Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 42
  • Kodi Kutukwana N’koipadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kutukwana N’koipadi?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha mafunso
  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?
  • Zimene mungachite
  • Chifukwa Chake Kunyoza Sikuli kwa Akristu
    Galamukani!—1992
  • Kodi Cholakwika Nchiyani Ndi Kutukwana Kamodzikamodzi?
    Galamukani!—1989
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingakanizire Chisonkhezero cha Kutukwana?
    Galamukani!—1989
  • Mungathe Kuphunzira Chinenero China!
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 42
Mnyamata wina amumata pakamwa kuti asamatukwane

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kutukwana N’koipadi?

“Ndinangozolowera kumva anthu akutukwana moti sindiona kuti pali vuto lililonse.”​—Christopher, wazaka 17.

“Ndinkatukwana kwambiri ndili mwana ndipo ndimaona kuti munthu sachedwa kutengera khalidweli koma zimavuta kuti asiye.”​—Rebecca, wazaka 19.

  • Kuyankha mafunso

  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

  • Zimene mungachite

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Kuyankha mafunso

  • Kodi mumamva bwanji athu ena akamatukwana?

    • Sindiona vuto lililonse.

    • Sizindisangalatsa koma ndinangozizolowera.

    • Ndimadana nazo kwambiri.

  • Kodi inuyo mumatukwana kangati?

    • Sinditukwana

    • Mwa apo ndi apo

    • Kawirikawiri

  • Kodi mumaona kuti nkhani ya kutukwana ndi yofunika kuiganizira?

    • Pang’ono

    • Kwambiri

Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

Kodi mumaona kuti kutukwana ndi nkhani yaikulu? Mwina mungayankhe kuti, ‘Osati kwenikweni. M’dzikoli muli mavuto aakulu kwambiri kuposa kutukwana. Komanso aliyense amatukwana.’ Kodi zimenezi n’zoona?

Dziwani kuti pali anthu ambiri amene satukwana. Iwo amadziwa mfundo zina zimene anthu ena sazidziwa. Mwachitsanzo:

  • Tikamatukwana timasonyeza mmene tilili. Tikutero chifukwa zimene munthu amalankhula zimasonyeza zomwe zili mumtima mwake. Choncho, ngati timatukwana tingasonyeze kuti sitiganizira mmene anthu ena amamvera. Kodi ndi mmene inuyo mulili?

    Baibulo limati: “Zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima.”​—Mateyu 15:18.

    Achinyamata akunyansidwa pamene mnyamata wina akulankhula zotukwana

    Kutukwana kuli ngati mpweya woipa umene umaipitsa zinthu

  • Kutukwana kungachititse kuti anthu ena asiye kukuonani kuti ndinu munthu wabwino. Buku lina limati: “Zimene timalankhula zingachititse kuti achibale ndi anzathu akuntchito asamatilemekeze ndiponso kuti tizivutika kupeza ntchito kapena kukwezedwa pantchito. Ngati sitilankhula bwino, anthu sangafune kucheza nafe, kumvera zimene timanena komanso sitingapeze anzathu abwino.” Bukuli limanenanso kuti: “Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikasiya kutukwana ndiye kuti ndingayambe kugwirizana kwambiri ndi ena?’”—Cuss Control.

    Baibulo limati: ‘Mawu achipongwe achotsedwe mwa inu.’​—Aefeso 4:31.

  • Kulankhula zotukwana sikusonyeza kuti ndinu wochenjera. Dr. Alex Packer analemba m’buku lake kuti: “Munthu akamakonda kulankhula zotukwana, anthu amatopa naye.” Iye ananenanso kuti, anthu akamatukwana kwambiri, “sanena zinthu zanzeru kapena zosonyeza kuti amamvera ena chisoni. Ndiye ngati salankhula zanzeru pakapita nthawi sakhalanso ndi nzeru.”—How Rude.

    Baibulo limati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.”—Aefeso 4:29.

Zimene mungachite

  • Khalani ndi cholinga. Yesetsani kuti musiye kulankhula zotukwana pasanathe mwezi umodzi. Ndiyeno mungalembe mmene mukuchitira papepala kapena pakalendala. Koma pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni pokwaniritsa cholingachi. Mwachitsanzo:

  • Muzipewa zosangalatsa zimene zimalimbikitsa kutukwana. Baibulo limati: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Tikamaonera mafilimu, kuchita masewera apakompyuta komanso kumvera nyimbo, zimakhala ngati tikucheza ndi anthu amene amachita zinthuzo. Mnyamata wina wazaka 17, dzina lake Kenneth, anati: “N’zosavuta kumaimba nawo nyimbo imene umakonda koma n’kumanyalanyaza mawu otukwana omwe ali m’nyimboyo. Ukhoza kuchita zimenezi chifukwa chongokonda mmene nyimboyo ikugundira.”

  • Muzisonyeza kuti mumaganiza ngati munthu wamkulu. Anthu ena amaganiza kuti akamatukwana ndiye kuti akusonyeza kukula. Koma zimenezi si zoona chifukwa Baibulo limanena kuti munthu wamkulu amene amaganiza bwino ‘amaphunzitsa mphamvu zake za kuzindikira kuti zizisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheberi 5:14) Anthu oterewa sachita zinthu zosayenera pongofuna “kugometsa” anthu ena.

Kunena zoona, mawu otukwana ali ngati mpweya woipa ndipo amaipitsa maganizo a munthu amene akuwalankhula komanso amene akuwamvetsera. M’dzikoli anthu ambiri ali kale ndi maganizo oipa, choncho sitikufuna kuipitsa maganizo a anthu enanso. Buku lina lomwe talitchula kale, limanena kuti: “Muzichita mbali yanu kuti musaipitse maganizo a anthu ndi mawu otukwana. Mukamachita mbali yanu, mudzamva bwino mumtima mwanu ndipo anthu ena adzasangalala nanu.”—Cuss Control.

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Jared

“Mukamalankhula mawu otukwana anthu ena angasiye kukulemekezani. Ngati simungakwanitse kufotokoza zinthu popanda kutukwana, zimangosonyeza kuti mukufunika kuphunzira mawu ena abwino.”​—Jared.

Jennifer

“Anthu amasankha okha mawu oti alankhule. N’zoona kuti kuganiza tisanalankhule kungakhale kovuta. Koma n’zotheka kusiya chizolowezi cholankhula mawu otukwana.”​—Jennifer.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena