Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Anthu amalankhula kawirikawiri za kubwera kwa Yesu Khristu. Kodi mukuganiza kuti tikufunika kusangalala kapena kuda nkhawa ndi kubwera kwa Yesu kumeneku? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mmene nkhaniyi inam’khudzira Yohane, amene analemba nawo Baibulo. [Werengani Chivumbulutso 22:20.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zidzachitike Khristu akadzabwera.”
Galamukani! Mar.
“Zikuoneka kuti atsogoleri ambiri padzikoli ndi onyada kwambiri. Kodi mukuganiza kuti mtima woterewu umathandiza kuti dziko likhale pamtendere ndiponso logwirizana? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pankhani ya kunyada. [Werengani Miyambo 16:18.] Nkhani iyi ikufotokoza ubwino wa kudzichepetsa.” M’sonyezeni nkhani yomwe yayambira pa tsamba 20.
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Pafupifupi tsiku lililonse timakhala ndi mafunso okhudza umoyo wathu, mabanja athu, ndiponso ntchito yathu. Kodi mukuganiza kuti mayankho odalirika ndiponso othandiza tingawapeze kuti? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa 2 Timoteyo 3:16. [Werengani.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Baibulo lingatithandizire m’njira zosiyanasiyana.”
Galamukani! Apr.
“M’madera ambiri, anthu akuona kuti makhalidwe a anthu akumka naipiraipira. Kodi inu mwaonapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Zinthu zimene tikuona masiku ano zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. [Werengani 2 Timoteyo 3:2-4.] Magazini iyi ikusonyeza zimene kuipiraipira kwa makhalidwe a anthu kukutanthauza ndiponso kuti mapeto ake n’chiyani.”