Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 1/8 tsamba 30-32
  • Moyo Wapaŵiri Kodi Ndani Ayenera Kudziŵa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wapaŵiri Kodi Ndani Ayenera Kudziŵa?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulingalira Kolakwa
  • Palibe Chobisika
  • Mmene Yehova Amamvera
  • Makolo Ovulazidwa Maganizo
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingasiye Motani Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri?
    Galamukani!—1994
  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?
    Galamukani!—1994
  • Achichepere Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 1/8 tsamba 30-32

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Moyo Wapaŵiri Kodi Ndani Ayenera Kudziŵa?

“Amayi ndi Atate anali kunditengera kumisonkhano Yachikristu, ndipo ndinadziŵa chabwino ndi choipa,” akuvomereza motero Robert. “Koma ndinafuna kukondedwa ndi kuvomerezedwa ndi ana ena kusukulu. Chotero kuti ndigwirizane ndi ena ndi kukhala wodziŵika, ndinayamba kusuta fodya m’giredi lachisanu ndi chimodzi. M’giredi lachisanu ndi chiŵiri, ndinayamba kugwiritsira ntchito LSD ndi kusuta chamba. M’giredi lachisanu ndi chitatu, ndinayamba kudzibaya jekiseni wa mankhwala oledzeretsa otchedwa speed. Ndinanyenga aliyense—komatu ndinali wovutika maganizo.”

ACHICHEPERE ambiri lerolino—kuphatikizapo ena oleredwa ndi makolo Achikristu—amakhala ndi moyo wapaŵiri. Sikuti onse amakhala ogwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa, monga momwe anachitira Robert. Koma popanda kudziŵa kwa makolo awo, achichepere ena amayenda ndi atsikana kapena anyamata mobisa, kumwa moŵa, kuvala zovala zachilendo, kumvetsera nyimbo zachiwawa, kukhala pamapwando aphokoso, ndi kuloŵa m’zochitika zambirimbiri zimene zimatsutsidwa kapena kuletsedwa ndi makolo awo. Kodi mukutsatira njira ya moyo yotero inumwini?

Ngati zili choncho, mwinamwake mumadziŵa kuti zimene mukuchita nzoipa. Monga Robert, mungavutikedi ndi chikumbumtima chaliŵongo. (Aroma 2:15) Chikhalirechobe, lingaliro la kuvumbula zolakwa zanu kwa makolo siliri lokondweretsa. Ndipo pamene mulingalira zimene zingakhale zotulukapo zake, lingaliro lakuti ‘Zimene makolo anga sadziŵa sizingawavulaze maganizo’ lingaonekere kukhala lanzeru. Komatu likhoza kuvulaza inuyo.

Kulingalira Kolakwa

Mwachitsanzo, mungalingalire kuti muli ndi zifukwa zoyenera zodandaulira ponena za njira imene makolo anu amachitira zinthu. Mwinamwake nzoyeneradi. Komabe ngakhale ngati iwo ali oletsa mosayenera panthaŵi zina, osalankhulika, kapena otsendereza, kodi zimenezo zimalungamitsa kupitirizabe kusawamvera? Osati mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, amene amalangiza kuti: “Mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) Ndipo bwanji ngati mulingalira kuti muli ndi chifukwa choyenera chokwiyira makolo anu? Kodi nkwanzeru kusonyeza mkwiyo wanuwo mwa kuswa mobisa miyezo yoperekedwa ndi Mulungu? Kwenikweni, inu mudzakhala mukuchita monga ngati kuti ‘mukukwiyira Yehova.’ (Miyambo 19:3, NW) Chinthu chabwino kuchita chingakhale kufikira makolo anu ndi kukambitsirana nawo mofatsa madandaulo anu alionse amene muli nawo.—Miyambo 15:22.

Chinthu china cholakwanso ndicho kukhulupirira kuti mwa kusalankhula mumatetezera makolo anu kuti asakwiye. Mnyamata wina wazaka 16 anati: “Sindinkalankhula kanthu kalikonse kamene kakanagwiritsa mwala [makolo anga].” Kachiŵirinso, kalingaliridwe kochenjera kotero ndiko kungodzinyenga basi. Monga momwe Baibulo limanenera, munthu “adzidyoletsa yekha m’kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.” (Salmo 36:2) Pamene musamaladi za malingaliro a makolo anu, mumapeŵa kusamvera pachiyambi pomwe. Ndiponso, kuyesayesa kulikonse kuwabisira mwinamwake kudzakhaladi kopanda pake, pakuti mosakayikira ena akudziŵa kale za moyo wanu wamtseri.

