Wonyenga Wamkulu Wochokera—M’Zigama
LARRY analingalira kuti anali kuchita misala. Kwamiyezi isanu ndi iŵiri iye ankamvabe phokoso lalikulu lolira mofuula ndi lodzuma. Iye anapita kwa katswiri wa matenda a mkati mwa thupi ndiponso kwa katswiri wa makutu. Onsewo sanakhoze kupeza chochititsa vuto lake.
Robert anawononga ndalama zoposa $3,000 (U.S.) akuyesayesa kuchiritsa mutu wake wopweteka kwambiri. “Ndinapita kwa akatswiri, ku zipatala zonse . . . kupyola njira zopimira zonse,” iye akutero. Adokotala analemba mankhwala akupha ululu ndi kufeŵetsa minofu, koma mutu unapitirizabe.
Pauline anadwala dzino losautsa kwazaka zambiri. Dokotala wake wamano sanapeze cholakwika ndi mano ake ndipo anamtumiza kwa dokotala. Dokotalayo anambwezera kwa dokotala wamanoyo, yemwe anachotsa dzinolo. Akumagwira dzinolo ndi mbano pafupi ndi nyali, dokotala wamanoyo anati: “Dzinoli liribwino zedi.” Pamene mankhwala oletsa kumva ululu analeka kugwira ntchito, kupwetekako kunayambanso.
Ngakhale kuti zizindikiro zawo zinasiyana, anthu atatuŵa anali ndi nthenda imodzimodziyo. Iyo imakantha anthu mamiliyoni khumi m’United States mokha. Popeza kuti imafanana ndi matenda ena ambiri, iyo yatchedwa dzina lakuti “Wonyenga Wamkulu.” Odwala ambiri samadziŵa kuti ali ndi nthendayo. Ambiri angakhale sanaimvepo.
Nthendayo imatchedwa TMJ (temporomandibular joint) syndrome.a Kuwonjezera pa mavuto ofotokozedwa pamwambapo, nthenda TMJ syndrome ingachititsenso kupweteka kwa minofu ya zigama, kupweteka kwa kumaso, khosi ndi mapewa, kwa m’maso, m’mphuno, chizwezwe, ndipo ngakhale kuleka kumva. Chifukwa cha zizindikiro zosiyanasiyana zimenezi, matenda a TMJ kaŵirikaŵiri amazindikiridwa molakwa kapena samazindikiridwa konse. Monga chotulukapo, anthu ambiri amamka kwa dokotala ndi dokotala, katswiri ndi katswiri, osakhoza kupeza mankhwala a kuvutika kwawo. Posoŵa chochita, ena amapita kwa akatswiri a nthenda zamaganizo, pamene kuli kwakuti ena amamwa mankhwala akupha ululu. Koma kupangana tsiku lokawonana ndi dokotala wamano wachidziŵitso nkwabwinopo. Iye mothekera angadzetse mpumulo—mpumulo womwe kaŵirikaŵiri ngwosapweteka ndipo wokhalitsa.
Wonyengayo Avundukulidwa
Talingalirani mpangidwe wa mkhalidwewo. Mfundo za zigama (aliyense wa ife alinazo ziŵiri) zimalunzanitsa chigama chapansi, kapena nsagwada, ndi chigaza. Mfundo zimenezi zimatitheketsa kuyendetsa chigama chathu m’mwamba ndi pansi, mkati ndi kunja, ndipo ngakhale chambali. Izo zimakhala pantchito nthaŵi zonse pamene tilankhula, kutafuna, kuyasamula, kumeza, kapena kumwetulira. Mfundo za zigama zimagwira ntchito mogwirizana ndi dongosolo locholoŵana ndi logwirizana la minyewa yolunzanitsa mafupa, mafupa, minofu, mitsempha, ndi mitsempha yamwazi. Mwa anthu ambiri zonsezi zimagwira ntchito pamodzi mogwirizana ndipo sizimachititsa vuto.
Komabe, ngati chigama chaguluka, chingakhale chopweteka kwambiri. Mkhalidwewo wayerekezeredwa ndi kukakamiza munthu wotalika masentimita 180 kuimirira m’chipinda chotalika masentimita 175. Iye angakhale m’mkhalidwe woŵerama mwakanthaŵi popanda kumva kupweteka, koma m’kupita kwanthaŵi kupweteka mwapang’onopang’ono kungakhale kovutitsa kwambiri. Mofananamo, pamene chigama chalephera kusunga mkhalidwe wake wamafupa woyenerera, minofu iyenera kuchichirikiza mosalekeza. Chotulukapo nchofanana ndi chija cha munthu wamtali pansi pa tswindwi lalifupi—kupweteka.
American Equilibration Society imanena kuti pamene mfundo za zigama zisemphana, zingadzutse “mtundu woipa koposa wa kupsinjika kwakuthupi chifukwa chakuti palibe njira imene thupi lingapezere mpumulo.” Mosiyana ndi mkono wovulala, womwe ungayezamitsidwe, mfundo za zigama ndi minofu yogwirizana nayo zimagwira ntchito nthaŵi zonse, usana ndi usiku.
Pothirira ndemanga pa ziyambukiro za kupsinjikako makamaka pa mfundo zimenezi ndi minofu, dokotala wamano wa ku New York, Harold Gelb, woyang’anira za mavuto a TMJ, akulemba kuti: “Kupsinjika kumapangitsa minofu yokwinjika kaleyo m’mutu, m’khosi, ndi m’mapewa kutazima. Kuyenda kwa mwazi m’minofu imeneyi kumakhala kochepera chifukwa cha kulimba kwawo, ndipo kumene kuyenda kwa mwazi kuli kosakwanira, zoipa za m’thupi zimaunjikana ndi kupanga magwero akupweteka mkati mwa minofu. Magwero akupwetekawo angapereke kupweteka kulikonse m’thupi; okhala m’phewa angachititse kupweteka kwakukulu kumbali kwa mutu, mofanana ndi ching’alang’ala. . . . Chifukwa chakuti kupsinjika kochititsidwa ndi kusemphana kwa chigama kumakhala kwakukulu m’minofu ya m’mutu, m’khosi, ndi m’mapewa, zizindikiro zambiri zimachitikira m’dera limenelo.”
Kodi Chochititsa Mavuto a Tmj Nchiyani?
Koma choyamba kodi ndimotani mmene mfundo zimenezi zimagulukira? Nthaŵi zina kumachititsidwa ndi kukanthidwa kumutu, pakhosi, kapena kuchigama. Zizoloŵezi za matafunidwe kapena mamezedwe oipa zikhoza kukhalanso zochititsa. Komabe, chochititsa chofala kwenikweni ndicho kusemphana kwa zigama, mkhalidwe umene mano apamwamba ndi apansi samakumana molondola.
Kaŵirikaŵiri kusemphana kwa mfundo za zigama kumakulitsidwa ndi zizoloŵezi zovulaza za m’kamwa, monga ngati kukukuta kapena kuluma mano, kuluma kaliwo, kuluma mapensulo ndi mapeni. Kapenanso kusemphanako kukhoza kukulitsidwa ndi kukhala koipa, monga ngati kukhala moyedzamira pa desiki kapena mwachizoloŵezi kuchirikiza chibwano chanu ndi dzanja lanu.
American Dental Association ikufotokoza kuti pamene minofu ya chigama ndi mfundo sikhozanso kugwira bwino ntchito pamodzi, chotulukapo kaŵirikaŵiri chimakhala kutazima kwa minofu. Kutazima kwa minofu kumachititsa kupweteka, kulefuka, ndi kuwonongeka kwa minofu. M’kupita kwanthaŵi mfundo ndi minofu yeniyeniyo imawonongeka, ndipo kukhoza kwawo kwakugwira ntchito bwino kumalepheretsedwa mowonjezereka. Izi zimawonjezera kutazima, kupweteka, ndi kuwonongeka.
Zimene Mungachite
Kodi kupweteka kwa TMJ kungathetsedwe motani? Nthaŵi zina kuika kutentha kwachinyontho kumaso kungakutonthoze. Mankhwala ena angathandizenso m’zochitika zina, koma uku ndiko chithandizo chabwino koposa chapakanthaŵi. Kupeza kuchiritsa kokhalitsa mwachisawawa kumaloŵetsamo kuwongolera zizoloŵezi zoipa zimene zimapsinja mfundo za zigama ndi minyewa yolunzanitsa mafupa yake yogwirizana nayo, minofu, mitsempha, ndi zina zotero. Kungaphatikizeponso kubwezera chigamacho m’malo ake.
Chizoloŵezi chovulaza kwenikweni ndicho kuluma kapena kukukuta mano. Mwachibadwa, mano a munthu ayenera kulekana pang’ono kusiyapo potafuna kapena kumeza. Komabe, pafupifupi 40 peresenti ya odwala TMJ amaluma mano awo mwachizoloŵezi pamene iwo ayenera kukhala olekana, makamaka usiku atagona. Kaŵirikaŵiri, chizoloŵezi choluma mano chimenechi chimachititsidwa ndi kupsinjika maganizo kapena kusemphana kwa mano.
Choncho, kodi chingachitidwe nchiyani ponena za kuluma mano? Ena akhoza kusiya chizoloŵezicho mwakuchepetsako kapena kuthetsa kupsinjika maganizo komwe kumachichititsa. Adokotala amano athandiza ena mwakuika pakati pa mano kachipangizo koluma kosakhoza kuwoneka (kochinjiriza kukukuta mano), kamene kamalaka ziyambukiro zovulaza za kuluma mano. Kovalidwa kaŵirikaŵiri usiku, kachipangizo kaplasitiki kameneka kamachinjiriza mano kusasemphana. Nthaŵi zambiri, kuvala kachipangizo kameneka kumadzetsa mpulumulo mofulumira.
Pali zinthu zina zimene mungachite kuchepetsako kukwinja kwa zigama. Peŵani kuyedzamitsa chigama chanu m’dzanja lanu. Osakowamira pa desiki lanu, ndipo osapanikiza telefoni kuphewa lanu ndi chigama. Kulitsani kayendedwe ka zigama kamene kali kofewa ndi kolamulirika. Ndipo osajedula mapeni kapena mapensulo.
Zimene Dokotala Wanu Wamano Angachite
Ngati mukuvutika ndi kupweteka kwa TMJ, mosakaikira mudzafunikira kuchiritsidwa ndi dokotala wamano. Popeza kuti kakhalidwe ka mano pamene pakamwa pali potseka kamadziŵitsa kakhalidwe ka chigama, dokotala wamano angasankhe kusintha njira imene mano amakumanira. Amatero mwakudzaza mano ena ndipo mwinamwake mwakumakulitsako ena—kachitidwe kotchedwa kulinganiza. Izi zimalola chigama kutenga kakhalidwe kolondola ndi kabwino. Kulinganiza kumalira nthaŵi ndi luso kwa dokotala wamano, koma nthaŵi zambiri sikumampweteka wodwalayo.
Zotulukapo kaŵirikaŵiri zimakhala zodabwitsa. Robert, wotchulidwa pachiyambi, anasinthidwa kakhalidwe ka mano mwa njirayi. “Mwadzidzidzi kunamveka ngati kuti ndinali ndi mano atsopano kotheratu m’kamwa mwanga,” iye anatero. “Ndipo chabwino koposa, mutu unaleka kupweteka.” Munthu wina anadzuma nati: “Ndikumva ngati kuti ndiri ndi kamwa yatsopano kotheratu!”
Chikhalirechobe, mosasamala kanthu za chipambano chochiritsa awo odwala TMJ syndrome, iyo njosakhoza kumvetsetsedwa mokwanira. Mwachitsanzo, kodi chochititsa zizindikiro chenichenicho nchiyani? Ndipo nchifukwa ninji ena okhala ndi kusemphana kwa zigama kwakukulu samavutika konse pamene kuli kwakuti ena okhala ndi kusemphana kwakung’ono amamva kupweteka kwambiri? Kodi umunthu ndiwo chochititsa? Ndiponso, ndimotani kwenikweni mmene kupweteka kumasamutsidwira kuchokera ku mbali imodzi ya thupi kumka ku ina?
Mayankho a mafunso ameneŵa ndi ena akufufuzidwa ndi kukambitsiridwa ndi adokotala amano. Komabe, pali Wina amene amamvetsetsa mokwanira kugwira ntchito ndi kucholoŵana kwa thupi la anthu. Ameneyu walonjeza kuthetsa kupanda ungwiro konse kumene kumachititsa kupweteka ndi kuvutika kwa anthu.—Chibvumbulutso 21:4.
Pakali pano, ngati mukulingalira kuti muli ndi nthenda ya TMJ syndrome, bwanji osapita kwa dokotala wamano yemwe amadziŵa za wonyenga wamkuluyo? Iye angakhoze kukuthandizani.
[Mawu a M’munsi]
a Iyo imatchedwanso “kusagwira bwino ntchito kwa TMJ.”
[Bokosi patsamba 30]
Kodi Chigama Chanu Nchoguluka?
Ngati muyankha kuti inde ku mafunso otsatiraŵa, icho chingakhale chotero.
1. Ikani zala zanu m’mbali mwa nkhope yanu kutsogolo pang’ono kwa khutu lirilonse, kumene mungakhudze mfundo zanu za zigama. Tsopano tsegulani ndi kutseka kamwa yanu kwanthaŵi zingapo. Kodi mukumva phokoso lirilonse?
2. Kenaka loŵetsani mwapang’onopang’ono nsonga za zala zanu za kaninse m’khutu lirilonse, mukumazikankhira kutsogolo chakutsogolo kwa khutu. Kachiŵirinso tsegulani ndi kutsekanso kamwa yanu. Muyenera kumva nsagwada yanu ikukankha zala zanu. Kodi kukumveka kwambiri kumbali imodzi koposa inayo? Kodi kuchita zimenezi kukupweteka?
3. Kodi nthaŵi zina mumavutika kutsegula kamwa yanu, kapena kodi mumamva kupweteka poitsegula kwambiri?
4. Kodi mumamva kulefuka kapena kupweteka m’chigama chanu kapena nkhope kapena mphepete mwa makutu?
5. Kodi mumamva kupweteka potafuna kapena poyasamula?
6. Kodi mumaluma kapena kukukuta mano kutulo? (Chizindikiro chakuti mumatero ndicho kumva kupweteka kapena kutopa kwa zigama mutadzuka.)
7. Kodi zigama zanu zimalimba kwakuti simukhoza kutsegula kapena kutseka pamwa panu?