Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 22-24
  • Zoŵaŵitsa Zimene Sizidzakhalakonso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoŵaŵitsa Zimene Sizidzakhalakonso
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoyesayesa za Kuzindikira Kupweteka
  • Maganizo ndi Thupi Lomwe Ziloŵetsedwamo
  • Mmene Mikhalidwe ya Kupweteka Imasinthidwira
  • Kupita Patsogolo m’Kusamalira Zoŵaŵitsa
    Galamukani!—1994
  • Koposa Mdani Wankhanza
    Galamukani!—1994
  • Posachedwapa—Dziko Lopanda Zopweteka!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Moyo Wopanda Zoŵaŵitsa Uli Pafupi!
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 22-24

Zoŵaŵitsa Zimene Sizidzakhalakonso

ZOŴAŴITSA zimene zidzachotsedwa mokwaniritsa lonjezo la Baibulo zidzakhala zoŵaŵitsa zimene zimadza chifukwa cha kupanda ungwiro kwa munthu woyamba. Zoŵaŵitsa zimenezi zimaphatikizapo zimene zingatchedwe kupweteka kosatha.

Mmalo mwa kukhala dongosolo lochenjezera nthenda kapena kuvulala, kupweteka kosatha kwagwirizanitsidwa ndi “belu la chenjezo lonama” limene lili losaletseka. Ndi mtundu umenewu wa kupweteka umene umachititsa ovutikawo kuthera madola mamiliyoni zikwizikwi chaka ndi chaka pofunafuna mpumulo, ndipo umawononga miyoyo ya mamiliyoni.

Katswiri wa kupweteka Dr. Richard A. Sternbach analemba kuti: “Mosiyana ndi kupweteka kwakukulu, kupweteka kosatha sikuli chizindikiro; kupweteka kosatha sikuli chenjezo.” Emergency Medicine inagogomezera kuti: “Kupweteka kosatha kulibe chifuno.”

Motero, madokotala ambiri m’zaka zaposachedwapa afikira pa kulingalira kupweteka kotero monga nsautso yeniyeni. “M’kupweteka kwakukulu kupwetekako ndiko chizindikiro cha nthenda kapena kuvulala,” Dr. John J. Bonica akufotokoza motero mu The Management of Pain, buku la muyezo wamakono wonena za kupweteka. “M’kupweteka kosatha kupweteka kwenikweniko ndiko nthenda.”

Zoyesayesa za Kuzindikira Kupweteka

Kupweteka sikunazindikiridwebe mokwanira. “Kukopa kosatha kwa kuyesayesa kudziŵa chimene chili kupweteka,” anatero magaziniwo American Health, “kwachititsa asayansi kugwira ntchito kwambiri.” Zaka makumi angapo zapitazo, analingalira kuti kupweteka kunali mpangidwe wa luntha, monga kuona, kumva, ndi kukhudza, zimene zimamvedwa ndi nsonga zapadera za minyewa m’khungu ndipo zimatengedwa ndi mtsempha wapadera wa minyewa kumka ku ubongo. Koma lingaliro losavuta limeneli la kupweteka linapezedwa kukhala lonama. Motani?

Chinthu chimodzi chimene chinatsogolera ku chidziŵitso chatsopano chinali kupenda kochitidwa pa mkazi wachichepere amene sanali kumva kupweteka. Pambuyo pa imfa yake mu 1955, kupima ubongo wake ndi dongosolo la mauthenga kunatsogolera ku lingaliro latsopano la chimene chimachititsa kupweteka. Madokotala “anafunafuna nsonga za minyewa,” inafotokoza motero The Star Weekly Magazine, ya July 30, 1960. “Ngati [iye] analibe zilizonse, zimenezo zikanakhala chochititsa cha kusamva kupweteka kwa msungwanayo. Koma anali nazo ndipo mwachionekere zinali zabwinobwino.

“Kenako, madokotala anapima mitsempha ya minyewa yolingaliridwa kukhala yogwirizanitsa nsonga za minyewa ndi ubongo. Ndithudi, pamenepa, akapeza chilema. Koma sizinali choncho. Mitsempha ya minyewa yonseyo inali yabwinobwino, malinga ndi mmene inaonekeramo, kusiyapo imene inaleka kugwira ntchito chifukwa cha kuvulala.

“Potsirizira pake, kupima kunachitidwa pa ubongo wa msungwanayo ndipo, kachiŵirinso, panalibe chilema cha mtundu uliwonse chimene chinapezedwa. Mogwirizana ndi chidziŵitso chonse chimene chilipo ndi chiphunzitso, msungwana ameneyu akanayenera kumva ululu mwachibadwa, komabe iye sankamvadi ngakhale kunyerenyetsa.” Komabe, iye anali kudziŵa pamene anapanikizidwa khungu ndipo ankatha kusiyanitsa pakati pa kukhudza mutu wa pini ndi nsonga ya pini, ngakhale kuti kulasa kwa piniyo sikunapweteke.

Ronald Melzack, amene m’ma 1960 anathandiza kulemba chiphunzitso chotchuka chatsopano chofotokoza kupweteka, akupereka chitsanzo china cha kucholoŵana kwake. Iye anafotokoza kuti: “Akazi a a Hull anapitirizabe kuloza phazi lawo limene kunalibe [linali litadulidwa], ndi kufotokoza za kupweteka kotentha kumene kunamveka ngati mtoso wotentha kwambiri wopisidwa m’zala zawo.” Melzack anauza magazini a Maclean’s mu 1989 kuti anali “kufunafunabe mafotokozedwe amene akuwatcha kuti kupweteka ‘kongoyerekezera.’” Ndiponso, pali chimene chimatchedwa kuti kupweteka kosokeretsa, m’kumene munthu angakhale ndi chiŵalo china chosagwira ntchito bwino kumbali ina ya thupi komano namamva kupweteka kumbali ina.

Maganizo ndi Thupi Lomwe Ziloŵetsedwamo

Kupweteka tsopano kukudziŵidwa monga “kuloŵerana kwa maganizo ndi thupi kocholoŵana kwambiri.” M’buku lake la mu 1992 lakuti Pain in America, Mary S. Sheridan akuti “kumva kupweteka kuli kwakukulukulu kwa maganizo kumene iwo angathe kukana kukhalapo kwake nthaŵi zina ndipo nthaŵi zina kukuumba ndi kukuchirikiza chivulazo chachikulu chitapita kale.”

Mkhalidwe wa munthuwe, kusumika maganizo, umunthu, kukhudzidwa ndi malingaliro, ndi zinthu zina zonsezo nzofunika ponena za mmene munthu amachitira ndi kupweteka. “Mantha ndi nkhaŵa zimachititsa machitidwe opambanitsa,” anatero katswiri wa kupweteka Dr. Bonica. Motero, munthu angaphunzire mmene angadziŵire kupweteka. Dr. Wilbert Fordyce, profesa wa zamaganizo amene ali katswiri wa zamavuto a kupweteka, akufotokoza kuti:

“Funso silili lakuti kaya kupwetekako kuli kwenikweni. Zoonadi iko kuli kwenikweni. Funso ndi lonena za zimene zili zochititsa zofunika zimene zimakusonkhezera. Ngati ndilankhula nanu ponena za ham sandwich tisanadye chakudya chamadzulo, mumadza mate m’kamwa. Zimakhala zenizeni. Koma zimachitika chifukwa cha kusonkhezeredwa. Pamenepa palibe ham sandwich. Anthu amakhudzidwa mtima kwambiri pamene asonkhezeredwa. Kumayambukira khalidwe la anthu, kudzetsa mate, kuthamangitsa mwazi, liŵiro la kupukusidwa kwa chakudya, kupweteka, ndi zinthu zina zosiyanasiyana.”

Monga momwe malingaliro anu amtima ndi mkhalidwe wamaganizo ungakulitsire kupweteka, akhoza kukuthetsa kapena kukuziralitsa. Lingalirani chitsanzo ichi: Dokotala wa opaleshoni ya ubongo anati pamene anali wachichepere anakopeka kwambiri ndi msungwana wina pamene anakhala naye pa khoma lozizira kwambiri kwakuti sanamve mkhalidwe wa kuzizira kwakukuluwo kapena kupweteka m’matako. “Ndinatsala pang’ono kuumitsidwa ndi chisanu,” iye akufotokoza motero. “Ndiyesa kuti tinali titakhala pamenepo kwa mphindi 45, ndipo sindinamve kanthu kalikonse.”

Zitsanzo zotero nzambiri. Oseŵera mpira odziloŵetsa kwambiri m’maseŵerawo kapena asilikali mkati mwa kulirima kwa nkhondo angavulale moipirapo komabe namva ululu wochepa kapena kusaumva kumene panthaŵiyo. Wotumba Afirika wotchuka kwambiri David Livingstone anasimba za kuukiridwa ndi mkango umene umampukusa “ngati momwe galu wosaka amachitira ndi khoswe. Mantha . . . anachititsa mtundu wa kulota umene unalibe kupweteka.”

Nkwachidziŵikire kuti atumiki a Yehova Mulungu, amene amayembekezera kwa iye mofatsa ndi chikhulupiriro chonse ndi chidaliro, nawonso nthaŵi zina aona kupweteka kwawo kukuzirala. “Ngakhele kuti zingaonekere kukhala zachilendo,” anasimba motero Mkristu wina amene anamenyedwa, “pambuyo pa nkhonya zoyamba zingapo, sindinamvenso kupweteka. Mmalomwake, kunali monga ngati kuti ndinali kungozimva, monga ngati kulira kwa ng’oma yokhala kutali.”—February 22, 1994, Awake!, tsamba 21.

Mmene Mikhalidwe ya Kupweteka Imasinthidwira

Poyesayesa kufotokoza zina za mbali zachilendo za kupweteka, mu 1965 profesa wa zamaganizo, Ronald Melzack, ndi profesa wa kapangidwe ka thupi, Patrick Wall, analinganiza chiphunzitso chotchuka cha kupweteka chotchedwa kuti gate-control. Buku lophunziridwa lotulutsidwanso la Dr. Bonica la 1990 lonena za kupweteka linati chiphunzitso chimenechi chinali “pakati pa kupita patsogolo kofunika koposa m’ntchito ya kufufuza kupweteka ndi mankhwala ake.”

Malinga ndi kunena kwa chiphunzitsocho, kutseguka ndi kutsekeka kwa chipata chongoyerekezera mu msana kumaloleza kapena kutsekereza njira ya mauthenga a kupweteka omka ku ubongo. Ngati mikhalidwe ina yosakhala ya kupweteka ichuluka pa chipatapo, pamenepo mauthenga oti akafike ku ubongo angachepetsedwe. Motero, mwachitsanzo, kupweteka kumachepetsedwa mwa kutikita kapena kugwedeza chala chotenthedwa pang’ono ndi moto, popeza kuti mwakutero mauthenga osakhala a kupweteka amatumizidwa mu msana kuti akadodometse njira ya mauthenga a kupwetekako.

Kutumbidwa kwa mu 1975 kwakuti matupi athu amatulutsa madzi onga morphine otchedwa endorphins kunathandizanso m’kufufuza kwa kudziŵa mbali zachilendo za kupweteka. Mwachitsanzo, anthu ena angakhale omva kupweteka pang’ono kapena osamva kupweteka chifukwa chakuti amatulutsa endorphins yochuluka. Endorphins ingafotokozenso chinsinsi chosonyeza chifukwa chake kupweteka kumachepetsedwa kapena kuthetsedwa mwa njira ya acupuncture, njira ya mankhwala imene asingano aang’ono kwambiri amaloŵetsedwa pathupi. Malinga ndi kunena kwa mboni zodzionera zokha, opaleshoni yotsegula mtima yachitidwa pamene mwiniwake anali wogalamuka, watcheru, ndi womasuka mwa kugwiritsira ntchito acupuncture monga chophera ululu chokha! Kodi nchifukwa ninji ululuwo sunamvedwe?

Ena amakhulupirira kuti asinganowo angasonkhezere kutulutsidwa kwa endorphins kumene kumachotsa ululu kwakanthaŵi. Kuthekera kwina ndi kwakuti acupuncture imapha ululu chifukwa chakuti asinganowo amasonkhezera mitsempha ya minyewa imene imatumiza mauthenga ena amene sali a kupweteka. Mauthenga ameneŵa amachuluka pa zipata za msana, akumaletsa mauthenga a kupweteka kupyola modzipanikiza kuti akafike ku ubongo, kumene kupwetekako kumamvedwa.

Chiphunzitso cha gate-control, ndi chenicheni chakuti thupi limatulutsa mankhwala ake opha ululu, zingafotokozenso chifukwa chimene mkhalidwe wa munthu, maganizo, ndi malingaliro zimayambukira mlingo wa kupweteka umene amamva. Motero, kugwidwa ndi mantha chifukwa cha kuukiridwa kwadzidzidzi ndi mkango kungakhale kutasonkhezera kutulutsidwa kwa endorphins ya Livingstone, ndiponso kudzadza msana wake ndi mauthenga ena osakhala a kupweteka. Chotero, kumva kupweteka kwake, kunachepetsedwa.

Komabe, monga momwe kwaonedwera poyamba, mkhalidwe wa maganizo wa munthu ndi malingaliro ungakhale ndi chiyambukiro chosiyana. Kutsenderezeka kochuluka kwa tsiku ndi tsiku kwa moyo weniweni wamakono kungawonjezere mkhalidwe wa kupweteka wa munthu mwa kudzutsa nkhawa, kumangika thupi, ndi kukhwinyata kwa minofu.

Komabe, mwamwaŵi, ovutika ndi kupweteka ali ndi chifukwa cha kukhala achiyembekezo. Zimenezi zili chifukwa chakuti ovutika ambiri tsopano akupindula ndi njira zowongoleredwa za mankhwala. Kuwongoleredwa kotero kwachititsidwa ndi kuzindikiridwa kwabwinopo kwa nsautso yowopsa imeneyi. Dr. Sridhar Vasudevan, prezidenti wa American Academy of Pain Medicine, anafotokoza kuti: “Lingaliro lakuti kupweteka nthaŵi zina kungakhale nthenda yeniyeniyo linasinthitsa chisamaliro m’ma 80.”

Kodi ndimotani mmene chisamaliro cha kupweteka chasinthidwira? Kodi ndizisamaliro zotani zimene zikutsimikizira kukhala zothandiza?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi ndimotani mmene “acupuncture” imachepetsera kapena kuthetsera kupweteka?

[Mawu a Chithunzi]

H. Armstrong Roberts

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena