Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Ambirife timadziwa chisoni chimene chimakhalapo munthu amene timamukonda akamwalira. Kodi mukudziwa za lonjezo lolimbikitsa ili? [Werengani Machitidwe 24:15. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Koma ambiri amadzifunsa kuti, Kodi ndani amene adzaukitsidwa? Kodi adzaukitsidwa liti ndipo adzaukitsidwira kuti? Magaziniyi ikuyankha mafunso amenewa kuchokera m’Baibulo.”
Galamukani! Mar.
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu. Koma n’zochititsa chidwi kuti wophunzira wa Yesu, Petro, anatcha Yesu Mwana wa Mulungu. [Werengani Mateyu 16:16.] Kodi mukuganiza kuti n’zotheka Yesu kukhala Mulungu komanso Mwana wa Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani yomwe ili pa masamba 12 ndi 13 m’magazini ino ikuyankha funsoli pofotokoza zimene Baibulo limanena.”
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Mawu odziwika kwambiri awa akufotokoza chifukwa chake kudziwa Mulungu kuli kofunika. [Werengani Mateyu 4:4.] Koma anthu ambiri zimawavuta kumvetsa Mawu a Mulungu. Kodi inunso zimakuvutani? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo zabwino zomwe zingakuthandizeni kumvetsa Baibulo.”
Galamukani! Apr.
“Anthu ambiri amafunafuna chimwemwe koma ndi ochepa amene amachipeza. Kodi mukuganiza kuti zinthu zomwe zatchulidwa apa zingathandize anthu kukhala ndi moyo wachimwemwe? [Sonyezani bokosi patsamba 9. Ndiyeno werengani lemba limodzi mwa malemba omwe asonyezedwa.] Galamukani! ino ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kupeza chimwemwe chenicheni.”