Chifuno Chenicheni cha Moyo
TANGOYEREKEZERANI kuti mukuchezera malo ogwirira ntchito a bwenzi lanu. Iye wangomaliza kumene kupanga chinachake, ndipo mwachita nacho chidwi kwambiri. Chinthucho chapangidwa mokongola ndi mosangalatsa. Koma ngakhale mutayesetsa kuchilingalira, mulephera kudziŵa chifuno chake. Kodi mungachidziŵe bwanji? Eya, mudzangofunsa bwenzi lanulo, ndipo mosapenekera lidzakhala lachimwemwe kukuuzani.
Chotero kodi tingachidziŵe motani chifuno cha moyo? Eya, bwanji osamfunsa Mulungu, ‘chitsime cha moyo’? (Salmo 36:9) Kodi mungachite motani zimenezo? Mosangalatsa, iye walankhula nafe kudzera m’Baibulo. Anachititsa anthu okhulupirira kulemba maganizo ake m’njira imene tikhoza kuwamva. Kwenikwenidi, chifuno cha moyo chafotokozedwa m’mawu oŵerengeka aŵa: Tiri pano kuti tiphunzire ponena za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake. Baibulo limati: ‘Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’—Mlaliki 12:13.
Kodi zimenezo zikumveka zokhweka? Eya, siziri tero. Kukhala kwathu pano kuti tiphunzire ponena za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake kuli ndi tanthauzo lalikulu lodabwitsa.
Chifuno Choyambirira cha Mulungu
Kuphunzira zimene Mulungu poyambirira analinganizira anthu kudzakuthandizani kumvetsetsa bwino chifuno cha moyo. Kudzasonyezanso chifukwa chake zinthu zina zotchulidwa m’nkhani yapitayo zimabweretsa tanthauzo ndi chifuno m’miyoyo ya ambiri lerolino.
Cholembedwa cha Baibulo chonena za kulengedwa kwa munthu chimati: ‘Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.’ (Genesis 1:26) Chotero, anthu anapangidwa ndi kuthekera kwakukhala monga Mulungu, kukhala ndi mikhalidwe yapadera imene iye ali nayo, kuphatikizapo nzeru, mphamvu, chilungamo, ndi chikondi. Pamenepo, kodi nzodabwitsa kuti ena amakupeza kukhala kokhutiritsa kufunafuna chidziŵitso chatsopano kapena kuchita ntchito imene imapereka chitokoso ku mphamvu zawo za maganizo kapena zakuthupi? Ndipo kodi nzosayembekezeredwa kuti kuthandiza ena kumapereka chifuno chokhutiritsa m’miyoyo ya ambiri? Kutalitali. Kumbali ina, chimenecho chiri chimodzi cha zinthu zomwe tinalengedwera.
Cholembedwa cha Baibulo chimapitiriza kunena kuti anthu anapatsidwa thayo lakuyang’anira zamoyo zina zonse padziko lapansi—“nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga . . . ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:26) Chotero, nkosadabwitsa kuti ngakhale lerolino ambiri amapeza chikhutiro kukhala pafupi ndi zinyama ndi kuseŵera nazo. Ena amadziwona kukhala ndi thayo pa zinyama kumlingo wakuti amagwira ntchito zolimba kusungitsa mitundu yowopsezedwa, kapena kuchita ndawala yotsutsa kusautsa zinyama mosayenerera.
Anthu analamulidwanso ‘kugonjetsa dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Ndithudi, sizinatanthauze kuti anthu ayenera kusakaza dziko lapansi mwadyera ndi mopanda thayo kufikira chuma chake chitatha, thambo lake litaipitsidwa, ndi nyanja ndi mtunda wake zitadzazidwa ndi zinyalala. Mmalomwake, Mulungu anapereka chitsanzo chogonjetsera dziko lapansi pamene ‘anabzala m’munda ku Edene chakum’mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.’ (Genesis 2:8) Munda wa Edene umenewu unali fanizo losonyeza mmene dziko lapansi liyenera kukhalira. Unasonyeza chifuno cha Mulungu cha pulaneti lathu.
