Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 18-20
  • Kodi Ndiyenera Kukhaliranji Wosiyana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kukhaliranji Wosiyana?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a Mulungu Amasiyana ndi Ena!
  • Akristu Ayenera Kukhala Osiyana ndi Ena
  • Mmene Mungakhalire Wosiyana ndi Ena
  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 18-20

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kukhaliranji Wosiyana?

“NKOVUTA kukhala wosiyana ndi ena.” Anatero wachichepere wina Wachikristu. Ngati inuyo ndinu Mkristu, ndithudi mumadziŵa bwino lomwe chimene akunenera zimenezo. Mofanana ndi achichepere ambiri, mumafuna kukondedwa ndi kulandiridwa ndi ena. Komabe vuto nlakuti, kukhala wolandiridwa ndi ena nthaŵi zonse kumafuna kugwirizana—m’kalankhulidwe, kavalidwe, ndi kuchita zinthu mofanana ndi ausinkhu wanu. Wachichepere amene amafuna kukhala wosiyana amadziika paupandu wakupeŵedwa ndi kusekedwa ndi ena.

Nchifukwa chake achichepere pakati pa Mboni za Yehova amayang’anizana ndi mkhalidwe wovuta. Kunena mwachidule, monga Akristu, iwo ali osiyana ndi achichepere ena. Sichifukwa chakuti ali ndi mzimu wodzikweza kapena kuti amadziwona kukhala anthu abwinopo kuposa ena. Mmalomwake, chifukwa cha kuphunzitsidwa kwawo Baibulo, kaŵirikaŵiri samavomerezana ndi ausinkhu wawo m’nkhani za makhalidwe. Malingaliro awo pa madzoma afuko, kukondwerera maholide achipembedzo, ndi kupangana kupita kocheza zingawasiyanitsenso ndi kukwiitsa ena ausinkhu wawo.a

Mkristu wina wachichepere amati kukhala wosiyana “ndiko mbali yovuta koposa m’moyo Wachikristu.” Wina anati: “Achichepere amandiseka. Nthaŵi zambiri amanditcha wachikale ndi buluthu.” Makolo anu Achikristu anganenenso kuti muyenera kukhala wosiyana osati m’mikhalidwe yokha komanso m’kavalidwe, kapesedwe, ndi nyimbo zimene mumazikonda.

Anthu a Mulungu Amasiyana ndi Ena!

‘Kodi nchiyani chimalakwika ngati wina achita mofanana ndi achichepere ena?’ mungafunse motero. Eya, anthu a Mulungu akhala osiyana ndi ena kuyambira pachiyambi penipeni. Nthaŵi ina kalelo, Mulungu anasankha Israyeli kukhala ‘chuma chapadera.’ (Eksodo 19:5) Zimenezo zinatanthauza kukhala osiyana ndi anthu ena onse. Pa Levitiko 18:3, Mulungu analamula kuti: ‘Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Aigupto, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m’malemba awo.’

Aigupto akale anamwerekera m’kulambira zinyama konyansa. Anakhulupiriranso kusakhoza kufa kwa moyo. Kugonana kwa pachibale kunali kofala. Mofananamo, Kanani linali dziko lodzala ndi kupembedza mafano, chisembwere, kukhetsa mwazi, kupereka ana nsembe, ndi uhule. Chifukwa chake Mulungu anachenjeza kuti: ‘Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; . . . osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi.’—Levitiko 18:24-26.

Yehova anachirikiza chenjezo limeneli ndi Chilamulo chimene chinalamulira mbali iriyonse ya miyoyo yawo: zakudya zawo (Levitiko 11), machitidwe awo aukhondo (Deuteronomo 23:12, 13), ndi zakugonana (Levitiko 18:6-23). Chilamulo chinaperekanso malangizo pa kavalidwe ndi kapesedwe! ‘Adziwombere mphonje m’mphepete mwa zovala zawo, mwa mibadwo yawo,’ anatero Yehova, ‘naike pamphonje m’mphepetemo thonje lamadzi.’ (Numeri 15:38) Amuna anayenera kusunga ndevu ndipo analetsedwa ‘kusenga m’mphepete mwa ndevu zawo.’ (Levitiko 19:27; 21:5) Myuda aliyense anayenera kumvera lamuloli ngakhale ngati sanafune zovala zamphonje kapena ngati anakonda kukhala ndi nkhope yopalidwa bwino ndevu.

Tsopano, tayerekezerani kuti munauzidwa kuti munafunikira kusunga ndevu ndi kuvala zovala zakutizakuti. Kodi simukaipidwa nazo zimenezo monga zododometsa zoyenera zanu? Komabe, malamulo a Mulungu anali ndi chifuno chachikulu ndi chopindulitsa. Yehova anapereka chifukwa naati: ‘Kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ (Numeri 15:38-41) Lamulo lakavalidwe linali chikumbutso champhamvu chowoneka chakuti Ayuda anali osiyana ndi ena—anthu osankhidwa monga opatulika a Yehova. Ziletso pazakudya sizinangotetezera thanzi lawo komanso zinathandiza kuwachinjirizanso kuyanjana m’zakakhalidwe ndi zakupembedza ndi osakhala Ayuda. Eya, kunalidi kosatheka kuyanjana ndi wakunja popanda kuswa mbali zina za Chilamulo cha Mulungu. Chotero, Chilamulo cha Mose chinakhala monga “khoma” limene linalekanitsa anthu Ake ndi mitundu ina.—Yerekezerani ndi Aefeso 2:14.

Akristu Ayenera Kukhala Osiyana ndi Ena

Akristu lerolino ‘anamasulidwa kuchilamulo’ cha Mose ndipo ali ndi ufulu wokulirapo wakudzisankhira zinthu. (Aroma 7:6) Komabe, Yesu Kristu anauza otsatira ake kuti: ‘Simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi. Chifukwa cha ichi likudani inu.’ (Yohane 15:19) Yesu sanatanthauze kuti Akristu anayenera kuchoka papulaneti Dziko Lapansi. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 5:10.) Anangotanthauza kuti anayenera kupatuka ku “dziko lonse lapansi”—mbali ya mtundu wa anthu opatutsidwa kuchoka kwa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “dziko lapansi ligona mwa woipayo,” malinga nkunena kwa mtumwi Yohane.—1 Yohane 5:19.

Tsopano talingalirani achichepere ena amene mumadziŵa pasukulu. Bwanji ponena za maganizo awo, machitidwe awo, malankhulidwe awo, nyimbo zimene amakonda ndi zovala? Kodi inu mumawona kuti achichepere amenewo amatsogozedwa ndi miyezo yaumulungu—kapena kodi amatsogozedwa ndi malamulo okhazikitsidwa ndi “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Satana Mdyerekezi? (2 Akorinto 4:4) Ngati mfundo yomalizirayi iri yowona, mumadziika patsoka lotani nanga ngati muchita zinthu, kulankhula, kapena ngakhale kukhala ndi mawonekedwe osasamala mofanana nawo! Kuipa kwake nkwakuti, choyamba mumawonedwa wonama ponena kuti ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndiyeno choipirapo, mumapeza kuti mukugonja ku zisonkhezero zoipa.

“Mabwenzi amayambukiradi machitidwe ako,” anavomereza motero mayi wachichepere wotchedwa Kim. “Pamene ndinali pasukulu, sindinali wolimba kwenikweni m’chowonadi [Chachikristu], motero ndinali ndi mabwenzi ambiri akudziko. Koma zimenezo sizinali zabwino chifukwa chakuti zinandiloŵetsa m’zoipa zambiri.” Komabe, sikuti kuchita tchimo lalikulu ndiko kokha kumene kumadodometsa unansi wanu ndi Mulungu. Onani mosamalitsa zimene Baibulo limanena pa Yakobo 4:4: ‘Kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.’

Kodi mumafunadi kudziika paupandu wakukhala mdani wa Mulungu? Ndithudi ayi! Pamenepo dzisonyezeni poyera kuti sindinu mbali ya dziko. Komabe, kuteroko kumaloŵetsamo zoposa kungopeŵa mankhwala oledzeletsa ndi chisembwere.

Mmene Mungakhalire Wosiyana ndi Ena

Mwachitsanzo, talingalirani za zovala zimene mumakonda. Zimene mumavala zimasonyeza amene inu muli, amene mumaimira, zimene mumakhulupirira. Komabe, mosiyana ndi makonzedwe Achiyuda, Chikristu chimakupatsani ufulu wokulirapo wakusankha zimene mumakonda monga munthu panokha. Kodi zimenezo zimatanthauza kuti mukhoza kutenga fashoni iriyonse imene yabwera?

Msungwana wina Wachikristu anafuna kutsatira sitayelo yovala malaya a jini ong’ambidwa pansi pake popita kusukulu. Mwachibadwa, palibe amene amafuna kuwoneka wachikale. Koma makolo anu ali anzeru kuika malire pamasitayelo osayenera, odzutsa malingaliro oipa, opambanitsa, kapena okhumudwitsa. Kodi mukavala mwanjira zoterozo, mukapangitsa ena kukulingalirani motani? Msungwana wotchedwa Jeffie anadziwonera pamene anameta tsitsi lake ndi sitayelo yamakono yosayenera. “Ndinangowona kuti linawoneka ‘losiyana,’” anakumbukira motero. “Ndipo anthu anayamba kundifunsa, ‘Kodi ulidi mmodzi wa Mboni za Yehova?’ zimene zinandichititsa manyazi kwambiri.”

Uphungu wachikatikati ukuperekedwa pa 1 Timoteo 2:9, pamene Akristu akulimbikitsidwa kuvala ‘chovala choyenera ndi chamanyazi.’ Kaŵirikaŵiri mukhoza kuvala bwino popanda kuwoneka wachikale. Zowona, mwina ambiri sangakukondeni chifukwa chosavala masitayelo atsopano kwambiri, koma kudzakuthandizani kuwoneka poyera kukhala wosiyana—ndipo kutero ndiko kungakupezetseni chiyanjo cha Mulungu!

Bwanji ponena za nyimbo zimene mumakonda? Achichepere ambiri amakhala akumvetsera nyimbo kwa maola ochuluka pamene ali maso. Pamene zikhala zachikatikati, nyimbo zikhoza kukhala zosangalatsa ndi zomangilira. Komabe, Eksodo 32:17-22, amasonyeza kuti nyimbo zikhozanso kudzutsa malingaliro ndi zilakolako zoipa. Ndipo nyimbo zambiri za lerolino zimakhala zosayenera kuzimvetsera Mkristu. Mwachitsanzo nyimbo za roko zotchedwa rap ndi heavy metal, nzotchuka, koma zambiri—mwina kuposa zina zonse—zimagogomezera chisembwere, chipanduko, chiwawa, ngakhale kukhulupirira mizimu. Kodi mumakonda nyimbo zimene achichepere ambiri amazikonda, kapena kodi mumalimbika mtima ndi kusankha zoyenera zokha?

Inde, muyenera kukhala wolimbika mtima kuti mukhale wosiyana. Pamene mukana kusonkhezeredwa ndi mabwenzi ndi anzanu akusukulu posankha zosangulutsa, zolankhula, kapena zovala, ndithudi ena adzachitapo kanthu. Yesu anachenjeza kuti: “Popeza simuli a dziko lapansi, . . . likudani inu.” (Yohane 15:19) Chotero kukhala wosiyana kungakhale chimodzi cha zinthu zovuta koposa zimene mungachite—koma nkotheka. Ndinjira imene imalemekeza miyezo ya Mulungu. Imakupatsani ulemu ndi chikumbumtima choyera. Tsopano funso, Kodi ndimotani mmene mungakhalire olimbika mtima kuti mukhale wosiyana? Nkhani yathu yotsatira idzayankha funsoli.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve zochuluka pankhanizi, onani brosha la School and Jehovah’s Witnesses, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Zithunzi patsamba 20]

Wachichepere amene amalephera kukhala wosiyana ndi ausinkhu wake amakaikiritsa kaimidwe kake monga Mkristu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena