Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 13-15
  • Nkulankhuliranji za Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkulankhuliranji za Mulungu?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Ena Amalekera Kutero
  • Thayo Lachikristu
  • Zimene Mungakwaniritse
  • Kodi Ndingalimbe Mtima Motani Kuti Ndikhale Wosiyana ndi Ŵena?
    Galamukani!—1992
  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Zingakhale Bwanji Ngati Nditakumana ndi Winawake wa Kusukulu Kwathu?
    Galamukani!—2002
  • Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 13-15

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Nkulankhuliranji za Mulungu?

“Aliyense ali ndi chipembedzo chake. Simuyenera kuyesa kukakamiza anthu ena kukhulupirira Mulungu wanu.”—⁠Racish wazaka 14, Guyana.

“Ndimazengereza kulankhula za Mulungu chifukwa chakuti ndimachita manyazi kuti ena adzandiseka.”—⁠Rohan wazaka 17, Guyana.

“Tiyenera kulankhula za Mulungu chifukwa chakuti ndiye Mlengi wathu ndipo anatipatsa moyo.”—⁠Marco wazaka 13, Germany.

MVETSERANI mosamalitsa pamene kagulu ka achichepere kakukambitsirana ndipo mosakayikira mudzafikira pa kunena zotsatirazi mogwiritsidwa mwala: Zoonadi, nkhani yonena za Mulungu siyofala kwambiri m’makambitsirano a achichepere. Tchulani maseŵero, zovala, akanema atsopano, kapena za anthu osiyana nawo ziŵalo, ndipo mosakayikira mudzadzutsa makambitsirano amphamvu. Koma, tangoyesani kutchula za Mulungu, ndipo onse adzangoti zii ngati kwagwa chowopsa.

Achichepere ena samakhulupirira konse mwa Mulungu. Iwo mwina amalingalira kuti popeza kuti samamuona, ndiye kuti kulibe​—⁠kulankhula za iye kumaoneka ngati kutaya nthaŵi. Chikhalirechobe, osakhulupirira kukhalako kwa Mulungu ali ochepa pakati pa achichepere. Malinga ndi kufufuza kwa Gallup, pafupifupi 95 peresenti ya achichepere a ku United States amakhulupirira mwa Mulungu. Kwenikweni, Gallup anati: “Kwa achichepere ambiri Mulungu amene amamkhulupirira sali lingaliro longopeka losamvetsetseka, koma ali Mulungu weniweni amene amaona zochita zawo nawafupa kapena kuwalanga monga mwa zochita zawozo.” Pamenepa, nchifukwa ninji achichepere ambiri amazengereza kulankhula za zimene amakhulupirira?

Chifukwa Chimene Ena Amalekera Kutero

Ambiri amaoneka kukhala akuganiza kuti ndi mwano kulankhula nkhani zachikhulupiriro ndi kuti malingaliro achipembedzo ali aumwini. Achichepere ena amaoneka kukhala akuchita manyazi ndi lingaliro chabe la kukambitsirana za Mulungu. Iwo amalingalira kuti, ‘Kuchita zimenezo sikwabwino ayi.’

Mosasamala kanthu za lingaliro la ausinkhu wanu, kodi inu mwaima pati pa nkhaniyi? Funso limeneli nlofunika kwambiri makamaka ngati munaleredwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kuchitira umboni, kuuza ena za Mulungu, kuli mbali yofunika kwambiri m’chipembedzocho!​—⁠Yesaya 43:​9, 10; Mateyu 24:⁠14.

Ngakhale kuli choncho, polefulidwa ndi udani umene zimakumana nawo nthaŵi ndi nthaŵi, Mboni zina zachichepere zimapeŵa kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira poyera​—⁠kapena zimatero chabe chifukwa chakuti zimakakamizidwa ndi makolo awo. Ena amakhala ndi phande m’ntchitoyo komano mumtima mwawo amalakalaka kuti mabwenzi awo akusukulu asawaone. Kusukulu, ena amayesa kubisa zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Kaŵiriŵiri chili chifukwa chakuti amawopa kusekedwa ndi a m’kalasi anzawo. “Ndinali kuwopa kulankhula za Mulungu,” akuvomereza motero Ryan wachichepere, “chifukwa chakuti anzanga ankandisinjirira ndipo ndinachita mantha kupitiriza makambitsiranowo.”

Ndiyeno pali awo amene amaleka kutero chifukwa chakuti amawopa kuti sangakhaledi ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo. Pokopeka ndi “zilakolako za unyamata,” iwo amalingalira kuti kungakhale bwino kusadzitcha Akristu kuwopera kuti mwina angachite cholakwa.​—⁠2 Timoteo 2:⁠22.

Ena samalankhula za Mulungu chifukwa chakuti amangoganiza kuti ali osakhoza. Wilton wazaka 19 ananena motere: “Kulankhula za Mulungu kwa antchito anzanga kunandivuta chifukwa chakuti ndinaganiza kuti ndinali wosakhoza kupereka maumboni a zimene ndinanena ponena za iye. Ndinaganiza kuti ngati ndikanafunsidwa za zikhulupiriro zanga, sindikanakhala ndi yankho lokhutiritsa.”

Thayo Lachikristu

Kodi mungakhale mutalephera kulankhula za Mulungu pazifukwa zofanana ndi zimenezo? Ngati zili choncho, sindinu nokha. Achichepere ena alimbana ndi malingaliro amodzimodziwo. Komabe, ambiri afikira pa kuzindikira kuti, mosasamala kanthu za zonse zimene zingalefule munthu kuchita zimenezo, pali zifukwa zamphamvu zolankhulira kwa ena ponena za Mulungu. Kodi zina za zimenezo nzotani?

Marco wachichepere, wotchulidwa poyamba, anafotokoza bwino kwambiri pamene anati Mulungu “ndiye Mlengi wathu ndipo anatipatsa moyo.” (Chivumbulutso 4:11) Inde, moyo uli mphatso yamtengo wapatali. Wamasalmo anati ponena za Mulungu: “Chitsime cha moyo chili ndi Inu.” (Salmo 36:⁠9) Pokhala munalandira mphatso imeneyi, kodi simuyenera kusonyeza chiyamikiro kaamba ka iyo?

Njira ina yosonyezera chiyamikiro ndiyo kutamanda Yehova Mulungu pamaso pa ena. Iye ndiye Magwero a dzuŵa, mwezi, mvula, mpweya umene timapuma, ndi chakudya chimene timadya. (Machitidwe 14:​15-17) “Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba,” wophunzira Yakobo anatero. (Yakobo 1:17) Kodi mumayamika Mulungu kaamba ka mphatso zimenezi? (Akolose 3:15) Kodi pali njira ina iliyonse yosonyezera chiyamikiro chanu kuposa kulankhula za Mulungu?​—⁠Luka 6:⁠45.

Ndipotu, Mulungu amatilamula kulankhula za iye. Mwana wake, Yesu Kristu, analamula Akristu kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:​19, 20) Achichepere sakupatulidwa pa thayo la kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi. Wamasalmo akulamula kuti: “Lemekezani Yehova  . . . anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.” (Salmo 148:​7, 12, 13) Komabe simufunikira kuona ntchito imeneyi monga mtolo. Kunena zoona, uli mwaŵi​—⁠mungakhaledi mmodzi wa “antchito anzake a Mulungu.”​—⁠1 Akorinto 3:⁠9.

Nanga bwanji ngati muganiza kuti mwangokhala wosayenerera? Mneneri Yeremiya anali ndi malingaliro otero m’nthaŵi za Baibulo. “Ha, Ambuye Mulungu!” iye anatero. “Taonani, sindithayi kunena pakuti ndili mwana.” Yankho la Yehova? “Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.” (Yeremiya 1:​6, 7) Mothandizidwa ndi Yehova Yeremiya anachita zimenezo kumene kwa zaka 40!

Mofanana ndi Akristu lerolino, “kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu.” (2 Akorinto 3:⁠5) Ngakhale ngati muli munthu wamanyazi ndi wamantha mwachibadwa, Mulungu angakuthandizeni kukhala wolimba mtima polankhula. Mumpingo Wachikristu muli makonzedwe amene angakuthandizeni kukhala ‘wokwanira’ monga mphunzitsi wa Mawu a Mulungu. Ngati muganiza kuti mukufunikira thandizo laumwini, bwanji osalankhula ndi mmodzi wa oyang’anira mpingo? Mwina mungangofunikira kukhala ndi programu ya phunziro laumwini la Baibulo kapena kugwira ntchito pamodzi ndi wina wozoloŵera kwambiri.

Zimene Mungakwaniritse

Kulankhula za Mulungu kungakudzetsereni chikhutiro chenicheni. Chinthu chotsimikizirika nchakuti, ausinkhu wanu ambiri akufunafuna mayankho, kufuna thandizo kwadzaoneni. Alibe chitsogozo ndipo alibe chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka mtsogolo. Iwo amadabwa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji tili pano? Kodi tikupita kuti? Kodi nchifukwa ninji dziko ladzala kwambiri ndi mavuto?’ Monga Mkristu, inu muli ndi mayankho, ndipo mwachionekere muli pamalo abwino a kupereka chidziŵitso chotero kwa ausinkhu wanu. Mkhalidwe wawo uli wofanana ndi wanu ndipo angafunedi kulankhula kwa wina wa usinkhu wawo koposa kwa wachikulire.

Zoona, nthaŵi zina mudzayang’anizana ndi chitsutso. Koma mukhozanso kupeza anthu omvetsera uthenga wa Baibulo. Mboni ina yachichepere inali khale m’basi ikumaŵerenga kope lake la buku la Mafunso Achichepere Akufunsa​—⁠Mayankho Amene Amathandiza.a Mnyamata wina amene anakhala pafupi naye anayamba kuŵerenga nayenso. “Bukuli nlabwinodi!” mnyamatayo anadzuma motero. “Bukuli limalankhula kwambiri za Mulungu. Anthu ochuluka samakondwera ndi chipembedzo.” Mboni yachichepereyo inagwiritsira ntchito zimenezi monga mpata wa kukambitsirana mwakuya ponena za dzina la Mulungu.

Zoona, pamene mudzidziŵikitsa monga Mkristu, mumakhala ndi thayo la kukhala monga wotero. (1 Petro 2:12) Koma khalidwe labwino Lachikristu lidzangowonjezera kudalirika kwa uthenga wanu. Talingalirani chokumana nacho cha wachichepere wina wotchedwa Eric. Iye anachita chidwi ndi khalidwe labwino la Mboni zachichepere pasukulu pawo. Zimenezi zinadzutsa chikondwerero chake cha kuphunzira zowonjezereka ponena za Mulungu. Phunziro la Baibulo linayambitsidwa kwa iye, ndipo lero ali Mkristu wobatizidwa ndipo akutumikira pamalikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova ku New York.

Kulankhula za Mulungu kungathandizenso inuyo! Kungatumikire monga chitetezo. Pamene mabwenzi anu adziŵa kuti muli mmodzi wa Mboni za Yehova, ambiri adzakulemekezani. Mwina sangakuumirizeni kwambiri kuchita cholakwa pamene azindikira kuti muli ndi miyezo yapamwamba ya makhalidwe ndipo ngati adziŵa kuti mwachionekere mudzawachitira umboni ngati atero.

Ndithudi, zimenezi sizitanthauza kuti paliponse pamene mulankhula muyenera kutchula malemba. Mudzakondabe maseŵero, zovala, kapena nyimbo ndipo mudzafuna kulankhula za zimenezo nthaŵi ndi nthaŵi. Koma kumbukirani: “M’kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Ngati chikondi cha pa Mulungu chilidi mumtima mwanu, mwachibadwa mudzafuna kulankhula za iye. M’kope la mtsogolo, tidzafotokoza njira zina zimene mungachitire zimenezo mogwira mtima.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi mumachita manyazi kuonedwa ndi anzanu akusukulu pamene muli m’ntchito yapoyera ya kulalikira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena