Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pr gawo 1 tsamba 3-6
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mikhalidwe Yovutirapo Kwambiri
  • Zimene Amanena
  • Chiyambukiro Chake
  • Jehova Mulungu wa Chifuno
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kufunafuna Cholinga Chabwino Pamoyo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
pr gawo 1 tsamba 3-6

Mbali 1

Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?

Nthaŵi zina, pafupifupi aliyense amadabwa kuti chifuno cha moyo nchiyani. Kodi ndicho kugwira ntchito zolimba kuwongolera mikhalidwe yathu, kugaŵira zosoŵa za mabanja athu, kufa pambuyo pa zaka 70 kapena 80, ndipo kenako kusakhalako kosatha? Wachichepere wina amene analingalira mwanjirayi ananena kuti moyo ulibe chifuno china koposa “kukhala ndi moyo, kukhala ndi ana, kukhala wachimwemwe ndipo kenako nkufa.” Koma kodi zimenezo nzowona? Ndipo kodi imfa ndiyo mapeto a zinthu zonse?

2 Anthu ambiri a m’maiko onse a Kum’maŵa ndi Kumadzulo amalingalira kuti chifuno chachikulu chokhalira moyo ndicho kupeza chuma chakuthupi. Iwo amakhulupirira kuti zimenezi zingadzetse moyo wachimwemwe, wokhala ndi tanthauzo. Koma bwanji za anthu amene ali nacho kale chuma chakuthupi? Wolemba nkhani wa ku Canada, Harry Bruce anati: “Chiŵerengero chodabwitsa cha anthu olemera amanenetsa kuti alibe chimwemwe.” Iye anawonjezera kuti: “Kupenda kochitidwa kumasonyeza kuti kupanda chiyembekezo kowopsa kwayambukira North America . . . Kodi pali munthu aliyense wachimwemwe m’dzikoli? Ngati alipo, kodi chinsinsi chake nchiyani?”

3 Prezidenti wakale wa United States Jimmy Carter anati: “Tapeza kuti kukhala ndi zinthu ndi kuzigwiritsira ntchito sikumakhutiritsa chikhumbo chathu chofuna kudziŵa tanthauzo. . . . Kukundika zinthu zakuthupi sikungakhutiritse kupanda pake kwa miyoyo imene ilibe chidaliro kapena chifuno.” Ndipo mtsogoleri wina wandale zadziko anati: “Kwa zaka zambiri tsopano ndakhala ndikufunafuna mwamphamvu chowonadi chonena za inemwini ndi moyo wanga; anthu ena ambiri amene ndimadziŵa akuchita zofananazo. Anthu ochuluka kuposa ndi kale lonse akufunsa kuti, ‘Kodi ndife yani? Kodi chifuno chathu nchiyani?’ ”

Mikhalidwe Yovutirapo Kwambiri

4 Ambiri amakayikira kuti moyo uli ndi chifuno pamene awona kuti mikhalidwe ya moyo yakhala yovuta kwambiri. Kuzungulira padziko lonse anthu oposa mamiliyoni chikwi akudwala kwakayakaya kapena amadya mosakwanira, kuchititsa pafupifupi ana mamiliyoni khumi kumafa chaka chilichonse mu Afirika mokha. Chiŵerengero cha anthu apadziko lapansi, chimene chikuyandikira pa mamiliyoni zikwi zisanu ndi chimodzi, chikupitiriza kuwonjezereka ndi oposa 90 miliyoni pachaka, ndipo yoposa 90 peresenti ya chiwonjezeko chimenechi ali m’maiko osatukuka. Kuwonjezereka kwa anthu kosalekeza kumeneku kumawonjezera kufunika kwa chakudya, nyumba, ndi maindasitale, kumene kumawonongetsa nthaka mowonjezereka, madzi, ndi mpweya kochititsidwa ndi zoipitsa zochokera m’maindasitale ndi zinthu zina.

5 Buku lakuti World Military and Social Expenditures 1991 likusimba kuti: “Chaka chilichonse nkhalango ya ukulu wofanana ndi dziko lonse la [Great Britain] imawonongedwa. Tikapitiriza (kugwetsa mitengo) pa liŵiro limeneli, pofika chaka cha 2000 tidzakhala titachotsa 65 peresenti ya nkhalango za kumalo otentha achinyontho.” M’madera amenewo, malinga nkunena kwa nthumwi ya Mitundu Yogwirizana, mitengo 10 imagwetsedwa pa mtengo 1 uliwonse umene umadzalidwa; mu Afirika chiŵerengerocho chimafikira mitengo yoposa 20 pa mtengo 1 uliwonse. Chotero zipululu zikukula, ndipo chaka chilichonse malo a ukulu wa Belgium amatengedwa kukhala a ulimi.

6 Ndiponso, zaka za zana la 20 zino zakhala ndi imfa zoposa kuŵirikiza kanayi zochititsidwa ndi nkhondo kuposa zaka mazana anayi zapitazo zitaphatikizidwa pamodzi. Kulikonse, upandu ukuwonjezereka, makamaka upandu wachiwawa. Kusweka kwa mabanja, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, AIDS, matenda opatsirana mwakugonana, ndi zinthu zina zoipa zikuchititsa moyo kukhala wovuta kwambiri. Ndipo atsogoleri adziko alephera kupereka mayankho a mavuto ambiri amene akukantha banja la anthu. Chotero, nkomvekera pamene anthu afunsa kuti, Kodi moyo uli ndi chifuno chotani?

7 Kodi funso limenelo layankhidwa motani ndi akatswiri ndi atsogoleri achipembedzo? Pambuyo pa nyengo ya zaka mazana ambiri imeneyi, kodi iwo apereka yankho lokhutiritsa?

Zimene Amanena

8 Katswiri wa chipembedzo cha Confucius Tu Wei-Ming anati: “Tanthauzo lalikulu la moyo limapezeka m’kukhalapo kwathu kwanthaŵi zonse, kwaumunthu.” Malinga nlingaliro limeneli, anthu angapitirize kubadwa, kumenyera nkhondo kukhalapo, ndi kufa. Lingaliro limenelo limapereka chiyembekezo chochepa. Ndipo kodi nlowona nkomwe?

9 Elie Wiesel, yemwe anapulumuka imfa m’misasa yachibalo yopherako anthu ya Nazi mu Nkhondo Yadziko II, anati: “Funso lofunika kwambiri limene munthu ayenera kudzifunsa nlakuti ‘Kodi nchifukwa ninji tili pano?’ . . . Ndikhulupirira kuti moyo uli ndi tanthauzo mosasamala kanthu za imfa zopanda tanthauzo zomwe ndawona.” Koma sanakhoze kunena chimene chinali tanthauzo la moyo.

10 Mkonzi Vermont Royster anati: “M’kulingalira kwa munthu mwiniyo, . . . za malo ake m’chilengedwechi, timawona kuti tili kutali kwambiri kuposa pamene tinayamba. Tidakali ndi mafunso akuti ndife yani ndipo nchifukwa ninji tili pano ndipo tikumka kuti.”

11 Wasayansi yachisinthiko Stephen Jay Gould anati: “Tingalakelake kupeza yankho ‘lapamwamba’​—⁠koma kulibeko.” Kwa okhulupirira chisinthiko oterowo, moyo ndiwo kumenyera nkhondo kukhala ndimoyo kwa amphamvu, imfa ndiyo imathetsa nkhondoyo. Mulibe chiyembekezo m’lingaliro limenelinso. Kachiŵirinso, kodi nlowona?

12 Atsogoleri achipembedzo ambiri amanena kuti chifuno cha moyo ndicho kukhala ndi makhalidwe abwino kotero kuti munthuyo akadzafa moyo wake udzapite kumwamba ndi kukhala kumeneko kwamuyaya. Ponena za anthu oipa amati adzapita ku chizunzo chosatha m’moto wahelo. Komabe, malinga ndi chikhulupiriro chimenechi, anthu adzapitiriza kukhala padziko lapansi popanda chikhutiro monga momwe achitira nthaŵi yonseyi. Koma ngati chifuno cha Mulungu chinali chakuti anthu akakhale kumwamba mofanana ndi angelo, nchifukwa ninji sanawalenge mwanjira imeneyo poyambapo, monga momwe anachitira angelo?

13 Ngakhale atsogoleri achipembedzo amavutika ndi malingaliro amenewo. Dr. W. R. Inge, yemwe kale anali wansembe wamkulu wa tchalitchi cha St. Paul Cathedral m’London, panthaŵi ina anati: “Kwa moyo wanga wonse ndakhala ndikuyesayesa kupeza chifuno cha moyo. Ndayesayesa kuyankha mafunso atatu amene nthaŵi zonse amawonekera kukhala ofunika kwambiri kwa ine: funso la umuyaya; funso la chikhalidwe cha anthu; ndi funso la choipa. Ndalephera. Sindinayankhe nlimodzi lomwe.”

Chiyambukiro Chake

14 Kodi malingaliro ambiri osiyana amenewo a akatswiri ndi atsogoleri achipembedzo pa funso lonena za chifuno cha moyo ali ndi chiyambukiro chotani? Ambiri amayankha monga momwe anachitira mwamuna wokalamba amene anati: “Ndakhala ndikudzifunsa kwa moyo wanga wonse chifukwa chake ndili pano. Ngati pali chifuno chake, ndilibe nazo kanthu tsopano.”

15 Anthu ambiri amene amawona kuchuluka kwa malingaliro pakati pa zipembedzo zadziko amanena kuti zimene munthu amakhulupirira zilibe kanthu mpang’ono pomwe. Amalingalira kuti chipembedzo changokhala kanthu kena kopumulitsira maganizo, kopatsa mtendere wamaganizo pang’ono ndi chitonthozo kuti munthu akhoze kulaka mavuto a moyo. Ena amalingalira kuti chipembedzo changokhala chinthu chongokhulupirira. Amalingalira kuti manenanena azipembedzo omwe akhalapo kwa zaka mazana ambiri sanayankhe funso lonena za chifuno cha moyo, ndiponso sanawongolere moyo wa anthu wamba. Ndithudi, mbiri imasonyeza kuti zipembedzo zadzikoli zatsekereza anthu kupita patsogolo ndipo zachititsa chidani ndi nkhondo.

16 Komabe, kodi nkofunikadi kupeza chowonadi cha chifuno cha moyo? Katswiri wa thanzi la maganizo Viktor Frankl anayankha kuti: “Kuyesayesa kupeza tanthauzo la moyo wa munthuwe ndiko chisonkhezero champhamvu mwa munthu. . . . Palibe chilichonse m’dziko, ndikunenetsadi, chimene chingathandize munthu kwambiri kupirira ngakhale mikhalidwe yoipitsitsa, koposa kudziŵa kuti moyo uli ndi tanthauzo.”

17 Popeza kuti nthanthi za anthu ndi zipembedzo sizinalongosole mokhutiritsa chifuno cha moyo, kodi tingatembenukire kuti kuti tidziŵe chifunocho? Kodi kuli magwero a nzeru yapamwamba amene angatiuze chowonadi pankhaniyi?

Baibulo limene tagwiritsira ntchito ndilo Revised Nyanja (Union) Version, kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina. Komabe, tatsatira kalembedwe ka orthography yatsopano. Pamene NW yasonyezedwa motsatira mawu ogwidwa, iko kumasonyeza kuti kutembenuzidwako kwachokera mu New World Translation of the Holy Scriptures​—⁠With References, Kope la 1984

[Study Questions]

1. Kodi nchiyani chimene chimafunsidwa kaŵirikaŵiri ponena za chifuno cha moyo, ndipo ndimotani mmene munthu wina ananenera?

2, 3. Kodi nchifukwa ninji kupeza chuma chakuthupi sikuli chifuno cha moyo chokhutiritsa?

4. Kodi nchifukwa ninji ena amakayikira kuti moyo uli nchifuno chilichonse?

5. Kodi nchiyani chikuchitikira zomera padziko lapansi?

6, 7. Kodi ndimavuto ena ati amene atsogoleri aumunthu sangathe kuwathetsa, chotero kodi ndimafunso otani amene ayenera kuyankhidwa?

8, 9. (a) Kodi katswiri wa ku China ananenanji ponena za chifuno cha moyo? (b) Kodi wopulumuka m’misasa yachibalo yopherako anthu ya Nazi ananenanji?

10, 11. (a) Kodi mkonzi wina anasonyeza motani kuti munthu alibe mayankho? (b) Kodi nchifukwa ninji lingaliro la wasayansi yachisinthiko lili losakhutiritsa?

12, 13. Kodi atsogoleri a tchalitchi ali ndimalingaliro otani, ndipo kodi ngokhutiritsa kwambiri kuposa a anthu akudziko?

14, 15. Kodi malingaliro osemphanawo ali ndi chiyambukiro chotani pa anthu ambiri?

16. Kodi kupeza chifuno cha moyo kungakhale kofunika motani?

17. Kodi ndimafunso otani amene tiyenera kufunsa tsopano?

[Picture on page 4]

“Chaka chilichonse nkhalango ya ukulu wofanana ndi dziko lonse la [Great Britain] imawonongedwa”

[Picture on page 5]

“Ndakhala ndikudzifunsa kwa moyo wanga wonse chifukwa chake ndili pano”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena