŵi 30 kuposa kuchuluka kwachibadwa kopezeka m’matanthwe. Iwo anadziŵa kuti kuchuluka koteroko kwa chinthu chachilendo chimenechi kungabwere kuchokera ku maziko a dziko kapena magwero a kunja kwa dziko lapansi. Iwo anamaliza kuti chitsulo chotchedwa iridium chimenecho chinaikidwa ndi asteroid yaikulu imene inagunda dziko lapansi, kupangitsa kusoloka kwamwadzidzidzi kwa madinosaur.

Pambuyo pa kupezedwa kwa makande odzaza ndi iridium pa Gubbio, zoikidwa zofananazo zinapezedwa m’mbali zina za dziko. Kodi izi zinagwirizana ndi nthanthi ya asteroid? Akatswiri asayansi ena akukaikirabe. Koma monga mmene bukhu lakuti The Riddle of the Dinosaur likudziŵitsira, nthanthi ya Alvarez inawonjezera “chotupitsa chatsopano ku phunziro la kusoloka ndi chisinthiko.” Ndipo katswiri wa zinthu zakale Stephen Jay Gould akuvomereza kuti ingathetse “kufunika kwa mpikisano pakati pa magulu a zolengedwa.”

Pothirira ndemanga pa nthanthi yatsopano imeneyi ndi kusoloka kwamwadzidzidzi kwa madinosaur, wolemba zasayansi wina anavomereza kuti: “Iwo angagwedeze maziko a sayansi ya zamoyo ya chisinthiko ndi kukaikira lingaliro laposachedwapa la kusankha kwachibadwa.”

Katswiri wasayansi wa pa University ya Arizona David Jablonski akumaliza kuti ‘kwa zomera zambiri ndi zinyama, kusoloka kunali kwadzidzidzi ndipo kwapadera mwa njira inayake. Kusoloka kwaunyinji sikuli chabe zotulukapo zounjikika za kufa kwa pang’onopang’ono. Panachitika chinachake chachilendo.’ Mmenemo ndi mmenenso ziriri ndi madinosaur. Kuwoneka kwawo kwamwadzidzidzi ndi kuzimiririka kumatsutsana ndi lingaliro lofala la chisinthiko cha pang’onopang’ono.

Kuika Madeti a Ma“dinosaur”

Mafupa a dinosaur amapezeka mokhazikika m’miyalo yapansi ya dziko kuposa mafupa a anthu, kutsogoza ambiri kumaliza kuti ali a nyengo yakale kwambiri. Akatswiri ofukula pansi amatcha nthaŵi imeneyi kukhala nyengo ya Mesozoic ndi kuigawagawa m’magulu otchedwa nyengo za Cretaceous, Jurassic, ndi Triassic. Mikhalidwe ya nthaŵi yogwiritsiridwa ntchito m’nyengo zimenezi iri m’magulu a zaka mamiliyoni makumi angapo. Koma kodi zimenezi zakhazikitsidwa motsimikizirika?

Njira ina imene ikugwiritsiridwa ntchito kuyesera msinkhu wa zinthu zakale ikutchedwa radiocarbon dating. Njira yoika madeti imeneyi imagwiritsira ntchito liŵiro la kuola kwa radioactive carbon kuyambira pa kufa kwa chamoyo. “Pamene chamoyo chafa, icho sichitenganso carbon dioxide kuchokera ku malo ake ochizinga, ndipo unyinji wa isotope umachepa m’kupita kwa nthaŵi pamene kuola kwa radioactive kukuchitika,” ikulongosola choncho Science and Technology Illustrated.

Komabe, pali mavuto ambiri ndi njira imeneyi. Choyamba, pamene chinthu chakale chikulingaliridwa kukhala cha zaka 50,000 zakubadwa, mlingo wake wa radioactive umakhala utatsika kwambiri kotero kuti ungapezedwe movuta kwambiri. Chachiŵiri, ngakhale m’zinthu zaposachedwa kwenikweni, mlingo umenewu umakhala utatsika kotero kuti nkovutabe kuyesa molongosoka. Chachitatu, akatswiri asayansi angayese liŵiro la kupangika kwa radioactive carbon kwa lerolino koma alibe njira yoyesera kuchuluka kwa carbon wakale kwambiri.

Chotero kaya agwiritsire ntchito njira ya radiocarbon kaamba ka kuika madeti a zinthu zakale kapena njira zina, mwakugwiritsira ntchito potassium, uranium, kapena thorium ya radioactive kuikira madeti matanthwe, akatswiri asayansi sali okhoza kukhazikitsa milingo yoyambirira ya zinthu zimenezo mkati mwa nyengo za nthaŵi. Chotero, profesa wa ukatswiri wa miyala Melvin A. Cook akulongosola kuti: “Wina angangolota unyinji umenewu [wa zinthu za radioactive], ndipo msinkhu wa zotulukapo zopezedwa sungakhale wabwinopo kuposa kulota kumeneku.” Zimenezo zikakhaladi tero ngati titalingalira kuti Chigumula cha m’tsiku la Nowa zaka zoposa 4,300 zapitazo chinabweretsa masinthidwe aakulu m’mlengalenga ndi pa dziko lapansi.

Akatswiri ofukula pansi a pa Dartmouth College Charles Officer ndi Charles Drake anawonjezera chikaikiro ku kulongosoka kwa kuika madeti kwa radioactive. Iwo akulongosola kuti: “Tikumaliza kuti iridium ndi zinthu zina sizinaikidwe mwadzidzidzi . . . koma kuti panali kulowa kwakukulu ndipo kosiyana kwa zinthu zimenezi mkati mwa nthaŵi yochepa ya ukatswiri wa miyala pa mlingo wa zaka 10,000 mpaka 100,000.” Iwo amatsutsa kuti kusweka ndi kuyenda kwa makontinenti kunasokoneza dziko lonse, kupangitsa kuphulika kwa matanthwe otentha, kutsekereza kuwala kwa dzuwa ndi kununkhitsa mpweya. Ndithudi, zochitika zosokoneza zoterozo zingasinthe milingo ya radioactive, mwakutero kusokoneza zotulukapo zamakono za koloko za radioactive.

Cholembedwa cha Genesis ndi Ma“dinosaur”

Pamene kuli kwakuti njira yoikira madeti ya radioactive imagwiritsira ntchito zinthu zatsopano, iyo njozikidwabe pa zokaikitsa ndi zongolingalira. Mosiyanitsa, cholembedwa cha Baibulo m’chaputala choyamba cha Genesis chimangonena dongosolo lachisawawa la chilengedwe. Icho chimalola kaamba ka mwinamwake zaka mamiliyoni zikwi zingapo a kupangika kwa dziko lapansi ndi zaka zikwi zina zambiri m’nyengo zisanu ndi imodzi za chilengedwe, kapena “masiku,” kukonzekeretsa dziko lapansi kaamba ka kukhalapo anthu.

Madinosaur ena (ndi mapterosaur) angakhaledi analengedwa m’nyengo yachisanu yondandalitsidwa mu Genesis, pamene Baibulo likunena kuti Mulungu anapanga “zolengedwa zouluka” ndi “zinsomba zazikulu za m’nyanja.” Mwinamwake mitundu ina ya madinosaur inalengedwa mkati mwa nyengo yachisanu ndi chimodzi. Mawonekedwe osiyanasiyana a madinosaur okhala ndi chikhumbo cha kudya chachikulu angakhale anali oyenerera polingalira kuchuluka kwa zomera zimene mwachiwonekere zinalipo mu nthaŵi yawo.—Genesis 1:20-24, NW.

Pamene madinosaur anakwaniritsa chifuno chawo, Mulungu anathetsa moyo wawo. Koma Baibulo silimanena mmene anachitira zimenezo kapena kuti ndiliti. Tingakhale otsimikiza kuti madinosaur analengedwa ndi Yehova chifukwa cha cholinga, ngakhale kuti sitikumvetsetsa cholinga chimenecho pa nthaŵi ino. Iwo sanali zophophonya, sanali chotulukapo cha chisinthiko. Mfundo yakuti anawoneka mwadzidzidzi m’cholembedwa cha zinthu zakale popanda kugwirizana kulikonse ndi zinthu zakale zoyambirira, ndiponso kuti anazimiririka popanda kusiya zinthu zakale zogwirizanitsa, ili umboni wotsutsana ndi lingaliro lakuti zinyama zoterozo zinasinthika kwa nyengo ya zaka mamiliyoni angapo. Chotero, cholembedwa cha zinthu zakale sichimachilikiza nthanthi ya chisinthiko. M’malomwake, chimagwirizana ndi lingaliro la Baibulo la machitidwe olenga a Mulungu.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Cholembedwa cha zinthu zakale cha madinosaur sichimachilikiza chisinthiko koma chilengedwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena