Kupulumutsidwa ku Imfa ndi Chithandizo Chamankhwala Popanda Mwazi
Monga momwe yasimbidwira ndi chiŵalo cha ogwira ntchito pamalikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova
MKHALIDWE unawoneka wachilendo. Mu February 1991, ndinapita ku Buenos Aires, Argentina, kukathandiza kuchititsa misonkhano ya kugwiritsiridwa ntchito kwa njira zina zoloŵa m’malo kuthiriridwa mwazi. Ndipo tsopano ndinali pafupi kufa, ndikumakha mwazi wochuluka m’mimba.
Vutolo linayamba mlungu wapapitapo, pamene ndinali ku Mexico. Ndinamva kupweteka m’mimba koma sindinaganize kuti kunali kowopsa. Dokotala wakomweko ananena kuti kunali kofala kwa alendo a ku Amereka kudwala m’mimba pamene akuyendera deralo. Anandipatsa mankhwala otontholetsa ululuwo.
Pamene ndinali kuyenda pandege kupita ku Buenos Aires patsiku lotsatira, ululuwo unakula. Ndinamva ululu wonga wamoto m’mimba, ndipo pambuyo pa masiku aŵiri unakhala ngati moto wovumba. Ndinabaidwa jekeseni yopha ululuwo. Imeneyi inanditheketsa kumaliza kupereka nkhani zanga paseminale. Pambuyo pake, ndinatengedwa kuchoka panthambi ya Mboni za Yehova, pamene mkazi wanga ndi ine tinali kukhala, kupita kuchipatala chakomweko. Kumenekoko anandipeza ndi chilonda cham’mimba chimene mwachiwonekere chinali chitasiya kukha mwazi posachedwa.
Chidziwitsocho chinali chodabwitsa pang’ono, popeza kuti sindinakhalepo ndi chilonda cham’mimba kapena ngakhale zizindikiro zake. Komabe, kunakhulupiriridwa kuti ndikachira mwakubindikiritsidwa pakama, kupatsidwa mankhwala opha ululu, ndi zakudya zosakoleretsa. Mwatsoka, nditabwerera kuchipinda cha odwala panthambi, kukha kwa mwazi kunayambanso.
Chimbudzi changa chinali chakuda, chodzala mwazi, ndipo ndinali woyera mbe. Pomalizira pake, ndinakomoka, ndikumasolola mwangozi paipi loloŵetsedwa mumsempha pamkono wanga. Mkazi wanga anathamangira m’likole akumaitana a nesi.
Kuchitidwa Opaleshoni Kapena Kusatero?
Madokotala aŵiri anadzaima pambali pa kama wanga patapita nthaŵi pang’ono. Kupyolera mwa womasulira, anandidziŵitsa kuti mlingo wanga wa hemoglobin unatsika kufikira magramu 6.8 pa deciliter imodzi (mlingo woyenera ndiwo pafupifupi 15). Iwo ananena kuti anali kukambitsirana pafoni ndi katswiri wochita opaleshoni popanda mwazi. Iye anali kuvomereza opaleshoni yamwamsanga. Ndinafunsa za njira zina zoloŵa m’malo opaleshoni.
Katswiri wa nthenda zam’mimba anafunsidwa. Iye ananena kuti kunali kotheka kuloŵetsa makina owonera m’mimba kudzera pammero panga kufika pachilonda chokhala pambali yoyamba ya thumbo laling’ono. Atafika pa malo akukha mwazi, khemikholo yotchedwa hemostat ikadonthetsedwa pachilondacho kuti iletse kukha kwa mwazi.
“Kodi chipambano nchothekera motani?” ndinafunsa motero.
“Pali kuthekera kolingana kwachipambano ndi kwakulephera,” iye anayankha motero. Komabe, dokotala wa opaleshoni anati ngati hemostat ilephera kugwira ntchito, kuchedwa ndi kutaika kwa mwazi mwinamwake kukalepheretsa kuchita opaleshoniyo. Zinawoneka ngati kuti panalibe njira ina kusiyapo kuchitidwa opaleshoni basi.
Nkhaŵa inakula. Mkazi wanga ndi ine tinakupatirana. Ndisanakwere ambulansi kupita kuchipatala, chikalata cha kugaŵiridwa kwa chuma mwini atafa chinakonzedwa, ndipo ndinachisaina. Mabwenzi athu anaganiza kuti mwina sindikapulumuka opaleshoniyo.
Opaleshoni
M’chipinda chochitira opaleshoni, ndinaikidwa pa chimene chinawoneka ngati thebulo lagalasi lalikulu. Magetsi anayaka moŵala pansi pake ndipo a m’mwamba anandiunikira. Ndinatekeseka kwambiri, kumene ndiganiza kuti kunali kwachiwonekere, pakuti mmodzi wa madokotala a opaleshoniwo anadza kwa ine. “Musavutike maganizo. Zonse zidzakhala bwino,” iye anatero. Kudera nkhawa kwachikondi kunali kotonthoza. Anandikoketsa m’mphuno mankhwala ogonetsa thulo, ndipo m’kanthaŵi kochepa, ndinachita chizwezwe, dzanzi, ndiyeno nkukomoka.
Ndinadzuka pamene anali kundichotsa pakama wamagudumu kundiika pakama wamba wa m’chipatala. Ndinayamba kutekeseka pamene ndinamva kupweteka kwa chilonda ndi mipopi m’mpuno ndi pam’mero panga. Mkazi wanga pamodzi ndi bwenzi, ananditonthoza. Ludzu langa lalikulu linachepetsedwa mwakupaka kwawo madzi pamilomo yanga. Ndinakondwa kukhala wamoyo.
Ngakhale kuti ndinauzidwa motsimikiza kuti opaleshoni yanga inali yachipambano, mlingo wa mwazi wanga unapitirizabe kutsika. Kodi nchiyani chimene chinalakwika? Kupimidwa kwa chimbudzi changa kunavumbula kuti ndinali kukhabe mwazi. Madokotala anali otsimikiza kuti sunali kuchoka pachilonda chimene anali atangokonza—nangano, unali kuchoka kuti?
Madokotala anaganiza kuti mwina ndinadya paizoni imene inapanga chilonda, mwinamwake m’thumbo lalikulu. Anati ndinali wofooka kwambiri mosakhoza kuchitidwanso opaleshoni.
Chitsenderezo cha Kulandira Mwazi
Pamene mlingo wanga wa mwazi unali kucheperachepera, chitsenderezo chakuti ndilandire kuthiriridwa mwazi chinakula. Nesi amene anali kundisamalira anati ngati anali a dokotala, akanangotenga mwazi ndi kundiika popanda kufunsa. Pafupifupi ola lachitatu m’maŵamaŵa, dokotala anabwera kwa ine naati: “Muyenera kuthiriridwa mwazi kuti mukhale ndi moyo.”
Ndinamfotokozera kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kuti ponse paŵiri pazifukwa zachipembedzo ndi zamankhwala, sindikalandira kuthiriridwa mwazi. (Levitiko 17:10-14; Machitidwe 15:28, 29) Iye anawonekera kukhala atakwiitsidwa, koma ndinawona mkhalidwe wake kukhala wochititsidwa ndi kusamvetsetsa kwake ndi kusalemekeza kaimidwe kanga.
Chifukwa cha chitsenderezo chomakulakula, limodzinso ndi mikhalidwe ina m’chipatala, ndinapempha kuchotsedwamo. Posapita nthaŵi ndinanyamulidwa pa ambulansi kubwerera kuchipinda cha odwala panthambi.
Chithandizo Chamankhwala Chopulumutsa Moyo Chachipambano
Ndinafunsa dokotala komweko, mmodzi wa Mboni za Yehova, ngati anandipatsadi EPO (erythropoietin), homoni yongopanga imene imasonkhezera mafuta a m’mafupa kupanga maselo ofiira a mwazi mofulumira. Iye anati anaterodi. Ndithudi, thupi limafunikirabe mirimo yofunika kuti lipange maselo ofiira a mwazi abwino. Mirimo imeneyi ndiyo folic acid, vitamini B, ndipo makamaka chitsulo. Dextran yachitsulo (Imferon) yopatsidwa kudzera mumsempha ndiyo njira yamwamsanga yoperekera chitsulo chofunikacho, ndipo ndinafunsira imeneyo.a
Komabe, kunalibe Imferon ku Argentina. Inali yovuta kupeza ngakhale ku United States, popeza kuti yambiri ya iyo inali itatumizidwa ku Middle East chifukwa cha nkhondo ya ku Persian Gulf. Komabe, ina inapezeka pomalizira, ndipo mwamsanga inapatsidwa kwa mmodzi wa Mboni za Yehova amene anali kubwera ku Argentina.
Panthaŵiyo hemoglobin yanga inali pamlingo wa 4 chabe. Podziŵa kuti kuchotseredwa mwazi wochuluka wokapima kungachititse nthenda yakuchepa mwazi, ndinauza a katswiri m’zamankhwala amene anadza kunthambi kuti sindikawalolanso kutenga mwazi. Iye anatsutsa kuti: “Tiyenera kuutenga kuti tidziŵe zimene zikuchitika.”
“Mukudziŵa zimene zikuchitika,” ndinayankha motero. “Ndiri kukha mwazi, ndipo kodi chinthu chofunika kwambiri m’thupi langa nchiyani?”
“Mwazi,” iye anayankha motero.
“Ndipo ndasankha kuti pakali pano ndisapereke mwazi wanga wowonjezereka uliwonse,” ndinayankha motero. Sindikudziŵa kuti mlingo wa mwazi wanga unatsika kwambiri motani.
Usikuwo ndinapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova, kupempha chitsogozo chake ndi kumfotokozera chikhulupiriro changa chakuti ndikadzukenso tsiku lotsatira. Ndinaterodi, koma ndinamva kuti mphamvu yanga ya moyo inali kundichoka. Imfa inawoneka kukhala pafupi. Mlingo wanga wa hemoglobin nthaŵi zambiri umakhala magramu 17.2 pa deciliter imodzi, wokhala kumbali yapamwamba ya mlingo wovomerezeka, choncho ndinataikiridwa ndi 75 peresenti ya mwazi wanga. Kanthu kenanso kanafukira kuchitidwa.
M’maŵa umenewo ndinapempha kuti ndikambitsirane ndi madokotala ondisamalira ponena za chithandizo changa chamankhwala. Vitamini K, yofunika kuti iletse kukha kwa mwazi, sinali kugwiritsidwa ntchito, koma tsopano anavomereza mosazengereza kuayamba kundipatsa. Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi ena a mankhwala amene mukugwiritsira ntchito sangakhale akuchititsa kapena kuwonjezera kukha kwa mwazi?”
“Ayi,” anayankha motero.
“Kodi muli otsimikiza?” ndinatero moumiriza.
M’maŵamaŵa patsiku lotsatira, mmodzi wa madokotala anabwera kwa ine nanena kuti pambuyo pakufufuza kwina anapeza kuti ena a mankhwala angakhale akuwonjezeradi kukha kwa mwazi. Kuwagwiritsidwa ntchito kwawo kunalekeka panthaŵi yomweyo. Kufunitsitsa kwa madokotala kumvetsera kwa ine mosamalitsa monga wodwala ndi kupenda chithandizo changa chamankhwala kunawonjezera ulemu wanga pa iwo.
Nditapempha, mabukhu azamwankhwala anabweretsedwa nkuikidwa pambali pa kama wanga, ndipo mkazi wanga ndi ine tinayamba kuwaŵerenga. Nkhani ina inasimba za madzi otchedwa hemostat, mankhwala oletsa kukha kwa mwazi. Titangoipeza nkhaniyo Dr. Marcelo Calderón Blanco, Mboni inzathu, analoŵa nalengeza kufunitsitsa kwake kugwiritsira ntchito mankhwala ofanana! Nsanganizoyo inaikidwa mwa ine m’njira yofanana ndi imene amapatsira mankhwala oloŵetsera kumatako. Pafupifupi panthaŵi yomweyo, Imferon inabwera kuchokera ku United States ndipo ndinapatsidwa kudzera mumsempha.
Chotsalira tinangoyembekezera basi. Patsiku lomwelo, ndinayamba kudzimva wamphamvupo. Pambuyo pa masiku atatu ndinawalola kutengako mwazi wokapima. Modabwitsa, mlingo wa hemoglobin unakwera kufikira pa 6! Komabe, pamene unapimidwa masiku asanu apapitapo, unali 4 ndipo umatsikabe! Madokotala anakaikira zimenezo. Analamula kuti kupima kwina kuchitidwe. Kumeneko kunatsimikizira koyambako. EPO ndi Imferon inali kugwira ntchito!
Katswiri wa kukiliniki amene anapima mwazi wanga anachita foni nanena kuti a dokotala mwachiwonekere anandiika mwazi. “Palibe aliyense amene mlingo wa mwazi wake ungakwere mofulumira chotero popanda kuthiriridwa mwazi,” anaumirira kutero. Dokotala anaumuuza motsimikiza kuti palibe mwazi umene unaperekedwa. “Kodi ndinjira yotani imene ikugwiritsiridwa ntchito imene ikukweza mlingo wa mwazi mofulumira chotero?” iye anafuna kudziŵa. Anauzidwa za EPO ndi Imferon imene inali kugwiritsiridwa ntchito.
Dr. Amilcar Fernández Llerena, mmodzi wa madokotala anga osakhala Mboni, anandichezera patsiku lomwe mwazi wanga unapimidwa. Atandipima, anati modabwa: “Ndikupatsa dzina latsopano—Lazaro.” (Yerekezerani ndi Yohane 11:38-44.) Ndinachita zonse zothekera kuti ndisagwetse misozi.
Dr. Llerena anati: “Muyenera kuyamika Mulungu wanu, Yehova, pokhala muli wamoyo.” Ndinamfunsa zimene anatanthauza. “Ngati munali kusuta fodya, kumwa anamgoneka, kapena chidakwa,” anayankha motero, “simukanapulumuka opaleshoni. Koma popeza kuti thupi lanu nloyera ndipo nlolimba chifukwa cha kumvera lamulo la Mulungu, munapulumuka.”
Chidziŵitso chimene ndinagwiritsira ntchito m’chokumana nacho changa chinali kwakukulukulu zimene tinali kuphunzitsa Makomiti Olankhula ndi Zipatala pamaseminale ku North America, Ulaya, ndi Latin America. Chimene programuyo imagogomezera ndicho njira zina zachipambano zimene zingagwiritsiridwe ntchito popereka chithandizo chamankhwala popanda mwazi. Mwachimwemwe, chidziŵitso chokhudza njira zina zolowa mmalo zimenezi chiri chopezeka kupyolera mwa Komiti Yolankhula ndi Chipatala, amene oposa 800 alipo tsopano padziko lonse.
Ndikhulupirira kuti chokumana nacho changa chidzathandiza Mboni zina zimene zimafuna chithandizo chamankhwala popanda mwazi. Chipatala chimene ndinachitidwirako opaleshoni chinatumiza mawu pambuyo pake kunthambi ya Argentina ya Mboni za Yehova. onena kuti tsopano chazindikira kuti tiri ndi njira yachipambano yoperekera chithandizo kwa odwala popanda zinthu zamwazi ndi kuti chikakhala chofunitsitsa kugwirizana nafe mtsogolo.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze ndandanda yatsatanetsatane ya misanganizo ina, wonani Galamukani! (Wachingelezi) wa November 22, 1991, tsamba 10.
[Chithunzi patsamba 23]
Kuchoka m’chipatala pambuyo pa opaleshoni yanga