Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 15
“Masiku ano, nkhanza zafala kwambiri. [Tchulani chitsanzo chimodzi cha kwanuko kapena cha m’magazini imene mukugawirayo.] Kodi munadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani anthu aipa motere? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo linalosera kuti nkhanza zidzachuluka. [Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.] Magazini iyi ikuyankha funso lakuti, ‘Kodi Nkhanza Zidzathadi’?”
Galamukani! Apr.
“Anthu ambiri masiku ano amati ndi Akhristu. Kodi mukamaganiza, mumati kukhala Mkhristu kumatanthauza chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu ananena pa lemba ili. [Werengani Yohane 15:14.] Nkhani iyi ikusonyeza kuti kungonena kuti ndine Mkhristu sikokwanira.” Musonyezeni munthuyo nkhani imene ikuyambira pa tsamba 26.
Nsanja ya Olonda May 1
“Mwana akamwalira, makolo amakhala ndi chisoni chachikulu kwa nthawi yaitali. Kodi mukuganiza kuti chingawatonthoze n’chiyani? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aroma 15:5.] Magazini iyi ikufotokoza njira zina zimene Mulungu amatonthozera onse olira.”
Galamukani! May
“Anthu ena ali ndi chuma chambiri, pamene anthu ena ambiri ali pa umphawi. Kodi mukuganiza kuti kupanda chilungamo kumeneku kudzatha? [Yembekezani ayankhe.] Tamverani mmene Mulungu amaonera anthu osauka. [Werengani Salmo 22:24.] Magazini iyi ikufotokoza chiyembekezo chimene Baibulo limapereka kwa anthu osauka.”