Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Misonkhano Yachikristu Ingandithandize Motani?
“Sindikuganiza kuti matchalitchi amakuthandiza munthuwe kupita patsogolo mwauzimu. Ndikutanthauza kuti, zimadalira pa munthuyo kaya akufuna kukhala wauzimu kapena ayi.”—Kevin, mnyamata wazaka 19 zakubadwa.
KEVIN ngolondola m’mbali zambiri. Zimadaliradi pa munthuyo kusankha “kaya akufuna kukhala wauzimu kapena ayi.” Koma popeza kuti mukuŵerenga nkhani ino, nkowonekeratu kuti mukufuna kukhala wauzimu. Komabe, simungakhale wotsimikiza kwenikweni amene munthu wauzimu ali kapena mmene mungakhalire munthu wauzimu.
Kunena mokhweka, munthu wauzimu ndimunthu amene amagonjetsera maganizo, malingaliro, ndi zochita zake ku chitsogozo cha Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova. Iye amalingalira Mlengi wake pamene akupanga zosankha zatsiku ndi tsiku, kukhazikitsa zonulirapo, kapena kundandalika zinthu zoyambirira m’moyo. Kunena m’mawu ena, munthu wauzimu ndi amene ali wokhoterera kwa Mulungu.
Monga wa zaka zapakati pa 13 ndi 19, mumapeza kuti “kulabadira kwa dziko lapansi” kumatsekereza kukula kwanu kwauzimu. (Mateyu 13:22) Kuyanjana tsiku lonse ndi anzanu akusukulu omwe angakhale ndi ‘ndingaliro yakuchita zoipa zokhazokha’ kungakhalenso kokhumudwitsa. (Genesis 6:5) Ena angachite ‘chiphwete nalankhula zoipa,’ kuzipangitsa kukhala zovuta kwa inu kusumika maganizo anu pa zinthu zabwino. (Salmo 73:8) Ndipo ngati makolo anu kapena ziŵalo zabanja ziribe chikhulupiriro chanu, iwo angapereke chilimbikitso chauzimu chochepa, kapena sangapereke chirichonse. Kodi mungachitenji kuti mulake zisonkhezero zoipa zimenezi ndikukula mwauzimu?
Chimene mungachite ndicho kufika pamisonkhano ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova mokhazikika. Mosiyana ndi mautumiki akutchalitchi, misonkhanoyo imakulimbikitsani ponse paŵiri kulondola “kudzipereka kwaumulungu monga chonulirapo chanu” ndi kukuthandizani kukula kuchoka pa ukhanda wauzimu kumka ku uchikulire wauzimu.—1 Timoteo 4:7, NW; Aefeso 4:13, 14.
Misonkhano Imene Imakuthandizani Kuphunzira
M’mipingo yoposa 63,000 padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zimatsatira uphungu Wabaibulo wa ‘kusonkhanitsa anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono . . . kuti amve ndi kuti aphunzire.’ (Deuteronomo 31:12) Choncho mudzapeza achichepere ambiri onga inu pakati pa Mboni.
Mboni za Yehova padziko lonse zimakhala ndi phande m’programu yakuphunzira imodzimodziyo. Iyo imaphatikizapo misonkhano isanu ya mlungu ndi mlungu, msonkhano uliwonse wochitidwa kwa pafupifupi ola limodzi. Nayi misonkhano isanuyo:
Msonkhano Wapoyera—nkhani ya Baibulo yogogomezera mutu wa Baibulo.
Phunziro la Nsanja ya Olonda—phunziro lozama la ziphunzitso Zabaibulo mwakugwiritsira ntchito magazini a Nsanja ya Olonda, chofalitsidwa chachikulu cha Mboni za Yehova.
Sukulu Yautumiki Wateokratiki—imaphunzitsa maluso akulankhula kaamba ka uminisitala Wachikristu.
Msonkhano Wautumiki—umasonyeza kukambitsirana ndi zitsanzo za njira zophunzitsira zogwira mtima za uminisitala wakukhomo ndi khomo ndi phunziro Labaibulo.
Phunziro Labukhu Lampingo—kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho kwa timagulu tating’ono mwa kugwiritsira ntchito chothandizira phunziro Labaibulo—kaŵirikaŵiri m’nyumba za anthu.
Maprogramu ophunzitsa pamisonkhano imeneyi angakuthandizeni kuphunzira “zakuya za Mulungu zomwe.” (1 Akorinto 2:10; Miyambo 2:5) Komabe, pali mapindu ambiri opezekerapo.
‘Chitsulo Chinola Chitsulo’
“Nkokhweka kukhala Mkristu pakati pa ena amene amatumikiranso Mulungu,” akutero Michelle wazaka 15 zakubadwa. “Koma pamene wapita kusukulu, kumakhala kovuta kwambiri chifukwa chakuti anzako am’kalasi amakhala ndi miyezo ndi zonulirapo zosiyana.” Chotero, phindu limodzi lopezekera pamisonkhano ndilo mwaŵi wakuyanjana ndi okhulupirira anzanu.
Mfumu yanzeru Solomo inati: “Monga momwe chitsulo chinola chitsulo, chomwecho munthu anola nzeru za mnzake.” (Miyambo 27:17, The New English Bible) Nthaŵi zina, “nzeru” zathu zauzimu, kutanthauza chidziŵitso chathu chauzimu, chimafunikira kusongoledwa. Koma monga momwedi kunola mpeni weniweni kumafunikira luso ndi ziwiya zoyenera, chomwecho nanunso mufunikira kuyanjana ndi anthu oyenera, awo amene ali ndi luso ‘lakugaŵira kwa inu mtulo wina wauzimu.’—Aroma 1:11.
Kunyumba Yaufumu, mudzapezako anthu otero, amisinkhu, mafuko, ndi mitundu yosiyana. Momvekera, mungakhoterere kuyanjana ndi ausinkhu wanu. Komabe, perekani chisamaliro chenicheni kwa awo amene athera zaka zambiri akutumikira Yehova mokhulupirika. (Levitiko 19:32) Kuzoloŵera kwawo m’moyo limodzi ndi chidziŵitso chawo Chabaibulo chozama zingakhale zothandiza kwenikweni kwa inu. Kodi mungawadziŵe motani anthu oterowo? Yesani kuwafunsa mafunso onga aŵa, ‘Kodi munabwera motani m’chowonadi?’ kapena, ‘Kodi munali kuulingalira motani utumiki wakumunda pamene munali wachichepere?’ Iwo angakutulutsireni mphatso zakutizakuti zauzimu!
Zowonadi, pofikira anthu ena mumpingo, poyamba mungalingalire ngati mmene anachitira Craig wazaka 12 zakubadwa, amene akuti: “Ndinkawopa kulankhula ndi achikulire. Ndinaganiza kuti nditanena chinachake cholakwika, ndidzapatsidwa uphungu.” Craig amadziŵa tsopano kuti malingaliro ake anali opanda maziko. “Ndine womasuka tsopano kulankhula nawo,” iye akufotokoza motero. Bwanji osakupanga kuyesayesa kofananako kuyanjana ndi achikulire mwauzimu mumpingo? Kuteroko kudzakupatsani mwaŵi wamtengo wake wakuwona ndi kutsanzira Akristu achikulire.—2 Atesalonika 3:9.
‘Lilime la Ophunzira’
Mbali ina imene muyenera kupanga kupita patsogolo ndiyo maluso anu akuphunzitsa. Mwachitsanzo, kodi ndinu wokhoza kufotokoza chowonadi Chabaibulo momvekera bwino? Kodi ndinu wokhoza kukoka chidwi cha omvetsera? Kodi mumadziŵa kuika tanthauzo lenileni m’kuŵerenga kwanu? Mneneri Yesaya ananena kuti: “Ambuye Yehova wandipatsa ine lilime la ophunzira.” (Yesaya 50:4) Ndipo mwakuphunzira, nanunso mungakhale ndi lilime la ophunzira. Pali msonkhano wina umene ungakupindulitseni mwapadera m’nkhaniyi: Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Kodi munalembetsa m’sukuluyo?
Sukulu Yautumiki Wateokratiki inalinganizidwira kulangiza Akristu polankhula ndi ena. Iyo ilibe malire a msinkhu, ndiponso ubatizo sindiwo chiyeneretso. Komabe, muyenera kukhala wokhoza kulemba ndi kuŵerenga, kukhala woyanjana mokangalika ndi mpingo, ndikukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu. Kodi sukulu yautumiki imeneyi imagwira ntchito motani?
Mutalembetsa, mudzagaŵiridwa kupereka nkhani yachidule pamutu wakutiwakuti Wamalemba. Gwirani ntchito zolimba pokonzekera nkhani yanuyo. Mwachitsanzo, chidziŵitso chowonjezereka pa mutu wanu wankhani kaŵirikaŵiri chingapezeke mwakufufuza zofalitsidwa Zabaibulo mwakugwiritsira ntchito Watch Tower Publications Indexes ndi kusanthula m’bukhu lanazonse la Baibulo, Insight on the Scriptures.a Ngati mukufuna thandizo m’nkhaniyi, afunseni makolo anu kapena Mkristu wozoloŵera kuti akuthandizeni. Kufufuza kumene mudzakuchita kudzawonjezera zochuluka ku nkhani yanu ndipo kungadzetse kukula kwanu kwauzimu.—Miyambo 2:1-5.
Pamene mukupereka nkhaniyo pamaso pa mpingo, minisitala woyeneretsedwa amene akuchititsa sukuluyo adzamvetsera mosamalitsa. Pamapeto pa nkhani yanu, iye adzapereka chilimbikitso ndi uphungu woyenerera wozikidwa pa chidziŵitso chopezeka mu Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki, bukhu lolinganizidwira kuthandiza alankhuli apoyera. Mvetserani mosamalitsa ku uphunguwo. Iwo sunalinganizidwire kukusulizani kapena kukuchititsani manyazi. Malingaliro operekedwawo ngoti akuthandizeni. Ngati ‘musamalira kuŵerenga,’ kupita patsogolo kwanu kwauzimu ‘kudzawonekera kwa onse.’—1 Timoteo 4:13-15.
‘Tamandani Yehova Ndi Milomo Yanu’
Njira ina yokulira mwauzimu pamisonkhano Yachikristu ndiyo kupereka mayankho kapena ndemanga pamene omvetsera apemphedwa kutengamo mbali. Kukonzekera pasadakhale ndiko mfungulo.b Koma mwinamwake mumakupeza kukhala kovuta kuthirira ndemanga ngakhale kuti mwakonzekera kaamba ka msonkhanowo. M’zochitika zotero, mpempheni Yehova kaamba ka thandizo. Mfumu Davide anapemphera kuti: ‘[Yehova, NW], tsegulani milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.’—Salmo 51:15.
Kumbukirani kuti: Yankho silitofunikira kukhala lalitali kapena locholoŵana kwenikweni kuti likhale lomangirira. Monga momwe Rachel wazaka 12 zakubadwa akunenera kuti: “Mmalo mopereka ndemanga yaitali kwambiri, ndemangayo ingangokhala chiganizo chimodzi.” Poyamba, kulankhula pamisonkhano kungawoneke kukhala kovuta, ndipo mungapemphe thandizo, koma m’kupita kwanthaŵi, mudzadzimva monga momwe anachitira Rachel. Iye akufotokoza kuti: “Pamene mupereka ndemanga yanuyanu, imakhaladi yanu, ndipo mumainyadira.” Kuwonjezerapo, mudzakula mwauzimu chifukwa cha kuyesayesa kwanu.
Kukhala wolingalira mwauzimu m’dziko lodzikonda lalerolino sikuli kokhweka konse. Koma ngati mumapezeka mokhazikika pamisonkhano, kukonzekera mokwanira, kukhalamo ndi phande, ndikupanga kuyesayesa kwakuyanjana ndi achikulire, misonkhano Yachikristu idzakuthandizanidi kukula mwauzimu.
[Mawu a M’munsi]
a Yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka chonena za kukonzekera ndi kukhala ndi phande pamisonkhano, onani Awake!, June 22, 1988, masamba 11-13.
[Chithunzi patsamba 21]
Sukulu Yautumiki Wateokratiki yathandiza achichepere zikwi zambiri kukhala aphunzitsi aluso a Mawu a Mulungu