Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingalimbe Mtima Motani Kuti Ndikhale Wosiyana ndi Ŵena?
“Nthaŵi zina chitsenderezo cha anzanga chimandichititsa kuchita zimene ndilingalira kuti nzolakwa, koma popeza kuti kusazichita kuli kosakondweretsa kwa anzanga, ndimangovomera.”—John.
“CHITSENDEREZO cha anzathu okula nawo chimayambukira mbali iriyonse ya miyoyo yathu.” Akutero mlembiyo Lesley Jane Nonkin. Anzanu okula nawo amayesayesa kukuuzani mmene mungavalire. Amapereka malamulo a mmene mungayendere, kulankhula, ndi kupesa tsitsi lanu. Kudzipatula sikumalekereredwa. Gonjani—kapena kanidwani!
Komabe, Akristu achichepere sali akapolo akuchita mogwirizana ndi ena. Potsatira lamulo limene Yesu anapereka pa Yohane 15:19, iwo ‘sali mbali yadziko’ la anthu opanda umulungu.a Komabe, kukhala m’dziko koma osakhala mbali yake nkotokosa. Kuli monga ngati kupalasa bwato m’nyanja yoŵinduka. Inu muli m’madzi ndipo muli wozingidwa ndi madzi, koma kuti mukhalebe ndi moyo mukuyesayesa kwambiri kuchotsa m’bwatomo madzi ambiri monga momwe mungathere! Mofananamo, achichepere amene ali pakati pa Mboni za Yehova amayesayesa kuletsa kupanda umulungu kwa dzikoli kuloŵerera m’miyoyo yawo.
Komabe, nthaŵi zonse zimenezi siziri zosavuta. Talingalirani Mboni ina yachichepere ku Japani yotchedwa Eiichiro. Chitsenderezo cha kugwirizana ndi ena nchamphamvu kwambiri m’dziko limenelo, pakati pa achichepere ndi achikulire omwe. Eiichiro akukumbukira kuti: “Mwachikumbumtima sindikanatha kukhala ndi phande m’madzoma okhudza zizindikiro zautundu ndi nyimbo kusukulu. Ndiponso, sindikanatha kuphunzira maluso ankhondo popeza kuti zimenezi zinali zotsutsana ndi malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo.” (Wonani Eksodo 20:4, 5 ndi Luka 4:8; Yesaya 2:4 ndi Luka 10:27.) Zimenezi zinachititsa Eiichiro kuwonekera—mwinamwake mochititsa manyazi—pakati pa anzake.
Achichepere a Mboni padziko lonse amayang’anizana ndi mikhalidwe yofananayo. “Maholide ndiyo nthaŵi yovuta koposa,” akutero Mkristu wachichepere wina. “Ana onse amafunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji sukusangalala nawo?’” Kwa msungwana wina wachichepere nkhani yovuta koposa nja “kumka kokayenda ndi anyamata kapena ayi.” Komabe Mkristu wina wachichepere akudandaula za chitsenderezo cha kucheza ndi ena. Iye akuti: “Nthaŵi zonse anthu amakufunsa kuti, ‘Kodi sukupita kupate ija?’” Achichepere ena a Mboni asekedwa kaamba ka kukana kujomba kusukulu kapena kubera pamayeso. Pamenepo, nkosavuta kuwona kuti, kukhala wosiyana ndi ena kumafunikiradi kulimba mtima kwakukulu, ndipo siachichepere onse amene amalingalira kuti ali nako.
Wachichepere wina analemba kuti: “Ndiri ndi miyoyo iŵiri—umodzi wa kusukulu ndi wina wa kunyumba. Ndimakhala ndi ana audziko kusukulu. Komatu ana ameneŵa amatukwana pafupifupi nthaŵi iriyonse pamene alankhula, ndipo ndikuyamba kufanana nawo. Kodi ndiyenera kuchitanji?” Yankho lake liri poyera: Pezani kulimba mtima kuti mukhale wosiyana ndi ena! Koma motani?
Magwero a Kulimba Mtima Kowona
Kulimba mtima ndiko nyonga ya maganizo kapena ya makhalidwe ya kugonjetsa upandu, mantha, kapena zovuta. Sionse amene ali nako, komabe kungapezedwe. “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha,” akufotokoza motero mtumwi Paulo, “komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.” (2 Timoteo 1:7) Inde, Mulungu angakupatseni nyonga yofunikayo kuti muyang’anizane ndi anzanu okula nawo.—Afilipi 4:13.
Koma kodi mumapeza motani nyonga imeneyi? Njira imodzi ndiyo mwakungoipempha. “Pemphani ndipo mudzalandira,” Yesu analonjeza motero pa Yohane 16:24. Makamaka pamene muyang’anizana ndi chiyeso chololera molakwa pemphero liyenera kusachoka pakamwa panu. “Ndinapemphera kwa Yehova kuti ndilamulire maganizo anga ndi mtima,” akutero wachichepere wina Wachikristu.
Achichepere Olimba Mtima m’Nthaŵi Zakale
Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pankhani zolembedwa m’Baibulo zimene zimasimba za atumiki olimba mtima a Mulungu ndiko njira ina yokuthandizani kukulitsa kusachita mantha. Mwachitsanzo, kodi ndinu wamanyazi kudziŵitsa ena kuti ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova? Pamenepotu phunzirani nkhani imene iri pa 2 Mafumu 5:1-5. Imasimba za msungwana wina Mwisrayeli wogwidwa ukapolo amene anasonyeza molimba mtima chikhulupiriro chake pamaso pa ena. Nkhani ina yosonkhezera iri pa Machitidwe 4:20. Pamenepo atumwi anauza molimba mtima owatsutsa kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziwona ndi kuzimva.” Kuŵerenga nkhani zimenezi kungakusonkhezereni kusonyeza kulimba mtima kofananako polankhula.
Nkhani ina yokondweretsa ndiyo ija ya Danieli ndi mabwenzi ake achichepere atatu, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Achichepere ameneŵa anali pakati pa achichepere angapo Achiyuda anzeru amene anatengedwera ukapolo ku Babulo. Mfumu ya Babulo inali kulingalira za kuphunzitsa achichepere ameneŵa malo audindo m’boma. Kuti awagwirizanitse ndi njira ya moyo Yachibabulo, anyamatawo anachotseredwa maina awo Achiyuda ndi kuphunzitsidwa chinenero ndi miyambo za Ababulo. Ndiponso owagwira awo anayesayesa kuwalekanitsa ndi chizoloŵezi cha machitachita Achiyuda mwa kuwadyetsa “chakudya cha mfumu.”—Danieli 1:7, 8.
Mwalingaliro la Ababulo, chakudya chotero chinali chokoma kwa munthu wokonda kusangalala ndi chakudya. Kwa Ayuda owopa Mulungu, chakudya cha Ababulo chinali chonyansa mwachipembedzo. Komabe, mwachiwonekere ochuluka a achichepere ogwidwawo anagonjera kuchiyesocho—onse amene kusiyapo Danieli ndi mabwenzi ake. Tayerekezerani chitsenderezo chimene ayenera kukhala anali nacho kuchokera kwa ausinkhu anzawo Achiyudawo! Kodi achichepere ameneŵa anachita motani kuzitsenderezo zimenezo? Dziŵerengereni nokha cholembedwa cholimbitsa chikhulupiriro chimenechi m’Danieli chaputala 1. Mwinamwake chidzakuthandizani kupeza kulimba mtima kukana ngati wina atakupatsani mankhwala oledzeretsa oletsedwa kapena chakumwa cholezeretsa!
“Khalani Wolimba Mtima”
Kuŵerenga za kulimba mtima sikuli kokwanira konse. Kuti mukulitse kulimba mtima kumene kudzakuthandizani kugonjetsa ndi chitsenderezo cha anzanu, tsiku ndi tsiku muyenera kutsatira chilangizo chimene Paulo anapereka kwa amuna ndi akazi mumpingo wa Akorinto chakuti: “Chirimikani m’chikhulupiriro; khalani wolimba mtima ndipo khalani amphamvu.”—1 Akorinto 16:13, The Jerusalem Bible.
Mwachitsanzo, kodi mumasintha kavalidwe kanu kapena kapesedwe ka tsitsi, kotero kuti mugwirizane ndi achichepere audziko pamene simuwonedwa ndi makolo anu ndi ziŵalo zampingo Wachikristu? Kapena kodi mumamamatira mosagonja kumiyezo Yachikristu? “Ndimakana kutsatira sitayelo iriyonse imene imatuluka,” akutero msungwana wina Wachikristu wolimba mtima.
Funso lina: Kodi muli wolimba mtima mokwanira kulola a m’kalasi anzanu kudziŵa kuti ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova? Ngati sukulu yanu imakulolezani kuchita motero, kodi mumanyamula Baibulo lanu ndi mabukhu ofotokoza za Baibulo limodzi nanu? Ngati nkhani zokhudza chisinthiko, madzoma autundu, kapena kuthiridwa mwazi zibuka m’kalasi, kodi ‘mumachita chodzikanira payense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu’? (1 Petro 3:15) Kapena kodi mumangokhala duu padesiki lanu mukumadera nkhaŵa? Yesu Kristu anati: ‘Aliyense amene achita nane manyazi ndi mawu anga, inenso ndidzamchitira manyazi.’—Marko 8:38.
Koposa ndi kukhala wamanyazi, Mkristu wolimba mtima amadzitamandira ndi chiyembekezo chake chozikidwa m’Baibulo! (Yerekezerani ndi Ahebri 3:6.) Eiichiro, wachichepere wa ku Japani wogwidwa mawu poyambirirapo, anaphunzira kuchita zimenezo. Kaŵirikaŵiri ankafunsidwa chifukwa chake sanakhale ndi phande m’madzoma autundu kapena maluso ankhondo. Kodi iye anali kutayikiridwa chifukwa cha kukhala wosiyana ndi ena? “Ayi,” iye akutero, “ndinafikira pakulingalira zonsezi monga chitokoso. Mwawona nanga, ndinafunikira kukonzekera mayankho anga kuti ndipange chodzikanira pamchitidwe wanga ndipo ndinafunikira kudalira chithandizo cha Yehova. Chotero pambuyo pake, kutayikiridwako kunafikira kukhala mapindu.”
Phunziraninso kudzilankhulira pamene mwayang’anizana ndi chiyeso. Miyambo 1:10-15 imati: “Mwananga, akakukopa ochimwa usalole, Akanena, Idza nafe, . . . mwananga, usayende nawo m’njira; letsa phazi lako kumayendedwe awo.” Ndithudi, zimenezi sizimatanthauza kwenikweni kuchita ulaliki. M’bukhu lake lakuti How to Say No and Keep Your Friends, mlangiziyo Sharon Scott akunena kuti nthaŵi zina mungangochoka, kukana chiitanocho—kapena kungochinyalanyaza. Koma panthaŵi zina, mungakhale wopanda chosankha kusiyapo kulankhula ndi kuuza enawo chifuka chake simungagwirizane nawo. Mlangiziyo Scott akuvomereza kuti muyenera kukhala ochirimika akumati: “Yesani kusawonekera muli wamphwayi . . . Ayang’aneni mwachindunji. . . . Lankhula mwamphamvu ndi mosadodoma.
Inu mungasinjiriridwebe kapena kusekedwa kaamba ka kaimidwe kanu. Komabe, ambiri adzakusirirani ngakhale asakufuna. Wachichepere wina, Mike, akuti: “Anyamata ambiri amadziŵa kuti ndine Mboni, ndipo amandilemekeza. Ngati afuna kuti ayambe kukambitsirana kanthu kena koipa, amati, ‘Mike, tikufuna kuyamba kukambitsirana, chotero ngati ufuna kuchoka, choka,’” Siachichepere onse amene adzakupatsani ulemu wotero. Koma Mulungu adzakondwadi ndi njira yanu. (1 Petro 4:3-6) Motero wachichepere wina Wachikristu anati: “Musadere nkhaŵa ndi mmene ana ena amaganizira za inu!” Lingaliro la Mulungu ndilo limene liri lofunika. Ndipo adzakudalitsani chifukwa cha kukhala kwanu ndi kulimba mtima kwa kukhala wosiyana ndi ena.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani nkhani yakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kukhala Wosiyana?” yotuluka m’magazini a June 8, 1992.
[Chithunzi patsamba 19]
Pamene mipata ya kufotokoza chikhulupiriro chanu ibuka, kodi mumala- nkhula?