Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Kodi mukuganiza kuti ziphunzitso za Yesu ndi zothandiza m’nthaŵi yathu ino? [Yembekezani ayankhe.] Ndikukhulupirira mukugwirizana ndi lamulo limene Yesu anapereka pa tsiku lomaliza la moyo wake. [Ŵerengani Yohane 15:12.] Yesu anaphunzitsanso mfundo zabwino tsiku limenelo. Nsanja ya Olonda iyi ikusonyeza mmene ifeyo tingapindulire ndi zimenezo.”
Galamukani! Mar. 8
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu anakonzeratu zoti anthu pamodzi ndi ana omwe, azivutika ndi matenda a kusowa kwa zakudya m’thupi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani lonjezo lolimbikitsa ili lopezeka m’Baibulo. [Ŵerengani Salmo 72:16.] Magazini ya Galamukani! iyi ikufotokoza zimene zimachititsa mavuto akusowa kwa chakudya, ndiponso lonjezo la Mulungu lofunika kwambiri loti adzathetsa vutoli posachedwapa.”
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Zimene mukuziona apa ndi Mgonero wa Ambuye. [Onetsani tsamba loyamba ndi lomaliza la magazini.] Kodi mukudziŵa kuti ndi mwambo wokhawu umene Akristu amalamulidwa kukumbukira? [Yembekezani ayankhe. Kenako ŵerengani Luka 22:19.] Magazini iyi ikufotokoza ubwino wa mwambo umenewu ndiponso mmene umakukhudzirani.”
Galamukani! Mar. 8
“Chifukwa cha kubwera kwa mavidiyo a nyimbo, achinyamata ambiri amaonerera zinthu zachiwawa ndi zachiwerewere. Kodi mukuganiza kuti ndi bwino kuti achinyamata azionerera mavidiyo otero? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena pano za mmene Mulungu amaonera chiwawa. [Ŵerengani Salmo 11:5.] M’magazini iyi ya Galamukani!, muli nkhani imene ikufotokoza za mavidiyo a nyimbo.”