Kodi Anthu a Fuko Lina Mumaŵalingalira Motani?
“Anthu atsitsi lalifupi a ku Amereka, mofanana ndi anthu amphamvu atsitsi lalifupi a ku Yuropu, ndiwo gulu la achichepere ogwira ntchito a fuko la Aryan. Timatsutsa chikhoterero cha miyambo yoipa ya malingaliro a chicapitalism ndi chicommunism yomwe ikuwononga fuko lathu la Aryan. . . . Vuto lathu lalikulu nkuloŵerera kwa fuko Lachiyuda.”
CHINATERO chikalata chochokera ku gulu la anthu atsitsi lalifupi okhala mu Chicago. Awa ndiwo anthu achichepere amene amameta tsitsi lawo, kuvala malaya apadera ozindikiritsa munthu kukhala wovuta opetedwa zithunzi za chizindikiro cha maswastika, amapititsa patsogolo chiwawa, amamvetsera ku nyimbo ‘zachingelezi,’ ndikupeputsa Ayuda, akuda, ndi anthu ena ochepa.
Mtsogoleri wa gululi wotchedwa Romantic Violence anafotokozera msonkhano wa atsogoleri atsankho la fuko la azungu okhaokha kuti gulu lake “nlankhondo,” ndipo anawonjezera kuti: “Ine ndine munthu wachiwawa. Ndimakonda fuko la azungu, ndipo ngati munthuwe umakonda chinthu chakutichakuti umakhala munthu wankhalwe kwenikweni padziko lapansi.”
Pamene maguluwa akutha, anthu atsitsi lalifupi ngoŵerengeka. Zolingalira zawo nzopambanitsa. Pali anthu oŵerengeka okha lerolino omwe ngomamatirako poyera ndi ankhalwe. Ndipo komabe, anthu ambiri amasungilirabe chidani mwachinsinsi kwa anthu a fuko lina ndikusawakhulupirira. Padziko lonse lapansi, anthu amaweruzidwa ndi kukhota kwa maso awo kapena mtundu wa khungu lawo. Kodi alipo maziko aliwonse a ichi? Kodi pamakhala kusiyana kobadwa nako kwa malingaliro kapena kaumbidwe m’mafuko? Kuti tiŵayankhe mafunsowa, choyamba tiyenera kusanthula mmene malingaliro osiyanasiyana okhudza fuko abukira m’zaka mazana ambiri.