Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 2/8 tsamba 21-23
  • Kodi Nchifukwa Ninji Izi Zikuchitika ku Thupi Langa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Izi Zikuchitika ku Thupi Langa?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nyengo Yakusamba—Temberero kapena Dalitso?
  • “Chozizwitsa Chapamwezi”
  • Kupeza Thandizo
  • Kutulutsa Ubwamuna Kwakutulo
  • Kuchita ndi Kudzukidwa
  • Kodi Thupi Langali Latani?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • ‘Kodi Chikuchitika N’chiyani M’thupi Mwangamu?’
    Galamukani!—2004
  • Kodi Nchiyani Chikuchitika ku Thupi Langa?
    Galamukani!—1990
  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuidziŵa Bwino
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 2/8 tsamba 21-23

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchifukwa Ninji Izi Zikuchitika ku Thupi Langa?

UNAMWALI—iyi ingakhale nthaŵi yosangalatsa m’moyo wanu. Inu pang’onopang’ono mukusintha kuchoka ku mwana kukhala wamkulu!

Komabe, mwinamwake makolo anu sanakambitsirane nanu pasadakhale za zimene muyenera kuyembekezera. Ngakhale ngati anakambitsirana nanu, zenizeni za unamwali zingapose zimene munayembekezera. Zinthu zingayambe kukuchitikirani zimene zingakudabwitseni kuti mwina chinachake ncholakwika kwambiri kwa inu. Komabe, motsimikizirika, zosiyanazo ndizo zowona!

Nyengo Yakusamba—Temberero kapena Dalitso?

Chifupifupi zaka ziŵiri unamwali utayamba, mtsikana wachichepere amakhala ndi kusintha kwakukulu—kuyamba kwa nyengo yakusamba. Komabe, popanda kukonzekera kokwanira, chochitika chozindikiritsachi chingakhale chochititsa mantha, chodabwitsa.a “Ndine wochititsidwadi mantha,” analemba tero mtsikana wotchedwa Paula. “Chifupifupi miyezi itatu yapita, ndinayamba kukha mwazi kwa masiku angapo pamwezi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ndiri ndi kansa? . . . Ndine wovutitsidwa kwenikweni polingalira za kukha mwazi kumeneku kotero kuti ndimangolira ndi kunjenjemera.”

Bukhu lakuti Adolescents and Youth likusimba kuti atsikana ena amakhaladi amanyazi ndi aliŵongo pamene nyengo yawo yakusamba iyamba. Pamenepa, nzosadabwitsa kuti atsikana ambiri amasunga chochitikacho kukhala chinsinsi. Mtsikana wachichepere wina ananena kuti: “Ndinachita manyazi kuwuza amayi. Iwo sanalankhulepo kwa ine ponena za izo ndipo ndinali ndi mantha ofa nawo.”

Koma kutalitali ndi kukhala chinachake chochita nacho manyazi, nyengo yakusamba iri umboni wakuti mphamvu zanu zakubala zikukhwima. Thupi lanu tsopano likhoza kutenga pathupi ndi kubala mwana. Eya, pakali zaka musanafikepo kwenikweni kukhala kholo. Koma sindinu nanga, muli chiimire pafupi kwenikweni ndi ukazi. Kodi zimenezi nzochita nazo manyazi? Kutalitali!

Pambali pa zimenezo, ichi ndi chinachake chimene akazi onse amakhala nacho. Baibulo limanena nyengo yakusamba kukhala “zochitika pa akazi.” (Genesis 31:35) Ndipo mosiyana ndi lingaliro la ena, iko sikuli temberero.b Komabe, mwinamwake zingachepetse mantha anu ngati mumvetsetsa bwino lomwe chifukwa chake ndi mmene kusamba kumeneku kumachitikira.

“Chozizwitsa Chapamwezi”

Liwu lakuti “menstruation” (kusamba) linatengedwa ku liwu Lachilatini lotanthauza “pamwezi.” Kamodzi pamwezi thupi lanu limakhala lokhoza kutenga pathupi. Choyamba, kukwera kwa mphamvu ya mahormone a thupi lanu kumadziŵitsa chibaliro chanu. Icho chimadzikonzekeretsa kulandira ndi kusamalira dzira lamoyo; muyalo wake wam’mbali umadzaza mwazi ndi zakudya. Chapafupi pali ziŵalo zampangidwe wonga katungulume zotchedwa maovary, iriyonse yokhala ndi zikwizikwi za timazira tating’nong’ono. Kadzira kalikonse kali mwana wothekera, kongofunikira kukhalitsidwa kamoyo ndi ubwamuna. Kamodzi pamwezi, dzira limakhwima nkutulukira m’maovary.

Tsopano tinthu tofeŵa tonga “zala” timakokera dziralo mu imodzi ya njira ziŵiri zotchedwa Fallopian tubes. Kadzira kakang’onoko tsopano kamayamba ulendo wa masiku anayi kufika ku asanu ndi limodzi kupyola m’menemo kupita ku chibaliro. Ngati mkazi satenga pathupi m’nthaŵi imeneyi, kadzirako kamaphwanyika. Muyalo wa m’chibaliro wochuluka mwaziwo nawonso umasweka. Chibaliro chimayamba kukwinyata ndipo pang’onopang’ono chimatulutsa muyalo umenewu kupyolera m’njira yopita kumpheto wachikazi.

Kwa masiku kuchokera pa aŵiri kufika ku asanu ndi aŵiri (malinga ndi kusiyana kwa akazi) kusamba kumachitika. Ndiyeno kachitidweko kamadzibwereza kokha, mwezi ndi mwezi, kufikira kuuma kwa mkazi.c Mlembi wina anakulongosola bwino kukhala “chozizwitsa chapamwezi”! Kali kachitidwe kosonyeza chizindikiro chosalakwika cha Mmisiri Wamkulukulu. Kulinso chifukwa china chothokozera, monga mmene anachitira wamasalmo kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsya ndi chodabwitsa”!—Salmo 139:14.

Kupeza Thandizo

Ngakhale kulitero, nyengo yakusamba imakudzetserani nkhaŵa ya zochitika zinazake. Mwachitsanzo, atsikana ambiri amada nkhaŵa kuti, ‘Kodi bwanji ngati ziyamba pamene ndiri kusukulu?’ Kusakubisani, izi zingawononge zovala zanu ndi kukuchititsani manyazi. Komabe, wophunzitsa zakugonana Lynda Madaras akutitsimikizira kuti, “atsikana ambiri kuchiyambi kwenikweni samakha mwazi wokwanira kuwonekera pa zovala zawo.” Chikhalirechobe, mufunikira kukonzekera mokwanira.

Mabuku ambiri amapereka chilangizo chabwino cha zamankhwala. Koma bwanji osagawana nkhaŵa zanu ndi amayi anu? Mosakaikira iwo adzapereka malingaliro angapo othandiza. “Amayi anga anali ngati bwenzi kwa ine,” akutero mkazi wina wachichepere. “Tinkakhala ndi makambitsirano aakulu, ndipo iwo ankayankha mafunso anga.”

Indedi, amayi ena zimawavuta kulankhula nkhani zoterezi. Koma ngati muwafikira mwaulemu ndikuwalola kudziŵa kuti nzofunika kwambiri kwa inu, iwo angangokhala okhoza kugonjetsa mphwayi yawo ya kulankhula nanu. Ngati izo zilephera, bwanji osadalira mwa mkazi Wachikristu wofikapo amene mudzamasuka naye?

Ngakhale kuti akazi ambiri amakhoza kuchita zochita zawo za masiku onse mkati mwa nyengo yawo yakusamba, bukhu lakuti Changing Bodies, Changing Lives limatikumbutsa kuti akazi ena amadwala “mutu, kupweteka msana, mavuto a khungu, kusintha kwa mkhalidwe wamaganizo, kupsyinjika, ulesi, nseru, ndi kulephera kutaya madzi.” Mibulu ya aspirin kaŵirikaŵiri imathetsa zizindikiro zimenezi. (Dokotala wanu angadziŵe ngati pafunikira mankhwala amphamvu.) Ndipo ngati nkotheka, mungapewe kupsyinjika kosayenera mwa kulinganiza zochita zanu mkati mwa nyengo yanu yakusamba.

Kutulutsa Ubwamuna Kwakutulo

Anyamata achichepere nawonso amakhala ndi mavuto angapo pamene dongosolo lawo lakubala likukhwima. Mwachitsanzo, ziŵalo zanu zogonanira zimayamba kutulutsa madzi otchedwa ubwamuna. Uwo uli ndi mamiliyoni a timaselo tating’ono totchedwa sperm, kalikonse kumakhala kokhoza kupangitsa dzira lamkazi kukhala lamoyo ndikupanga mwana ngati katulutsidwa mkati mwa kugonana.

Popeza kuti sindinu wokwatira, ubwamuna umangochuluka. Wina umayamwidwa ndi thupi lanu. Koma nthaŵi ndi nthaŵi, wina udzatuluka usiku pamene muli gone. Kumeneku kumatchedwa mofala monga kudziipsira kutulo. Komabe, dzina lake labwinopo, ndilo kutulutsa ubwamuna kwakutulo, popeza kuti kutulutsako kaŵirikaŵiri kumachitika kokha, mochititsidwa ndi loto lakudzukidwa kapena ayi.

Chokumana nacho choyamba cha mnyamata cha kutulutsa ubwamuna kwakutulo chingakhale chovutitsa. “Ndinadziipsira kutulo kwa nthaŵi yoyamba pamene ndinali wazaka chifupifupi khumi mphambu ziŵiri ndi theka,” akukumbukira tero wachichepere wina wazaka zapakati pa 13 ndi 19. “Sindinadziŵe chomwe chinkachitika. . . . Ndinadzuka nkupeza kuti pogona panali ponyowa. Ndinaganiza kuti mwina ndinakodzera pogona kapena chinachake.” Komabe, khalani otsimikiziridwa kuti kutulutsa koteroko nkwachibadwa. Ngakhale Baibulo limakutchula. (Levitiko 15:16, 17) Iko kuli chizindikiro chakuti dongosolo lanu lakubala likugwira ntchito ndikuti mwayandikira kufika ku umuna.

Mokuvomerezani, lingaliro lakuti amayi anu angawone nsalu zanu zogonapo zonyowa lingakuchititseni mantha. Koma sikwenikweni kuti zimenezi zikawathetsa nzeru kapena kuwadabwitsa. Ngakhale kulitero, kukambitsirana izo ndi atate wanu kapena wachikulire wina wofikapo kungathandize. Kuteroku kungakuchotsereni nkhaŵa iriyonse yovutitsa imene mungakhale nayo. Mungakhaledi okhoza kupeza njira yanu yosamalira zamseri zanu m’nkhaniyi.

Kuchita ndi Kudzukidwa

Pamene dongosolo lakubala likukhwima, ponse paŵiri anyamata ndi atsikana kaŵirikaŵiri amadzukidwa mofulumira kwenikweni ku zinthu zodzutsa chilakolako. Pamene izi zichitika kwa mnyamata, chiŵalo chachimuna chogonanira, kapena mbolo, imakhuta mwazi, kuipangitsa kudzuka kapena kulimba. “Komabe,” likukumbutsa tero The New Teenage Body Book, “kudzukidwa kwambiri kumachitika kaamba ka zifukwa zosachita ndi zakugonana—ndipo nthaŵi zina mwachiwonekere, popanda chifukwa chirichonse! Kunthunthumira kwa basi, kuvala zothina, kuzizira, mantha, ndi zoputa zina zingadzutse mpheto.” Atsikana achichepere mofananamo angadzukidwe popanda chifukwa chenicheni.

Kudzukidwa kosafunika kungakhale kopweteketsa mtima, kochititsa manyazi. Koma kuli mbali ya kukula ndipo kungachitike mobwerezabwereza. Achichepere ena amadzutsa kapena kuseŵera ndi ziŵalo zawo kotero kuti apeze chitonthozo cha zakugonana. Kutero nkulakwa ndipo, m’kupita kwanthaŵi, kungapangitse mavuto ena.d Kulibwinopo kungokhazika maganizo ndi kuchotsa nkhaniyo m’maganizo anu. Kudzukidwako kudzatha mwamsanga. Pamene mukukulirako ndi mphamvu ya mahormone anu ikhazikika, mudzapeza kuti kudzukidwa kodzichitikira kukuchitika mwakamodzikamodzi kwambiri.

Unamwali sumakhala kosantha. Mwinamwake tsiku lina mudzakhozadi kuseka zinthu zina zokunyazitsani tsopano. Pakalipano, khazikani mtima ndi nsonga yakuti inu mulibwino.

[Mawu a M’munsi]

a M’kufufuza kwina, 20 peresenti ya amayi ofunsidwa sanauze ana awo aakazi kalikonse ponena za kusamba. 10 peresenti ina anangopereka chidziŵitso chapamwamba chochepera.

b Nzowona kuti Chilamulo cha Mose chinalengeza mkazi wosamba kukhala “wodetsedwa.” (Levitiko 15:19-33) Koma chimenechi chinali kokha m’lingaliro lamwambo. Mwachiwonekere, malamuloŵa anatumikira kuphunzitsa ulemu wa kupatulika kwa mwazi. (Levitiko 17:10-12) Panthaŵi imodzimodziyo, malamulowo anatumikira kukumbutsa mtundu Wachiyuda kuti mtundu wa anthu ngobadwira mu uchimo ndipo umafunikira mombolo.

c Pangapite miyezi kapena zaka dongosolo la nyengo yakusamba lisanakhazikike.

d Onani nkhani pa mphyotomphyoto m’makope a Galamukani! a March 8, 1989, November 8, 1987 (Chingelezi), ndi March 8, 1988 (Chingelezi).

[Chithunzi patsamba 23]

Makolo angakuthandizeni kuchita ndi masinthidwe a unamwali

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena