Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 4/1 tsamba 27
  • Yehova Anadalitsa Kaimidwe Kawo Kolimba Kaamba ka Lamulo Lake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anadalitsa Kaimidwe Kawo Kolimba Kaamba ka Lamulo Lake
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Sitili Amatsenga Kapena Milungu
    Galamukani!—1994
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kupulumutsidwa ku Imfa ndi Chithandizo Chamankhwala Popanda Mwazi
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 4/1 tsamba 27

Ripoti la Olengeza Ufumu

Yehova Anadalitsa Kaimidwe Kawo Kolimba Kaamba ka Lamulo Lake

MU dziko la ku Middle East, tate anali kukonza tayala yophulika m’mphepete mwa msewu pamene galimoto linagunda mwana wake wamwamuna wa zaka zinayi zakubadwa ndipo kenaka inathaŵa. Ndi mwana wovulalayo pa miyendo ya mayiyo, tateyo analunjika ku chipatala chapafupi kokha kukatsogozedwa ku chipatala china makilomita 25 kutali. Dokotala analingalira kuti mnyamatayo anali ndi kukha mwazi kwa mkatikati ndipo kuti anafunikira kutumbulidwa ndi kuthiridwa mwazi. Madokotala ena asanu ndi atatu anavomereza. Akumadziŵa lamulo la Mulungu motsutsana ndi kuthiridwa mwazi, makolowo anakana. “Muli kokha ndi mphindi zisanu zakuti muganizire kupanda apo sitidzakhudza mwana wanu ngakhale ngati mutavomereza ku kuthiridwa mwazi pambuyo pake,” anawopsyeza tero dokotalayo. Panthaŵiyo, mimba ya mwanayo inapitiriza kutupa ndipo inali kufika pa mkhalidwe wowopsya kwambiri.

Mbale wakuthupi wa tateyo, wosakhala m’chowonadi, anaika chitsenderezo pa tateyo kuti avomereze kuthiridwa mwazi. Iye anafikira pa kunena kuti: “Chonde mulingalireni mnyamatayo osati wanu koma wanga. Popeza chikumbumtima chanu chikukuvutitsani, ndidzatenga thayo lonse, kuphatikizapo malipiro a chipatala, a kupatsa mwanayo mwazi wofunikawo. Uyu ndi mwana wanu yekha.” Chitsenderezocho chinali chovuta kuchipirira, koma makolowo anali olimba m’chosankha chawo.

Iwo anamtenga mnyamatayo ndi kuchoka, kukafuna chipatala china, koma anasokera m’njira. Mwamwaŵi anawona chizindikiro cha chipatala china, ndipo anapita ku icho, ngakhale kuti sichinali chimene anali kufunafuna. Pambuyo pa kuwona mwanayo, dokotala ananena kuti: “Kutupa kwa mimba ya mwanayo kungakhale ndiponso sikungakhale chizindikiro cha kukha mwazi kwa mkatikati. Mloleni mnyamatayo agone, ndipo m’mawa tidzapanga mafufuzidwe oyenerera kuti tipeze.” Mafufuzidwewo anasonyeza kuti panalibe kukha mwazi, koma kutupako kunali chifukwa cha ngoziyo. Panalibe chifukwa cha kumtumbula. M’chenicheni, dokotalayo ananena kuti kutumbulidwako kukanakhala kowopsya kwambiri. “Tiyamikire Yehova,” anatero makolowo, “kaamba ka chisungiko cha mwana wathu wa mwamuna ndi kutitsogolera ife ku chipatala cholondola ndi dokotala wolondola.”

Zaka khumi pambuyo pake, kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo cha mkhalidwe umenewu? Tateyo akulongosola: “Mbale wanga wakuthupi yemwe anaika chitsenderezo pa ine m’chipatala anafikira kukuyamikira kaimidwe kathu ndi kuwona chitsogozo cha Yehova m’nkhaniyi. Ichi chinadzutsa chikondwerero chake m’chowonadi, chimene iye anachilandira, ndipo iye tsopano ali wobatizidwa ndipo akutumikira monga mkulu mu mpingo. Mkazi wake ndi ana akutumikira Yehova mokangalika limodzi naye. Abale anga ena aŵiri alinso m’chowonadi limodzi ndi mabanja awo, ndipo mmodzi wa iwo akutumikira monga mtumiki wotumikira. Atate wanga ndi amayi wanga anabatizidwa posachedwapa mosasamala kanthu za msinkhu wawo wa ukalamba. Chotero ngakhale kuti chinali chokumana nacho chowopsya kwa mkazi wanga ndi ine, chifukwa cha icho ziwalo zina 30 za banja langa zalandira chowonadi; zina zabatizidwa kale ndipo zikutumikira monga akulu ndi atumiki otumikira. Ena ali panjira yawo ya ku ubatizo. Mwana wanga yemwe tsopano ali ndi zaka 14 zakubadwa, ali waumoyo wabwino, wofalitsa wokangalika, ndipo akuyang’ana kutsogolo ku ubatizo. Mkazi wanga ndi ine tiri oyamikira chotani nanga kwa Yehova kaamba ka kutithandiza ife kupanga chosankha cholondola m’chigwirizano ndi lamulo lake lolembedwa pa Machitidwe 15:29!”

[Chithunzi patsamba 27]

“Pitirizanibe kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi mwazi”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena