Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 9/8 tsamba 31
  • “Kutengapo Phunziro la Kulolera”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kutengapo Phunziro la Kulolera”
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Kuteteza Ufulu—Motani?
    Galamukani!—1999
  • Kulolera Kuchita Mopambanitsa Mbali Zonse Ziŵiri
    Galamukani!—1997
  • Kukhala Ololera
    Galamukani!—2015
  • Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Ololera
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 9/8 tsamba 31

“Kutengapo Phunziro la Kulolera”

PAMENE tikuyandikira mapeto a zaka za zana la 20, kodi anthu onse atengapo maphunziro alionse pa mbiri yake yachiwawa chiyambire 1914? Federico Mayor, mtsogoleri wamkulu wa bungwe la UNESCO (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization), ananeneratu zowona za mtsogolo pamene analemba nkhani ya mu The Unesco Courier. “Dziko limene tsoka lake likuonekeratu . . . silimapatsa chisangalalo cha mtima wonse. Kusunga mwambo kwachipembedzo, tsankho la mtundu, chidani cha fuko kapena miyambo, kuda Ayuda: mphepo za ufulu zakolezanso moto wa udani. . . . Kunyonyotsoka kwa makhalidwe akale kwatsegulira mpata mtundu uliwonse wa njira zatsopano zochitira zinthu, zina za izo zachipolowe ndithu—ndipo chiwawa chikufalikira popanda choletsa chilichonse.”

Kodi nchifukwa ninji chiwawa chikufalikira? Nchifukwa ninji anthu amada ndi kupha anzawo kokha chifukwa cha kusiyana kwa zipembedzo kapena miyambo yawo? Kaya kukhale kudziko limene kale linali Yugoslavia, India, Northern Ireland, United States, kapena kwina kulikonse m’dziko, chimodzi cha zochititsa zazikulu chikuoneka kukhala maphunziro olakwika. Mmalo mophunzira kulolerana ndi kulemekezana, anthu aphunzira kusakhulupirirana ndi chidani kwa makolo awo, m’sukulu zawo, ndi chitaganya chonse.

Federico Mayor anapitiriza kuti: “Tiyeni tisiye kulolera konyenga kumene kumatilola kulolera zosaloleka—umphaŵi, njala ndi kuvutika kwa anthu mamiliyoni ambiri. Tikatero, tidzapeza chimwemwe chochokera m’chifundo ndi ubale.” Mawu ameneŵa ngabwino kwambiri. Koma kodi ndinjira yogwira ntchito yotani imene ilipo imene ingasinthe mzimu waudani wokuta dziko lathu lolingaliridwa kukhala lopita patsogolo?

Zaka zoposa 2,500 zapitazo, Yesaya analemba mawu awa a Yehova: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Popeza kuti “Mulungu ndiye chikondi,” awo amene amakhaladi ndi moyo mogwirizana ndi malamulo ake a mkhalidwe adzaphunzira mtendere, osati nkhondo; chikondi, osati chidani; kulolera, osati kusalolera.—1 Yohane 4:8.

Kodi ndani amene akuchilikiza chiphunzitso chimenechi chotsogolera anthu kumtendere ndi chikondi ndi kulolera? Kodi ndani amene akukhala muumodzi mosasamala kanthu za mtundu wawo? Kodi ndani alandira maphunziro a Baibulo amene asintha mkhalidwe wawo wa maganizo kuchoka pa chidani kukhala chikondi? Tikukulimbikitsani kupenda ziphunzitso ndi ntchito za Mboni za Yehova kuti mupeze chifukwa chimene izo ziliridi ndi umodzi wa padziko lonse.—Yohane 13:34, 35; 1 Akorinto 13:4-8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena