Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 1/8 tsamba 8-13
  • Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mboni za Yehova mu Soviet Union
  • Kupita Patsogolo m’Poland
  • Ufulu wa Chipembedzo m’Romania
  • Mbiri Yabwino Yochokera ku Hungary
  • Pakuguba m’Chekoslovakiya
  • Ziyembekezo Zamtsogolo
  • Chiwonjezeko Chodabwitsa
    Galamukani!—1992
  • ‘Ndipo Khoma Linagwa Pansi’
    Galamukani!—1991
  • Anadabwa ndi Zimene Anawona
    Galamukani!—1992
  • Anasangalala Kum’maŵa kwa Yuropu
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 1/8 tsamba 8-13

Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu

PAMENE Khoma la Berlin linagwa mu November 1989, Asiaweek inasimba kuti “nzika 2 miliyoni za Jeremani ya Kum’mawa zinathamangira kukaloŵa kutheka lakumadzulo la dziko lawo logawanikanalo m’masiku aŵiri pambuyo pakutsegula malire kwa Berlin ya Kum’mawa.” Kodi unali ulendo wanji?

Kwa amponda matiki, unali ulendo wogula zosangulutsa. Kwa ena, udali ulendo wongokhumbira katundu m’masitolo ndikulaŵa ufulu wawo wopezedwa chatsopanowo. Anthu ambiri anapeza Mboni za Yehova ziri m’makwalala a Berlin ndi mizinda ina ndipo analandira mabuku opatsidwa ndi iwo. Chiyambire nthaŵiyo, ena alembera ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu Selters, pafupi ndi Frankfurt am Main, akumafotokoza chivomerezo chodabwitsa.

Kalata ina inati: “Pamene ndinakacheza Kumadzulo kwa Berlin kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinalandira kope la Nsanja ya Olonda monga mphatso yochokera kwa Mboni za Yehova pakhwalala. Chiyambire pamenepo, ndayambanso kuŵerenga Baibulo, ndipo ngakhale kuti ndiri nawo mavuto ambirimbiri, wapezekanso wina wondipatsa chiyembekezo ndi chisangalalo cha kukhala ndi moyo. Ndingakondwere kwambiri kuŵerenga bukhu lakuti Your Youth—Getting the Best out of It. Ndingakondenso kugwirizana ndi Mboni za Yehova.”

Wocheza wina analemba motere: “Pamene ndinkapyola mlikole kunka kuchitesheni chachikulu mu Nuremberg, dona wina anandipatsa makope a Galamukani! ndi Nsanja ya Olonda. Ndinakondwera pamene ndinaŵaŵerenga. Kwamasiku angapo ndakhala ndikugwiritsiranso ntchito Baibulo tsiku ndi tsiku.”

Misonkhano ya Mboni za Yehova inachitidwira m’mizinda yaikulu Kum’mawa kwa Yuropu m’chilimwe cha 1990. Bwalo Lamaseŵera la Olympia lokhala m’yomwe kale inkatchedwa kwa Berlin Kum’madzulo ndilo linali malo amsonkhano umodzi kumene Mboni zidapezekako kuchokera m’maiko ambiri, kuphatikizapo kum’mawa kwa Jeremani. Kwayerekezedwa kuti pakati pa anthu 44,532 omwe anapezekapo, anthu 30,000 anachokera kum’mawa kwa Jeremani. Nyuzipepala yakuti Berliner Morgenpost inasimba kuti Mboni zatsopano 1,017 zinabatizidwa m’dziŵe losambira la Olympic, akumagwiritsira ntchito njira ya kumiziratu munthu m’madzi, imene “okhalamo ndi phandewo anamamatira nayo kunjira ya Akristu oyambirira.”

Kodi zinthu zasintha motani kum’mawa kwa Jeremani? Mu March 1990 manyuzipepala a Jeremani Yakum’mawa analengeza kulembetsedwa mwalamulo kwa Mboni za Yehova. M’mutu wakuti “Mboni za Yehova Zikhalanso Zalamulo,” nyuzipepala ya ku Jeremani Yakum’mawa yotchedwa Mitteldeutsche Zeitung inati: “March 14 inatsimikizira kukhala mapeto a chiletso chimene chinakhalapo kwa zaka makumi anayi. Patsikuli oimira Mboni za Yehova a ku Jeremani anakhoza kutuluka m’nyumba Yaboma Yosamalira Ntchito za Tchalitchi ya G[erman] D[emocratic] R[epublic] ali ndi chikalata chalamulo m’thumba mwawo chovomerezanso kulondola chikhulupiriro cha chipembedzo chawo mwaufulu m’dziko la GDR.”

Kalata yolandiridwa m’nyengo ya ngululu yapita kuchokera kwa Mboni yokhala mu Leipzig ikusimba nkhani motere: “Mlungu umodzi wapitawo tinkalowetsabe chakudya chauzimu mwachinsinsi pang’onopang’ono. Tsopano [March 14, 1990] tazindikiridwa mwalamulo! Posachedwapa tidzakhala tikutsitsa katundu wa mabuku wolemera matani anayi pagalimoto!” Kwenikweni, galimoto loyamba kuloŵa m’Jeremani Yakum’mawa linalongedwa ndi matani 25 a mabuku Abaibulo, ndipo m’miyezi iŵiri yotsatira, matani owonjezereka 250 anatumizidwanso. Iyi inali njala yauzimu ya Mboni zomwe zinamanidwa ufulu kwa zaka 40!

Titakumbukira kuti zonse ziŵiri Chinazi (1933-45) ndi Communism anayesa kuthetsa Mboni m’Jeremani, ntchito yawo yamphamvu yamakedzana ndi yamakono ndiyo umboni wabwino waumphumphu wawo ndi dalitso la Mulungu pa iwo.

Mboni za Yehova mu Soviet Union

Mu December 1989, Mikhail Gorbachev anakumana ndi Papa John Paul II mu Vatican. Nyuzipepala ya ku Soviet Pravda inasimba Gorbachev kukhala akunena za makambitsiranowo kuti: “Tinali ndi makambitsirano omvana ndi atanthauzo. . . . Tinakambirana za chipembedzo ndi njira zofananazo zomwe zikuchitika m’Yuropu, m’dziko, ndi Soviet Union.” L’Osservatore Romano, nyuzipepala yalamulo ya ku Vatican, inasimba kuti Bwana Gorbachev m’kufotokoza kwake kwa papa anati: “Anthu a zikhulupiriro zambiri, kuphatikizapo Akristu, Asilamu, Ayuda, Abuddha ndi ena, alimo mu Soviet Union. Onseŵa ali ndi kuyenerera kwa kukhutiritsa zosoŵa zawo zauzimu. Posachedwapa, Lamulo pa Ufulu wa Chikumbumtima lidzavomerezedwa m’dziko mwathu.”

Mogwirizana ndendende ndi mawuwo, mu September 1990 bungwe la ku Soviet lopanga malamulo linavomereza lamulo lolola ufulu wa chikumbumtima. Mfundo 3 ya lamulo lolembedwalo ikuti: “Mogwirizana ndi kuyenerera ufulu wa chikumbumtima, nzika iriyonse iyenera kudzisankhira chipembedzo choti igwirizane nacho, ali nako kuyenerera kulondola chipembedzo chirichonse payekha kapena limodzi ndi ena kapena kusalondola chirichonse, ali nako kuyenerera kwa kufotokoza ndi kufalitsa zikhulupiriro zogwirizana ndi chipembedzo chake.”

Muli Mboni za Yehova zikwi zambiri mu Soviet Union zomwe zikuyembekezera kusonyeza ufulu wa chipembedzo. (Onani patsamba 22.) Kaamba ka Misonkhano ya “Chinenero Choyera” ya mu 1990, nthumwi zoposa 17,000 zochokera ku Soviet Union zinapezeka pamsonkhano wa ku Russia mu Warsaw kuimira Mboni zofalikira mu Soviet Union monse. Iwo akuyembekezera tsiku limene kudzakhala kothekera kukhala ndi misonkhano mu Soviet Union.

Kupita Patsogolo m’Poland

Mboni za Yehova zinavomerezedwa mwalamulo m’Poland mu May 1989. Chiyambire pamenepo ofesi yanthambi yakhazikitsidwa, ndipo nyumba yofutukulidwa ikumangidwa pafupi ndi Warsaw. Poyamba, Mboni zachichepere mazana ambiri zinkaikidwa m’ndende chifukwa cha nkhani yauchete Wachikristu. Tsopano akupatulidwa pautumiki wankhondo ndikupatsidwa chilango atangosonyeza chikalata choyenerera.

Misonkhano yochitidwira m’Poland mu 1989 ndi 1990 yakhala chosonkhezera china chachikulu kwa Mboni zokhala kumeneko. Lipoti lina linati chiŵerengero cha Mboni zokangalika m’Poland chinakwera mwezi uliwonse chaka chatha, ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano choposa pa 97,000. Poland posachedwapa idzakhala dziko la nambala 12 lokhala ndi Mboni zoposa pa 100,000.a Opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu April anali anthu 188,861.

Ufulu wa Chipembedzo m’Romania

Mboni zokhala mu Romania zinasangalatsidwa kumva kuti gulu lawo linavomerezedwa mwalamulo mu April 1990. (Onani bokosi, patsamba 13.) Mosataya nthaŵi misonkhano yadera inalinganizidwa m’dziko lonselo, ndipo m’mpambo umodzi anthu oposa 44,000 anapezekapo, chikhalirecho munali Mboni pafupifupi 19,000 zokha m’dzikolo panthaŵiyo. Motsimikizirika nzika za ku Romania zambiri zikuvomereza ku uthenga wa Ufumu.

Misonkhano yachigawo yapadziko lonse yokhala ndi mutu wa mu 1990 wakuti “Chinenero Choyera” inachitidwira m’mizinda ya Brasov ndi Cluj-Napoca. Programu inatsogozedwa m’chinenero cha ku Romania ndi cha ku Hungary. Anthu oposa 36,000 anapezekapo, ndipo 1,445 anabatizidwa.

Ndi kope January 1, 1991, la Nsanja ya Olonda m’chinenero cha ku Romania inayamba kufalitsidwira panthaŵi imodzi ndi ya Chingelezi ndikusindikizidwa m’mitundumitundu.

Mu Bulgaria wapafupi, kumene tchalitchi cha Eastern Orthodox chiri chofala kwambiri, Mboni sizidavomerezedwebe mwalamulo koma zikuchita lendi zipinda kaamba ka misonkhano yawo yampingo. Anthu oposa mazana aŵiri ananka ku Salonika, Grisi, kaamba ka Msonkhano wa “Chinenero Choyera” wochitidwa m’chinenero cha ku Bulgaria ndi Chigiriki.

Mbiri Yabwino Yochokera ku Hungary

June 27, 1989, linali tsiku lam’mbiri kwa Mboni mu Hungary. Nyuzipepala yotchedwa Magyar Nemzet inalengeza kuti: “Ofesi Yaboma Yosamalira Nkhani za Tchalitchi inalengeza gulu la chipembedzo cha Mboni za Yehova mu Hungary, mogwirizana ndi lamulo lomvana ndi ufulu wachipembedzo, kukhala chikhulupiriro chachipembedzo chovomerezedwa mwalamulo.” Nyuziyi inalengezedwa pawailesi ndi pa TV. Nzika za ku Hungary zinamva kuti pomalizira pake Jehova Tanúi (Mboni za Yehova) zinavomerezedwa kuchita ntchito yawo mwalamulo.

Kuti akwaniritse zigawo zazikulu za dzikolo, Misonkhano ya “Chinenero Choyera” inachitidwira m’Pecs, Miskolc, Debrecen, ndi Budapest. Anthu okwanira 2,000 omwe analankhula chinenero cha ku Hungary anachokera ku Chekoslovakiya ndi Soviet Union. Kuzindikiritsa umodzi wa mitundu yonse wa Mboni za Yehova, gulu la nthumwi zodzacheza 700 zochokera ku Finland zinapezekapo. Chiwonkhetso cha opezekapo mu Hungary chinali 21,568, kuphatikizapo nthumwi za ku Romania zoposa 2,000.

Chiyambire January 1990, Mboni za ku Hungary zakhala zikulandira magazini awo m’mitundumitundu mokhazikika, yotembenuzidwa ndikutulukira pamodzi ndi chinenero choyambirira cha Chingelezi.

Pakuguba m’Chekoslovakiya

M’dziko lokongolali la mapiri okakala ndi zipululu zachonde, Mboni za Yehova nzotanganitsidwa kuthandiza anansi awo kuphunzira zambiri ponena za Baibulo. Lipoti lonena za ntchito yawo likuti: “Ntchito ikuchitidwira poyera, ndipo misonkhano yaikulu ikuchitidwa.”

Pambuyo pamasinthidwe ozizwitsa a Kum’mawa kwa Yuropu ochitika kumapeto kwa 1989, Mboni za mu Chekoslovakiya zinavomereza mofulumira ndikulinganiza mpambo wa misonkhano yadera m’miyezi ya April mpaka June 1990. Monga chotulukapo, kwanthaŵi yoyamba, padali malipoti abwino m’manyuzipepala onena za Mboni. Pakali pano, muli Mboni zoposa 21,000 mu Chekoslovakiya, ndipo mu 1990 panali opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu okwanira 40,295. Mipingo yoposa theka yayamba kale kuchita lendi malo ochitirako misonkhano, ndipo mipingo 12 ilidi nazo Nyumba zawo Zaufumu.

Msonkhano unachitidwa mu Prague mu August 1990, ndi chiŵerengero cha opezekapo okwanira 23,876, ndipo 1,824 anabatizidwa. Kuti apangitse bwalo lamaseŵeralo kuwoneka laudongo kaamba ka msonkhano, Mboni zoposa 9,500 zinawononga maola 58,000 mwaufulu zikuyeretsa ndikupaka utoto. Woimira TV ya ku Chekoslovakiya anathirira ndemanga kuti: “Ife takhala tikuchezera zochitika zamayanjano zambirimbiri, koma takukhumbira kulinganizika kwanu m’bwalo lamaseŵera muno. Nchovuta kuti tikhulupirire kuti inuyo mukulinganiza msonkhanowu kwanthaŵi yoyamba.” Wodzacheza wina anati: “Ndimakhumbira mkhalidwe wauzimu, unansi wabwino, ndi chikondi chokhala pakati pa abale anu. Ndinabwera kuno monga bwenzi; ndikuchokapo ndiridi bwenzi lenileni.”

Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akufalitsidwa m’mitundumitundu m’zinenero za ku Chekoslovakiya ndi Slovak, ndipo Nsanja ya Olonda ikutulukira panthaŵi imodzi ndi ya Chingelezi m’zinenero zonse ziŵirizi. Titakumbukira mkhalidwe wopondereza wa m’chaka chimodzi chokha chapitacho, mukhoza kuvomereza kuti aŵa ndimasinthidwe odabwitsa.

Ziyembekezo Zamtsogolo

Kodi nziti zomwe ziri ziyembekezo za kulalikira kwa Mboni m’maiko kumene mibadwo yatsopano yaleredwera m’kukhulupirira kusakhalako kwa Mulungu? Lipoti lina likuti: “Muli umbuli wa kusadziŵa Baibulo ndi Mulungu. Komabe, chabwino nchakuti, anthu ngosasokonezedwa ndi ziphunzitso zonama zachipembedzo zimene zingafunikire kuchotsedwa. Chikuwoneka kuti kututa kudzakhala kwakukulu.”

Chotero, kodi ndiuthenga uti umene Mboni za Yehova zidzafunikira kuwupereka kwa anthu a Kum’mawa kwa Yuropu kuchokera m’Baibulo? Nkhani yotsatira idzayankha.

[Mawu a M’munsi]

a Maiko ena 11 ndiwo Brazil, Briteni, Canada, Falansa, Jeremani, Italy, Japan, Mexico, Nigeria, Philippines, ndi United States.

[Bokosi pamasamba 8, 9]

Pomalizira Pake Wapezeka Ufulu Wachipembedzo!

Zotsatirazi ndizo ndemanga zothiriridwa ndi Mboni zochokera ku yomwe kale inali Jeremani Yakum’mawa zimene zinapezeka pa Msonkhano wa “Chinenero Choyera” m’Berlin, July 1990.

“Dzina langa ndine Lydia. Ndiri ndi zaka zisanu ndi zitatu zakubadwa, ndipo ndichokera ku GDR [German Democratic Republic]. Ndasangalala kwambiri kupezeka pamsonkhano wachigawo uno chifukwa chakuti chaka chimodzi chapitacho, malire anali otsekedwa. Tidafunikira kuchita phwando la Chikumbutso mwakabisira. Tsopano tikuchitira zinthu poyera! Pamene munthu aliyense ayamba kuimba, misozi imatuluka. Ndasangalatsidwa kwambiri kwakuti ndidzafunikira kuchisimba ichi kusukulu!”

“ Tadzazidwa ndi chikondwerereo ndi chiyamikiro cha kukhala alendo a Yehova muno mu Berlin pakati paubale wa m’mitundu yonse.”—Bernd.

“Chenicheni chakuti abale a ku GDR analiponso paprogramu chikusonya kumbali yapadera yakuti: Yehova amaphunzitsa ndi kuyeneretsa anthu ake ngakhale pamene ali pansi pa chiletso.”—Gottfried.

“Kuwomba m’manja ndikuimba kunasonyeza kuti aliyense anali wachimwemwe. Kudali kuimba kwamphamvu kumene kunapangitsa munthuwe kufuna kuvina. Yehova ayenera kukhala anasangalatsidwa chotani nanga!”—Egon.

“Pambuyo pa kubatizidwa kwanga abale ena anandifunsa ngati madziwo adali ozizira kwambiri. Ndinangoŵayankha kuti sindikudziŵa. Dalitso la Yehova lidali lofunda kwambiri kwakuti madziwo sindinawamve ngati anali ozizira kapena ofunda.”—Heidrun.

“Unansi wokhala m’nyumba zogonamo unali wosafotokozeka! Ochokera ku Denmark, Mozambique, Mangalande, California, kum’mwera kwa Jeremani, Spanya, GDR—tonsefe tinaimbira pamodzi, tonsefe tinkalankhula ‘chinenero choyera.’”—Jutta.

“Nthaŵi zonse tinasimbira ana athu zikumbukiro za misonkhano ya mu 1958 ndi mu 1960 ya ku Berlin, yomwe tinapezekako kwanthaŵi yomalizira. Koma chomwe tinakumana nacho tsopano chinaposa zikumbukiro ndi ziyembekezo zathu zonsezo.”—Wolfgang.

“Chomwe chinatisangalatsa koposa chinali pamene zikwi zambiri zinaimirira ndikuimba ndi kutamanda Yehova, makamaka m’nyimbo ndi pemphero lomalizira. Tinalephera kugwira misozi yathu.”—Monika ndi Reinhard.

[Bokosi patsamba 13]

“Chisalungamo Chinawongoleredwa”

Pansi pamutu wankhani umenewo nyuzi inasimbidwa m’magazini a ku Romania Tineretul liber (Achichepere Aufulu) ya August 11, 1990. Iyo inati: “Inde, chisalungamo chinawongoleredwa. Gulu lachipembedzo lowukiridwa kwambiri la ‘Mboni za Yehova,’ zomwe zasunga umphumphu wawo monga atsatiri a Kristu kwazaka zoposa 40, lavomerezedwa mwalamulo, lapatsidwa chikalata cha kukhazikitsidwa kwalamulo. Gululi limachita ntchito yake pansi pauyang’aniro wa Bungwe Lolamulira, monga gulu lapadziko lonse, lomwe nlokangalika m’maiko ndi zisumbu 210.” Nyuziyo inamaliza mwa kulengeza msonkhano wochitidwa mu August mu Brasov ndi Cluj-Napoca.

[Zithunzi patsamba 9]

Ntchito pamsonkhano: (kuchokera chakunsi kumanzere, kunka motsatizanatsatizana) kugaŵira brosha yatsopano mu Warsaw; maplatifomu a ku Hungary ndi Romania, Budapest; kulemba mfundo, m’Berlin; kuyeretsa bwalo lamaseŵera msonkhano usadakhale, m’Prague

[Zithunzi patsamba 10]

Ntchito zapamsonkhano: (kuchokera kulamanzere, kunka motsatizanatsatizana) ubatizo, m’Romania; bwalo lamaseŵera, m’Prague; banja liri ndi bukhu la “Mankind’s Search for God” mu Berlin; mlankhuli m’Budapest; kusanthula Baibulo m’Poland

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena