Kodi Mose Anali Wolotera Madzi?
“MOSE, amene anatulutsa madzi mwakumenya thanthwe ndi ndodo (Numeri 20:9-11), watchedwa wolotera madzi woyamba.” (The Encyclopedia Americana) Limeneli ndilingaliro limene limabuka kaŵirikaŵiri pamene nkhani yolotera ikambidwa. Posachedwapa magazini a National Wildlife motsimikiza anatcha ndodo ya Mose kuti “ndodo yopenduzira.” Ndipo olotera ena amakhulupirira kuti mphamvu yawo imachokera kwa Mose.
Komabe, mosiyana ndi zimenezi, Mose ndiye amene analemba lamulo lotsutsa kuchita ula! (Deuteronomo 18:10) Ndipo chozizwitsa cha pa Meriba chinali chosiyana kotheratu ndi kulotera madzi. Olotera ambiri amadalira ndodo kufufuza madzi obisika; amailondola, akumaiyembekezera kuti igogode kapena kuphiriphitha. Koma Mose sanalondole konse ndodo yake akumayembekezera kuti igogode pansi; kwenikweni, iye sanafufuze madzi nkomwe. Yehova, Mlengi wa dziko lapansi ndi mitsinje yake yamadzi pansi panthaka, anasonyeza Mose pamalo enieni amadzi ndi mmene angapezere madziwo: “Munene ndi thanthwe,” Mulungu analamula motero, “kuti liwapatse madzi.”—Numeri 20:8.
Ndiponso, kaŵirikaŵiri olotera amangouza anthu malo oti akumbe. Pamene ndodo ya Mose inamenya thanthwelo, panatuluka mtsinje wa madzi—okwanira kuthetsa ludzu la mtundu wonsewo. Mose anadzidzetsera mkwiyo wa Mulungu pamene anadzitamandira pachozizwitsa chimenechi. Kukanakhala koipa kwambiri chotani nanga chikhala kuti anatamanda ndodo yake—mtengo wopanda pake!