Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso
Mbali 1c: Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso Chifukwa Ninji?
“Galamukani!” njokondwa kulengeza mpambo wankhani zamutu wakuti “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso”
PALIBE amene angatsutse kuti ndale za maboma zakhala ndi chisonkhezero pa mbiri yadziko ndi pa aliyense wa ife payekha. Chinenero chimene mukulankhula, moyo umene mukulondola, mtundu wa ntchito imene mukuchita, dongosolo la mayanjano limene mukusangalala nalo, mwinamwake ngakhale chipembedzo chimene mumalondola, mwanjira inayake zasonkhezeredwa kwa inu ndi masinthidwe ofulumira andale zadziko.
Popeza kuti boma nlofunika, kodi ndani waife amene safuna kukhala pansi paboma limene lidzakhutiritsa zosoŵa zathu mwanjira yabwino koposa yothekera? Koma kodi boma labwino koposa nlamtundu wotani? Ndipo kodi tiri ndi chosankha chirichonse m’nkhani yaulamuliro?
Galamukani! njokondwa kulengeza mpambo wankhani zamutu wakuti “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso.” Nkhani zimenezi zidzapitirizabe m’makope otsatira a maganizini ano. Mkati mwanthaŵi yotsala ya 1990, idzasimba chiyambi cha mbiri yakale ya boma la mfumu, aristokrase, oligake, ndi ulamuliro wa okhupuka. Idzasimba mwatsatanetsatane mademokrase osiyanasiyana, limodzi ndi malipabuliki amitundumitundu. Idzasumika chisamaliro pamaboma a otokrase, otsendereza ufulu, ndi a totalitariyani onga Chifasi ndi Chinazi zam’nyengo ya Nkhondo Yadziko II. Maboma a Sosholizimu ndi a Komyunizimu nawonso adzalingaliridwa.
Kucholoŵana kwa ulamuliro wa anthu nkochuluka ndipo kumathetsa nzeru, motero sizonse zimene mungafune kudziŵa ponena zamaboma zimene zingaperekedwe. Nkhanizo sizinalinganizidwire kukhala buku lophunzitsa ndale zadziko. Sizidzachirikiza kapena kutamanda zabwino za maboma a anthu onse kapena mpangidwe uliwonse pawokha. Kuyerekezera kulikonse pakati pa mipangidwe yosiyanasiyana sikudzakhala n’cholinga chokweza wina pamwamba paunzake. Galamukani! idzamamatira mosamalitsa kuzitsogozo zake zotchulidwa patsamba 5, pamene timaŵerenga kuti: “Imapenda zakuya ndi kusonyeza tanthauzo lenileni la zochitika zamakono, komabe imakhala yachete kundale zadziko.”
Nkhani zamutu wakuti “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso” zalinganizidwira kukhala mbali yakupenda “zakuya” kumeneko. Zidzasonya ku “tanthauzo lenileni la zochitika zamakono,” zochitika zimene zimasonyeza kuti ulamuliro wa anthu ukuyang’anizana ndi vuto.
Buku lakuti The Columbia History of the World limalongosola vutolo mwanjira iyi: “Mkhalidwe wa boma, chipembedzo, makhalidwe abwino, kuloŵana kwa makhalidwe, chinenero, maluso, ndi maziko enieni a moyo wotsungula, chiyembekezo cha onse, zimatilola kuwoneratu mwachimbuuzi ukulu wa zochitika za nyengo yamakono. Boma ndiro loyamba pandandanda ndiponso loyamba pakufunika. . . . [Pali] kuda lamulo, ndi Boma lolipereka, kudanso a bwanamkubwa amene akali kuchirikiza ziŵirizo. . . . Chiyembekezo chamkhalidwe wamakono wazinthu nchosiyana kotheratu ndi chimene chinalipo zaka za zana limodzi zapitazo . . . M’mbali zambiri zadziko, magulu a anthu ali okonzekera kugudukira kuholo lamzinda, kubalalitsa kuzenga mlandu kwapoyera, kuwononga yunivesite, kapena kuphwanya embase. . . . Mkwiyo wofuna ufulu wotheratu ngwaupandu. . . . Kunena mwachidule, cholinga chimodzi chandale zadziko ndi chamayanjano, kapena chifuno chowasonkhezera chanthaŵi ino ndicho kufuna Kudzigangira, mosasamala kanthu za mpangidwe wa nthanthi yakale imene yapangidwako. Ngati uku sindiko Kulephera, mosapeŵeka ndiko Kusweka.”
Kodi “Kusweka” kudzatsogolera mwamsanga ku “Kulephera,” ndipo ngati n’choncho, kodi padzakhala zotulukapo zotani kudziko limene tikukhalamoli? Kunena zowona, ulamuliro wa anthu ukuyesedwa, koma osati kokha ndianthu amene akhala akuyesa maboma awo kwazaka mazana ambiri ndikuwapeza kukhala opereŵera mobwerezabwereza. Panthaŵi ino Mlengi wachilengedwe chonse mwiniyo akulengeza kuŵerengera. Kodi mbiri ya ulamuliro wa anthu ya zaka mazana ambiri ikulungamitsa kuti uloledwe kupitirizabe? Kapena kodi kuyesedwa kwake pamiyeso ya Mulungu kumasonyeza kuti uyenera kuchoka? Ndipo ngati n’choncho, kodi uyenera kuloŵedwa m’malo n’chiyani?
Mpambo wankhani zakuti “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso” udzawonjezera chidziŵitso chanu cha boma. Ndipo udzakupatsani chiyembekezo chifukwa chakuti muli ndi chifukwa chabwino chokhalira wachidaliro. Boma labwinopo liri m’njira. Ndipo chabwino koposa zonse, mungakhale ndi moyo kudzasangalala nalo!
[Zithunzi patsamba 9]
Pamene mbiri ya ulamuliro wa anthu iyesedwa pamiyeso ya chilungamo chaumulungu, kodi chiweruzo cha Mulungu chidzakhala choiyanja?
[Mawu a Chithunzi]
WHO photo/PAHO by J. Vizcarra