Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 7/8 tsamba 10-11
  • Kufufuza Nyama—Kawonedwe Kolinganizika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufufuza Nyama—Kawonedwe Kolinganizika
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lingaliro Labaibulo
  • Kufufuza Nyama—Zivomerezo Zachiwawa
    Galamukani!—1990
  • Kodi Nkulakwa Kudya Nyama?
    Galamukani!—1997
  • Kuzunza Nyama—Kodi Nkulakwa?
    Galamukani!—1998
  • Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 7/8 tsamba 10-11

Kufufuza Nyama—Kawonedwe Kolinganizika

NGAKHALE kuti mtengo wolipiridwa ungakhale wodzetsa m’kangano, anthu ambiri amakhulupirira kuti kufufuza nyama kwatulukapo zabwino zambiri kwa anthu. Ngakhale awo amene amachilikiza chiwawa motsutsana ndi kugwiritsira ntchito kuyesa nyama akhala opindula ndi chidziŵitso chatsopano chamankhwala ndi maluso a opareshoni limodzinso ndi mankhwala olimbana ndi matenda.

Martin Stephens wa pa Humane Society of the United States anati: “Tiyenera kukhala owona mtima ndi kuzindikira kuti pali mapindu ena kuchokera ku kufufuza nyama. Koma chonulirapo chathu chachikulu ndicho kufufunafuna cholowa m’malo zinyama.” (Parade Magazine, October 9, 1988) Vicki Miller, prezidenti wa Toronto Humane Society anati: “Ndikuvomereza kuti kugwiritsira ntchito kwina kwabwino kwa zinyama kunachitidwa kuchiyambi kwa zaka za zana lino. Kuchepetsedwa kwa nthenda ya suga kunatengedwa ku kufufuza nyama. Koma tsopano palibe kufunika kwa kutero popeza kuti tiri nazo zolowa m’malo za mtundu uliwonse za luso la zopangapanga.”—The Sunday Star, Toronto, Canada.

Wosuliza mmodzimodziyu adafunsidwa mmene angayankhire omwe angatsutse kuti: Ngati khoswe ayenera kufa kuti moyo wa khanda upulumutsidwe, nkoyenera. Ngati zinyama zisiyidwa m’kufufuza, makanda amafa chifukwa chofuna kupulumutsa makoswe. Yankho lake ku Toronto Globe and Mail linali lakuti: “Iri nkhani yodzetsa malingaliro ambiri, ndipo kuchokera ku lingaliro loterolo chakhala chosatheka kulaka . . . Pali nkhani yokhudza khoswe kapena khanda ndipo nthaŵi zonse mumalephera.”

M’nkhani yapita munafunsidwa funso lakuti: “Ngati kufufuza kochitidwa pa nyama kukanapulumutsa inu kapena wokondedwa wanu ku matenda opweteka kapena imfa, kodi mukanakukana?” John Kaplan, profesa wa lamulo pa Stanford University, California, analemba yankho m’magazine a November 1988 a kope la Science kuti: “Awo amene amatsutsa kufufuza zinyama kaŵirikaŵiri samachilikiza lamulo lamakhalidwe abwinolo ndi kulangiza asing’anga awo kusagwiritsira ntchito zotulukapo za kufufuza kwa sayansi ya zamankhwala pa zinyama pamene zikawapindulitsa okondedwa awo kapena iwo. Ndipo sanakhalenso ofunitsitsa kudzipatula iwo okha ku mapindu a zotulukapo zamtsogolo zirizonse za kufufuza nyama. Tingakhumbire malamulo amakhalidwe abwino amene amasonkhezera Mboni za Yehova kukana kuthiridwa mwazi . . . ndi omwe amatsutsa kusaka nyama zokhala ndi ubweya mwa kusavala zaubweya. Koma tiyenera kulimbana mwamphamvu ndi lingaliro limene limatsogoza omwe amatsutsa kufufuza nyama kuti akwaniritse cholinga chawo osati mwa chitsanzo koma mwakumenyera ndi zitsutso zosawona mtima kuti alande aliyense mapindu ake.”

“Unyinji uyenera kudziŵitsidwa,” analemba motero mkonzi wa magazine a Science a pa March 10, 1989, “kuti kufufuza pa zinyama kumapindulitsanso zinyama zina. Kwenikweni, katemera wa chigodola, kachirombo kamene kamapha mamiliyoni ambiri a ng’ombe mwapang’onopang’ono ndipo mopweteka, anapangidwa mwa kufufuza nyama; katemerayo tsopano amagwiritsiridwa ntchito ku ng’ombe mamiliyoni ambiri ndi World Health Organization mu Afirika.”

Lingaliro Labaibulo

Chitapita Chigumula cha tsiku la Nowa, Yehova Mulungu anapereka lamulo iri kwa Nowa ndi mbadwa zake, zimene zimaphatikizapo mbadwo wathu: ‘Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.’ (Genesis 9:1, 3, 4) Zikopa za nyama zikanagwiritsiridwanso ntchito monga zovala. Chimenechi sichikalakwira ulamuliro wa munthu woperekedwa ndi Mulungu pa nyama.—Genesis 3:21.

“Ngati zinyama zingagwiritsidwe ntchito monga chakudya chochirikiza miyoyo ya anthu,” analemba motero magazine a Galamukani! wa March 8, 1981, “kukuonekera kukhala kwanzeru kuzigwiritsira ntchito pochita mafufuzidwe m’zamankhwala populumutsa miyoyo. Komabe, chimenechi sichilolezo konse cha kuchitira mafufuzidwe osalamulirika ndi amene kawiri-kawiri ali osafunika, ndi obwereza-bwereza ophatikizapo kubvutitsa zinyama kopambanitsa.” Ndithudi, kuchokera ku lingaliro Labaibulo, nkhalwe yopanda chifundo kwa zinyama singalungamitsidwe.—Eksodo 23:4, 5, 12; Deuteronomo 25:4; Miyambo 12:10.

Adokotala ambiri ndi asayansi amavomereza kuti ubwino wina watulukapo ku magulu olimba a omwe amatsutsa kufufuza nyama. “Mfundo zambiri zopangidwa ndi magulu ochilikiza ubwino wa nyama nzopambanitsa koma nzabwinodi,” anavomereza motero wasayansi wina. “Miyoyo ndi kuvutika kwa zinyama kuyeneradi kuŵerengera kaamba ka chinachake,” analengeza tero Jeremy J. Stone, wasayansi wa ku Amereka. “Chidziŵitso chinachake chingapezedwe pa mtengo waukulu kwambiri,” anavomereza motero katswiri wa thupi la anthu wa ku Briteni, Dr. D. H. Smith. “Tikuvomerezana ndi chikhumbo chakupanga kufufuza kukhala kosapweteka kwambiri, kusamalira bwino ndi kuchepetsa chiŵerengero cha zinyama zogwiritsiridwa ntchito m’kuyesa,” anatero Dr. J. B. Wyngaarden wa ku U.S. National Institutes of Health. Ndipo wochilikiza nyama wina anavomereza kuti: “Kudali kulingaliridwa kukhala umuna kugwiritsira ntchito zinyama ndikusalingalira chirichonse ponena za izo. Lerolino, kulingalira ponena za zolowa m’malo ndiko chinthu choyenera kuchitidwa.”

“Zolowa m’malo” ndilo liwu lenileni. Asayansi amavomereza kuti sangafike pa nsonga yeniyeni yolekeratu kugwiritsira ntchito zinyama m’kufufuza, koma kumene kuli kothekera iwo akufunafuna mokhazikika zolowa m’malo. Mwachitsanzo, akalulu sakugwiritsiridwanso ntchito kutsimikizira kukhala ndi pakati kwa anthu, popeza kuti tsopano njira ya mankhwala iripo. Mbira sizikugwiritsiridwanso ntchito tsopano kupatula kachirombo koyambitsa chifuwa chachikulu. Njira zopanga zinthu zikugwiritsiridwa ntchito kupulumutsa miyoyo ya zinyama zimenezi zomwe zikadafa. Njira zina zopanga minyewa zalowa m’malo kuyesera kopangidwa pa mbewa zina. Ndipo akalulu ambiri ondandalikidwa kaamba ka kuyesa kopweteka kwa Draize angapulumutsidwe chifukwa cha kugwiritsira ntchito kolowa m’malo kwa mtsempha wa dzira la nkhuku yofungatira monga malo oyesera. Ndithudi, anthu amene amazindikira kupweteka kwa zinyama amayembekezera kuti zolowa m’malo zambiri zipezedwe, ndipo mofulumira.

Komabe, cholowa m’malo chachikulu koposa cha kufufuza nyama chidzakhala Paradaiso wapadziko lapansi woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali amene Akristu owona akumupempherera. Yehova Mulungu, Mlengi wachikondi, walonjeza kuti matenda onse ndi imfa yeniyeniyo zidzathetsedwa kotheratu. M’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu, munthu ndi zinyama zidzakhala pamtendere kosatha wina ndi mnzake, ndipo palibe chimene chidzawachititsa mantha. Ndipo sipadzakhalanso matenda ndipo motero sipadzafunikira kukhala kuyesa nyama. Nkhalwe idzakhala chinthu chakale.—Yesaya 25:8; 33:24; 65:25; Mateyu 6:9, 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena