Kuyang’anizana ndi chothetsa Nzeru cha Matenda
“SINDIDZAKUBISA; uli ndi fundo lowopsa. Ngati sitilichotsa mofulumira, lidzawononga ziŵalo zina zofunika kwambiri. Nchifukwa chake ndikuti tidule mwendo wako.”
Mawu a dokotala amenewo anandidzidzimutsa ngati madzi ozizira a m’chitini, malinga ndi zimene timanena kuno ku Peru. Ndinali chabe ndi zaka 21. Mwezi umodzi zisanachitike zimenezi, ndinayamba kumva kupweteka kwa bondo langa lakumanzere ndipo anandipatsa mankhwala a kusweka malungo. Komabe, pambuyo pa masiku angapo, ndinalephera ndi kuimirira komwe.
Panthaŵiyo, ndinali kutumikira monga mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova kumapiri a Andes chapakati pa Peru. Nditabwerera ku tauni yakwathu ya Huancayo, ndinapita ndi amayi ku mzinda wa Lima kugombe. Kumeneko, pa July 22, 1994, ndinaloŵa m’chipatala cha kansa chabwino koposa m’dzikoli, kumene anandiuza kuti nthenda yanga inali osteosarcoma.
Nkhani ya Chikumbumtima
Posapita nthaŵi anandiuza kuti chipatalacho sichinali kuchita maopaleshoni popanda kugwiritsira ntchito mwazi. Ndipo dokotala wina anati: “Ndingakonde kuti ukafere kunyumba osati m’manja mwanga.” Koma Hospital Liaison Committee (HLC) yakumaloko, kagulu ka Mboni za Yehova zimene zimalimbikitsa mgwirizano pakati pa chipatala ndi odwala, kanandikambirako. Chotero, dokotala wamkulu wa opaleshoni pachipatalacho analoleza dokotala aliyense pa antchito ake kuchita opaleshoniyo ngati anali wokonzekera kulimbana ndi vutolo. Dokotala wina anali wokonzekera, ndipo mosataya nthaŵi anandikonzekeretsa kaamba ka opaleshoni.
Ndisanapite ku opaleshoni ndinalandira alendo ambiri. Wansembe wina, ndi Baibulo kumanja, anadza kudzandiona ndipo anati nthenda yanga inali chilango cha Mulungu. Anandilimbikitsa kulandira mankhwala alionse amene akanapulumutsa moyo wanga. Ndinamuuza kuti ndinali wotsimikiza kutsatira lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi.’—Machitidwe 15:19, 20, 28, 29.
Manesi nawonso anali kubwera ndi kunong’onezana kuti: “Nchitsiru ichi, nchitsiru!” Ndiponso madokotala anabwera m’timagulumagulu. Anafuna kuona mnyamata amene anakana kuikidwa mwazi pa mtundu wa opaleshoni imene iwo anaganiza kuti inafunikira mwazi. Komabe, alendo ofunika kwambiri kwa ine anali Akristu anzanga ndi achibale. Manesi anachita chidwi kwambiri ndi alendo ambiri olimbikitsa ameneŵa.
Machiritso Opambana Popanda Mwazi
Mphindi zingapo asanandigoneke, ndinamva mmodzi wa ogonetsa tulo akunena kuti: “Sindidzakhala ndi mlandu wa zimene zidzachitika!” Koma wogonetsa tulo winayo, limodzi ndi dokotala wanga wa opaleshoni ndi akulu a chipatala, analemekeza pempho langa la kusaikidwa mwazi. Ndiyeno ndinadzangomva wogonetsa tuloyo akunena kuti: “Samuel, dzuka. Opaleshoni yako yatha.”
Ngakhale kuti mwendo wanga wonse unachotsedwa, ndinayamba kumva kupweteka kwambiri kumwendo umene kunalibe. Ndinafuna kululuza kupwetekako mwa kusisita nchafu, koma imene kunalibe. Ndinali kumva kupweteka kwachilendo kotchedwa phantom pain (kupweteka kongoyerekezera). Ndinamvadi kupweteka, ndipo kunali kosautsa kwambiri, ngakhale kuti mwendo umene ndimaganiza kuti unali kupweteka anali atauchotsa kale.
Ndiyeno, ndinayenera kuchiritsidwa ndi chemotherapy. Ziyambukiro zoipa za machiritso ameneŵa ndizo kuchepa maselo a mwazi m’thupi ofiira ndi oyera ndi ma platelet a mwazi, amene afunika kwambiri kuti mwazi uzigwirana. Zimenezi zinatanthauza kuti kagulu kena ka madokotala kanafunikira kuuzidwa za kukana kwanga kuikidwa mwazi. Apanso a HLC analankhulana ndi amene anali ndi thayo, ndipo madokotalawo anavomera kupereka machiritsowo popanda mwazi.
Pambuyo pa chemotherapy imeneyo panatsatira ziyambukiro zake zachizoloŵezi—tsitsi langa linathothoka ndipo ndinayamba kumva nseru, kusanza, ndi kuchita tondovi. Ndiponso anali atandiuza kuti ngozi yakuti ubongo wanga ukhe mwazi inali yotheka ndi 35 peresenti. Ndinakakamizika kufunsa mmodzi wa madokotala chimene chidzandipha—kansa kapena chemotherapy.
Pambuyo pake, madokotala ananena kuti sakanandipatsanso mankhwala ena a chemotherapy popanda kuwonjezera mwazi wanga mwa kundiika mwazi. Dokotala wina anandiuza mwaukali kuti ngati anali wokhoza, akanandigoneka ndi kundipatsa mwazi. Ndinamuuza kuti zimenezo zisanachitike, ndikanalekeratu machiritso a chemotherapy. Dokotalayo anachita chidwi ndi kulimba kwanga.
Ndinavomera kupatsidwa erythropoietin kuti iwonjezere mwazi wanga. Atandipatsa, mwazi wanga unawonjezeka. Pambuyo pake, anapitiriza ndi chemotherapy mwa kundipatsa mankhwala kudzera m’mitsempha masiku angapo. Ndinali kukhala chigonere, ndikumadzifunsa kuti, ‘Kodi mankhwalawa ndiwo adzachititsa ubongo wanga kukha mwazi?’ Mwamwaŵi ndinalandira mankhwala onse popanda zotulukapo zoipa.
Opaleshoni yanga isanachitike, lamulo la chipatalacho linali la kukana kuchiritsa anthu amene anali kukana kuikidwa mwazi. Koma lamulolo linasintha. Kwenikweni, tsiku lotsatira opaleshoni yanga, dokotala amene anandichita opaleshoni anachitanso opaleshoni ina popanda kugwiritsira ntchito mwazi, ndipo wodwalayo sanali wa Mboni za Yehova! Tsopano madokotala ambiri m’chipatalacho akugwirizana kwambiri ndi a HLC, ndipo avomera kulandira odwala amene akufuna opaleshoni yopanda mwazi.
Kuzoloŵera Kupereŵera Kwanga
Kuyambira pamene ndinali mwana, ndinaphunzitsidwa njira za Mulungu. Ndikhulupirira zimenezi zinandithandiza kusunga zikhulupiriro zanga zozikidwa pa Baibulo pa chothetsa nzeru cha matenda chimenechi. Komabe, posachedwapa, ndapsinjika mtima kuti sinditha kuchita zochuluka zimene ndimafuna kuchita muutumiki wa Mulungu. Ndinauza amalume, amenenso ndi mkulu wachikristu, mmene ndinamvera. Iwo anandikumbutsa kuti ndi mtumwi Paulo yemwe anali ndi chimene iye mwini anatcha ‘munga m’thupi lake’ ndi kuti chimenecho chinamlepheretsa kutumikira Mulungu kwambiri monga mmene akanafunira. Koma Paulo anachita zomwe anakhoza. (2 Akorinto 12:7-10) Zimene anandiuza amalume zinandithandiza kwambiri.
Posachedwapa ndinaikidwa mwendo wopanga. Ndikhulupirira kuti udzanditheketsa kupereka utumiki wowonjezereka kwa Mulungu, Yehova. Ndiyamikira kwambiri kuti ndinasunga chikumbumtima chabwino pa chothetsa nzeru changa cha matenda. Ndili ndi chidaliro chakuti ndikakhalabe wokhulupirika, Yehova adzandifupa ndi thupi labwino ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso, mmene simudzakhalanso zopweteka ndi kuvutika.—Chivumbulutso 21:3, 4.—Yosimbidwa ndi Samuel Vila Ugarte.