Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 9/8 tsamba 14-16
  • “Kodi Nchifukwa Ninji Sindingamalize Zimene Ndayamba?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Nchifukwa Ninji Sindingamalize Zimene Ndayamba?”
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusanthula Mosamalitsa Zochititsa
  • Konzekerani Pasadakhale!
  • Pitirizanibe KufunafunaZabwino za Ena
  • Lankhulanani!
  • Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?
    Galamukani!—2017
  • Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndingachitenji ndi Homuweki Yochuluka Motero?
    Galamukani!—1993
  • Kuzengereza—Mbala ya Nthaŵi
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 9/8 tsamba 14-16

Lingaliro la Baibulo

“Kodi Nchifukwa Ninji Sindingamalize Zimene Ndayamba?”

“Ngati ntchitoyo njosasangalatsa ndi yogwetsa ulesi, ndimangotaya kuleza mtima kwanga.”

“Zocheutsa. Limenelo ndilo vuto langa. Wailesi yakanema, mabwenzi.”

“Nthaŵi zina ndimakhala wochulukidwa ndi zinthu zofunikira kuzichita!”

“Kukuwonekera kuti nthaŵi zonse ndimadikirira mpaka pamapeto penipeni. Ndiyeno, kumakhala kuchedwa kwenikweni.”

“Ndimamaliza zimene ndayamba. Koma siziwoneka kukhala zabwino konse kwa makolo anga!”

ACHICHEPERE ameneŵa akufotokoza vuto lofala muunyamata: kusamaliza zimene amayamba. Siachichepere onse amene ali aulesi kapena ali ndi mkhalidwe woipa wamaganizo kulinga ku mathayo. Ndithudi, pamene gulu lina la achichepere linafunsidwa kuti: “Kodi ndintchito ziti zimene mukuganiza kuti achichepere ayenera kumachita panyumba?” ambiri anandandalitsa ntchito zonga kukonza bwino zipinda zawo, kuyala makama awo, ndi kukataya zinyalala.

Mosasamala kanthu za zolinga zabwino, ntchito zofunika koposa zimasiyidwa zosamalizidwa, kupangitsa makolo, aphunzitsi, ndi ena kudandaula nthaŵi zonse. Chotero dzifunseni kuti: ‘Kodi nchiyani chimandiletsa kumaliza zimene ndayamba?’ Kusanthula mosamalitsa zochititsazo kudzakutheketsani kuwongolera vutolo.

Kusanthula Mosamalitsa Zochititsa

Bukhu lakuti I Hate School—How to Hang In and When to Drop Out limatipatsa lingaliro labwino la zimene zimacheutsa achichepere ambiri kusamaliza homuweki yakusukulu. “Pamene tikhala pansi kuti tilembe, kaŵirikaŵiri timanyamukanyamuka kukatenga chakudya kapena kukasongola mapensulo. Ndiyeno timafunikira kutumiza foni kapena kupenyerera kanema ya pa TV yomwe takhala tikuyembekezera. Posakhalitsa imafika nthaŵi yakuti tidyetse mphaka ndipo sitinachitebe chirichonse.”

Ofufuza Claudine G. Wirths ndi Mary Bowman-Kruhm ananena kuti “kupenyerera TV kwa maola ochuluka kumakupangitsa kukhala kosatheka kwa anthu ena kuŵerenga ndi kuphunzira mokangalika pambuyo pake. Mu TV muli mtundu winawake wakuodzeretsa umene umakusiyani wotopa ndi watulo. Mumadziŵa nokha kuti nthaŵi zina mumakhala mukupenyerera kwa maola ambiri pamene munafuna kupenyerera programu imodzi yokha.” Wirths ndi Bowman-Kruhm anapezanso kuti ophunzira ena amatengera zizoloŵezi zoipa zakuphunzira m’zaka zawo zoyambirira zakusukulu, ngakhale kuti kwakanthaŵi amatha kukhoza bwino. Komabe, “pamene afika kumakalasi oyambirira akusekondale, samadziŵa kwenikweni mmene angakhalire pansi, kugwira ntchito, ndikuphunzira zinthu zovuta kapena zosasangalatsa.”

Chirichonse chimene chingakhale chifukwa chanu chosamalizira zimene mwayamba, vutolo silidzatha lokha. Ngati mumafunadi kumaliza zimene mwayamba, pamenepo lamulirani moyo wanu m’njira yathayo ndipo pangani masinthidwe oyenerera.

Konzekerani Pasadakhale!

Ngati ndinu wachichepere Wachikristu, mosakaikira ndinu wotanganidwa. (1 Akorinto 15:58) Nthaŵi zina mumadzimva kukhala wochulukidwa ndi mathayo Achikristu, homuweki, ntchito zapanyumba, ndi ntchito zanu. Ndithudi, palibe amene ali ndi zochita zambiri kuposa Mlengi wathu. Komabe, nthaŵi zonse amamaliza ntchito zake. Ichitu sichifukwa chakuti ali wotiposa mphamvu ndi nzeru komanso chifukwa chakuti iye ‘sali Mulungu wachisokonezo koma wa mtendere.’ Nanunso mungamalize ntchito zanu mwakulola ‘zonse kuchitika koyenera ndi kolongosoka.’—1 Akorinto 14:33, 40.

Panthaŵi ina Yesu anati: ‘Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ake, osakhoza kuimaliza, anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye, ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.’—Luka 14:28-30.

Phunziro panopa nlakuti konzekerani pasadakhale. Dr. Janet G. Woititz analemba kuti: “Anthu amene amamaliza ntchito samazichita mwachisawawa. Iwo amachita zimene zimatchedwa ‘maseŵera akukonzekera.’” Chotero yesani kuyang’ana mathayo anu motsimikiza ndikumvetsetsa zimene zikafunikira kuti muwamalize. Kodi mukafunikira kupanga makonzedwe a sitepe limodzi ndi limodzi? Kodi kukakhala kothandiza kugawa ntchitoyo m’mbali zazing’onozing’ono? Kodi ikakutengerani nthaŵi yaitali motani kuti muimalize?

Anthu ena amakonda kusunga ndandanda ya “zinthu zoti zichitidwe,” akumalemba ntchitozo m’dongosolo la kufunika kwake. Ndiyeno ntchitozo zimafafanizidwa pamene zamalizidwa. Kuti mulimbane ndi chikhoterero chakudukizadukiza, phunzirani kulamulira nthaŵi yanu. Ngati mwakhazikitsa malire a nthaŵi yomalizira ntchito, tsimikizirani kuika ntchito zoterozo pamwamba pa ndandanda yanu m’dongosolo la malire omalizirawo.

Kulamulira nthaŵi kwanzeru nkofunika. Kumbali ina, mumafuna kuika malire a nthaŵi pa ntchito zosafunika kwenikweni, monga ngati kupenyerera TV. Kumbali ina, muyenera kusamalira kusachepetsa zinthu zofunika, monga ngati kugona tulo tabwino. Bukhu lakuti I Hate School limadziŵitsa kuti anthu “amasiyanasiyana m’kuchuluka kwa tulo timene amafunikira, koma anthu ambiri sangakhale bwino mwakugona maola anayi kapena asanu usiku umodzi. . . . Kumakhala kovuta kwambiri kusumika maganizo pa malingaliro ovuta ngati muli ndi tulo ndi wotopa.” Kuphunzira kugwiritsira ntchito nthaŵi yanu mwanzeru kudzatsimikizira kukhala kopindulitsa m’zaka zakutsogolo.

Pitirizanibe KufunafunaZabwino za Ena

Komabe, achichepere ena anganene kuti kulamulira nthaŵi kwabwino ndi kulinganizika kwaumwini kumawonekera kukhala kosapindulitsa kwenikweni pamene ntchito imene mukuchita iri yosasangalatsa ndi yogwetsa ulesi. Kugwiritsira ntchito uphungu Wabaibulo wa pa 1 Akorinto 10:24 kudzakuthandizani kukulitsa chisonkhezero chofunikira. Umati: ‘Munthu asafune [zabwino, NW] za iye yekha, koma za mnzake.’ Mwinamwake ndi ntchito zapanyumba zoŵerengeka zokha zimene zimakhaladi zopereka chitokoso kapena zokhutiritsa. Koma pamene muzichita kufuna kuthandiza kapena kukondweretsa wokondedwa, pamenepo pamakhala chikhutiritso ndi chikhumbo chakuzichita bwino. Choncho nthaŵi ina pamene mufuna kuleka ntchito, lingalirani awo amene adzapindula ndi zimene mukuchita, ndipo nyadirani kuchita ntchito yabwino.

Kaŵirikaŵiri nanunso mudzapindula ndi ntchito zowonekera kukhala zosasangalatsa. Mwachitsanzo, talingalirani za ntchito imene nthaŵi zonse mumaisiya yosamaliza. Kodi ndiyo kutsuka mbale? Kapena kusesa chipinda chanu? Tsopano dzifunseni, ‘Kodi mbalezo nzayani?’ Kodi izo siziri mbale zanunso? Kodi sichiri chipinda chanu ndi nyumba yanu? Kufunitsitsa kwanu kulandira mathayo ameneŵa ndi kuwachita mokwanira kudzakupindulitsaninso mtsogolo. Polankhula ndi makolo, bukhu lakuti Simply Organized! limati: “Ngati sitiphunzitsa ana athu kukhala osamalira nyumba, iwo adzavutika akadzachoka panyumba.”

Lankhulanani!

Komabe, bwanji ngati mugwira ntchito zolimba kuti mumalize ntchito, koma makolo anu adandaulabe kuti simunaimalize? Kaŵirikaŵiri vuto limakhala la kulankhulana. Mwachitsanzo, bwanji ngati mwatumidwa kutaya zinyalala. Zimenezo zikumveka zopepuka kwenikweni. Komabe, kuli kwanzeru kufunsa malangizo akutiakuti. Tsimikizirani kuti mukudziŵa ndimotani, ndiliti, ndipo ndikuti. Kodi ntchitoyo ikuphatikizapo kusankha zinyalalazo m’magulumagulu? Kodi ikuphatikizapo kutsuka zotairamo zinyalalazo?

Kulankhulana kwabwino kudzathandizanso makolo anu kumvetsetsa malingaliro anu. Kodi mukuganiza kuti kagawidwe kantchito sikolinganiza? Kodi mumadzipeza kuti mwachulukidwa ndi zofuna za makolo anu? Pamenepo pezani nthaŵi yabwino, ndikuwauza makolo anu mmene mumamverera.

Makolo ena amafunsa ana awo kukhala ndi phande m’kupanga zosankha pamene ntchito zapanyumba zikugaŵiridwa. Dr. Jeffrey Rubin ndi Dr. Carol Rubin, akonzi a bukhu lakuti When Families Fight, akulangiza makolo kukhala ndi kukambitsirana kosalekeza ponena za ntchito zabanja, kugaŵa mathayo, ndikuwalola ana kusankha ntchito zawo. Ngati mumakonda njira imeneyi, bwanji osapereka lingaliroli kwa makolo anu?

Bukhu lina limayamikira kuti mukhale pansi ndi makolo anu ndi “kupanga pulani imene imakupatsani mpata wakuchita homuweki panthaŵi imene ili yabwino koposa kwa inu. Aliyense ali ndi nthaŵi yabwino koposa ya tsiku kapena usiku pamene amasumika maganizo bwinopo. . . . Aloleni ena adziŵe kuti ndi nthaŵi yanu ndipo asakudodometseni. Ngati simugwiritsira ntchito nthaŵi imeneyo kupenyerera TV kapena kulankhula pa foni, iwo adzadziŵa kuti mukunena zowona.” Mwakukambitsirana mwabata nkhani zimenezi ndi makolo anu popanda kupatsa aliyense liŵongo, mungakhale okhoza kuchita makonzedwe abwino kwanonsenu.

Koma kumbukirani kuti chofunika koposa chimene chidzakubweretserani chimwemwe ndi dzina labwino ndicho chikhumbo chanu chakukondweretsa Mlengi, Yehova Mulungu. Baibulo limati: ‘Chirichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW], osati kwa anthu ayi.’ (Akolose 3:23, 24) Tsatirani uphungu umenewu ndipo sangalalani ndi kudziŵika kukhala wakhama, wantchito wathayo chifukwa chakuti mumamaliza zimene mwayamba!

[Chithunzi patsamba 15]

Kuyamba ntchito ndichina, kuimaliza kuli chinthu chinanso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena