Kutetezera Ana Kunkhalwe, 1882
“GULU LOTETEZERA ANA KUNKHALWE, 1882. Gulu Lotetezera Ana Kunkhalwe linayambidwa mu New York mu 1875 ndi Henry Bergh. Zaka zisanu ndi ziŵiri pambuyo pa kuyambidwa kwake, Gulu limeneli, limene liri gulu loyamba kupereka chitetezo chirichonse kwa ana ochitiridwa nkhanza mumzinda [wa New York], linali kusamalira madandaulo zikwi zambiri chaka chirichonse, kuchotsa ana m’mabanja osayenera ndi kulanga olakwa kupyolera mwa mabwalo amilandu. Chithunzithunzi chozokotedwa mwatanthauzo chimenechi chikuimira kuphatikizidwa kwapanthaŵi yake kwa maulamuliro m’nkhaniyo.”—New York in the Nineteenth Century, lolembedwa ndi John Grafton.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
New York in the Nineteenth Century, lolembedwa ndi John Grafton, Dover Publications, Inc.