Kuganiza kwa Nyani
Mu Sierra Leone, Kumadzulo kwa Afirika, kuli mwambi wakuti: “Nyani samangowuza mwana wake kuti, ‘Gwiritsa!’ Amanena kuti, ‘Dziyang’ana pansi.’”
Izi zimatipangitsa kulingalira chithunzi cha nyani wamng’ono ali m’mwamba mumtengo, akumamatira kumsana kwa mayi ŵake. Tanthauzo la mwambiwo nlakuti ngati Amayi angonena kuti gwiritsa, mwana ŵake angatero kwakanthaŵi, koma popeza kuti sakudziŵa chifukwa cha lamulolo, angaiwale mwamsanga ndikutairira.
Komabe, ngati mwanayo akuyang’ana pansi, angawone mtunda womwe ulipo kuchokera pansi ndipo angatsimikiziridwe mwamphamvu kuti moyo wake ukuloŵetsedwamo. Mwachitsanzo, iye angavulazidwe moipa kapena ngakhale kufa kumene! Pokhala atamvetsetsa ngoziyo mokwanira, amakhala ndi chisonkhezero champhamvu chogwirira zolimba. Tsopano chenjezo kapena lamulo lina lirilonse lowonjezeredwa lidzalemekezedwa kwenikweni.
Ha, ndilamulo lamakhalidwe abwino lotani nanga lophunzitsira ena, makamaka ana. Phunziro lothandiza la nkhaniyi nlakuti m’malo mongopereka malamulo, kuli kofunika kumpangitsa kuzindikira.
Ndithudi, pazochitika zina sipangakhale nthaŵi yokwanira kuchita zimenezo poyamba. Mwachitsanzo, ngati mwana wanu ayamba kudutsa msewu wokhala ndi magalimoto ambiri popanda kuyang’ana choyamba, mungamulamule kuima ndikubwerera mofulumira. Kupereka lamuloli choyamba panopa kuli kofunika koposa. Komano kufotokoza ngozi yomwe mwanayo analimo kungampangitse kuzindikira.
Phindu la kachitidwe kameneka—kusangopereka lamulo komanso kumpangitsa kuzindikira—likupezeka m’mwambi wa m’Baibulo uwu: ‘Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira.’—Miyambo 28:7.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
© Zoological Society of San Diego