Mmene Mungachitire Zambiri mu Nthaŵi Yochepa
‘Kodi nthaŵi yatha bwanji?’ Kodi mwadzifunsa funsolo kaŵirikaŵiri motani? Ngati ndinu wofanana ndi anthu ena ambiri, mwinamwake mumadzifunsa kaŵirikaŵiri kwenikweni mosakhoza kukumbukirika.
Zotsatirazi zikupereka malingaliro a kuganiza kwa mkazi, koma popeza kuti onse aŵiri akazi ndi amuna ali ndi mlingo wofanana wa nthaŵi mlungu uliwonse, funso lakuti, ‘Kodi ndingachite motani zochuluka m’nthaŵi yomwe ndirinayo?’ nlomwe onse aŵiri amuna ndi akazi angakonde kuti liyankhidwe.
Khazikitsani Zoyambirira
Popeza kuti chochita chirichonse m’moyo chimadya nthaŵi, pali zinthu zina zimene mwachibadwa zimakhala zoyamba pa zina. Mwachitsanzo, m’nyengo yachisanu yozizira, mayi amakonda kugonereza m’kama wake wofunda kuposa chinthu china chirichonse. Koma koloko imamuuza kuti nthaŵi yakwana yokonza chakudya cham’mawa ndi kulola mwamuna wake kupita kuntchito ndipo ana kusukulu.
Zoyambirira ziyeneranso kukhazikitsidwa ngati nyumba yanu iti igwire ntchito moyenera. Pali nthaŵi yogula zakudya ndi nthaŵi yoziphika; nthaŵi yosesa m’nyumba ndi nthaŵi yochapa; nthaŵi yopuma ndi nthaŵi yophunzira; nthaŵi yoyang’anira ntchito yochitira kunyumba ya ana akusukulu ndi ntchito zapanyumba—ndandandayo ingopitirizabe.
Kodi mumagwira ntchito? Ngati nditero, pokhala ndi ntchito zowonjezereka zochita, nthaŵi imakhaladi yamtengo kwenikweni. Simungafune kuiwononga pachabe, ndipo simungathe kuimitsa zinthu nkudzazichita tsiku lina nthaŵi zonse. Ndicho chifukwa chake akazi ambiri amavomereza kuti ndandanda njofunika kotheratu ngati ati amalize ntchito zawo.
“Popanda ndandanda ya tsiku ndi tsiku,” akutero Josephine, nakubala wa ana asanu ndi mmodzi amsinkhu wa zaka 2 kufika ku 15 zakubadwa, “sindikanatha mpang’ono pomwe kukwaniritsa zonulirapo zanga za tsiku lirilonse.” Sandra, yemwe ali ndi ana atatu, amagwira ntchito kwa maola 25 pa mlungu, ndipo akuvomereza motere: “Eya, ndikadakhala wopanda ndandanda, ndiganiza kuti ndikanapenga.”
Ndiponso, zoyambirira zanu mosakaikira zimakhazikitsidwa ndi mtengo umene mumaika pa nthaŵi yeniyeniyo. Ziri motero kwa Lola. Iye sali kokha ndi mwamuna wosamalira komanso amathera maola 90 mpaka 100 pa mwezi kuntchito yake ya maphunziro a Baibulo. Iye akuti: “Nthaŵi njofunika kwambiri kwa ine. Ndiganiza kuti nkwabwinodi kusapangitsa anthu kukudikirira. Ndipo pamene awo amene angakhale osasamala awona kuti ndimasamalira nthaŵi kwenikweni, amalemekeza nthaŵi yanga mowonjezereka.”
Linganizani Ntchito Zochita
Kodi nchifukwa ninji akazi ena samamaliza konse ntchito zawo? Kapena kodi nchifukwa ninji ena nthaŵi zonse amadandaula ponena za kusoŵa nthaŵi? Kodi chifukwa chimodzi chingakhale chakuti amalephera kulinganiza ntchito yawo? M’mibadwo yapita akazi anafunikira kuthera tsiku lonse akuchapa ndi tsiku lina akusita, pamene kuli kwakuti ankagula ndi kuphika tsiku ndi tsiku. Komabe, m’maiko ambiri lerolino, mkazi angayeretse nyumba, kuchapa ndi kuwumika zovala, ndi kuphika panthaŵi imodzi ngati amadziŵa kulinganiza. Ziwiya zopeputsa zamakono zamasula akazi ambiri kukagwira ntchito kunja kwa nyumba ndi kusamalirabe zosoŵa zabanja.
Koma bwanji ponena za nthaŵi yowonongeredwa kunja kwa nyumba? Mbali yake yaikulu, pambali pa nthaŵi yotheredwadi pantchito, imathera paulendo wopita kuntchito ndi kubwera, poyembekezera m’maofesi a adokotala ndi adokotala amano ndi kwinakwake. Kodi yochuluka ya nthaŵiyi ingagwiritsiridwe ntchito mwanzeru? Mwachitsanzo, kodi mumaluka majuzi, kuluka zidoilo, kusoka ndi singano, kapena kupeta maluŵa pa nsalu? Kodi mungandandalitse ena a maluso ameneŵa panthaŵi zimenezi ndi malowa? Akazi ambiri amaŵerenga, kupanga ndandanda za zinthu zofunikira kugula, kapena kulemba makalata. Kwenikweni, nthaŵi yotsatira pamene mudzakhala pansi kupenyerera TV, bwanji osasoka kapena kupangira banja zinthu zina? Iwo angaziyamikire kuposa zogulidwa m’sitolo, ndipo mudzakhala ndi chitsimikizo chowoneka ndi maso chakuti simunataye nthaŵi pachabe!
Komabe, kulinso mbali ina ku nkhaniyi. Munthu ayenera kupeŵa kukhala woumakhosi mwakuyesera kugwiritsira ntchito mphindi iriyonse. Mungakhale kapolo wa nthaŵi, ndipo chimenecho chidzakulandani chimwemwe. Pali nthaŵi pamene wina amafuna kukhala chete ndi kumalingalira pa zimene wachita. Nthaŵi zoterozo zingakhaledi zamtengo wapatali!
Lamulo lamakhalidwe abwino lofananalo lingagwire ntchito ponena za kusunga ndalama. Kulinganizika nkofunikira. Inu mungayendetse galimoto kuzungulira tauni yonse kuti musunge makobiri angapo, komabe mwakutero mukuwononga nthaŵi yochuluka ndi petulo. Ndithudi, pamene muli ndi ndandanda ya zogula yovuta, kusunga ndalama nkofunika kwambiri. Choncho mwinamwake kugula m’shopu yaikulu imodzi kungathandize. Mumadziŵa kumene zinthu zikupezeka (chimene chimawombola nthaŵi), ndipo mumadziŵa pamene kuli selu (chimene chimakuwombolerani ndalama).
Kusankha Nthaŵi Yabwino Koposa
Mkazi aliyense ali ndi koloko yakeyake mwa iye yekha. Ena amagwira ntchito bwino kwambiri m’mawa; ena samagwira ntchito bwino kufikira masana. Ngati ndinu wam’mawa, pamenepo ndandalitsani ntchito zanu zovuta nthaŵiyo. Gwiritsirani ntchito mphamvu zanu pa nthaŵi zimene mukudzimva wanyonga koposa. Ngati mumagwira ntchito, bwanji osalankhula kwa bwana wanu? Zidzakhala bwino kwa inu ndi kwa iyenso kugaŵa ntchito yanu moyenerera. Kumbali ina, ngati mumakhala waulesi m’mawa, sungirani ntchito yanu yofunika kwambiriyo nthaŵi ina pamene mumagwira ntchito bwino.
Mary ndi munthu wanyonga m’mawa. Iye amalingalira nthaŵi imene amathera muuminisitala wake kukhala mbali yofunika koposa ya tsiku lake. Chotero anapeza ntchito yapambali yogwira masana. Ichi chimamukhozetsa kupereka maola ake abwino koposa ku ntchito yake yophunzitsa Baibulo. Kodi nanunso mungachite zofananazo ndi ndandanda yanu?
Khalani Wowona
Kuti ndandanda ikhale yopindulitsa, siiyenera kuphatikizapo ntchito zambirimbiri. Kuyesera kukhala Nakubala, Mkazi, kapena Wantchito Wopambana kungatsogolere ku kukhumudwitsidwa ndi kulefulidwa. Izi nzowona makamaka ngati muli ndi matenda. Phunzirani kugwira ntchito molingana ndi mphamvu zanu.
Dolly, amene ali ndi matenda osatha, akulongosola kuti: “Nthaŵi yanga imadalira pa zochita za mwamuna wanga. Iye ndi minisitala woyendayenda. Popeza kuti timakhala m’nyumba yaing’ono yoyenda nayo, atamaliza ntchito yake, pamenepo ndimachita yanga. Nthenda yanga imandiletsa kuchita zonse zimene ndingafune kuchita. Koma pamene ndiri wokhoza, uminisitala wanga umatenga malo oyamba. Zinthu zina panyumbapo sizimachitidwa pa tsikulo.”
Khalani Wokhoza Kusintha
Kuyesa chipambano cha mkazi ndiko kuwona mmene amagwirira ntchito atatsenderezedwa. Ngati angakhale wodekha m’vuto, iye adzakwaniritsa zambiri kuposa ndi kusweka maganizo.
Sandra anapeza chinsinsi chopirira ndi chitsenderezo. Iye akuti: “Pamene zamwadzidzidzi zabuka ndipo ndidzimva wopanikizidwa konsekonse, ndimangodekha mtima. Ndikudziŵa kuti chimenecho nchachilendo, koma chimagwira ntchito. Nditadzilamulira, pamenepo ndingadziŵe chimene chiyenera kuchitidwa choyamba. Ngati sindidekha mtima, sindingathe kukhazikitsa zoyambirira kuchita zabwino. Izi zitakhazikitsidwa, pamenepo ndimachita ntchito yanga mofulumira kuti ndigwirizane ndi zakugwa mwadzidzidzi ndipo zinthu zimachitidwa. Mwachitsanzo, nthaŵi ina alendo anafika maola angapo nthaŵi yachakudya chamadzulo isanakwane. M’malo mopanikizika, ndinkaphika ndikumacheza nawo panthaŵi imodzimodziyo monga mmene ndinakhozera. Onse anadzimva olandirika ndipo anasangalala.”
Pezani Thandizo
Munthu wina ananenapo kuti mkulu wabwino koposa pantchito ndi amene amavomereza thandizo la odziŵa. Kodi mumagwiritsira ntchito thandizo la ena pantchito? Pamene antchito anzanu adziŵa kuti thandizo lawo likuyamikiridwa, amalipereka modzifunira kwenikweni. Nchimodzimodzinso ndi panyumba. Mwatsoka, akazi ena amadzilingalira mopambanitsa kukhala akatswiri oyeretsa nyumba ndi ophika bwino kwakuti samafuna kuwathandiza. Ndipo mkhalidwe umodzimodziwo ungakhale chifukwa chimene akazi ena ndi anakubala nthaŵi zonse amakhala yakaliyakali pamene ziŵalo zabanja lawo ziri phee mosada nkhaŵa.
Tsopano bwanji ponena za inu? Pamene mumafunikira thandizo, kodi mumalilimbikitsa? Kodi mumapempha thandizo, kapena kodi mumalifuna mokakamiza? Mawu akuti “Kodi chonde” amamveka abwino kwambiri kuposa akuti “Ndifuna kuti”—kaya mukulankhula kwa ana anu kapena kwa mwamuna wanu.
Mkazi wina, poyamikira mwamuna wake kaamba ka thandizo limene amampatsa akuti: “Iye ngwabwinodi pa ichi. Pamene sindikumva bwino, amandiuza kuti ndipite kukagona, ndipo amaphika chakudya chamadzulo; iye ndi ana onse amagwirizana ndi kundithandiza kuchita ntchito zapanyumba. Ndimayamikiradi chimenecho!”
Ndi mkhalidwe wabwino chotani nanga umene banja liyenera kukhala nawo! Koma munthu wofunika kwambiri pankhaniyi ndiye mayi. Iye angaphunzitse ana ake kuzindikira phindu la nthaŵi ndi kukulitsa mkhalidwe wabwino kulinga ku ntchito. Ana oterowo mwachibadwa adzafuna kuthandiza chifukwa amapeza chisangalalo m’kuthandizira ku chonulirapo chimodzi cha banja.
Nzowona kuti, anthu ena adzawonongabe nthaŵi mosasamala kanthu za zimene ena anganene kapena kuchita. Sitingaŵasinthe; tingangodziwongolera tokha. Tingatsimikizire kukhala wowona ponena za nthaŵi, kukhala wolinganizika bwinopo, kukhazikitsa zoyambirira zoyenerera, ndi kupeza thandizo pamene lifunikira.
[Chithunzi patsamba 30]
Zoyambirira ziyenera kukhazikitsidwa ngati banja lanu liti ligwire ntchito bwino