Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Tsiku lililonse, timamva za mavuto, matenda ndi imfa. Kodi mumaganiza kuti zonsezi zidzatha? [Yembekezani ayankhe.] Lemba la m’Baibulo ili limapatsa anthu ambiri chiyembekezo. [Werengani Yohane 3:16.] Mungamve zambiri m’magazini iyi yomwe ikufotokoza nkhani yakuti, ‘Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?’”
Galamukani! Mar.
“Kodi mumaganiza kuti zikhulupiriro za makolo n’zothandiza, kapena zovulaza? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo lili ndi mfundo yosangalatsa iyi. [Werengani Yesaya 65:11.] Nkhani iyi ikufotokoza ngati zikhulupiriro za makolo zili zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.” Asonyezeni nkhani imene ikuyambira pa tsamba 10.
Nsaja ya Olonda Apr. 1
“Kodi mungakonde kuona ulosi uwu utakwaniritsidwa? [Werengani Yesaya 2:4, ndipo yembekezani ayankhe.] Dziwani kuti Mulungu adzalowerera pa zochita za anthu ndi ‘kuwadzudzula.’ Baibulo limanena kuti Mulungu adzamenya nkhondo ya Aramagedo imene idzathetsa nkhondo zonse. Magazini iyi ikufotokoza kuti Aramagedo n’chiyani, ikufotokozanso chifukwa chimene tiyenera kuiyembekezera.”
Galamukani! Apr.
“Kodi mukuganiza kuti tikukhala m’nyengo imene yafotokozedwa apayi? [Werengani 2 Timoteyo 3:1-4, ndipo yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza kuti pali chifukwa chabwino chochitira chidwi ndi masiku otsiriza, popeza kuti chimenechi ndi chizindikiro chakuti zinthu zabwino zatsala pang’ono.”