Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 12/8 tsamba 8-10
  • Dziko Lopanda Matenda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lopanda Matenda
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero a Nthenda
  • Mankhwala Enieni
  • Kuchiritsa Kosatha Kuli Pafupi
    Galamukani!—1987
  • Mmene Kulumala Konse Kudzathere
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Moyo Wopanda Zoŵaŵitsa Uli Pafupi!
    Galamukani!—1994
  • Zimene “Mulungu Woona Yekha” Walonjeza
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 12/8 tsamba 8-10

Dziko Lopanda Matenda

“Nthenda ya malungo njochenjera kuposa momwe munthu aliyense angayerekezere,” akutero katswiri wa katemera Dr. Dan Gordon. “Tikuyesayesabe kupeza mankhwala ake.”

“SITIKUDZIŴABE zambiri ponena za mmene [kachilombo ka kholodzi] kamagwirira ntchito,” akutero Barry Bloom wa ku Howard Hughes Medical Institute. “Sitimadziŵa mokwanira mmene mankhwala alionse amagwirira ntchito. Sitikudziŵa bwino.”

“Kwenikweni chidziŵitso sichimachititsa kusintha kwa mkhalidwe,” akudandaula motero mneneri wa Centers for Disease Control, powona kulephera kwa mikupiti ya “kugonana kotetezereka” yochepetsa chindoko. Monga momwe mawuwo akusonyezera, nkhondo zolimbana ndi malungo, kholodzi, ndi chindoko zakhala zogwiritsa mwala. Kodi mtsogolomu mudzakhala mankhwala abwino kwambiri a nthenda zimenezi?

Mwinamwake zingatero. Koma pamene kuli kwakuti anthu angagonjetse matenda ena ndi kuchititsa ena kukhala opiririka, pali chifukwa chachikulu chimene sangapambanire kotheratu nkhondo yolimbana ndi matenda.

Magwero a Nthenda

Nkhondo yolimbana ndi nthenda siili chabe nkhondo yolimbana ndi tizilombo. Baibulo limafotokoza kuti matenda ndiwo chotulukapo cha choloŵa cha uchimo chochokera kwa atate wathu woyamba waumunthu. (Aroma 5:12) Uchimo sunangowononga unansi wa munthu ndi Mlengi wake komanso unamchititsa kunyonyosoka mwamaganizo, mwamalingaliro, ndi mwakuthupi. Motero, mmalo mwa kupitirizabe kukhala muungwiro m’paradaiso wa padziko lapansi, anthu anakhala opanda ungwiro ndipo anayamba kunyonyosoka kufikira imfa inawapeza.—Genesis 3:17-19.

Ngakhale patakhala mankhwala abwino koposa, munthu sangasinthe mkhalidwe wake wauchimo kapena zotulukapo zake. Vuto limeneli ‘lagonjetsa [mtundu wa anthu] kuutsiru [“kukupereŵera kwambiri,” Phillips].’ (Aroma 8:20) Ndipo zimenezi nzowona ponena za kugonjetsa nthenda. Kupita patsogolo kwa kupulumutsa moyo kumbali ya mankhwala kaŵirikaŵiri kumafooketsedwa ndi kunyonyosoka kwa chitaganya kowopseza moyo.

“Tili ndi vuto,” akulemba motero Jerold M. Lowenstein m’magazini otchedwa Discover. “Pamene tipeza chipambano pomenyana ndi nthenda ndi kutalikitsa moyo wa munthu, mpamenenso kuthekera kwa kusolotsedwa kwathu kumafulumira” chifukwa cha kuchuluka kwa anthu ndi kusasamala malo okhala.

Mankhwala Enieni

Mankhwala enieni a nthenda sali kwa munthu koma ali kwa Mlengi. Nchifukwa chake wamasalmo analengeza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Baibulo limanenanso kuti: “Wodala munthu amene . . . chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake; amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 146:3, 5, 6) Mulungu yekha ndiye amene ali ndi mphamvu ya kuchotsa matenda kuyambira pamagwero pake. Ndipo malinga nkunena kwa Baibulo, iye walinganiza kuchita motero. Nthaŵi imeneyo ikuyandikira.

Yesu Kristu ananeneratu kuti “miliri” ikakhala umodzi wa maumboni akuti tikukhala kumapeto a dongosolo la zinthu lilipoli ndipo pafupi ndi kudza kwa dziko latsopano. Iye ananeneratunso za kuwonjezereka kwa mikhalidwe yeniyeniyo imene imachirikiza kukhalapo kwa nthenda, monga ngati nkhondo, njala, ndi kusayeruzika.—Luka 21:11; Mateyu 24:3, 7, 12; 2 Timoteo 3:1-5, 13.

Pamene anali padziko lapansi, Yesu anachiritsa anthu odwala mozizwitsa, motero akumayamba kukwaniritsa ulosi wakuti: “Ananyamula zoŵaŵa zathu, ndi kusenza zisoni zathu.” (Yesaya 53:4; Mateyu 8:17) Motero iye anasonyeza pamlingo waung’ono zimene Mulungu walinganiza kuchita posachedwa pamlingo wa dziko lonse. Baibulo, ponena za Yesu limati: “Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya.”—Mateyu 15:30, 31.

Anthu amene anapenyerera zozizwitsa zimenezo analemekeza Mulungu chifukwa chakuti anazindikira kuti anali iyeyo amene anapatsa Yesu mphamvu ya kuchita zozizwitsa zimenezo. Mphamvu imene Yesu anagwiritsira ntchito inali mphamvu imodzimodziyo imene inagwiritsiridwa ntchito polenga chilengedwe chathu chochititsa manthachi. Inali mzimu woyera wa Mulungu, mphamvu yake yogwira ntchito.—Genesis 1:1, 2; Chivumbulutso 4:11.

Mneneri Yesaya analemba za nthaŵi pamene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndipo pa Chivumbulutso 21:4, 5 pamalengeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.”

Baibulo limasonyeza kuti tikukhala ndi moyo m’nthaŵi ya kusintha kwa zinthu. (1 Yohane 2:15-17) Posachedwapa dzikoli, limodzi ndi matenda ake, chisoni, upandu, chiwawa, ndi imfa, zidzakhala zinthu zakale. Mulungu adzalichotsa limodzi ndi masoka ake, akumalambulira njira dziko latsopano padziko lapansi pano, mmene ‘mudzakhala chilungamo.’ (2 Petro 3:11-13) Yesu anafotokoza za dziko latsopano limenelo limene likudza kukhala “Paradaiso,” popeza kuti lidzafanana ndi munda wa Edene wa Paradaiso woyamba, koma wokuta dziko lonse lapansi.—Luka 23:43; Genesis 2:7, 8.

Motero Akristu ali ndi chiyembekezo, osati cha kungochiritsidwa kwakanthaŵi chabe, koma kumasulidwa kukupanda ungwiro, matenda, ndi imfa kwachikhalire. Amayembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kotheratu kwa lonjezo la Mulungu lakuti: “Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.” “Ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.”—Eksodo 15:26; 23:25.

[Zithunzi patsamba 9]

Yesu anapatsidwa mphamvu ndi Mulungu ya kuukitsa akufa ndi kuchiritsa odwala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena