Sitili Amatsenga Kapena Milungu
YOSIMBIDWA NDI MERCY UWASI, KU NIGERIA
NDINAYAMBA kumva kupweteka m’mimba pamasana ena a dzuŵa lotentha m’March 1992 kuno ku West Africa. Ndinamka kumunda ndi a m’banja mwathu kuti tikazule chinangwa. Pamene tinali kumeneko, ndinayamba kumva kupweteka kwambiri m’mimba mwanga. Pofika kunyumba, kupwetekako kunalidi kwakukulu kwambiri. Ndinali kusanza; sindinali kupuma bwino. Ngakhale kuti kupwetekako kunandilepheretsa kuimirira kapena kuyenda, amayi anakhoza kundiloŵetsa m’takisii, imene inathamangira kuchipatala chapafupi.
Kuchipatalako dokotala amene ndinaonana naye anali mwamuna amene panthaŵi ina ndinamchitira umboni wonena za chiyembekezo cha Baibulo. Dokotalayo anagwira mimba yanga; inali yotupa. Iye anafunsa ngati ndinali kukodza magazi, ndipo amayi anavomereza kuti inde ndinali panyengo yanga ya kusamba.
“Mwana wanuyu ali ndi pathupi pamiyezi isanu,” dokotalayo anatero. “Chomwe akukhera mwazi nchakuti wayesa zoti achotse pathupipo.”
Amayi anatsutsa kuti: “Ayi, a Dokotala! Iyeyutu si mtsikana wa mtundu wotero.”
“Musatero. Masiku ŵano atsikana amanamiza makolo awo. Ali ndi pathupi ameneyu.”
Ndiyeno ndinadzinenera ndekha. Ndinati ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo ndinaleredwa m’nyumba Yachikristu ndi kuti chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo sichingandilole kuchita chisembwere.
Dokotalayo poyankha anati kwa amayi: “Amayi, tiyeni tikankhire chipembedzo pambali kuti tinene zenizeni. Ndikukuuzani zowona kuti mtsikanayu ali ndi pathupi pa miyezi isanu.”
“Nyamuka,” Amayi anatero kwa ine. “Tikumka kuchipatala china.” Pamene tinatuluka m’chipatalamo, ndinamka kukakhala pansi pakapinga ndikumalira chifukwa chakuti kupwetekako kunali kwakukulu. Amayi ananditengera kunyumba mofulumira nauza atate zimene dokotala anali atanena.
Iwo anasankha kunditengera kuchipatala chokulirapo ndi chamakonopo, chipatala chophunzitsira antchito za chipatala. Paulendo wanga womka kumeneko, ndinapemphera kwa Yehova kuti andipulumutse kotero kuti anthu asatonze dzina lake loyera mwa kunena kuti ndinafa chifukwa cha pathupi pa chisembwere. Ndinanena kuti ngati ndikafa, pamene dokotala uja akadzaona Mboni za Yehova zikufika kudzamlalikira, iye adzanena kuti: ‘Kodi sanali mmodzi wa anthu inu uja anafika pano ali ndi pathupi papitapo?’ Ndinapempheranso kuti mwina ndidzakhale wokhoza kupitanso kwa dokotalayo ndi kukamchitira umboni kachiŵirinso.
“Adakali Namwali!”
Kuchipatala chokulirapocho, mkangano umodzimodziwo umene unachitika kuchipatala choyamba chija unabukanso; madokotala analingalira kuti ndinali ndi pathupi. Kupweteka kwake kunali kwakukulu. Ndinali kulira. Dokotala wina analankhula mwaukali, akumati: “Ndi zimene atsikananu mumachita nthaŵi zonse. Mumakhala ndi pathupi, ndiyeno n’kumafuula.”
Iwo anandipima. Zidakali choncho anayamba kundifunsa mafunso ambirimbiri. “Kodi ndiwe wokwatiwa?”
“Ayi,” ndinatero.
“Uli ndi zaka zingati?”
“Khumi ndi zisanu ndi zitatu.”
“Uli ndi zibwenzi zingati?”
“Ndilibe chibwenzi chilichonse.”
Ndiyeno dokotala wamkulu anayamba kukalipa kuti, “Ukuti chiyani? Kodi ukundiuza kuti ulibe chibwenzi chilichose pausinkhu wa zaka 18?” Kachiŵirinso, monga momwe zinalili kuchipatala choyamba kuja, ndinafotokoza kaimidwe kanga Kachikristu. Ndiyeno iye anafunsa ngati ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinavomera. Zitatha zimenezo, sanafunsenso funso lina.
Kupimako kunasonyeza kuti ndinalibe pathupi. Amayi anamva mmodzi wa madokotala akumanena kwa anzake kuti: “Adakali namwali!” Madokotalawo anapepesa, akumati: “Musatiimbe mlandu chifukwa cha kuganizira kumene tachita. Timakunana ndi zinthu za mtundu wotero kwa atsikana tsiku lililonse.” Komabe, vuto limenelo linali chiyambi chabe cha ziyeso zanga.
‘Udzapatsidwa Mwazi’
Kupima kotchedwa ultrasound kunasonyeza chotupa chachikulu m’chibereko changa. Chinali chachikulu monga nyumwa laling’ono. Opaleshoni inafunika.
Mosazengereza ndinawauza kuti sindidzathiridwa mwazi ngakhale kuti ndingavomereze kuthiridwa zinthu zina za madzi. Iwo anaumirira kuti mwazi unali wofunika.
Mmodzi wa madokotala ophunzira anandinyodola, akumati: “Zimene ukunenazo ndi zimene mmodzi wa ziŵalo zanu ananena papitapo. Koma pamene matenda ake anakula, anavomereza zothiridwa mwazi.”
“Inetu ndine wina,” ndinayankha motero, “pakuti inde wanga ndi inde ndithu ndipo ayi wanga ndi ayi. Sindidzalolera molakwa umphumphu wanga.”
Pambuyo pake, madokotala atatu anafika pa mbedi wanga akumafuna kudziŵa za kaimidwe kanga pa mwazi. Ndinafotokoza kuti Baibulo limanena kuti Akristu ayenera ‘kusala . . . mwazi.’—Machitidwe 15:20.
“Komatu sudzaulowetsa mwapakamwa,” iwo anachonderera motero. “Udzauloŵetsa kupyolera mumtsempha.”
Ndinati zilibe kanthu kuti kaya munthu akuudya kapena akuuloŵetsa kupyolera mumtsempha, zonsezo nzofananabe.
Pa Loŵeruka, March 14, patatha mlungu umodzi kupwetekako kutayamba, dokotala wamkulu wa opaleshoni anandipenda. Anali atapatsidwa ntchito yondichita opaleshoni. Panthaŵiyo kutupako kunali kutafika pachifuwa.
Iye anafunsa kuti, “Kodi akudziŵitsa kuti udzathiridwa mwazi?”
“Anandiuza zimenezo, komatu sindidzathiridwa mwazi, a Dokotala,” Ndinayankha motero.
“Taima ndikuuze kanthu kena,” napitiriza. “Udzathiridwa. Ngati suutero, udzafa. Pa Lolemba, pamene ndifika, ngati palibe mwazi pa iwe, sindidzachita opaleshoniyo. Popanda mwazi, palibenso opaleshoni.”
Ndiyeno iye anaona buku pambali pa mbedi wanga nafunsa kuti: “Kodi ili ndi Baibulo lako?” Ndinati ayi; linali kope langa la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhakalako.a Iye anati ndiyenera kugwiritsira ntchito bukulo popemphera kuti ndisafe. Ndinafotokoza kuti sitimaŵerenga mapemphero athu kuchokera m’buku. Nthaŵi iliyonse pamene tili ndi vuto, timapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima mwathu.
Mkati mwa masiku aŵiri otsatira, madokotala ndi manesi anali kumangofika kudzandiumiriza kuti ndivomereze kuthiridwa mwazi. Anandiuza kuti ndinali wachichepere kwambiri kosafunikira kufa. “Thiridwa mwazi ndi kukhala ndi moyo!” iwo anatero.
“Yehova ndi Wanga”
M’nthaŵi za nsautso zimenezo, ndinaŵerenga Salmo 118, limene mwapang’ono limati: “M’mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. Yehova ndi wanga; sindidzawopa; adzandichitanji munthu?”—Salmo 118:5, 6.
Nditasinkhasinkha pamavesi ameneŵa, chikhulupiriro changa mwa Yehova chinalimbitsidwa. M’maŵa umenewo makolo anga anafika kuchipatalako. Ndinawasonyeza salmo limenelo, ndipo nawonso analimbitsidwa m’chikhulupiriro.
Izi zidakali choncho, Amayi ndi Atate sanangochirikiza chabe chosankha changa cha kusalandira mwazi komanso anali kundipempherera. Ziŵalo za mumpingo wanga zinapitiriza kundipempherera ndi kundilimbikitsa ndi Malemba.
“Sitiri Amatsenga”
Pa Lolemba, March 16, mmaŵa umene opaleshoniyo inalinganizidwa kuchitidwa, mmodzi wa madokotalawo analoŵa m’chipinda changa nandiona nditagwira m’manja khadi la Medical Directive, limene limafotokoza kaimidwe kanga pakuthiridwa mwazi. Iye anati, “Ichi nchiyani? Kodi ukutsimikizadi zimene wakhala ukunena?”
“Inde, sindidzathiridwa mwazi.”
“Chabwino,” iye anatero, “ndiye kuti tileka kukuchita opaleshoni yako. Palibenso opaleshoni.”
Ndiyeno dokotalayo anaimbira foni amayi kuchokera m’chipinda changa. Amayiwo anati: “Iye ngwamkulu woti nkudzisankhira yekha. Sindingamsankhire chochita. Iye akuti chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo sichingamlole kuthiridwa mwazi.”
Pomva zimenezo dokotalayo anaponyera pansi mapepala a zolembedwa zanga natuluka m’chipindacho mwaukali. Sitinamve kalikonse kwa maola asanu. Ndinali kumva kupweteka kwambiri ndipo sindinkatha kudya. Ndipo panalibenso chipatala china m’deralo.
Ndiyeno, ndinadabwa kuona kuti abweretsa machira odzanditengera kumka nane kuchipinda cha opaleshoni. Ndinali nditagwirira khadi langa la “No Blood” m’manja. Popita kuchipindako ndinaona ziwiya zochitira opaleshoni limodzi ndi matumba a mwazi. Ndinayamba kulira mosaletseka, ndikumati sindikufuna kuthiridwa mwazi. Mmodzi wa manesi anati ndiyenera kutayira pansi khadilo. Iye anati sindiyenera kuloŵa nalo m’chipinda cha opaleshoni. Ndinati sindidzaloŵa popanda khadilo ndi kuti ndinafuna kulionetsa kwa dokotala wamkulu wa opaleshoni. Ndiyeno nesiyo anandilanda khadilo m’dzanja langa naloŵa nalo m’chipindamo ndi kusonyeza dokotala wa opaleshoniyo. Nthaŵi yomweyo dokotalayo ndi madokotala ena asanu ovala zovala za m’chipinda cha opaleshoni anafika pamene ndinali.
Dokotala wamkulu wa opaleshoniyo anakwiya. Iye anaitana amayi, naloza mimba yanga, nati kwa iwo: “Amayi inu, taonani. Sitikudziŵa zimene tidzapeza mkati mwake. Ngati tidzafunikira kucheka kwambiri, zimenezo zidzachititsa kuchucha kwa mwazi wambiri. Kodi mukufuna kuti afe ndi kuchucha mwazi?”
Poyankha Amayi anamuuza kuti: “A Dokotala, ndidziŵa kuti Yehova adzakhala ndi mtsikanayu. Ndipo adzakhala nanunso. Ingochitani zimene mukhoza ndi kusiyira nkhani yonse kwa Yehova.”
Ndiyeno dokotalayo anati: “Ifetu sitiri amatsenga kapena azitsamba. Timachita zimene tinaphunzira. Sindingathe kuchita opaleshoni imeneyi popanda mwazi.”
Kachiŵirinso amayi anamchonderera kuti angochita zimene angathe. Potsirizira pake, iye anavomereza kuchita opaleshoni popanda mwazi. Iye anandifunsa ngati ndinali ndi mantha. Poyankha ndinati: “Sindikuopa imfa. Ndidziŵa kuti Yehova ali nane.”
“Pitirizabe Kutumikira Mulungu Wako”
Opaleshoniyo inachitidwa mkati mwa ola limodzi chabe. Anandicheka nachotsa chotupacho mosavuta, zikumadabwitsa antchito a pachipatalapo.
Pambuyo pake mmodzi wa madokotalawo anauza Amayi kuti madokotala ophunzirawo amanena za ine usiku m’zipinda zawo zogona. Tsopano pamene Amayi kapena ine tipita kuchipatalako, amatilemekeza mwapadera.
Patapita masiku aŵiri pambuyo pa opaleshoni yanga, dokotala wa opaleshoniyo analoŵa mu wadi yanga, nafunsa kuti ndinali kupeza bwanji, ndiyeno anati: “Uyenera kupitirizabe kutumikira Mulungu wako. Anakuthandizadi.”
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.