Pamene AIDS Siirinso Chiwopsezo
Pamadzulo a October 3, 1984, Kyle Bork wachichepereyo anabadwa milungu isanu ndi iŵiri nthaŵi yake ya kubadwa isanakwane. Mapapu ake aang’onowo anali osakhoza kugwira ntchito bwino, chotero anasamutsidwira ku Chipatala cha Ana cha ku Orange County pamtunda wa makilomita 56, kumene zipangizo zinali zopezeka kusamalirira ana odwala kwambiri chotero.
Dokotala ananena kuti mwazi wa Kyle ukafunikira kuwonjezeredwa mwa kuthiridwa mwazi; apo phuluzi iye mosakaikira akafa. Ngakhale kuti zinali zovuta kwa makolowo, iwo anaima nji pa chosankha chawo chozikidwa pa Baibulo cha kusalola khanda lawo kuthiridwa mwazi. (Genesis 9:4, 5; Levitiko 17:10-14; Machitidwe 15:28, 29) Dokotalayo anali womvetsetsa ndi wogwirizanika. Komabe, iye anati, ngati mkhalidwewo ukafika pakayakaya, iye akapempha chilolezo cha kukhoti ndi kumthira mwazi.
Modabwitsa, Kyle anasonyeza kuwongokera kwapang’onopang’ono, ndipo podzafika tsiku lachisanu ndi chinayi, iye anachotsedwa m’makina othandizira kupuma. Masiku aŵiri pambuyo pake makolowo anamtengera kunyumba, ndipo anafikira pakukhala mwana wachimwemwe, wathanzi, monga momwe mungawonere pachithunzithunzichi. Koma aŵa sindiwo mapeto a nkhaniyi.
Chaka chatha kuulutsidwa kwa nkhani za pawailesi ya kanema ya ku Los Angeles kunasimba kuti chiŵerengero cha ana amene anakhala m’Chipatala cha Ana cha ku Orange County pafupifupi nthaŵi imene Kyle anali kumeneko anali anatengako AIDS mwa kuthiridwa mwazi woipa. A chipatalawo ankayesayesa kufikira mabanja a pafupifupi ana 3,000 kotero kuti akapendedwe za kachirombo ka AIDS.
Mofulumira, makolo a Kyle anachitira foni kuchipatala kuti atsimikizire kuti iye sanathiridwe mwazi popanda kuwadziŵitsa. Mwamsanga, a chipatala anayankha foni yawo yowatsimikiziritsa kuti sanalandire mwazi uliwonse ndipo sanali m’ngozi ya kutenga AIDS. “Tinagwadadi pansi ndi kuthokoza Yehova,” anatero makolowo, “kaamba ka kutipatsa malamulo ake olungama ndi nyonga ya kusunga umphumphu wathu poyang’anizana ndi chiyeso choterocho.”