Kupita Patsogolo m’Kusamalira Zoŵaŵitsa
KUFIKIRA posachedwapa panali madokotala oŵerengeka okha amene anadziŵa za kupweteka, ndipo ambiri samadziŵabe. Dr. John Liebeskind, yemwe kale anali prezidenti wa International Pain Foundation, zaka zingapo zapitazo anati: “Sindiganiza kuti pali sukulu yazamankhwala m’dzikoli kumene maola oposa anayi m’zaka zinayi amatheredwa kuphunzitsa ophunzira kupima ndi kusamalira mavuto a kupweteka.”
Komabe, kupita patsogolo m’kudziŵa kupweteka kwachitikira pamodzi ndi kuyesayesa kokulirapo m’kukusamalira. Motero, chiyembekezo cha ovutika ndi kupweteka chaŵalitsidwa. “Tonsefe tikuthokoza,” anasimba motero magazini a American Health, “kuti tsopano madokotala amazindikira kuti kupweteka kosatha sikuli chizindikiro wamba, koma ndiyo nthenda yokhoza kuchiritsidwa.” Lingaliro limeneli lachirikiza chiwonjezeko chachikulu cha chiŵerengero cha zipatala zodzipereka pa kusamalira kupweteka.
Kumene Kupweteka Kumasamaliridwa
Dr. John J. Bonica anatsegula chipatala choyamba chosamalira kupweteka kosiyanasiyana mu United States. “Podzafika 1969 panali zipatala 10 zokha zotero m’dziko,” iye anasimba motero. Koma chiŵerengero cha zipatala zodzipereka pa kusamalira kupweteka chawonjezeka mofulumira m’zaka 25 zapitazo. Tsopano pali zipatala zosamalira kupweteka zoposa chikwi, ndipo woimira bungwe la dzikolo lothandiza anthu akutali ovutika ndi kupweteka kosatha anati “zatsopano zimatsegulidwa pafupifupi tsiku lililonse.”a
Tangoganizani kuti zimenezo zikutanthauzanji! “Tsopano odwala amene anali kuyenda mitunda makilomita mazana kapena zikwi kuti akapeze mpumulo pa kupweteka kwakukulu angaupeze pafupi ndi kwawo,” anatero Dr. Gary Feldstein, katswiri wochititsa dzanzi mu New York City. Ngati ndinuyo mukudwala, lingakhale dalitso lotani nanga kulandira chithandizo kuchokera ku kagulu ka akatswiri ophunzitsidwa kusamalira kupweteka!
Linda Parsons, mkazi wa woyang’anira womayendayenda wa Mboni za Yehova, anavutika ndi kupweteka kwa msana kwa zaka zambiri. Iye anafunafuna thandizo kwa madokotala osiyanasiyana, komabe kupweteka kwakeko kunapitirizabe mosaletseka. Tsiku lina m’May chaka chatha, ali pafupifupi kusoŵa chochita, mwamuna wake anatenga buku la manambala a foni ndi kuyang’ana pamalo olembedwa kuti pain. Pamenepo panali nambala ya foni ya chipatala chosamalira kupweteka chosakhala patali ndi kumene anali kutumikira kummwera kwa California. Lonjezo linapangidwa, ndipo masiku oŵerengeka pambuyo pake Linda anakumana ndi dokotala kuti adzafunsidwe ndi kupimidwa kwanthaŵi yoyamba.
Makonzedwe a kusamalira Linda monga wodwala wogonera kunyumba anapangidwa. Anayamba kupita ku chipatala katatu pa mlungu kukalandira mankhwala ndiponso anatsatira programu ya chisamaliroyo kunyumba. M’milungu yoŵerengeka, iye anayamba kumva kusintha kwabwino. Mwamuna wake akufotokoza kuti: “Ndikukumbukira akunena modabwa madzulo ena kuti, ‘Sinditha kukhulupirira kuti sindikumvanso kupweteka kulikonse.’” M’miyezi yochepa, kupita ku chipatala kunalekeka.
Chithandizo chimene Linda analandira kuletsera kupweteka kwake ndi chofanana ndi chija choperekedwa ndi zipatala zosamalira kupweteka kosiyanasiyana. Chipatala chotero chili ndi kagulu ka akatswiri antchito yazaumoyo, amene, malinga ndi kunena kwa Dr. Bonica, ali “odziŵa bwino kwambiri kusamalira kupweteka kosatha.” Mwachitsanzo, kodi ndimotani mmene Linda anasamaliridwira pa vuto lake la kupweteka?
Mmene Kupweteka Kungasamaliridwire
Brosha la ku chipatala limafotokoza njira yake pamene munthu afika: “Munthu aliyense amapimidwa ndi dokotala kuti adziŵe maziko a kupwetekako ndiyeno zonulirapo zotsimikizirika ndi maprogramu a chisamaliro zimakhazikitsidwa. . . . Njira zaukatswiri ndi machitidwe zimagwiritsiridwa ntchito kuthandiza thupi kutulutsa ‘endorphins’ (makemikolo otulutsidwa mwachibadwa m’thupi) kuchepetsa kupweteka ndi nkhaŵa ndi kupeŵa kudalira pa mankhwala.”
Pakati pa chisamaliro chimene Linda analandira panali acupuncture ndi TENS, kuimira transcutaneous (kupyoza khungu) electrical nerve stimulation. Analandira chithandizo cha kutsitsimulidwa ndi magetsi ku chipatala ndipo anapatsidwa makina aang’ono a TENS okagwiritsira ntchito kunyumba. Biofeedback—njira imene wodwala amaphunzitsidwa kupenda kayendedwe ka zinthu m’thupi lake ndi kusintha kuti achepetse mphamvu ya kupweteka—inagwiritsiridwanso ntchito.
Kuchiritsa kopanda mankhwala, kuphatikizapo kutikita minyewa, kunali mbali ya dongosolo la chisamalirocho. M’kupita kwa nthaŵi, komano kokha pamene Linda anali woikonzekera, programu yolimbitsa thupi m’bwalo la maseŵera inayambidwa, ndipo inakhala mbali yofunika ya chisamalirocho. Kulimbitsa thupi nkofunika, popeza kuti kwapezedwa kuti kumabwezeretsa endorphins yochepetsedwa ndi kupweteka kosatha. Komabe, chitokoso chake chili pa kuthandiza anthu omva kupweteka kukhala ndi programu yothandiza yolimbitsa thupi.
Ovutika ndi kupweteka kosatha ambiri ofika ku zipatala akumwa mankhwala ambiri oletsa kupweteka, ndipo Linda anali kuchita chimodzimodzi. Koma analeka mankhwala akewo mofulumira, chimene chili chonulirapo chofunika cha zipatala zosamalira kupweteka. Linda sanavutike ndi zotulukapo za kulekako, komabe zimenezo si zachilendo. Katswiri wa za kupweteka Dr. Ronald Melzack anati mu “kupenda opsa ndi moto oposa 10,000 . . . , palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anakhala womwerekera chifukwa cha anamgoneka operekedwa kuletsa kupweteka mkati mwa kukhala pa chipatala.”
Popeza kuti kaŵirikaŵiri pamakhala mbali yaikulu ya maganizo yogwirizanitsidwa ndi kupweteka kosatha, zipatala zimayesa kuthandiza odwala, kwenikweni, kuthetsa kupweteka kwawo. “Zimene mumaganiza,” akufotokoza motero Dr. Arthur Barsky, profesa wa pa Harvard Medical School, “zimene mumayembekezera, mmene mumasamalirira malingaliro anu—zinthu zonsezi zili ndi chiyambukiro chachikulu pa zimene inuyo kwenikweni mumamva.” Chotero odwalawo amathandizidwa kusamalira zinthu zosiyana ndi kupweteka kwawo.
Ziyembekezo za Kuchira
Kodi zipatala zosamalira kupweteka zimenezi ndizo yankho la mavuto opweteka a mtundu wa anthu? Ngakhale kuti njira za chisamaliro cha kupweteka zofotokozedwa muno zingakhale zothandiza, munthu ayenera kusamala posankha chipatala chokhoza kapena katswiri wodziŵa kusamalira kupweteka. Komabe ngakhale panthaŵiyo, ziyembekezo ziyenera kukhala zosapambanitsa.
Nali fanizo la chochitika chenicheni chachipambano: Stephen Kaufman, yemwe kale anali wa maseŵera onyamula zitsulo wa Olympic, anatsala pang’ono kupuŵala chifukwa cha kupweteka kosatha kumene anakhala nako pamene mbala inamuwombera pakhosi. Pambuyo pa miyezi isanu ndi itatu ya programu ya chisamaliro cha kupweteka, anali wokhoza kubwerera kukagwira ntchito yanthaŵi yonse ndipo potsirizira pake kuchitanso mpikisano wa kunyamula zitsulo. Komabe iye anati: “Nthaŵi zambiri, zala zanga zakumapazi zimawotcha monga ngati kuti zili m’madzi oŵira.”
Chotero mosasamala kanthu ndi kupita patsogolo kosangalatsa, kuli kwachiwonekere kuti munthu sangakhoze kukwaniritsa lonjezo la Baibulo lakuti: ‘Sipadzakhalanso choŵaŵitsa.’ (Chivumbulutso 21:4) Nangano, kodi ndimotani mmene chonulirapo chimenecho chingapezedwere?
[Mawu a M’munsi]
a Galamukani! samachirikiza chipatala chakutichakuti chilichonse cha chisamaliro cha kupweteka kapena njira yochiritsira.
[Zithunzi patsamba 26]
Njira zosamalirira kupweteka, kuphatikizapo kutsitsimula minyewa ndi magetsi
[Mawu a Chithunzi]
Mwa chilolezo cha Pain Treatment Centers of San Diego