Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 10/8 tsamba 16-18
  • Kodi Ndikukula Bwino Lomwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndikukula Bwino Lomwe?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zopweteka Pomakula
  • Ochedwa Kusinkhuka
  • Zimene Mungachite
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndikukula Mofulumira Kwambiri?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Nchiyani Chikuchitika ku Thupi Langa?
    Galamukani!—1990
  • ‘Kodi Chikuchitika N’chiyani M’thupi Mwangamu?’
    Galamukani!—2004
  • Zimene Zingakuthandizeni Mukatha Msinkhu
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 10/8 tsamba 16-18

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndikukula Bwino Lomwe?

“Ndinali mmodzi wa ana aang’ono kwambiri m’kalasi lathu—ndipo ndinali wowonda kuposa onse. Sindinakonde mikono yanga. Ndinalingalira kuti inali yowonda kwambiri. Ndinalemba ngakhale kalata yofunsira maseŵera odzinzanitsa thupi olengezedwa kuchikuto kwa buku la nkhani zoseketsa. Komabe maseŵerawo sanathandize.”—Eric.

“Sindili wamtali mokwanira. Ndili ndi zaka 13, koma ndili ndi msinkhu wa [masentimita 150] okha. Aliyense m’kalasi langa amandipitirira! Eya, alipo anyamata ofupikirapo, koma mwinamwake iwo adzatalika m’chilimwe. Sindimafuna mpang’ono ponse kukhala kanjipiti! Sindimaona chilichonse! Ndikulakalaka kuti ndikanatalika tsopano lino.”—Kerri.

KUTALIKITSA! Ukanjipiti! Kunenepetsa! Kuwondetsa! Ameneŵa sali kokha mawu amene mabwenzi ankhanza amatonzera nawo anzawo. Achichepere ambiri amadziona mwanjira imeneyo nthaŵi zonse atayang’ana pakalilore. “Pamene ndinali ndi zaka 13,” akukumbukira motero mkazi wina wowonda wa fuko la Hispanic wotchedwa Mari, “ndinanyansidwa kwambiri ndi mphuno yanga; inali yaikulu kwambiri kwakuti ndinalingalira za kupita ku opaleshoni! Ndipo ndinali ndi chithupi chosaoneka bwino chobulungika! Mkulu wanga anali ndi delesi limene linaoneka bwino pathupi lake loumbika bwino. Koma, pamene ine ndinalivala, aliyense anali kuseka.”

Pamene muli mu “unamwali,” makamaka m’nyengo yakusinkhuka pamene pamakhala kusintha kofulumira m’thupi ndi maganizo, nkwapafupi kudzilingalira moipa. (1 Akorinto 7:36) Malinga ndi zimene mukuona, ausinkhu wanu akusinkhuka kukhala achikulire okongola. Koma kungaonekere ngati kuti inuyo simukukula konse—kapena kuti mukusinkhuka kwambiri. Kupenda kwina kunasonyeza kuti chiŵerengero chachikulu cha 56 peresenti cha azaka 13 mpaka 19 sali okhutiritsidwa ndi matupi awo. Ofufuza ena Jane Norman ndi Myron W. Harris akunena kuti ambiri a achichepere osakhutiritsidwawo analingalira kuti anali “akanjipiti” kapena kuti anali “opinimbira.”

Achichepere ambiri alinso odera nkhaŵa ndi kakulidwe ka ziŵalo za matupi awo; iwo akukayikira ngati ziŵalozo zili bwino lomwe. Buku lakuti Growing Into Love, lolembedwa ndi Kathryn Watterson Burkhart likunena kuti, mwa achichepere “malingaliro a kudziona kukhala wofunika, kukhoza zinthu bwino ndi ulemu waumwini amazikidwa kwambiri m’matupi awo, motero kumakhala kofunika kwambiri kuti matupi awo akule mwanjira yoyenera.” Chifukwa chake, mposadabwitsa kuti achichepere kaŵirikaŵiri amakhala akuda nkhaŵa m’mikhalidwe (yonga ngati paphunziro la P.E. kusukulu) pamene matupi awo angaonedwe—kapena kuyerekezeredwa. “Ndimachita manyazi kwambiri kusamba pamodzi ndi anyamata kusukulu,” anaulula motero mnyamata wina.

Kodi mumaipidwa ndi mmene thupi lanu likukulira? Eya, musade nkhaŵa! Mwachionekere inu muli bwino lomwe.

Zopweteka Pomakula

Unamwali uli chochitika chachibadwa ndi choyenera. Ngakhale Yesu Kristu anakhalapo namwali, ‘akumakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu.’ (Luka 2:52) Unamwali umaloŵetsamo kukhwima kwa ziŵalo zanu zobalira.a Komabe, umaloŵetsamonso kusintha kwa kukula kofulumira kwambiri, kaŵirikaŵiri kuŵirikiza kaŵiri mlingo wa munthu wakukula kwake kwa pachaka. “Ndinayamba kukula [masentimita khumi] pachaka,” akukumbukira motero mnyamata wina wotchedwa Danny. “Pofika zaka 13 ndinafikira msinkhu wa [masentimita 180].”

Komabe, kaŵirikaŵiri atsikana amayamba kukula mofulumirako pafupifupi zaka ziŵiri anyamata asanayambe. Chotero pausinkhu wa zaka 12, mtsikana angatalike kupitirira anyamata a m’kalasi lake. Mwachionekere iye adzangosangalala ndi utali umenewu kwa nthaŵi yaifupi chabe. M’zaka zingapo zotsatirapo, anyamata ambiri amatalika ndi kumpitirira.

Ngakhale ndichoncho, kukula kofulumira kuli ndi mavuto ake. Kaŵirikaŵiri, ziŵalo zimene zimayamba kukula ndizo mapazi anu. Ndiyeno, kwakanthaŵi, mapazi anu angakhale aakulu kwambiri mosayenerera ukulu wa thupi lanu. Wolemba nkhani Lynda Madaras anagwira mawu mtsikana wina amene anati: “Ndinali kupitirira pang’ono [pamasentimita 150] pamene ndinali ndi zaka khumi ndi chimodzi, koma ndinkavala nsapato za saizi 6. Ndinada nkhaŵa kuti ngati mapazi anga akapitiriza kukula, akakhala ngati achimphona! Tsopano ndili ndi zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, ndipo ndine wamtali [masentimita 170], koma ndikuvalabe saizi 6.” Ndiyeno posapita nthaŵi, miyendo yanu, ntchafu, ndi thupi nazonso zimakula mofulumira.

Chovutitsa maganizo kwambiri chingakhale kusintha kwa chithunzi chanu m’kalirole. Wolemba nkhani Lynda Madaras akufotokoza m’buku lake lakuti The What’s Happening to My Body? Book for Girls kuti: “Pamene mukupyola muunamwali, nkhope yanu imasintha. Mbali yapansi ya nkhope yanu imatalika ndipo nkhope yanu imayamba kubulungika.” Zimenezi zimachitika kwa atsikana ndi anyamata omwe. Pangapitepo kanthaŵi kuti nkhope yanu iumbike bwino lomwe.

Chifukwa chakuti ziŵalo zosiyanasiyana za thupi lanu zimakula mosiyanasiyana, mikono ndi miyendo yanu ingaonekerenso kukhala yaitali momvetsa manyazi. “Mikono yanga inaonekera ngati kuti idzafika pansi,” akukumbukira motero Christine, amene pambuyo pake anakula nakhala mkazi wokongola. Nyengo yakusaoneka bwino kwa thupi kumene kaŵirikaŵiri kumamvetsa manyazi ingakhaleponso thupi lanu lisanaonekere kukhala “lokoŵanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse.”—Aefeso 4:16.

Ochedwa Kusinkhuka

Komabe, unamwali ungakhale chinthu chodabwitsa. Nthaŵi zina wazaka 12 zakubadwa angaonedwe molakwa kukhala wazaka 20. Koma kwa achichepere ena, mahomoni okulitsa thupi samayamba kugwira ntchito mwamsanga. Wachichepere wina wotchedwa Willie akudandaula kuti: “Ndine mmodzi wa akanjipiti m’kalasi lathu, ndipo ndidziŵa mmene zimapwetekera ngati ena akuseka.” Ngati muona kuti mumachita kunyanyamphira kuti mulingane msinkhu ndi ausinkhu wanu, musade nkhaŵa. Kaŵirikaŵiri, zimangotanthauza kuti thupi lanu likukula pang’onopang’ono kusiyana ndi anzanu a m’kalasi.b

Ndithudi, kukhala kanjipiti kapena kuoneka wamng’ono kuposa ausinkhu wanu kungakhale kosakondweretsa. “Ndidziŵa kuti ndimaoneka ngati kamwana, ndipo zimandinyansa kwambiri!” akudandaula motero Allison wazaka 16. Kodi mungathe kufulumizitsa kukula kwanu? Ayi, koma mukhoza kukumvetsetsa. Pa Yobu 8:11, Baibulo limati: “ [Kodi] gumbwa aphuka popanda chinyontho? [Kodi] manchedza amera popanda madzi?” Monga momwe mbewu imakulira panthaka yabwino ndi yachonde, momwemonso mufunikira kupuma kokwanira ndi chakudya choyenera. Kudya nthaŵi zonse chakudya chosapatsa thanzi kudzalepheretsa thupi lanu kupeza zakudya zimene limafunikira kuti likule bwino.

Kusiyapo kusamalira thanzi kodziŵika bwino lomwe, palibe zimene inuyo mungachite kwenikweni pakakulidwe ka thupi lanu. Koma m’kupita kwanthaŵi thupi lanu lidzayamba kukula mofulumira. Kwenikweni, inu mungapitirize kukula pambuyo pakuti ausinkhu wanu afika pamsinkhu wawo wokwanira. “Pamene ndinali m’giredi 8,” akukumbukira motero mwamuna wachichepere wotchedwa John, “ndinali wachiŵiri m’kufupika m’kalasi lathu, koma m’chilimwe, ndinasinkhuka. Pamene ndinali kuyamba giredi 9, ndinali pafupifupi wamtali koposa onse m’kalasi.” Timakumbutsidwa za mwambi wakale wakuti: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.”—Miyambo 13:12.

Ndithudi, palibe chitsimikiziro chakuti nthaŵi zonse mudzakhala wamtali ngati woseŵera basketball wa ku America. Ngati muli ndi makolo aafupi, mwachionekere nanunso mudzakhala wamfupi. Komabe, kukhala wamfupi pa anzanu kungapangitse mavuto kwa inu.

Zimene Mungachite

Pamene kuli kwakuti Mulungu samaweruza munthu mwa maonekedwe ake, anthu ochepa maganizo nzimene amachita kaŵirikaŵiri. Kufufuza kumasonyeza kuti achichepere kaŵirikaŵiri amaona awo amene amakula pang’onopang’ono kukhala osakongola ndi osakhoza kuchita bwino zinthu kuposa achichepere osinkhukirapo ooneka bwino. Iwo angakane ngakhale mabwenzi awo akale kukhala osawayenera chifukwa chakuti amaoneka kukhala achichepere. Zimenezi zingadodometse kwambiri ulemu wanu waumwini. Kupenda kwina kunasonyeza kuti pambuyo pakuti achichepere ochedwa kusinkhuka akula ndi kulingana ndi anzawo a m’kalasi, malingaliro akudziona kukhala osakwanira amakhalapobe kwa nthawi yaitali.

Kodi mungachitenji? Achichepere ena amene amasinkhuka mochedwa amakhala chete ndi osayanjana ndi ena. Komabe ena—makamaka anyamata—amakhala odzitama kapena odzitukumula opanda mantha poyesayesa molakwa kuti adziŵike. Koma njira zonse ziŵirizi sizidzakupezerani mabwenzi enieni. M’kupita kwanthaŵi, anthu adzakukondani chifukwa cha amene muli, osati chifukwa cha maonekedwe anu. Ngati musonyeza chikondwerero chenicheni kwa ena ndi kukulitsa kukoma mtima ndi mtima wopatsa, anthu ambiri adzakukondani. (Miyambo 11:25; Afilipi 2:4) Ngati ena apitiriza kukusekani kapena kukunyalanyazani, yesani kukambitsirana nkhaniyo ndi makolo anu. Iwo angakhale ndi malingaliro othandiza amene angakupatseni.

Kumbukiraninso kuti Mulungu “ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Baibulo limanena kuti Mfumu Sauli anali mmodzi wa amuna aatali kwambiri ndi okongola koposa mu Israyeli. Koma iye analephera ponse paŵiri kukhala mfumu yabwino ndi mwamuna wanzeru. (1 Samueli 9:2) Kumbali ina, mwamuna wotchedwa Zakeyu anali “wamfupi msinkhu.” Komabe iye anadalitsidwa ndi mwaŵi wakusonyeza kuwoloŵa manja kwake kwa Mwana wa Mulungu. (Luka 19:2-5) Motero zimene munthuyo ali mkati mwake nzimene zilidi nkanthu. Ndipo ngati thupi lanu silikukula mofulumira monga momwe mungafunire, simuyenera kuda nkhaŵa podziŵa kuti zimenezo zili bwino lomwe. “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake,” ndipo potsirizira pake thupi lanu lidzafika paunamwali. (Mlaliki 3:1) Modabwitsa, achichepere ambiri amadandaula kuti matupi awo akukula mofulumira kwambiri. Vuto lawolo nlimene tidzakambitsirana m’nkhani yotsatirayo.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani zakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . .” zopezeka m’kope la Galamukani! la February 8, 1990.

b Akatswiri ena amapereka lingaliro lakuti ngati wachichepere sanakhalepo ndi masinthidwe alionse apaunamwali pofika zaka 15, ayenera kupimidwa ndi dokotala kotero kuti atsimikizire kuti palibe matenda aakulu alionse amene alipo.

[Chithunzi patsamba 18]

Kaŵirikaŵiri atsikana amayamba kukula mofulumirako pafupifupi zaka ziŵiri anyamata asanayambe. Komabe, anyamata ambiri amawapeza ndipo potsirizira pake amatalika ndi kupitirira atsikana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena