Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 12/8 tsamba 10-11
  • Chifukwa Chake Kunyoza Sikuli kwa Akristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Kunyoza Sikuli kwa Akristu
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Nkofala Chotero?
  • Lingaliro la Mulungu la Kunyoza
  • Kanani Mawu Onyoza!
  • Kodi Cholakwika Nchiyani Ndi Kutukwana Kamodzikamodzi?
    Galamukani!—1989
  • “Pa Chilankhulo Chathu Palibe Mawu Otukwana”
    Galamukani!—2005
  • Kodi Kutukwana N’koipadi?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingakanizire Chisonkhezero cha Kutukwana?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 12/8 tsamba 10-11

Lingaliro la Baibulo

Chifukwa Chake Kunyoza Sikuli kwa Akristu

WOULUTSA mawu panyumba yamphepo ya BBC ya Wales anadzudzulidwa chifukwa cha kukana kuchotsa “mawu oputa” pofunsa wamathanyula amene, malinga ndi mneneri wa BBC wogwidwa mawu mu nyuzipepala ya The Guardian, “anagwiritsira ntchito mawu oipa kopambana kufotokoza machitachita amene akapangitsa munthu kugwidwa ndi AIDS.” Ndiponso, 22 peresenti ya maprogramu oyang’aniridwa m’kapendedwe ka milungu iwiri ka kuulutsa nkhani m’ngalande zinayi za wailesi yakanema ya Britain anali ndi “mawu oipa, otukwana [kunyoza] ndi/kapena amwano.”

Nkhani zoterozo zimasonyeza vuto lenileni la kaimidwe kamaganizo. Kwa anthu ambiri makambitsirano odzala ndi mnyozo amanyansa ndi kuputa. Ena amangonyalanyaza mawuwo monga okondweretsa ndi osangalatsa, osadetsa nkhawa kwenikweni. Komabe, kodi kunyoza kuyenera kupezeka m’mawu a Akristu, amene amawona unansi wawo ndi Mulungu ndi wa anthu anzawo kukhala wamtengo wapatali kwambiri?

Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Nkofala Chotero?

Kunyoza ndiko “mtundu uliwonse wa chizolowezi cha mawu onyansa.” Mwano, kutemberera, ndi kutukwana ziri pakati pa kufotokozaku. Minyozo imasonyeza ukali, ngakhale chitsutso chachipongwe. Mary Marshall, wolemba bukhu lakuti Origins & Meanings of Oaths & Swear Words, akunena kuti “malumbiro ndi zowinda ali kwenikweni mawu olankhulidwa koposa ndi kulembedwa.” Komabe, mabukhu a nkhani zongopeka ambiri ngodzala ndi mawu onyoza.

Kodi nchifukwa ninji kunyoza kuli kofala kwambiri? Anthu ena ochepekedwa mawu angatolere mawu mwa kugwiritsira ntchito kwambiri mawu otemberera. Ena amalankhula mawu oipa kugogomezera. Pofotokoza, kunyoza kaŵirikaŵiri kumagwirizanitsidwa ndi malingaliro a kuipidwa, kugwiritsidwa mwala, ndi mkwiyo. Ndithudi, pokumana ndi mikhalidwe yovuta, ambiri amalola mawu osayenera kutuluka pamilomo yawo monga “njira yotulutsira . . . malingaliro oipa osungidwa.” Wofufuzayo Marshall akunena kuti mpambo wa chisonyezero cha mawu olembedwa mwamaalifabeti wa mawu otukwana Achingelezi ngwokhuthala kopambana pachigawo cha mawu amene amayamba ndi makonsonanti a mawu olalata amtsonyo.

Ngakhale kutukwana kungawonekere kukhala kukumasula malingaliro awo, ambiri awona kuti kunyoza kumabala kunyoza. Kodi ziri choncho chifukwa ninji? Mawu onyansa amaputa mkwiyo. Mwachitsanzo, pakati pa chisokonezeko cha magalimoto ambirimbiri m’likulu la dziko lina la ku Kumadzulo kwa Afirika, woyendetsa galimoto wina wokwiya analumpha m’galimoto yake kukadzudzula wina amene galimoto yake inampinga. Pamene kupsa mtima kunakulakula, kunamveka mawu onyansa, aliyense akumayesa kuposa mnzake m’kutukwana. Oyendetsa magalimoto ena otsekerezedwawo anatulutsa mitu pamawindo a magalimoto awo nachemerera okanganawo kukolezera kutukwanizanako.

Zipongwe zimene zimaluluza munthu zingasonkhezere kutulutsidwa kwa mawu oipa. Ophatikizidwamo angakhale mawu amene amayerekezera wonenedwayo ndi chinyama kapena ngakhale kachilombo, mawu onyodola makolo a munthuyo kapena mzera wa makolo wosadziŵika bwino, mawu amene amasumikidwa pamikhalidwe ina yakuthupi, ndi, zimene zingakhale zoputa kwambiri, mawu onyansa, mawu amwano, ndi mawu osonkhezera chisembwere.

Lingaliro la Mulungu la Kunyoza

Ndithudi, kugwiritsira ntchito molakwa dzina laumulungu ndiko tchimo lowopsa. Eksodo 20:7 amafotokoza kuti: “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe.” Koma kodi kuchita motsutsana ndi lamuloli kunaika paupandu unansi wa wolambirayo ndi Mulungu? Inde; Lamuloli linapitirizabe kuti: “Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.”

Kusonyeza mmene kumvera lamulo limeneli kunaliri kofunika kwambiri, Baibulo limasimba za mkangano wa pakati pa Mwiisrayeli ndi munthu wina. Munthu winayo “anachitira DZINA mwano, natemberera.” Kodi Mulungu anaweruza motani mkhalidwewo? Iye analamulira kuti: “Iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu.” (Levitiko 24:10-16) Ngakhale silipereka tsatanetsatane wa kutembererako, komabe chitsanzo chamalemba chimenechi chimavumbula lingaliro la Mulungu lonena za mawu ndi mkhalidwe zopanda ulemu.

Malemba Achikristu Achigiriki akuneneratu za tsiku lathu kuti “zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala . . . amwano [Chigiriki blaʹsphe·moi], . . . kwa iwonso udzipatule.” (2 Timoteo 3:1, 2, 5) Liwu Lachigirikilo bla·sphe·miʹa limapereka lingaliro loposa la mawu opanda ulemu oneneredwa zinthu zowonedwa kukhala zopatulika. Ndithudi, tanthauzo lake limaphatikizapo mawu ovulaza ndi oipitsa amene amavulaza munthu wina.

Anthu amene mawu awo ali achipongwe amasonyeza “munthu wakale” amene Akristu akulimbikitsidwa ‘kuvula’ mofanana ndi chovala chakunja chonunkha chimene sadzachigwiritsiranso ntchito.a Mtumwi Paulo akulangiza kuti: “Tayani inunso zonsezi mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu.” “Chiwawo chonse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.” (Akolose 3:8, 9; Aefeso 4:31) Ndiponso, chonde wonani kuti awo amene amachitira chipongwe ndi kuchitira mwano ena, amene Paulo akuwafotokoza kukhala “olalatira,” akuphatikizidwa pakati pa “osalungama [amene] sadzalandira ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.

Kanani Mawu Onyoza!

Kukonda Mulungu mowonadi kudzasonkhezera Mkristu kuchita zimene Iye amakondwera nazo. (1 Yohane 5:3) Monga momwedi Mulungu amasonyezera nkhawa ndi anthu onse, chotero Mkristu adzafuna kusonyeza lingaliro lofananalo m’khalidwe lake kwa ena, mwa kutero kumvera malamulo aakulu kopambana awiri, ndiko kuti, kukonda Mulungu ndi mnansi. (Mateyu 22:37-39) Tsonotu, “yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.” (Aroma 15:2) Chotero dzifunseni kuti, ‘Kodi mawu amene ndimasankha amakhumudwitsa kapena kodi amalimbikitsa?’

Ndithudi, kuyeretsa kalankhulidwe ka munthuwe sikudzakhala kosavuta ngati kunyoza kwakhala chizolowezi chozika mizu. Komabe, nkotheka—mwachithandizo. Mzimu wa Mulungu ungathandize munthu kusintha kalankhulidwe. Komatu, munthuyo ayenera choyamba kukhala wofunitsitsa kukulitsa mpambo wamawu wodzazidwa ndi mawu abwino—ndiyeno kuwagwiritsira ntchito nthaŵi zonse.—Aroma 12:2.

“Lilime lolankhula zoipa lidzatontholetsedwa,” anachenjeza motero Solomo Mfumu yanzeruyo. Chotero musalole zinyansi za kunyoza kudetsa mawu anu. Mmalo mwake, limbikirani kukhala munthu amene amadziwa cholankhula choyera ndi amene amachilankhula mwachisomo!—Miyambo 10:31, 32, Today’s English Version; Akolose 4:6.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani pa Aefeso 5:3, 4, pamene mawu apatsogolo ndi apambuyo amapereka “kulankhula zopanda pake” ndi “zopusa” kukhala zosonya kuzakugonana. Chotero, mawu oipa ndi mawu opusa azakugonana saali a Akristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena