Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
“‘Kodi nchifukwa ninji tiri pano?’ ndifunso lofunika kwambiri limene munthu ayenera kudzifunsa. . . . Ndikhulupirira kuti moyo uli ndi tanthauzo mosasamala kanthu za imfa yopanda tanthauzo yomwe ndawona. Imfa ilibe tanthauzo, moyo uli nalo.”
MAWU ameneŵa analembedwa ndi Elie Wiesel, wolemba nkhani wotchuka yemwe anapulumuka m’misasa yachibalo ya Nazi. Anali mmodzi wa anthu ambiri amene anayankha funso lofunsidwa ndi magazini a Life lakuti: “Kodi nchifukwa ninji tiri pano?” Iye anauwona moyo utafika poipitsitsa, komabe anatsimikiza kuti moyo uli ndi tanthauzo.
Komabe, sionse amene amavomereza zimenezo. Woyendetsa teksi wotchedwa José Martínez anayankha funso limodzimodzilo motere: “Tiri pano kudikirira kufa, kungokhala ndi moyo kenaka nkufa. Ndimayendetsa teksi. Ndimawedza nsomba, kupita kocheza ndi bwenzi langa lalikazi, kukhoma misonkho, kuŵerenga pang’ono, ndiyeno kukonzekera kufa . . . Moyo ndichinyengo chachikulu.” Mwachiwonekere malinga ndi kuganiza kwa José, moyo ulibe tanthauzo kwa iye, ulibe chifuno.
Modabwitsa, anthu ambiri ophunzira anawoneka kukhala akugwirizana ndi woyendetsa teksi ameneyo mmalo mwa wolemba nkhaniyo. Akatswiri achisinthiko Richard E. Leakey ndi Roger Lewin, m’bukhu lawo lakuti Origins, akupereka lingaliro lakuti: “Mwinamwake mtundu wa anthu unakhalako mwangozi yaikulu imene inachitika m’zamoyo zina, ndipo unasinthika kufika pa mlingo wosakhoza kudzichilikiza wokha mogwirizana ndi zinthu zouzinga.” Kwa iwo okha, moyo wa munthu ulibe tanthauzo.
Mofananamo, katswiri wachisinthiko Stephen Jay Gould analemba kuti: “Tiri pano chifukwa chakuti gulu lina la nsomba zachilendo linali ndi zipsepse zapadera zomwe zinasanduka miyendo ya zolengedwa zapamtunda; . . . chifukwa chakuti mtundu wa chamoyo china chaching’ono ndipo chofooka, wobuka ku Afirika zaka zokwanira kota ya miliyoni zapitazo, wapitiriza kukhalapo mwamwaŵi. Tingalakelake kupeza yankho ‘lapamwamba’—koma kulibeko.” Malinga ndi kuganiza kwa Gould, moyo wa munthu uli mwaŵi wopanda tanthauzo kwa iye.
Gould ananena zowona m’mbali imodzi yokha. Ambiri amalakalaka yankho “lapamwamba” kuposa limene iye anapereka. M’nthaŵi zatsoka, ambiri amaganiza monga momwe anachitira Jason wa zaka zakubadwa 11. Mnyamata wamng’ono ameneyu analemba motere ponena za imfa ya bwenzi lake laling’ono: “Pamene bwenzi langa Kim anamwalira ndi kansa ndinawafunsa Amayi kuti ngati Mulungu analinganiza kuti Kim akamwalire ali ndi zaka 6 zokha, nchifukwa ninji anamlola kubadwa?” Jason analingalira mwachibadwa kuti moyo uyenera kukhala ndi chifuno, ndipo imfa yomvetsa chisoni ya bwenzi lake laling’ono inawonekera kuti inadodometsa chifuno chimenecho.
Kufunika kwa Funsolo
Kodi nkofunika kudziŵa ngati moyo uli ndi chifuno kapena ayi? Kodi ndifunso lozikidwa pa nthanthi, kapena kodi liyenera kukukhudzani? Ambiri akhala ndi moyo osalingalira mwamphamvu nkhaniyo. Ndipo ngati José Martínez ananena zowona, ndiye kuti njira ya anthu oterowo ingakhale yanzeru kuilondola.
Komabe, ngati Elie Wiesel ananena zowona ndipo moyo ulidi ndi tanthauzo, ndithudi tiyenera kuyesayesa kupeza tanthauzolo. Apo phuluzi, tingaphonye mfundo yofunika koposa ya kukhala ndi moyo. Kungakhale ngati kuyenda m’nyumba yosonyezera zithunzithunzi popanda kuyang’ana zithunzithunzizo kapena kukhala m’lesitilanti popanda kuitanitsa chakudya.
Kodi tingapeze motani ngati moyo uli ndi chifuno kapena ayi? M’nkhani yotsatira, tidzafotokoza mfundo zina zimene zimathandiza kuyankha funso limeneli.