Cholembedwa cha Baibulocho chikufotokoza kuti: ‘Mulungu ndipo anadalitsa iwo [mwamuna ndi mkazi oyamba], ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.’ (Genesis 1:28) Mulungu anafuna kuti anthu akhale ndi ana ndi kukhala padziko lapansi. Anabweretsa pamodzi mwamuna ndi mkazi oyamba ndipo, kwenikweni, anachititsa ukwati woyamba weniweniwo. (Genesis 2:22-24) Nkosadabwitsa kuti ukwati ndi banja zimawonjezera tanthauzo ndi chifuno ku miyoyo ya ambiri!
Mmene Moyo Ukadakhalira
Tikamaphunzira Baibulo, kumakhala kowonekeratu kuti Mulungu anafuna kuti banja la Adamu likule ndikuti iye ndi ana ake afutukule malire a munda wa Edene kufikira anthu atadzaza dziko lonse lapansi. Ndipo dziko lapansi logonjetsedwalo likanakhala paradaiso. Zowonadi, munthu akagwiritsira ntchito chuma cha dziko lapansi kuti apindule. Koma izi zikachitidwa mwathayo. Munthu anafunikira kukhala mdindo wa dziko lapansi, osati wolisakaza. Kuwonongedwa kwa dziko lapansi kumene timawona lerolino kuli kotsutsana ndi chifuniro cha Mulungu, ndipo amene amakhala ndi phande m’zimenezo akuchita mosemphana ndi chifuno cha moyo.—Chivumbulutso 11:18.
Tikuphunziranso chinachake m’cholembedwa choyambirira cha Baibulo, kuti sichinali chifuno cha Mulungu kuti anthu adzifa. Makolo athu oyamba anafa kokha chifukwa chakuti sanamvere Mulungu. (Genesis 2:16, 17) Chifukwa chosamvera, anasiya kukwaniritsa chifuno cha moyo—anasiya kuchita chifuniro cha Mulungu. Chotero iwo sanangofa komanso ana awo onse ayambukiridwa ndi imfa chifukwa cholandira kupanda ungwiro kuchokera kwa iwo. (Aroma 5:12) Komabe, poyambirira anthu analengedwa kuti akhale ndi moyo kosatha, osati kufa. Mwachiwonekere ndicho chifukwa chake ambiri amakupeza kukhala kolefula kulingalira kufupikitsidwa kwa ntchito ya moyo wawo kochititsidwa ndi imfa.
Kukwaniritsa Chifuno cha Mulungu
Chifuno choyambirira cha Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansili sichinasinthe. Iye akufunabe kuti dziko lapansi likhale paradaiso wokhala ndi fuko la anthu angwiro. Komabe, iye anapanga makonzedwe akuthetsa zotulukapo zomvetsa chisoni za kulephera kwa makolo athu oyamba. Lerolino kuchita chifuniro cha Mulungu kumaphatikizapo kuchita mogwirizana ndi makonzedwe onsewa a Mulungu. Mosangalatsa, Baibulo limapereka malongosoledwe a kukwaniritsidwa kopita patsogolo kwa chifuno chake.
Timaŵerenga m’bukhu loyamba la Baibulo kuti Mulungu analankhula za ‘mbewu’ yomwe ikachotsa chivulazo chonse chobweretsedwa ndi Adamu ndi Hava chifukwa cha kulephera kuchita chifuniro Chake. (Genesis 3:15) M’Malemba Achikristu Achigiriki (“Chipangano Chatsopano”), timaŵerenga za kuwonekera kwa Yesu Kristu monga ‘mbewu’ imeneyo, za moyo wake wopanda tchimo, ndi imfa yake yochititsidwa ndi adani ake. Kwenikweni, imfa ya Yesu inali nsembe yoperekedwa mmalo mwathu, kutitsegulira njira yopezeranso moyo wamuyaya umene Adamu ndi Hava anautaya. (Ahebri 7:26; 9:28) Inde, Baibulo limati: ‘Yense wakukhulupirira iye [sadzataika koma adzakhala] nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16.
Ndipo pali zina zambiri. Atafa, Yesu anaukitsidwa monga cholengedwa chauzimu chosakhoza kufa ndipo tsopano akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Posachedwapa Ufumu umenewo udzachitapo kathu kuchotsa maboma apadziko lapansi omwe alipowa ndi kuikapo chitaganya cha dziko latsopano chomwe chidzalamulira zochita za anthu. Ulosi wa Baibulo umalonjeza kuti: ‘[Ufumuwo] sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.’—Danieli 2:44.
Pambuyo pake, Ufumu umenewu udzayang’anira ntchito yosangalatsa yobwezeretsa Paradaiso padziko lapansi ndi kufikitsa anthu ku ungwiro. Baibulo limalankhulanso za kuuka kwa akufa, kotero kuti nawonso adzakhale ndi mwaŵi wakukhala ndi phande m’kukwaniritsa chifuno chachikulu cha Mulungu kwa anthu. (Machitidwe 24:15) Pamenepo lonjezo labwino ili lidzakwaniritsidwa: ‘Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.’—Salmo 37:11, 29.
Kupindula Mwaumwini
Kuti tipindule ndi kukwaniritsidwa kwa chifuno chachikulu cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi, choyamba tiyenera kumdziŵa Mulungu. Yesu Kristu anati: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’ (Yohane 17:3) Kodi tingachite motani zimenezo? Timaphunzira zinthu zina ponena za Mulungu mwakuyang’ana dziko lotizinga, zolengedwa, kuphatikizapo miyamba yodzaza ndi nyenyezi. (Salmo 19:1) Komabe, timaphunzira zambiri ponena za Mulungu—limodzi ndi Mwana wake, Yesu Kristu—makamaka kupyolera m’Baibulo. Timaphunzira dzina lake ndi mikhalidwe yake, ndipo timapeza mwatsatanetsatane zimene Mulungu wachitira anthu. Chidziŵitso choterocho chimatipangitsa kumkonda ndi kutiyandikitsa kwambiri kwa iye ndi Mwana wake.
Kudziŵa Mulungu kumatisonkhezera kufuna kuchita chifuniro chake. Mwinamwake tinapempherapo monga momwe Yesu analangizira kuti: ‘Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’ (Mateyu 6:10) Chifuno chenicheni cha moyo—chimene chimadzetsa chikhutiro chowona—ndicho kukhala mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu chimenecho.
Komabe, kodi kuchita chifuniro cha Mulungu kumaphatikizapo chiyani? Kwa Adamu ndi Hava, kunaphatikizapo kuyang’anira zinyama ndi kugonjetsa dziko lapansi ndi kulidzaza ndi ana angwiro. Ngati tichita chifuniro cha Mulungu lerolino, tiyenera kuphunzira ndi kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe yadipo ya Yesu. Ndipo tiyenera kutsanzira chitsanzo cha Yesu mwakuuza ena ponena za ‘mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu.’—Mateyu 24:14, NW.
Kuchita chifuniro cha Mulungu kumaphatikizaponso kukulitsa umunthu waumulungu. Chotero timazindikira zinthu zimene Mulungu amazida—monga ngati kunama, kuba, miseche yovulaza, mkwiyo wosalamulirika—ndipo timazikana. Timaphunziranso mikhalidwe imene Mulungu amakonda—monga ngati chikondi, chimwemwe, mtendere, chifundo, ndi ubwino—ndipo timaikulitsa mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:19-24) Ngati tifuna kupeza moyo wamuyaya, tiyenera kukhala mtundu wa anthu amene Mulungu amafuna kukhala nawo kwamuyaya. Ndithudi, kuphunzira ponena za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake kumapatsa miyoyo yathu chifuno ndi tanthauzo kuposa chinthu china chirichonse!
Kusiyana Kumene Kumakhalapo
Miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse imatsimikizira kuti kupeza chifuno chenicheni cha moyo kumakhaladi ndi chiyambukiro chachikulu pa munthu. Talingalirani chitsanzo cha Wayne, amene anasweka mtima ndi imfa ya mkazi wake woyamba. Mtsogoleri wake wachipembedzo analephera kumtonthoza, choncho Wayne anadzitanganitsa ndi ntchito yodzipereka mwaufulu. Anatumikira monga kazembe wa Gulu Lankhondo la America ndipo anali wokangalika m’magulu andale. Ndiyeno anakwatiranso, koma ukwatiwo unali ndi mavuto ambiri. Iye ndi mkazi wake analibe chitsogozo m’miyoyo yawo.
Komabe, tsiku lina Wayne anatenga Baibulo nayamba kuliŵerenga. Analimaliza m’miyezi itatu, ndiyeno anati: “Tsopano ndikudziŵa kuti panali chifuno cha kukhala kwathu pano ndi chiyembekezo cha moyo pambuyo pa imfa.” Iye anamuuza mkazi wake kuti: “Tiyenera kupeza anthu oyanjana nawo amene amamamatira ku Baibulo.” Posakhalitsa anakumana ndi Mboni za Yehova, ndipo kukambitsirana kwawo kunalimbitsa chikhumbo chawo chakuchita chifuniro cha Mulungu. Wayne ndi mkazi wake anapatulira miyoyo yawo kwa Mulungu, ndipo moyo wawo wabanja unakhala wopindulitsa kwambiri.
Susan, mwana wamkazi wa amishonale a Presbyterian anafuna kuchita chinachake m’moyo wake chomwe chikathandizadi dziko. Nkhani yonena za maupandu a mphamvu ya nyukiliya inamkhutiritsa kuti inali nkhani yofunika koposa. Chotero anachoka pakoleji kuti akathere nthaŵi yake yonse kuphunzitsa anthu ponena za vutolo. Pamene anali ndi zaka 21, anatumikira monga mgwirizanitsi wa msonkhano waukulu wotsutsa zida za nyukiliya. Pambuyo pake anachezeredwa ndi Mboni za Yehova nasonyezedwa zimene Baibulo limanena ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, anapeza chifuno chenicheni cha moyo. Ngakhale kuti mosakaikira adakali kuda nkhaŵa ndi kuwononga dziko lapansi kumene anthu akuchita, iye amazindikira kuti Mulungu adzathetsa mavutowa kupyolera mu Ufumu wake. Chifukwa chake, amathandiza anthu kukhulupirira zimenezo.
Marielle anapanga kusangalala ndi zinthu zimene dziko limapereka kukhala chifuno chake m’moyo. Anapeza ntchito. Anasangalala ndi zinthu zonse zopezeka ku Los Angeles, California, U.S.A., kuphatikizapo mapwando ndi mankhwala oledzeretsa. Koma pamene anayamba kuphunzira Baibulo, anadziŵa Mulungu nayamba kumtumikira, ndipo anazindikira kuti zinthuzo zidali zopanda tanthauzo. Iye akunena kuti moyo wake ngwatanthauzo tsopano popeza kuti umagwirizana ndi zifuno za Mulungu.
Chiŵerengero cha anthu amene miyoyo yawo yalemeretsedwa mwakuphunzira chifuno chenicheni cha moyo chikuwonjezereka ndi mazana ambiri tsiku lirilonse. Kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chowona cha moyo chimenecho mwakuchita chifuniro cha Atate wathu wachikondi, wakumwamba, kumapangitsadi kusiyana. Ndichinthu chomwe chingasinthe moyo wanu wonse kukhala wabwinopo. Tikupemphani kupenda nkhaniyo nokha. Moyo wanu udzakhala wokhutiritsa kwambiri ngati muchita zimenezo.
[Chithunzi patsamba 19]
Mpatsi wa moyo adali ndi chifuno polenga anthu
[Chithunzi patsamba 20]
Mulungu sanasinthe chifuno chake chokhala ndi dziko lapansi laparadaiso lodzazidwa ndi fuko la anthu angwiro