Kum’mawa kwa Yuropu—Kodi Kukuvomerezanso Chipembedzo?
KUPONDEREZA ufulu wa kunenapo kanthu m’zaka makumi ambiri zapitazo m’maiko a Kum’mawa kwa Yuropu kwaphatikizapo ziletso zamphamvu pachipembedzo. Kusakhulupirira Mulungu kunkalalikiridwa mokangalika, ndipo nyumba zina zopempherera ndi matchalitchi zinasinthidwa kukhala mowonetsera mfundo za kusakhulupirira Mulungu, monga ngati imene imachezeredwa ndi odzacheza ambiri mu Leningrad. Mtsogoleri wachipembedzo wokangalika aliyense anakhala kapolo wa ufumu wapanthaŵiyo. Popeza kuti nyumba zonse zolambirira, monga ngati, mamonastery, matchalitchi, ndi misikiti, zinatsekedwa mwalamulo mu 1967, Albania inalengezedwadi ndi Nyumba ya Wailesi ya Tirana kukhala “dziko loyamba la osakhulupirira Mulungu padziko.”
Tsopano, popeza kuti ufulu ukutumphuka kulikonse Kum’mawa kwa Yuropu mofanana ndi maluŵa a m’nyengo ya ngululu, kodi nchiyani chomwe chikuchitikira chipembedzo? Wolemba nkhani Wachifrench wotchedwa Jean-François Kahn analemba motere: “Chipembedzo choponderezedwa ndi nkhalwe chingagwirizane ndi dziko limene laponderezedwa ndi nkhalwe. Izi zinachitika dzulo mu Iran. Zikuchitikanso lerolino m’Soviet Azerbaijan. Mawa zingafalikire ku Russia mofanana ndi moto wa m’nkhalango.” Ngakhale tsopano lino zipembedzo zina zikudzigwirizanitsa zokha ndi malingaliro ndi maloto autundu ndipo zikukhala chimodzi cha zinthu zazikulu zofalitsira kuwukira kwandale zadziko, naziyeretsa ndikukhalamo kwa ansembe awo Achikatolika ndi a Orthodox ndi apasitala a Lutheran.
Chotero kodi ufulu wa chipembedzo ukusamaliridwa motani mumkhalidwe wa democracy yatsopano?
Mmene Zinthu Zasinthira!
Zipembedzo zazikulu za Kum’mawa kwa Yuropu, makamaka Tchalitchi cha Katolika, zachitapo kanthu mofulumira kulembetsa mwalamulo m’maboma atsopanowo. Mwachitsanzo, L’Osservatore Romano inasimba kuti “pa 9 February [1990], Chikalata cha Chimvano chinasainidwa pakati pa Malikulu Oyera ndi Ripabuliki la Hungary.” M’chimvanochi magulu aŵiriwo anamvana kukhazikitsanso maunansi awo. (Vatican payokha imalingaliridwa kukhala boma lolamulira.)
Lipoti lina lochokera ku Vatican likunena kuti Tchalitchi cha Katolika cha ku Ukrainian Rite, choponderezedwa mu 1946, chapemphanso kuti chilembetsedwe mwalamulo ndipo chayamba kukambirana “ndi Boma ndi Tchalitchi cha ku Russia cha Orthodox pamafunso opindulitsa onena zamoyo wa Tchalitchi mu Ukraine.”
Mu April 1990 papa anakacheza ku Chekoslovakiya ndipo analonjeredwa pabwalo la ndege la Prague “ndi nduna zazikulu za Tchalitchi ndi Boma, kuphatikizapo . . . Mr. Vaclav Havel, Pulezidenti wa Ripabulikilo.” (L’Osservatore Romano) Unansi watsopano wachipembedzo ukuyambikanso kumeneko.
Tchalitchi cha Katolika nthaŵi zonse chakakamiza kuzindikiridwa m’Poland. Tsopano, ndiufulu wake wopezedwa chatsopanowu, icho chikuchokocha mphamvu zake ndikuchita ndawala ya kutsegulanso makalasi achipembedzo m’sukulu. Wansembe wina anati: “Sukulu ndizo chuma chadziko. Dziko la Poland liri ndi Akatolika oposa 90 peresenti. . . . Pofuna kulemekeza zipembedzo zina, malangizo achipembedzo m’sukulu adzabwezeretsa ulamuliro kwa aphunzitsi, ndi . . . akuluakulu chifukwa amakhudza mabande a munthu.”
Lipoti losimba za Tchalitchi cha Orthodox m’Romania likuti: “Akuluakulu atchalitchi ndi abishopu ambiri amene anagwirizana ndi ufumu [wa Ceauşescu] anakakamizidwa kuleka ntchito. Komiti inakhazikitsidwa kukangalitsanso Tchalitchi. Ambiri omwe kale sanali akhulupiriri akutembenukira kuchipembedzo ndikudzaza matchalitchi a kumaloko . . . Tchalitchi cha Katolika cha pa Byzantine ku Romania, chomwe chinakakamizidwa kutsekedwa zaka 40 zapitazo, chaloledwa kulinganidwazanso.”—Orthodox Unity, July 1990.
Masinthidwe m’Albania
Mogwirizana ndi malipoti am’nyuzi, masinthidwe odabwitsa akuchitika pang’onopang’ono m’Albania, dziko laling’no lamapiri lokhala ndi nzika mamiliyoni atatu ndi nusu, lokhala pamtunda pa gombe lotchedwa Adriatic Coast pakati pa Yugoslavia ndi Grisi. Nyuzipepala Yachijeremani yotchedwa Die Welt inasimba kuti: “Mu Albania, dziko lotsirizira kumamatira kunjira ya communism yakale mu Yuropu, anthu ayamba kuchita masankho ndi zala zawo zakumapazi” mwa kufunafuna kothaŵira m’maofesi a akazembe a Kumadzulo, kuchokera uku mpomwe adaloledwa kunka ku Italy, Jeremani, ndi maiko ena.
Lipotilo likupitiriza motere: “Mu May 1990 nzika za ku Albania zinalonjezedwa kupatsidwa mapasipoti ndikuchotsapo malamulo oletsa kuloŵa chipembedzo chirichonse.” (Mawu ogwidwa kuchokera mu The German Tribune, July 15, 1990) Monga momwe profesa wa mbiri yakale Denis R. Janz analembera motere: “Nkhondo yanthaŵi yaitali yomenyera malamulo mwakalavulagaga idalingaliridwa kuti inanyalanyazidwa.” Komabe, iye akuwonjezera kuti: “Pali umboni . . . wakuti kwenikweni chipembedzo chapululutsidwa m’chitaganyachi.”
M’vutoli Mboni za Yehova zikusungabe mwambo wawo wauchete mosamalitsa. Pamaziko a malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, iwo samadziphatika m’mipatuko yandale zadziko ndi yautundu. Iwo amakhulupirira Mulungu kuwapatsa makhazikitsidwe amtendere okwaniritsira ntchito yawo yapadziko lonse lapansi ya kulalikira Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 22:21; 1 Timoteo 2:1, 2; 1 Petro 2:13-15.
Chotero, bwanji ponena za Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu? Kodi izo zapita patsogolo pansi pa chiletso? Kodi ali nawo ufulu wa chipembedzo?
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi anthu adzabwerera ku matchalitchi a Kum’mawa kwa Yuropu?