Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Popeza kuti anthu akuwononga zinthu zachilengedwe padziko lapansili, ambiri akuda nkhawa kuti dzikoli liwonongekeratu. Kodi inuyo mumaganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani lonjezo lolimbikitsa ili. [Werengani Salmo 104:5.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena za tsogolo la dziko lapansili.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 10.
Galamukani! Apr.
“Anthu ambiri zimawavuta kupeza nthawi yolambira Mulungu chifukwa chotanganidwa. Kodi inunso zimakuvutani? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Aefeso 5:15-17.] Baibulo limafotokoza momveka bwino za kuchuluka kwa nthawi ndi mphamvu zimene Mulungu amayembekezera kuti tizigwiritsa ntchito pomulambira. Zimenezi zafotokozedwa m’nkhani iyi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 20.
Nsanja ya Olonda May 1
“Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira zimene angaone basi. Kodi inunso mumatero? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Aroma 1:20.] Magazini iyi ikufotokoza atatu mwa makhalidwe a Mulungu amene tingawaone m’chilengedwe ndipo ikufotokozanso mmene tingapindulire tikadziwa makhalidwe amenewa.”
Galamukani! May
“Masiku ano anthu ambiri amaopa zam’tsogolo. Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwino kapena zidzaipa kwambiri? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chimene tingakhulupirire kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa mavuto akuluakulu amene anthu akulephera kuwathetsa.”