Palibe Chobisika

Aisrayeli akale anadziŵa zimenezi pamene anayesa kuzemba chilango pa kuchita cholakwa chobisika. Mneneri Yesaya anachenjeza kuti: “Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wawo, ndi ntchito zawo zili mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziŵa ife?” (Yesaya 29:15) Aisrayeli anaiŵala kuti Mulungu anaona ntchito zawo zoipa. M’kupita kwanthaŵi, anawaimba mlandu wa zolakwa zawo.

Zimenezi zinali chonchonso kwa Akristu a mpingo wa m’zaka za zana loyamba. Dziŵerengereni pa Machitidwe 5:1-11, za chochitika cha Hananiya ndi mkazi wake, Safira. Pamene thumba la ndalama lapadera linakhazikitsidwa kusamalira Akristu osoŵa, Hananiya anagulitsa munda nanena mwamphamvu kuti adzapereka ndalama zake zonse. Komabe, m’chenicheni, Hananiya ‘anapatula pa mtengo wake’ kaamba ka phindu lake. Kodi Mulungu ananamizidwa ndi kuwoloŵa manja konyengezera kumeneku? Kutalitali. Mtumwi Petro anati: “Sunanyenga anthu, komatu Mulungu. Koma Hananiya pakumva mawu awa anagwa pansi namwalira.” Safira, amene anali pamodzi naye, anakanthidwa mwamsanga pambuyo pake. Mwachionekere aŵiriwo anaiŵala kuti Mulungu “adziŵa zinsinsi za mtima.”—Salmo 44:21.

Mofananamo lerolino, ngakhale ngati mwachipambano mukubisira makolo anu khalidwe loipa, inu simungabisire Yehova Mulungu amene amayang’anitsitsa khalidwe loipalo. “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake,” pamatero pa Ahebri 4:13, “koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.” Kodi mungakhale pambalambanda kuposa pamenepo? Ndipo m’kupita kwanthaŵi machimo anu obisikawo adzavumbulidwa kwa enanso. Miyambo 20:11 imati: “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” Mwambi wina umati: “Wobisa machimo ake sadzaona mwaŵi.”—Miyambo 28:13.

Msungwana wina wotchedwa Tammy anadziŵa zimenezi pamene anali wachichepere. Ngakhale kuti analeredwa ndi makolo Achikristu, iye anayamba kusuta fodya, kumwa, ndi kuyenda ndi anyamata osakhulupirira. Tammy anayesayesa mwamphamvu kubisa zochitachita zake zoipazo, koma akukumbukira kuti: “Makolo anga anaona kusintha kwanga. Ndinakhala wopanduka ndipo ndinakulitsa mkhalidwe wamaganizo odzigangira. Pamene munthu ali ndi moyo wapaŵiri, umakhala wotsimikizirika kudzavumbuluka mwamsanga kapena pambuyo pake. Kwa ine, zinachitika mwamsanga. Atate anandigwira ndili ndi mnyamata wina pasukulu yapafupi.”

Mmene Yehova Amamvera

Chotero, zimene makolo anu sadziŵa zingathe—ndipo mwinamwake zidzatero—kuwavulaza maganizo m’kupita kwanthaŵi. Chinthu chofunika koposa nchakuti, kodi mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi Yehova amamva bwanji ndi awo amene amakhala ndi moyo wabodza?’ Salmo 5:5, 6 limayankha kuti: ‘Yehova amada onse akuchita zopanda pake. Adzawononga iwo akunena bodza: munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.’ Musadzinyenge mwa kuganiza kuti mukhoza kutonthoza Mulungu mwa kungovala mkhalidwe wa kudzipereka pamene mufika pamisonkhano yachipembedzo. Iye amadziŵa pamene anthu ‘amlemekeza ndi milomo yawo, koma mtima wawo ukhala kutali ndi iye.’—Marko 7:6.

Wachichepere wina wotchedwa Ricardo, amene analoŵa m’khalidwe loipa lachisembwere, anaulula kuti: “Munthu samapeza bwino pamene adziŵa kuti wachititsa chisoni Yehova.” Koma kodi kuchititsa chisoni Yehova nkothekadi—ndiko kuti, kumvutitsa mtima? Ndithu nkotheka! Pamene mtundu wakale wa Israyeli unaleka kutsatira Chilamulo cha Mulungu, iwo ‘anapweteketsa mtima Woyerayo wa Israyeli.’ (Salmo 78:41, NW) Iye ayenera kukhala wopwetekedwa mtima chotani nanga lerolino pamene achichepere oleredwera “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW]” achita zinthu zoipa mwachinsinsi!—Aefeso 6:4.

Makolo Ovulazidwa Maganizo

Pamenepo, zindikirani kuti simudzabisala nthaŵi zonse. Muli ndi thayo kwa Mulungu, kwa makolo anu, ndi kwa inumwini kuti munene zowona ndi kuulula zimene mwakhala mukuchita mwachinsinsi. Zowonadi, zimenezi zingachititse manyazi ndipo mwinamwake ngakhale zotulukapo zopweteka. (Ahebri 12:10, 11) Ngati mwakhala mukutsatira njira ya kunama ndi chinyengo, mwawononga chidaliro cha makolo anu mwa inu. Chotero musadabwe ngati akhala okukanizani kwambiri kuposa kale. Tammy akukumbukira kuti: “Pamene ndinapezereredwa ndi bwenzi langa lachinyamatalo, atate anachita mantha. Iwo tsopano anadziŵa kuti sindikanadaliridwa. Zimenezi zinatanthauza kundilonda nthaŵi zonse.” Koma Tammy anazindikira kuti anali kokha kututa zimene anali atafesa.—Agalatiya 6:7.

Mungayembekezerenso makolo anu kukhala ovulazidwa maganizo ndi okwiya. Dzina lawo ndi mbiri zadetsedwa. (Yerekezerani ndi Genesis 34:30.) Ngati atate wanu ali mmodzi wa Mboni za Yehova, iwo mwina angafunikire kutula pansi mathayo awo ena ampingo. (Tito 1:5-7) Inde, monga momwe Miyambo 17:25 imanenera, wachichepere wopanduka angakhale ‘wochititsa atate wake chisoni, namvetsa zoŵaŵa amake wombala.’

Wolemba mabuku Joy P. Gage akufotokoza momvetsa chisoni mmene makolo ena amamvera pamene mwana apanduka. Iye akuti: “Ena amalira kachetechete. Ena amalira mofuula. Ena amalilira mtseri. Amalilira nthaŵi yawo yonse yakaleyo. Amalira chifukwa chakuti palibenso chiyembekezo chamaŵa. Amalilira zimene amayembekezera kuchita. Amalira chifukwa cha zimene motsimikizirika zidzachitika. Amalira chifukwa cha kukwiya. Amalira chifukwa cha kugwiritsidwa mwala.” Zowonadi, sikudzakhala kosavuta kuyang’anizana ndi anthu aŵiriwo amene amakukondani koposa wina aliyense m’dziko amene mwawamvetsa chisoni. Tammy akuti: “Ndimangolakalaka kuti bwenzi sindinamvetse chisoni chachikulu atate ndi amayi.”

Ngakhale zili choncho, simungathe kusintha zimene munachita kalezo. Ndipo popeza kuti mosakayikira zimenezi zidzakhala zopweteka ndi zovuta, inu muli ndi thayo la kuyesayesa kuwongolera zinthu. (Yerekezerani ndi Yesaya 1:18.) Zimenezo zitanthauza kuuza makolo anu chowonadi, kuvomereza kuvutika maganizo kwawo ndi mkwiyo wawo, kulandira chilango chilichonse chimene angapereke. Kunena kwanu chowonadi kungakhale mchitidwe woyamba wobweretsa chisangalalo m’mitima ya makolo anu, ndi mumtima wa Yehova Mulungu, ndiponso kupeza chikhutiro chosangalatsa cha kukhala ndi chikumbumtima chanu choyera.—Miyambo 27:11; 2 Akorinto 4:2.

Koma kodi mungauze motani makolo anu? Kodi mungapeŵe motani kukhala ndi moyo wapaŵiri? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’kope lathu lotsatira.

Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)

[Chithunzi patsamba 31]

Kunena chowonadi kungadzetse mpumulo kwa inu ndi makolo anu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena