Moyo Wopanda Zoŵaŵitsa Uli Pafupi!
DONGOSOLO locholoŵana la thupi limene limatitetezera pa ngozi lili lozizwitsa ndithu. Kulipenda kuyenera kutisonkhezera kutamanda Mlengi, monga momwe wamasalmo wa Baibulo anachitira yemwe analemba kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza.” (Salmo 139:14) Zoonadi, ndi Mulungu yekha amene angakhoze kudzetsa moyo wopanda zoŵaŵitsa! Koma kodi zimenezi zidzakwaniritsidwa motani?
Onani kuti poyambirira lonjezo la kuchotsedwa kwa zoŵaŵitsa ndi misozi lisananenedwe, Baibulo limasimba za “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka.” (Chivumbulutso 21:1, 4) Ndithudi, Baibulo silikunena za kuchoka kwa m’mwamba mwenimweni ndi dziko lapansi lenileni. Mmalomwake, ilo likunena mwachidule, kuti, dongosolo latsopano kotheratu la zinthu lidzaloŵa m’malo limene lilipoli. Inde, boma latsopano, loposa la anthu lidzatheketsa kusangalala ndi moyo wopanda zoŵaŵitsa pompano padziko lapansi.
Pofotokoza boma limeneli, Baibulo limati “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kapena, boma] . . . [umene, NW ] udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anatiphunzitsa kupempherera boma la Ufumu limeneli pamene anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.
Komabe, kodi ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwa pemphero limenelo kungatanthauzire moyo wopanda zoŵaŵitsa kwa inu?
Wolamulira Wokhala ndi Mphamvu Yoposa ya Munthu
Chinsinsi chake chagona mu nzeru ndi mphamvu ya uyo amene Mulungu wasankha kutsogolera boma Lake. Ameneyo ndiye Yesu Kristu mwiniyo. Za iye, ulosi wa Baibulo umati: “ [Boma lidzakhala, King James Version] pa pheŵa lake, . . . Za kuenjezera [boma lake, KJ] ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7.
Nzeru ya Yesu, amene tsopano ali kumwamba, ndi yaikulu koposa madokotala onse apadziko lapansi. Iye amazindikira mokwanira kagwiridwe kantchito ka thupi lathu, kuphatikizapo madongosolo ake odzitetezera pa kuvulala. Pamene anali padziko lapansi zaka zoposa 1,900 zapitazo, panalibe nthenda kapena nsautso imene sakanatha kuchiritsa. Motero iye anasonyeza zimene adzachita pa mlingo wokulirapo monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. Za nthaŵi ina, Baibulo limanena kuti:
“Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya.” (Mateyu 15:30, 31) Pakati pa matenda amene Yesu adzachiritsa mkati mwa ulamuliro wake wa Ufumu pali ija yoipa kwambiri, kupweteka kosatha.
Ndithudi, limenelo lidzakhala dalitso lokondweretsa kwambiri chotani nanga! Ndipo silidzangokwaniritsidwa kwa oŵerengeka chabe. Lonjezo la Mlengi ndi lakuti: “Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndiyeno, pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, lonjezolo lidzakwaniritsidwa, “sipadzakhalanso . . . choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:4.
Pansi pa ulamuliro waulemero wa Ufumu wa Kristu, madongosolo athu ambiri athupi, kuphatikizapo aja amene amatitetezera pa ngozi, adzagwira ntchito mwangwiro chifukwa chakuti choloŵa cha uchimo chidzakhala chitachotsedwa. Dongosolo lathu lochenjeza la thupi silidzakhalanso konse lozunza. Mwachisangalalo, malinga ndi kunena kwa maulosi a Baibulo amene tsopano akukwaniritsidwa, tili pakhomo pa dziko latsopano limenelo, mmene zoŵaŵitsa sizidzasautsanso.—Mateyu 24:3-14, 36-39; 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:11-13.
Mungathe kusangalala ndi moyo pansi pa Ufumu wa Mulungu pamene mtundu wa kupweteka umene tsopano umasautsa mamiliyoni a anthu sudzakhalakonso. Koma mufunikira kuchita kanthu kena. Yesu Kristu anasonyeza chofunika chachikulu pamene anati m’pemphero kwa Mulungu: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kukuthandizani kupeza chidziŵitso chofunika chimenechi. Ingopemphani mmodzi wawo m’dera lanu, kapena lemberani ofalitsa magazini ano, mukumafotokoza chikhumbo chanu cha kukhala ndi phunziro la Baibulo panyumba panu kapena kumalo ena alionse oyenerera. Pamenepo makonzedwe adzapangidwa kuti inu muphunzire zambiri ponena za zifuno za Mulungu kwa anthu kuti asangalale ndi moyo wopanda zoŵaŵitsa.