Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 8/8 tsamba 25-26
  • Kumwerekera ndi Crack—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumwerekera ndi Crack—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malo Osayenerera
  • Munganene Kuti Ayi!
  • Kumwerekera ndi Crack—Mliri Wake wa Chiwawa
    Galamukani!—1990
  • Kumwerekera ndi Crack—Tsoka kwa Ana Osabadwa
    Galamukani!—1990
  • Mmene Mankhwala Oletsedwa Amakhudzira Moyo Wanu
    Galamukani!—1999
  • Kodi Tingapambane Pankhondo Yolimbana ndi Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 8/8 tsamba 25-26

Kumwerekera ndi Crack—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?

PALIBE chikaikiro chakuti kumwerekera ndi crack kwafika pamlingo woopsa, ndipo vutolo likukulabe. Mawailesi ndi mawailesi akanema amaulutsa vutolo. Limapanga mitu yankhani pamanyuzipepala ndi magazini. Zipinda zachipatala zosamalira ovulala mwangozi ndi zipatala za odwala thenda zamaganizo zimayang’anizana ndi chiwawa cha vutolo. Zipinda za anakubala zimadzala ndi makanda ovulazidwa ndi kumwerekerako. Zipinda zosungiramo zinthu zikugwiritsiridwa ntchito “kusungiramo” makanda onyanyalidwa mmalo mwakusungiramo zinthu.

Malo ochiritsirako nthenda zamaganizo ndikulimbitsirako thupi akuchiritsa ana amene sanafikire unyamata wawo. Mabungwe otumikira anthu akupempha ndalama zothandizira kulimbana ndi mliriwo. Pali anthu amene amati amalephera kugonjetsa kumwerekera kwawo ndi ena amene safuna kuleka. Kwa osafunawo, tsoka, kugwiritsidwa mwala, chiwawa, ndipo mwinamwake imfa zikuwayembekezera. Kwa olephera kulekawo, chiyembekezo chiripo.

“Chaka chimodzi chokha chapitacho,” inasimba motero The New York Times ya August 24, 1989, “crack analingaliridwa ndi ambiri kukhala mankhwala ogodomalitsa atsopano, osamvetsetsekabe koma ochititsa mikhalidwe yapadera yochititsa kumwerekera kumene kuli pafupifupi kosachiritsika.” Komabe, tsopano ofufuza akupeza kuti kumwerekera ndi crack, pansi pa mikhalidwe yabwino, kungachiritsidwe mwachipambano, inatero nyuzipepalayo. “Kumwerekera ndi crack kungachiritsidwe,” anatero Dr. Herbert Kleber, wachiŵiri kwa William J. Bennett, woyang’anira lamulo lakaperekedwe kamankhwala ogodomalitsa mu U.S. Mfungulo yake, iye anatero, ndiyo kupatsa omwerekerawo malo m’banja ndi m’chitaganya kumene sanakhaleko. Iye anagogomezera kuti iwo afunikira “mkhalidwe watsopano mmalo mwakuwabwezeretsa ku wapoyambapo.”

Ofufuza apeza kuti njira yogwira mtima koposa yochiritsira omwerekera ndi crack iri ndi masitepe atatu—kuletsa kusuta, kupereka uphungu ndi kuphunzitsa kwakhama, ndipo kuposa zonse, chichirikizo choperekedwera m’malo oyenerera. Kuleketsa womwerekerayo kusuta mankhwalawo, sindiko vuto lalikulu. Kaŵirikaŵiri, chifukwa cha mikhalidwe, munthu angachite chimenechi payekha. Kusoŵa ndalama yogulira mankhwala ogodomalitsa kungakhale, ndipo kaŵirikaŵiri kuli, chochititsa kuleka. Kubindikiritsidwa m’ndende yokhaulitsira kumene mankhwala ogodomalitsa sakupezeka kungakhalenso choleketsa china, kapena kukhala m’chipatala kungafunikiritse kuleka. Komabe, vuto lenileni, ndiro kuletsa womwerekerayo kubwereranso kumankhwala ogodomalitsa pamene ampezekeranso.

Ngakhale kuli kwakuti omwerekera ena mwachipambano amasuka kuukapolo wa crack pokhala pamaprogramu olinganizidwa mwapadera ochiritsira, akatswiri ochiritsa agogomezera mfundo yakuti omwerekera ochuluka koposa samapambana konse pamilungu yoŵerengeka yoyambirira. Mwachitsanzo, Dr. Charles P. O’Brien, katswiri wa nthenda zamaganizo pa Yunivesite ya Pennsylvania, ananena kuti mbali ziŵiri mwazitatu za omwerekera olembetsedwa paprogra-mu yake yakuchiritsa amalephera m’mwezi woyamba. Maprogramu ena samafikadi pamenepo.

Malo Osayenerera

Mkulu wa pamalo ochiritsira anati: “Tingafunikire kuwachotsa m’midzi yawo. Uyenera kusamutsa omwerekerawo m’malo opezekamo mankhwala ogodomalitsa. Malowo ali motchale kwa iwo.” Zimene ofufuza azipezazi, ndizo chifukwa chachikulu chimene chimachititsa omwerekera ochuluka kwambiri ochiritsidwawo kubwereranso kumankhwala ogodomalitsa amene anali adawaika muukapolo. Chifukwa chimenechi nchowonekeratu. Kodi malo amenewa sindiwo amene anawapangitsa kupita kuzipatalazo poyambirirapo? Kodi crack sanali kupezeka pamakwalala onsewo, kumene chipsinjo chamabwenzi, kaŵirikaŵiri chochokera kwa am’banja lawo ndi mabwenzi apamtima, chinawachititsa kuyamba kusuta kaliwo wa crack? Kodi ndani nanga ali kumeneko tsopano kuwalimbikitsa kumamatira kuprogramu yawo yakuchiritsidwa ndi kuwaonjola ku nkhondo yolimbana ndi mankhwala ogodomalitsa kuti atetezere miyoyo yawo?

Maprogramu achipambano kwambiri anagogomezera mfundo yakuti malo osayenerera ndiwo nakatande wopangitsa womwerekerayo kupitirizabe kusuta mankhwala ogodomalitsa. The New York Times ikusimba kuti: “Wodwalayo anaphunzitsidwa njira zotalikirirana ndi mankhwala ogodomalitsa, kuphatikizapo mmene angapeŵere mikhalidwe yodzutsa chilakolako chake. Kuwona khwalala limene munthuyo panthaŵi ina anagulapo crack, kuwona kaphukusi kotayidwa, kuwona ofesi ya dokotala wa mano kapena kumva fungo lamankhwala m’malo opangira mankhwala lofanana ndi fungo la crack,” zonsezo ndizo zinthu zimene zingadzutse chikhumbo chofuna mankhwala ogodomalitsa, inatero nyuzipepalayo. Maprogramu ogwira mtima anagogomezeranso kufunika kwakuti omwerekera “adule maunansi onse ndi mabwenzi kapena achibale amene akadagwiritsirabe ntchito mankhwala ogodomalitsa.” Mmalo mwake, iwo anapatsidwa uphungu wakupanga mabwenzi atsopano ndi anthu amene sasuta mankhwala ogodomalitsa. Ndithudi, uphungu wanzeru.

Munganene Kuti Ayi!

Buku lakuti Self-Destructive Behavior in Children and Adolescents likupereka ndemanga iyi: “Kaŵirikaŵiri koposa achichepere amayambitsidwa ‘kuphunzitsidwa’ mankhwala ogodomalitsa osiyanasiyana ndi bwenzi lapamtima . . . Zolinga [zake] zingakhale kugawana chochitika chosangalatsa kapena chosangulutsacho.” Komabe, chisenderezo cha mabwenzi sichiri cholekezera paachichepere, monga momwe omwerekera okulirapo angachitire umboni; ndiponso uphungu wanzeru wa Malemba uli panopa suunalekezera kwa achichepere okha, koma umagwira ntchito kwa anthu a misinkhu yonse, monga momwe wolemba Baibulo akunenera kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”—Miyambo 13:20.

Ngati mwathedwa nzeru ndi mavuto owonekera kukhala osagonjetseka, musapeze pothaŵira ku mankhwala ogodomalitsa. Kutero kudzangowonjezera mavuto anu. Kambitsiranani mavutowo ndi kholo lanu kapena mkulu wina wathayo amene angafunedi kukuthandizani. Kumbukiraninso, uphungu wa Baibulo wakuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.—Afilipi 4:6, 7.

[Bokosi patsamba 26]

Ice, Wopambana Crack

“Ajapani amamtcha shabu, Akorea amati hiroppon. Omwerekera aku Amereka amene akungotulukira kumene kuchangamula kwake kwamphamvu ndi kugodomalitsa kopambanitsa, amangomtcha ‘ice,’” amatero magazini a Newsweek ponena zamankhwala ogodomalitsa amenewa ochokera ku Asia. Iwo ndiwo mtundu wa namgoneka wotchedwa methamphetamine, kapena speed, wopangidwira m’laboratore kuchokera kumakhemiko osavuta kupeza. Kuchangamula kwa crack kumatenga mphindi zokha; koma kwa ice kumatenga maola angapo, kufikira 24. Kaŵirikaŵiri kumapangitsa osutawo kukhala achiwawa. Kumgwiritsira ntchito kwanthaŵi yaitali kumachititsa kuwonongeka maganizo ndi kuchititsa mavuto kumapapu ndi impso okhoza kupha munthu. Newsweek ikuti “ziyambukiro za ice pamakanda obadwa chatsopano nzoopsa.” Wofufuza wina akuti: “Ngati munaganiza kuti kumwerekera ndi cocaine nkoipa, zimenezo nzochepa poyerekezera ndi mankhwala ogodomalitsa ameneŵa.” Ngwovuta kwambiri kuwaleka kuposa kumwerekera ndi cocaine ndipo kuwona zizimezime kungakhaledi kwamphamvu pambuyo pa zaka ziŵiri za kuchiritsidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena