Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 12/8 tsamba 4-7
  • Zomwe Timadziŵa Ponena za Fuko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Timadziŵa Ponena za Fuko
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuika Anthu M’magulumagulu
  • Zilengezo za UNESCO
  • Mliri wa Tsankho Laufuko
  • Kodi Fuko Nchiyani?
    Galamukani!—1993
  • Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere
    Galamukani!—1993
  • Kusankhana Mitundu
    Galamukani!—2014
  • Kodi Nchifukwa Ninji Nkhani ya Fuko Ili Yaikulu Motero?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 12/8 tsamba 4-7

Zomwe Timadziŵa Ponena za Fuko

PAMENE anthu a ku Yuropu ananyamuka ulendo wapanyanja kukazonda dziko lapansi zaka 500 zapitazo, iwo anadabwa kuti adzakumana ndi anthu a mtundu wanji. Panali nthano zomwe zinasimba kuti kunali zimphona zomwe zidakhoza kuyenda m’nyanja ndikuswa chombo ndi dzanja limodzi. Panali nthano zomwe zinasimba kuti kunali anthu okhala ndi mutu wa galu omwe ankapuma malaŵi a moto. Kodi iwo akakumana ndi anthu omwe anatchedwa kukhala “osayanjana ndi ena,” omwe ankadya nyama yosaphika ndi omwe milomo yawo yaikulu, yotundumuka idawachitira mthunzi kudzuŵa? Kapena kodi iwo akawona anthu opanda pakamwa, omwe anakhala ndi moyo mwa kununkhiza fungo la maepo? Ndipo bwanji ponena za anthu omwe adali ndi makutu aakulu kwambiri kwakuti nkuwuluka nawo kapena anthu omwe anasimbidwa kuti ankagona chagada mumthunzi wa phazi lawo limodzi, lalikulu?

Anthu anapita paulendo wapanyanja, anaŵakwera mapiri, anadidiriza mnkhalango, nayenda uku ndi uko m’zipululu, komatu iwo sanazipeze zolengedwa zachilendo zoterezi kulikonse. Mmalomwake, azondiwa anadabwitsidwa kupeza anthu ofanana kwenikweni ndi iwo. Christopher Columbus analemba kuti: “M’zilumbazi [West Indies] pakali pano sindinapezemo munthu wonga chilombo, monga mmene ambiri anayembekezera, mmalomwake, pakati pa anthuwa kukongola ndiko kwakukulu. . . . Chotero sindinapezepo munthu wonga chilombo kapena mbiri iriyonse yonena za iwo, kupatulapo . . . anthu . . . omwe amadya anthu anzawo . . . Iwo saali osaumbidwa bwino kuposa enawo.”

Kuika Anthu M’magulumagulu

Chotero, ndikuzonda dziko lapansi, kusiyanasiyana kwa anthu kunathetsedwa m’nthano wamba ndi nthanthi. Anthu anapenyetsetsedwa ndi kuphunziridwa. M’kupita kwanthaŵi, asayansi anayesa kuwaika m’magulumagulu.

Mu 1735 katswiri wa zomera wa ku Sweden wotchedwa Carolus Linnaeus anafalitsa Systema Naturae yake. Mu iyo munthu anapatsidwa dzina lachilendo lakuti Homo sapiens, kutanthauza kuti “munthu ngwanzeru,” liwu limene mlembi wina anati mwachiwonekere linali ndi kamasuliridwe koipa kodzikweza kwenikweni koperekedwa ku mtundu uliwonse! Linnaeus anaŵagawa anthu m’magulu asanu, omwe anawafotokoza motere:

M’FIRIKA: Wakuda, wankhokera, waphee. Tsitsi lake nlakuda, lomanganamangana; wakhungu lonyezimira; wamphuno yophaphatala; wamilomo yotundumuka; wokonda kuwumba, waulesi, wosasamala; amadzola mafuta; wolamulidwa ndi malamulo osinthasintha.

WA KU AMEREKA: Wakhungu loyera ngati mkuwa, wamtima wapachala, wongwala; watsitsi lakuda, lowongoka, lochindikala; wamphuno zotseguka; wankhope yokakala; wandevu pang’ono; wosagonjetseka mopepuka, wosakhutiritsidwa; amadzipaka mizere yaing’ono ndi utoto wofiira; amalamulidwa ndi miyambo.

WA KU ASIA: Wamawonekedwe aukali, wosasunthika; watsitsi lakuda; maso ngodera; wozaza, wodzitama, wosirira; wovala malaya osera; wolamulidwa ndi malingaliro.

WA KU ULAYA: Wabwino pang’ono, wodzala ndi chiyembekezo, wanyonga; tsitsi nlachikasu, lofiirira, lonyololoka; maso ake ngobiriŵira; wodekha, waluntha, wokonda kutumba zinthu; amavala malaya okwana; amalamulidwa ndi malamulo.

MUNTHU WAMTHENGO: Wa miyendo inayi, salankhula, waubweya.

Onani kuti pamene kuli kwakuti Linnaeus anaŵaika anthu m’magulumagulu mogwirizana ndi zikhoterero zobadwa nazo (mtundu wakhungu, mawonekedwe a tsitsi, ndi zina zotero), iye analinso wothengera m’kusanthula kwake maumunthuwo. Linnaeus analengeza kuti anthu a ku Ulaya anali “odekha, aluntha, okonda kutumba zinthu,” pamene anthu a ku Asia anawafotokoza kukhala “ozaza, odzitama, osirira” ndipo a ku Afirika anawatcha kukhala “okonda kuwumba, aulesi, osasamala”!

Komatu Linnaeus analakwa. Zikhoterero za maumunthu zoterozo mulibemo m’magulu a fuko lamakono, popeza kuti kufufuza kwasayansi kwasonyeza kuti m’gulu lirilonse la anthu, mumapezeka kusiyanasiyana kwa chibadwa chofanana limodzinso ndi ukulu wofanana wa luntha. Kufotokoza m’mawu ena, m’fuko lirilonse la anthu timawonamo mikhalidwe yabwino ndi yoipa imodzimodziyo.

Madongosolo amakono kaŵirikaŵiri amaika anthu m’magulu atatu ozikidwa kwenikweni pakusiyana kwakuthupi awa: (1) Caucasoids, anthu a khungu losalala ndi tsitsi lowongoka kapena lokwinyanakwinyana; (2) Mongoloids, anthu akhungu lachikasu ndi okhala ndi makwinya m’zikope; ndi (3) Negroids, anthu akhungu lakuda ndi tsitsi lopotanapotana. Komatu simunthu aliyense amene amayenerana ndendende mu lirilonse la maguluwa.

Mwachitsanzo, otchedwa a San ndi a Khoikhoi a kum’mwera kwa Afirika ali ndi khungu lowoneka ngati mkuwa, nditsitsi lopotanapotana, ndi kawonekedwe kankhope kofanana ndi m’gulu la Mongoloid. Amwenye ena ali ndi khungu lakuda koma nkhope zawo nzofanana ndi a m’gulu la Caucasoid. Anthu a ku Australia otchedwa ma Aborigine ali ndi khungu lakuda, komano tsitsi lawo lopotanapotana kaŵirikaŵiri limakhala lofiirira. Anthu a m’gulu la Mongolia ali ndi maso ofanana ndendende ndi amgulu la Caucasoid. Mfundo yabwino yoŵagaŵira anthuŵa kulibeko.

Mavutowa achititsa akatswiri a munthu ndi miyambo yake kuleka kuyesayesa kwawo kuika anthu m’magulumagulu, nangoti liwu lakuti “fuko” liribe tanthauzo kapena phindu lausayansi.

Zilengezo za UNESCO

Mwinamwake zilengezo zamphamvu kwambiri zausayansi zokhudza fuko ndizimene zinapangidwa ndi gulu la akatswiri omwe anasonkhanitsidwa pamodzi ndi UNESCO (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization). Misonkhano inachitidwa mu 1950, 1951, 1964, ndi 1967 pomwe gulu la mitundu yonse ya akatswiri a munthu ndi miyambo yake, akatswiri a nyama, adokotala, akatswiri a ziŵalo zathupi, ndi ena mogwirizana anatulutsa ndemanga zinayi pa fuko. Ndemanga yomalizira inagogomezera mfundo zitatu zotsatirazi:

A “Anthu onse amene ali ndi moyo lerolino ngamtundu umodzi ndipo amachokera ku magwero amodzi.” Mfundoyi yatsimikiziridwadi ndi bukhu lotchuka kwenikweni. Baibulo limati: “[Mulungu] ndi mmodzi [Adamu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.”—Machitidwe 17:26.

Ndemanga ya UNESCO ikupitiriza motere:

B “Kugawidwa kwa magulu a mitundu ya anthu ‘m’mafuko’ mwapang’ono nkochititsidwa ndi miyambo ndipo mwapang’ononso nkochititsidwa ndi zammutu ndipo sikutanthauza gulu lirilonse mpang’ono pomwe. . . .

C “Chidziŵitso chamakono cha zolengedwa sichimativomereza kugwirizanitsa zokwaniritsidwa m’mwambo ndi kusiyana m’maubwino achibadwa. Kusiyana kwa zinthu zokwaniritsidwa ndi anthu osiyanasiyana kuyenera kugwirizanitsidwa kwakukulukulu ndi mbiri ya miyambo yawo. Anthu amdziko lerolino amawonedwa kukhala ndi maubwino achibadwa ofanana a kufikira pamlingo uliwonse wa kutsungula.”

Mliri wa Tsankho Laufuko

Chotero palibe maziko okhulupirira kuti fuko lirilonse nlopambana mwachibadwa kapena kuti liri ndi kuyenerera kulamulira lina. Komano anthu nthaŵi zonse sanagwirizanepo ndi mfundozi. Mwachitsanzo, talingalirani malonda aukapolo a ku Afirika.

Pamene maiko a ku Ulaya anayamba kupanga ufumu wolamulira maiko ena, kunali kodzetsa phindu kwa iwo kudyerera masuku pamutu nzika za maikowo. Komatu padali ukavuŵevuŵe panopa. Nzika mamiliyoni ambiri za ku Afirika zinkakakamizidwa kuchoka m’midzi yawo, kusiyana ndi okondeka awo, kumangidwa unyolo, kukwapulidwa, kuikidwa mikwingwirima, kugulitsidwa monga nyama, ndikukhamanitsidwa kugwira ntchito popanda malipiro kufikira atamwalira. Kodi chinthu choterechi chidalungamitsidwa bwino motani ndi maiko omwe adati anali Achikristu ndi omwe anafunikira kukonda mnansi wawo monga iwo eni?—Luka 10:27.

Yankho limene iwo analisankha linali lakuchitira nkhanza minkhole yawoyo. Uku ndiko kunali kulingalira kwa katswiri wina wa munthu ndi miyambo yake m’ma 1840:

“Ngati Anegro ndi anthu a ku Australia sindiwo zolengedwa zinzathu ndipo sabanja lathu koma anthu a m’gulu la abulutu, ndipo ngati ntchito zathu kwa iwo sizinali zogwirizana . . . ndi malamulo abwino aliwonse pomwe makhalidwe abwino a dziko Lachikristu azikidwa, ndiko kuti unansi wathu ndi mafuko ameneŵa udzalingaliridwa kukhala wosasiyana ndi umene ungalingaliridwe kukhalapo pakati pa ife ndi fuko la anyani.”

Anthu amene anafunafuna kuchilikiza malingaliro akuti anthu omwe siazungu sadali anthu anatenga mfundozi m’nthanthi ya chisinthiko cha Darwin. Iwo anatsutsa naati, anthu olamulidwa ndi maiko enawo adali a mumzere wapansi wa chisinthiko kuposa azungu. Ena anati anthu omwe saali azungu adachokera m’dongosolo la chisinthiko chosiyana ndipo sadali anthu enieni. Ena anagwira mawu a Baibulo, napotoza malemba ncholinga cha kuchilikiza malingaliro awo atsankho laufukolo.

Ndithudi, anthu ambiri sanakhulupirire malingalirowa. Ukapolo unathetsedwa m’maiko ambiri adziko. Koma kupatulana, kunyada, ndi tsankho laufuko nzomwe zakhalapobe ndipo zafalikira m’magulu achilengedwe omwe adali mafuko m’malingaliro okha a anthu. Profesa wina wa nyama adati: “Popeza kuti kungawoneke kuti aliyense ngwaufulu kudzipangira mafuko oyenera kuganiza kwake, andale zadziko, ochonderera apadera, ndi ofufuza zinthu poyera adziphatika m’ntchito yogaŵa mafuko. Iwo anapanga maina ambiri a mafuko kuti asindikize kutchuka kwaulemu wa ‘sayansi’ pamalingaliro awo ochepawo ndi kunyada.”

Malamulo atsankho laufuko a Jeremani Yachinazi ndiwo chitsanzo chachikulu. Chinkana kuti Adolf Hitler anakweza fuko la Aryan, mwachibadwa palibe chinthu choterechi. Kunalibe ngakhale kumbuyoko. Muli Ayuda atsitsi lofiirira, amaso obiriŵira m’Sweden, muli Ayuda akuda mu Ethiopia, ndipo muli Ayuda m’gulu la Mongoloid mu China. Komabe, Ayuda, ndi ena, adali minkhole ya lamulo la tsankho laufuko. Lamulo limenelo linatsogolera kuika anthu m’ndende zachibalo, ndende zapaizoni, ndi kuphedwa kwa Ayuda mamiliyoni asanu ndi mmodzi ndi ena ambiri, onga ngati anthu a Slavic a ku Poland ndi Soviet Union.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kufufuza kwa sayansi kwasonyeza kuti m’gulu lirilonse la anthu, mumapezeka kusiyanasiyana kofanana kwa luntha

[Mawu Otsindika patsamba 6]

‘Andale zadziko, atsogoleri apadera, ndi ofufuza zinthu poyera apanga maina ambiri a mafuko kuti asindikize kutchuka kwaulemu wa “sayansi” pamalingaliro awo ochepawo ndi kunyada’

[Zithunzi patsamba 7]

Monga mmene chidziŵitsochi chikusonyezera, anthu a ku Afirika anasatsidwa malonda ndikugulitsidwa ngati kuti adali ng’ombe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena