Kufunafuna Chifuno
CHIYAMBIRE nthaŵi ya Charles Darwin, pakhala chitsenderezo chachikulu chochokera kwa akatswiri a zamoyo cha kuvomereza nthanthi yakuti moyo, monga chotulukapo cha chisinthiko, ulibiretu chifuno. Komabe, ambiri amakana lingaliroli mwachibadwa. Okwatirana achichepere, akumayang’ana khanda lawo lokongola lobadwa kumene, angakupeze kukhala kovuta kukhulupirira kuti moyo watsopanowu ulibe chifuno. Kwa iwo, uli chozizwitsa, chodabwitsa chomwe chimapangitsa moyo wawo kukhala watanthauzo kwenikweni ndi wokhutiritsa.
Ngakhale asayansi ena samavomereza kuti moyo uli mwaŵi wopanda tanthauzo. Chifukwa ninji satero? Chifukwa cha zimene The Encyclopedia Americana ikutcha “kucholoŵana kwakukulu ndi kulinganizika kwa zolengedwa zamoyo.” Americana ikupitiriza kunena kuti: “Kupenda mosamalitsa maluŵa, tizilombo, kapena nyama zoyamwitsa kumasonyeza kulinganizidwa kwa ziŵalo kwadongosolo kodabwitsa kwambiri.”
Polingalira kucholoŵana ndi kulinganizika kokongola kumeneko—komwe kumapezeka ngakhale m’zolengedwa zamoyo zazing’ono kwenikweni—wasayansi wa ku South Africa Dr. Louw Alberts anagwidwa mawu mu Cape Times akunena kuti: “Ndimakhala ndi chikhutiro chamaganizo chokulira mwakuvomereza kuti kuli Mulungu mmalo mongovomereza kuti [moyo] unakhalako mwamwaŵi.” Polankhula za kapangidwe kamakemikolo ka zinthu zamoyo, katswiri wopenda zakuthambo wa ku Briteni Bwana Bernard Lovell analemba kuti: “Kuthekera kwa . . . chochitika cha mwamwaŵi chochititsa kupangidwa kwa imodzi ya mamolecule aang’ono kwambiri a protein nkwakung’ono zedi. . . . Kulidi kosatheka.”
Mofananamo, katswiri wopenda zakuthambo Fred Hoyle analemba kuti: “Dongosolo lonse la maphunziro a zamoyo losasintha limanenabe kuti moyo unayambika wokha. Komabe pamene akatswiri a misanganizo ya zinthu zamoyo akupeza zowonjezereka ponena za kucholoŵana kodabwitsa kwa moyo, kuli kowonekeratu kuti kuthekera kwakuti unakhalako mwamwaŵi nkwakung’ono kwakuti kumanyalanyazidwa kotheratu. Moyo sunakhaleko mwamwaŵi.”
Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Ngati moyo sunakhaleko mwamwaŵi, ndiye kuti unachita kulinganizidwa. Ndipo ngati ziri choncho, uyenera kuti uli ndi Wolinganiza. Ndipo ali Wolinganiza wodziŵa chotani nanga! Molondola wamasalmo ananena kuti: ‘Chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza.’ (Salmo 139:14) Koma kodi zimenezi zikutiuzanji ponena zakuti kaya moyo uli ndi chifuno kapena ayi?
Eya, anthu nawonso amalinganiza ndi kupanga zinthu. Amapanga ndege za jet. Amapanga makina oyengera mafuta. Amapanga malo opangira magetsi. Ndipo amapanga zinthu zina zosaŵerengeka zomwe ziri zocholoŵana kwambiri. Koma anthuwo samalinganiza ndi kupanga zinthu zocholoŵana zoterozo popanda chifukwa. Chirichonse chimapangidwa ndi chifuno.
Popeza kuti palibe chirichonse chimene anthu anapanga chomwe chiri chofanana ndi kucholoŵana kwa zinthu zamoyo, ndithudi Wolinganiza wa moyo sakadalenga moyowo popanda chifuno chake. Nkopanda nzeru kukhulupirira kuti ‘chipangidwe [chathu] ndi chodabwiza’ ndiyeno nkusiidwa popanda chitsogozo ndi chifuno.
Kufunafuna Chifuno
Chenicheni chakuti Mlengi analenga anthu kuti akwaniritse chifuno chimachilikizidwanso mwamphamvu ndi mfundo yakuti mwachibadwa anthufe timafunafuna chifuno m’miyoyo yathu. Gilbert Brim, katswiri wa zamaganizo, analankhula ponena za chibadwa cha munthu chakufuna chifuno pamene ananena kuti: “Anthu ambiri amapeza mwaŵi wakupita patsogolo ndi chitokoso pantchito. Koma amene sangazipeze amafunafuna zitokoso zapadera ndi zipambano kwinakwake: kutaya kulemera kwathupi, kukhala katswiri woseŵera golf, kudziŵa kuphika mazira kapena kufunafuna zitokoso zina—kaya kukhale kulendewera kapena kulaŵa zakudya zatsopano.” Katswiri wa matenda amisala Viktor Frankl ananenadi kuti: “Kukalimira kupeza tanthauzo la moyo wa munthuwe ndiko chisonkhezero chachikulu mwa munthu.”
Tiyeni tipende zonulirapo zina zimene anthu amadzikhazikitsira m’moyo.
Kodi Nchiyani Chimapangitsa Moyo Kukhala ndi Chifuno?
Wachichepere wina, atafunsidwa ponena za chifuno chake m’moyo, anati: “Ndimalingalira zokhala ndi chinyumba chabwino, galimoto yabwino, ndi mwamuna wabwino woyenda naye m’galimotomo. Ndidzakhutiritsa zokhumba zanga. Ndine munthu wodzikonda. Ndikufuna zimene zidzandisangalatsa, osati zimene zidzasangalatsa anthu onse.” Ngati zimenezi zikumveka zadyera kwa inu, mukuganiza molondola. Ndidyeradi. Komabe, momvetsa chisoni, umenewu simkhalidwe wachilendo.
Komabe, kodi kungolondola zinthu zakuthupi ndi zosangulutsa kumakhutiritsa kufunika kwakukhala ndi tanthauzo m’moyo? Ayi. Pamene zosangulutsa zikhala cholinga chathu chokha, zimakhala zosakhutiritsa. Kaŵirikaŵiri anthu amene amazipanga kukhala chonulirapo chawo chachikulu m’moyo amakhala akubwereza m’mitima mwawo malingaliro a mfumu yachuma ya nthaŵi zakale yomwe inagwiritsira ntchito mphamvu zake ndi chuma kufufuza mbali zosiyanasiyana za zosangulutsa zomwe zidaliko panthaŵiyo. Tamverani chigamulo chomwe anachifikira:
‘Ndinakundikanso siliva ndi golidi ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira zamitundumitundu. . . . Ndipo tawona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima.’—Mlaliki 2:8, 11.
Ambiri amapeza chikhutiro m’ntchito kapena kugwiritsira ntchito luntha lawo kapena nyonga kufikira zimene zikuwoneka kukhala zonulirapo zopindulitsa. Komabe, pambuyo pakanthaŵi, ntchito simakhutiritsa kotheratu kufunika kwakukhala ndi chifuno m’moyo. Peter Lynch, wofotokozedwa kukhala “katswiri weniweni wa kampani yosunga ndalama,” anasiya ntchito yake yopindulitsa pamene anazindikira kuti chinachake chofunika koposa m’moyo wake chinali kusoŵeka. Kodi chinali chiyani? Unansi wake ndi banja lake. Iye anavomereza kuti: “Ndinakonda zomwe ndinkachita, koma ndinapanga chigamulo, ndipo ngakhale anthu ena anatero: Kodi . . . tikuchitiranji zimenezi? Sindidziŵa munthu aliyense amene pakufa analakalaka kuti akadathera nthaŵi yochuluka ku ofesi.”
Chifukwa chake, msungwana wina wachichepere anasonyeza chikatikati pamene analingalira zonulirapo zake m’moyo nati: “Chimodzi cha zokhumba zanga ndicho kupeza ntchito. Koma ndiganiza kuti chokhumba changa chachikulu ndicho kukhala ndi banja lachimwemwe.” Inde, banja lathu lingapereke tanthauzo ndi chifuno m’moyo. Mkazi wokwatiwa wachichepere anati: “Kale kwambiri ndinawona kukhala kholo monga chimodzi cha zinthu zimene anthu anabadwira, chimodzi cha zifuno za moyo, ndipo sindinakaikire konse chimenecho.”
Ena amafunafuna chifuno cha moyo m’zolondola zina. Ena—mosapenekera kuphatikizapo asayansi amene amanena kuti moyo ndi mwaŵi wopanda tanthauzo—amapeza chifuno m’kulondola chidziŵitso. Katswiri wachisinthiko Michael Ruse analemba kuti: “Tiri ndi chikhumbo chakudziŵa, ndipo chimatipangitsa kukhala osiyana ndi zinyama. . . . Pakati pa zosoŵa zathu zazikulu ndi mathayo pali chija chakupatsira ana athu, nzeru zakale zomwe tinakundika, limodzi ndi changu chathu ndi zipambano zathu. . . . Kufunafuna chidziŵitso, ndi zipambano, kumapanga mbali yapadera ya chibadwa cha munthu.”
Ena amapeza kuti kugwira ntchito yochilikiza chikhulupiriro chinachake kumapereka chifuno m’miyoyo yawo. Iwo amagwira ntchito kufuna kusunga mitundu yosawonekawoneka ya nyama. Kapena amalimbana ndi kuipitsa ndi kuwonongedwa kwa malo otizinga. Anthu osamalira amachilikiza kuyenera kwa ana kapena kugwirira ntchito anthu osoŵa pokhala kapena osauka. Kapena amagwira ntchito kuletsa kufalikira kwa kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa. Nthaŵi zina anthu oterowo amachita zabwino zochuluka, ndipo zimene amachita zimalemeretsa miyoyo yawo ndi chifuno.
Zolefulitsa ndi Zogwiritsa Mwala
Komabe, tiyenera kuvomereza kuti kaŵirikaŵiri anthu amalefulidwa polondola zonulirapo ngakhale ngati zonulirapozo ziri zopindulitsa. Makolo amene amaika chikondi ndi kuyesayesa kwakukulu polera ana awo nthaŵi zina amawataya m’ngozi, upandu, matenda, kapena kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa. Kapena pamene anawo akula, angayambukiridwe ndi mzimu wadyera wadziko lino nalephera kubwezera chikondi cha makolo awo.
Amene amagwira ntchito zolimba kuwongolera malo otizinga kaŵirikaŵiri amalefulidwa ndi zifuno za malonda kapena chenicheni chakuti ena samasamala. Amene amagwira ntchito zolimba kuwongolera mkhalidwe wa osauka amalephera chifukwa cha kuchuluka kwa ntchitoyo. Munthu amene amapeza ntchito yake kukhala yokhutiritsa amalefulidwa pamene zaka zake zakuleka ntchito zikwana. Wofufuza amene amapeza kuti kulondola chidziŵitso kumakhala kokhutiritsa kotheratu amalefulidwa pamene moyo wake uyandikira mapeto ake ndipo padakali mafunso ambiri osayankhidwa. Munthu amene wathera moyo wake kukundika chuma amapeza kuti pomalizira pake, akafunikira kuchisiya kwa anthu ena.
Mfumu yakale yogwidwa mawu poyambirirapo inafotokoza zina za zokhumudwitsa zimenezi pamene inalemba kuti: “Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno, pakuti ndidzazisiya zipatso zake kwa munthu amene adzanditsata. Kodi munthu amene adzanditsata adzakhala wotani, amene adzalandira zonse zimene ena anakundika? Kodi adziŵa ndani ngati adzakhala munthu wanzeru kapena chitsiru? Koma adzalamulira zipatso zonse za ntchito yanga ndi luso.”—Mlaliki 2:18, 19, The New English Bible.
Pamenepo, kodi moyo ulibiretu chifuno monga mmene mawu ameneŵa onenedwa mowona mtima akusonyezera? Kodi zonulirapo zosiyanasiyana zimene anthu amalondola zidzangowafikitsa ku zaka 70, 80, kapena 90 za moyo zimene ambiri amakhala nazo? Ndiponso, kodi zonulirapo zimenezi zilibedi tanthauzo? Ayi. Kwenikwenidi, zimasonyeza chinachake chapadera kwambiri ponena za mmene tinapangidwira, ndipo zimapereka umboni wakuti moyo ulidi ndi chifuno chabwino kwambiri. Koma kodi tingachipeze motani chifuno chimenechi?
[Zithunzi patsamba 17]
Ena amapeza kuti kulondola chidziŵitso kumadzetsa tanthauzo ndi chifuno m’miyoyo yawo
Anthu samapanga zinthu zocholoŵana popanda chifuno
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi cha NASA