Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 9-10
  • Kanthu Kabwinopo Koposa Kosanunkha Kanthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kanthu Kabwinopo Koposa Kosanunkha Kanthu
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wolephera Yemwe Anafikira Kukhala Wopambana
  • Chuma cha Mtengo Wapatali
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 9-10

Kanthu Kabwinopo Koposa Kosanunkha Kanthu

PAFUPIFUPI otchova juga onse amakhala amphaŵi kwadzawoneni kuposa pamene sanali kutchova juga. Kaŵirikaŵiri, ngakhale oŵerengekawo omwe amapambana ndalama zambiri amapeza kuti zipambano zawo sindizo njira yopezera chimwemwe.

Mwamuna wina wosakwatira wazaka 36 ku Japani anapambana lotale ya ndalama zokwanira $45,000. Anafuna kugula nyumba ndi ndalama zakezo, koma anthu anamsirira ndi kumneneza kwambiri kotero kuti sanazifunenso. Zinawadabwitsa kwambiri anzake a pantchito pamene iye anawotcha tikiti lake lokatengera ndalamazo.

Apolisi ku Florida anagwira mkazi yemwe, mosasamala kanthu ndi kupambana lotale ya ndalama zokwanira $5 miliyoni, analinganiza chiŵembu chakupha mpongozi wake. Mwana wake wamwamuna ananena kuti mkaziyo anakwiya chifukwa cha kusayendetsa bwino malonda ndi kuwawanya ndalama komwe kunawononga chuma chake chonse.

Wolephera Yemwe Anafikira Kukhala Wopambana

Domingo anali wotchova juga womwerekera ndi atate wa ana asanu. Iye akufotokoza kuti: “Nditapambana, mpamene zinthu zinaipirapo. Ndinadziwona kukhala munthu waluso lapadera kwambiri, ndipo sindinazengereze kupitanso kuthebulo lotchovera juga kukasonyeza kuti zimenezo sizinangochitika mwangozi.

“Pamene mzimuwo unazama mwa ine, ndinakhala ngati munthu wogodomala. Ndinali wokonzekera kusiya mkazi wanga ndi ana chabe kuti ndikapitirize kutchova juga. Ngakhale kuti mobwerezabwereza ndinalumbira kwa mkazi wanga kuti sindikatchovanso juga, ndinadziŵa pansi pa mtima kuti zimenezo zinali bodza lankunkhuniza. Ndikumbukira kuti nthaŵi ina ndinauza mkazi wanga motsimikiza kuti ndidalekeratu kutchova juga, pamene panthaŵi yomweyo, ndinali kulingalira za njira yopezera ndalama zokatchovera juga.

“Ndinataya ndalama zanga zonse, za mkazi wanga, ndi za bizinesi yanga, ndipo ndinagwera m’ngongole zowopsa. Tsiku silinali kupita popanda kubetcha kanthu, kufikira pamene kanthu kena kanachitika komwe kanandikakamiza kudzipenda ndekha. Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinachita chidwi ndi zimene ndinaphunzira, koma sindinasiye pomwepo kutchova juga. Ndikuyamikira Mboni yomwe inaphunzira nane chifukwa chakuleza mtima kwake.

“Koma mwamsanga, uthenga wa Baibulo unayamba kundiyambukira. Unandithandiza kuchoka m’dziko langa lamaloto ndi kudziwona ine mwini monga momwe Mulungu amandiwonera. Zinali zachilendo. Ndinamva manyazi kwambiri, mofanana ndi amene mtumwi Paulo analembera m’zaka za zana loyamba kuti: ‘Ndipo munali nazo zobala zanji nthaŵi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chiri imfa.’—Aroma 6:21.

“Kufika pakudziŵa Mulungu, dzina lake, umunthu wake, ndipo makamaka chifundo chake kunandisonkhezera kufuna kusintha njira zanga, kulingalira za ena mmalo mwa ine ndekha. Potsirizira ndinawonjoka kotheratu ku chizoloŵezi chakutchova juga, ndipo ndinabatizidwa pamodzi ndi mkazi wanga.

“Yesu ananena kuti chowonadi chidzatimasula. (Yohane 8:32) Ndithudi zimenezo zinachitikadi kwa ineyo. Chowonadi cha Mawu a Mulungu ndicho chinandipatsa kanthu kena kofunika kokhalira moyo, chinandibwezera ulemu wanga, ndi kundidzetsera chikhutiro chachikulu. Ndinakhozanso kuthandiza mmodzi wa mabwenzi anga akale otchova nawo juga kusintha moyo wake monga momwe ndinachitira. Pamene anabatizidwa pamodzi ndi mkazi wake, zinandipatsa chimwemwe chachikulu koposa chimene ndinakhala nacho popambana juga.

“M’zaka 20 zapitazo, sindinabetche kalikonse, ngakhale kanthu kakang’ono. Sindikunena kuti zakhala zosavuta, komanso sizinakhale zovuta kwambiri. Ndipo zimene Mulungu wandipatsa zakhutiritsa kwambiri zosoŵa zanga zomwe ndinafuna kukhutiritsa mwakutchova juga.”a

Lingaliro la Malemba nlofunika kwambiri kwa amene afuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndipo amene amatsatiradi uphungu wa Mulungu samangopeŵa chisoni chomwe kutchova juga kumadzetsa komanso amapeza kuti iye amapereka kanthu kena koposa zipambano za kutchova juga.

Chuma cha Mtengo Wapatali

Paulo, polembera Timoteo m’zaka za zana loyamba, anati: “Uwauze [iwo] kusasumika ziyembekezo zawo pa kanthu kosatsimikizirika monga ndalama, koma pa Mulungu, yemwe amatipatsa molemera zinthu zomwe tiri nazo. Uwauze achite chabwino . . . , akhale okonzeka kupatsa ndi kugaŵira, motero apeze chuma chomwe chidzapanga maziko olimba a mtsogolo. Motero adzapeza moyo, moyo weniweni.”—1 Timoteo 6:17-19, The New English Bible.

Chuma chomwe adzapeza ndicho dzina labwino ndi Mulungu. Chimenechi chimatsogolera ku “moyo, moyo weniweni”—moyo wasatha, mfupo yaikulu yoposa zonse zoperekedwapo. Yesu anati m’pemphero kwa Mulungu: ‘Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’—Yohane 17:3.

Mosiyana ndi mfupo za ndalama zosatsimikizirika, mfupo imene Mulungu amapereka ingapezedwe ndi aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu. Ndiponso, kuchita chifuniro cha Mulungu kumadzetsa chimwemwe chonse chimene munthu angafune, ndipo kumadzetsera munthu ulemu ndi moyo watanthauzo. Pakali pano, polingalira za zotulukapo zoŵaŵa za kutchova juga, kumbukirani uphungu wopezeka m’mwambi wakale Wachingelezi wakuti: “Kubetcha kwabwino ndiko kubetcha kuti simudzatchovanso juga.”

[Mawu a M’munsi]

a Mboni za Yehova zathandiza otchova juga ambiri omwerekera kulaka vuto lawo. Ena athandizidwa ndi magulu onga a Gamblers Anonymous.

[Chithunzi patsamba 10]

Moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso uli mfupo yaikulu koposa iriyonse yopezeka mwakutchova juga

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena