Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 8/8 tsamba 21-22
  • Anthu Aang’ono, Zipsinjo Zazikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Aang’ono, Zipsinjo Zazikulu
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Olera Ana Ali Okha Amakhala ndi Mavuto Ambiri
    Galamukani!—2002
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Thandizani Ana Anu Kulaka Kupsinjika Maganizo
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 8/8 tsamba 21-22

Anthu Aang’ono, Zipsinjo Zazikulu

“Zisoni za ana nzazing’ono, indetu, koma nayenso mwana ali wamng’ono.”—Percy Bysshe Shelley.

TAYANG’ANANI chipeŵa chojambulidwa pansi pano. Poyamba chimaonekera kukhala chachitali mumsinkhu kuposa muukulu wake. Komabe, kwenikweni, mbali zonse ziŵiri utali ndi ukulu wake nzofanana. Ukulu ndi utali ungaonedwe molakwa mosavuta.

Kulinso kosavuta kwa achikulire kulingalira molakwa ukulu wa kupsinjika maganizo kwa mwana. ‘Mavuto a ana ngaang’ono kwambiri,’ ena amaganiza motero. Koma ganizo limeneli nlolakwa. “Achikulire sayenera kupima mavuto ndi msinkhu,” likuchenjeza motero buku lakuti Childstress! “koma ndi ukulu wa kupweteka kumeme amakuchititsa.”

M’zochitika zambiri mavuto a mwana amakhala aakulu koposa mmene achikulire amawalingalirira. Zimenezi zinatsimikiziridwa ndi kupenda kumene makolo anafunsidwa kuyerekezera mkhalidwe wamaganizo wa ana awo. Pafupifupi onse anayankha kuti ana awo anali “achimwemwe kwambiri.” Komabe, pamene anawo anafunsidwa ali okha popanda makolo awo, ambiri a iwo anati ali “osakondwa” ndipo “osautsikadi.” Ana amayang’anizana ndi mantha amene makolo amaderera kwambiri.

M’kupenda kwina, kochitidwa ndi Dr. Kaoru Yamamoto, gulu la ana linapatsidwa zinthu zowavuta m’moyo zokwanira 20, ndi kuwapempha kuziika pamuyeso wosonyeza ukulu wa kupsinjika. Ndiyeno gulu la achikulire linaika zovuta zofananazo m’malo pa muyesowo malinga ndi mmene anaganizira kuti mwana akaziikira izo. Achikulirewo anaphonya pa zinthu 16 mwa 20 zimenezo! “Tonse timaganiza kuti timadziŵa ana athu,” akumaliza motero Dr. Yamamoto, “koma kaŵirikaŵiri sitimaonadi kapena kumva, ngakhale kuzindikira, chenicheni chimene chikuwavutitsa.”

Makolo ayenera kuphunzira kuona zochitika za moyo mwalingaliro latsopano: kuonera m’maso a mwana. (Onani bokosi.) Zimenezi nzofunika kwambiri makamaka lerolino. Baibulo lidaneneratu kuti “m’masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zovutitsa za kupsinjika kwakukulu . . . zovuta kuchita nazo ndipo zovuta kupirira.” (2 Timoteo 3:1, The Amplified Bible) Ana sali osayambukiridwa ndi kupsinjika koteroko; kaŵirikaŵiri, amakhala mikhole yake yaikulu. Pamene kuli kwakuti zipsinjo zina za ana zili chabe “zilakolako zaunyamata,” zina nzachilendo kwambiri ndipo zimafunikira chisamaliro chapadera.—2 Timoteo 2:22.

[Bokosi patsamba 22]

Kuonera m’Maso a Mwana

Imfa ya Kholo = Liŵongo. Pokumbukira mkwiyo umene panthaŵi zina anakhala nawo kwa kholo lake, mwana angakhale ndi malingaliro akudzimva kukhala wochititsa imfayo.

Chisudzulo = Kukanidwa. Nzeru ya mwana imamuuza kuti ngati makolo angaleke kukondana, angalekenso kumkonda iye.

Uchidakwa = Nkhaŵa. Claudia Black analemba kuti: “Mkhalidwe wa masiku onse wa mantha, kudzimva kukhala wotayidwa, wokanidwa, kutekeseka, ndi chiwawa chenicheni kapena kuyambana zokhala m’nyumba yauchidakwa umakhala wosautsa kwambiri.”

Kumenyana kwa Makolo = Mantha. Kupenda kwina kwa ophunzira 24 kunasonyeza kuti kumenyana kwa makolo kumakhala kopsinja maganizo kwakuti kumachititsa kusanza, kuyabwa kunkhope, kuthothoka tsitsi, kuwonda kapena kunenepetsa, ndipo ngakhale zilonda za m’mimba.

Kufuna Chipambano Konkitsa = Kulefulidwa. “Pamene ana abwerako,” akulemba motero Mary Susan Miller, “amaoneka ngati kuti akuthamanga kuti apulumutse miyoyo yawo m’makani oikiridwa ndi achikulire.” Poumirizidwa kuti akhale wopambana kusukulu, panyumba, ndipo ngakhale pamaseŵera, mwanayo samapambana konse, ndipo makaniwo samatha konse.

Mwana Wobadwa = Kutaikiridwa. Tsopano popeza kuti padzakhala kugaŵana chisamaliro ndi chikondi cha kholo, mwana angaone kuti wataikiridwa kholo m’malo mokondwera kuti wapeza mng’ono wake.

Sukulu = Nkhaŵa ya Kulekanitsidwa. Kwa Amy, kusiya amake ndi kupita kusukulu kunali ngati kufa pang’ono.

Zophophonya = Kuchititsidwa Manyazi. Ndi kudzilingalira kwawo kotekeseka, ana “amakulitsa zinthu,” akutero Dr. Ann Epstein. Iye anapeza kuti kuchititsidwa manyazi kunali chimodzi cha zochititsa kwambiri ana kudzipha.

Kupunduka = Kukwiyitsidwa. Kusiyapo kusekedwa ndi anzake opanda chifundo, mwana wopunduka mwakuthupi kapena mwamaganizo angakhale akuvutika ndi kusaleza mtima kwa aphunzitsi ndi ziŵalo za banja amene amasonyeza kugwiritsidwa mwala chifukwa cha zinthu zimene mwanayo satha kuchita.

[Chithunzi patsamba 21]

Chipewa cha mtundu wachikale

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena