Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 4/8 tsamba 3-4
  • Zopinga Mtendere Pakati pa Munthu ndi Chilombo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zopinga Mtendere Pakati pa Munthu ndi Chilombo
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Munthu Ali Chopinga
  • Zodya Anthu
  • Mtendere Wapadziko Lonse Unanenedweratu
  • Nyalugwe—Mphaka Wochita Zinthu Mwakachetechete
    Galamukani!—1995
  • Kulimbana ndi Zilombo Ziwiri Zoopsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudzanso Adani a Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Munthu ndi Chilombo Angakhale Pamtendere?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 4/8 tsamba 3-4

Zopinga Mtendere Pakati pa Munthu ndi Chilombo

Zithunzithunzi zonga chomwe chiri pachikuto cha magazini ano nzosangalatsa kwa ana. Akulu nawonso amakopeka ndi malo oterowo.

Kodi nchifukwa ninji anthu amachita mwanjira imeneyi? Kodi mtendere weniweni pakati pa munthu ndi chilombo ngakhale cholusa koposa uli chabe loto lachibwana? Kapena kodi udzakhala weniweni?

Munthu Ali Chopinga

Chopinga chachikulu cha mtendere woterowo ndi munthu iyemwini. Mwambi wakale umati: ‘Wina apweteka mnzake pomlamulira.’ (Mlaliki 8:9) Ndipo mbiri ya munthu yakupweteka munthu mnzake imasonyezedwa ndi mmene amachitira ndi nyama.

Mwachitsanzo, zilombo zakuthengo zosiyanasiyana zinagwidwa ndi kumenyanitsidwa m’mabwalo a Roma wakale. Zikusimbidwa kuti mu 106 C.E., wolamulira Wachiroma Trajan anakonza maseŵera amene anthu omenyana ndi zilombo okwanira 10,000 ndi zilombo 11,000 anafa kaamba kofuna kukhutiritsa chilakolako cha ochemerera okondweretsedwa ndi nkhanza ya kukhetsa mwazi.

Zowona, maseŵera amtundu umenewo siotchuka masiku ano. Koma ndandanda yomakulakulabe ya mitundu ya nyama zosoloka ndi zokhala paupandu ikuchitira umboni kuti chinachake ncholakwika ndi mmene munthu akuchitira nazo zolengedwa zakuthengo. Pamene chiŵerengero cha anthu chikukula mopambanitsa, malo okhalako nyama zakuthengo akucheperachepera. Ndipo chifukwa cha umbombo wa anthu, zikopa za nyama, nyanga, ndi minyanga zachilendo zikufunidwa. Akatswiri ena akuwopa kuti mitundu ya nyama zazikulu koposa m’kupita kwa nthaŵi idzangotsala m’mapaki osungiramo nyama.

Zodya Anthu

Chopinga mtendere china chingawonekere kukhala zilombo zakuthengo zenizenizo. Mu Afirika ndi Asia, sikwachilendo kuŵerenga malipoti onena za zilombo zakuthengo zomwe zagwira ndikupha anthu. The Guinness Book of Animal Facts and Feats imanena kuti nyama za m’banja la mphaka “mothekera zimachititsa pafupifupi imfa 1000 pachaka.” Mu India mokha, ma tiger amapha anthu oposa 50 chaka chirichonse. Anyalugwe ena m’dzikolo akhalanso odya anthu.

M’bukhu lake lakuti Dangerous to Man, Roger Caras amalongosola kuti anyalugwe nthaŵi zina amayamba kudya anthu pambuyo podya mitembo ya anthu ophedwa ndi miliri yachaola. Iye akulongosola kuti, miliri yoteroyo kaŵirikaŵiri “yatsatiridwa ndi miyezi yochititsa mantha pamene anyalugwe amadya nyama yatsopano ya anthu ndikuyamba kumawapha.”

Koma Caras akunena kuti miliri yachaola imeneyi sindiyo imachititsa kuukira konse kwa anyalugwe. Chochititsa china ndi kumyuka mtima kwa nyamayo, makamaka pamene ili pafupi ndi ana.

M’zaka za 1918-26, nyalugwe wina mu India anapha anthu 125, malinga ndi lipoti loperekedwa ndi Colonel J. Corbett m’bukhu lake lakuti The Man-Eating Leopard of Rudraprayag. Zaka makumi angapo pambuyo pake, anyalugwe odya anthu anapha pafupifupi anthu 82 m’boma la Bhagalpur.

Wogwira ntchito yoyang’anira nyama m’Tanganyika (tsopano yokhala mbali ya Tanzania) anasimba mmene anathera miyezi isanu mu 1950 akuyesayesa mosaphula kanthu kuti aphe ndi mfuti nyalugwe yemwe anasakaza anthu apamudzi wa Ruponda. Potsirizira pake, atapha ana 18, anakoledwa mumsampa wa munthu wakumudzi Wachiafirika. Nyalugwe wina anapha akazi ndi ana 26 m’mudzi wa Masaguru.

Kenaka pali mkango wa mu Afirika. Pamene usinthira kukudya anthu, kaŵirikaŵiri minkhole yake imakhala amuna achikulire. “M’zaka makumi aŵiri mphambu zitatu zomwe ndagwira ntchito m’Dipatimenti Yazanyama,” akulemba motero C. Ionides m’bukhu lake lakuti Mambas and Man-Eaters, “Ndinapha ndi mfuti mikango yoposa makumi anayi, yochuluka ya iyo inali yodya anthu, pamene yotsalayo inali inangoyamba kukhala yodya anthu kapena yogwira ziŵeto.” Mogwirizana ndi Ionides, mikango imalusira anthu pamene munthu amapha kwakukulu minkhole yawo ya nthaŵi zonse.

Mtendere Wapadziko Lonse Unanenedweratu

Mosasamala kanthu za zopinga mtendere zoterozo pakati pa munthu ndi chilombo, Baibulo limati: ‘Mtundu uliwonse wa zilombo . . . zimazoloŵeretsedwa, ndipo zazoloŵeretsedwa ndi anthu.’—Yakobo 3:7.

Baibulo limaneneratu pa Ezekieli 34:25 kuti: ‘[Ine Mulungu] ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndikuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m’chipululu, ndi kugona kunkhalango.’

Kodi maulosi Abaibulo oterowo ali maloto wamba? Musanatsutse chiyembekezo cha mtendere wapadziko lonse pakati pa munthu ndi chilombo, talingalirani zilozero zina zosonyeza kuwona kwake kwa zimene Baibulo limanena. Zitsanzo zina zozizwitsa za kugwirizana kokhala pakati pa anthu osamalira ndi zilombo zolusa kwenikweni zalembedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena