Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Anthu padziko lonse amalemekeza ziphunzitso za Yesu. [Werengani mawu ogwidwa patsamba 3, ndime 1.] Koma kodi mukuganiza kuti ziphunzitso zimenezo, monga chitsanzo chimene chili mu lemba ili, n’zothandiza masiku ano? [Werengani Mateyu 5:21, 22a. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Yesu anaphunzitsa ndi mmene tingapindulire nazo.”
Galamukani! Apr. 8
“Anthu ambiri amakonda mapiri chifukwa ndi okongola, koma kodi mumadziwa kuti mapiri amachirikiza moyo padziko lapansi lino? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake timafunika mapiri ndiponso zimene zikuchitikira mapiri amenewa masiku ano. Ikufotokozanso mmene Mlengi adzatetezere mapiri amenewa.” Werengani Salmo 95:4.
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Kodi munamvapo zoti sayansi ndi Baibulo zimatsutsana? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mbiri ya mkangano wa pakati pa sayansi ndi chipembedzo. Koma ikuperekanso umboni wosonyeza kuti sayansi yoona imagwirizana ndi Baibulo.” Muonetseni masamba 6 mpaka 7. Kenako werengani Mlaliki 1:7.
Galamukani! Apr. 8
“Kodi mukuganiza kuti makolo angachite chiyani kuti athandize ana awo kupewa mavuto pa zaka zawo za unyamata? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yesaya 48:17, 18.] Magazini iyi ikulongosola mmene kugwiritsira ntchito malangizo a m’Baibulo kungathandizire makolo kulimbikitsa kulankhulana kwabwino ndi ana awo ndiponso kuwaikira malire oyenera.”